-
2 Mbiri 36:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwachenjeza kudzera mwa atumiki ake. Ankawachenjeza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo ndiponso malo ake okhala. 16 Koma iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona,+ kunyoza mawu ake+ ndiponso kuseka aneneri ake.+ Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.+
-
-
Nehemiya 9:33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Inu mwachita zinthu molungama pa zonse zimene zatichitikira. Mwachita zinthu mokhulupirika koma ife ndi amene tachita zinthu zoipa.+
-
-
Danieli 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ifeyo tadzibweretsera manyazi* ngati mmene zilili lero. Manyazi agwira amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kutali, kumayiko onse amene munawabalalitsirako chifukwa choti anakuchitirani zinthu zosakhulupirika.+
-