-
Ezekieli 7:15-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Lupanga lidzapha anthu amene ali kunja kwa mzinda+ ndipo mliri ndi njala zidzapha amene ali mkati mwa mzinda. Aliyense amene ali kunja kwa mzinda adzaphedwa ndi lupanga ndipo amene ali mumzinda adzafa ndi njala komanso mliri.+ 16 Anthu awo amene adzapulumuke adzathawira kumapiri ndipo mofanana ndi njiwa zamʼzigwa, aliyense adzalira chifukwa cha zolakwa zake.+ 17 Manja awo onse adzafooka ndipo mawondo awo onse azidzangochucha madzi.*+
-