-
1 Samueli 21:1-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Kenako Davide anafika ku Nobu+ kwa Ahimeleki wansembe. Ahimeleki ataona Davide anayamba kunjenjemera, ndipo anamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani uli wekhawekha?”+ 2 Davide anayankha Ahimeleki wansembe kuti: “Mfumu yandituma kuti ndikachite zinazake ndipo yandiuza kuti, ‘Usauze aliyense zimene ndakutumazi komanso malangizo amene ndakupatsa.’ Ndapangana ndi anyamata anga kuti ndikumane nawo penapake. 3 Ndiye ngati muli ndi mikate 5 kapena chakudya chilichonse mundipatseko.” 4 Koma wansembeyo anayankha Davide kuti: “Palibe mkate wamba, koma pali mkate wopatulika.+ Nditha kukupatsa umenewu ngati anyamatawo ayesetsa kudzisunga osagona ndi akazi.”+ 5 Davide anayankha wansembeyo kuti: “Akazi sanatiyandikire ngati mmene zinalilinso poyamba pamene ndinapita kukamenya nkhondo.+ Anyamatawo amakhala oyera ngakhale pamene tili pa ntchito wamba, ndiye kuli bwanji lero?” 6 Choncho wansembeyo anamupatsa mkate wopatulika,+ chifukwa panalibe mkate wina koma mkate wachionetsero umene anauchotsa pamaso pa Yehova tsiku limenelo kuti aikepo watsopano.
-