-
Ezekieli 45:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
45 “‘Mukamagawana dzikoli kuti likhale cholowa chanu,+ mudzatenge malo ena nʼkuwapereka kwa Yehova monga gawo loyera.+ Malowo adzakhale mikono 25,000* mulitali ndi mikono 10,000 mulifupi.+ Malo onsewo* adzakhale gawo loyera. 2 Mkati mwa gawo loyeralo mudzakhale malo ofanana mbali zonse kuti adzakhale malo oyera. Malowa adzakhale mikono 500 mbali zonse*+ ndipo kumbali iliyonse kudzakhale malo odyetserako ziweto okwana mikono 50.+
-