March
Lamlungu, March 1
Mumalamulira chilichonse.—1 Mbiri 29:12.
Tikawerenga Genesis chaputala 1 ndi 2 titha kuoneratu kuti Adamu ndi Hava anali ndi ufulu umene anthu amaulakalaka masiku ano. Iwo ankakhala moyo wa mwanaalirenji, sankaopa chilichonse ndipo palibe amene ankawapondereza. Sankadera nkhawa za mavuto monga njala, kusowa ntchito, matenda kapena imfa. (Gen. 1:27-29; 2:8, 9, 15) Koma mfundo imodzi imene tiyenera kuikumbukira pa nkhaniyi ndi yakuti Yehova Mulungu yekha ndi amene ali ndi ufulu wopanda malire. Tikutero chifukwa chakuti iye ndi amene analenga chilichonse ndipo ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. (1 Tim. 1:17; Chiv. 4:11) Choncho tinganene kuti ufulu umene anthu komanso angelo angakhale nawo umakhala ndi malire ake. Onse ayenera kudziwa kuti Yehova ndi woyenera kuwapatsa mfundo zoti aziyendera ndipo mfundo zake ndi zachilungamo, zothandiza komanso zosapanikiza. Ndipo izi n’zimene Yehova anachita ndi anthu oyambirira. w18.04 4 ¶4, 6
Lolemba, March 2
Mapazi a munthu yemwe . . . [akubweretsa] uthenga wabwino, ndi okongola kwabasi!—Yes. 52:7.
M’dziko loipali, Yehova ndi amene amatithandiza kupirira. (2 Akor. 4:7, 8) Ndiye mukuganiza kuti anthu amene sali pa ubwenzi ndi Yehova amapirira bwanji mavuto amene amakumana nawo? Mofanana ndi Yesu, mtima wachifundo umatilimbikitsa kuti tiziwalalikira “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” Choncho tizileza mtima ndi anthu amene timawaphunzitsa. Tizikumbukira kuti anthuwo mwina sanaganizirepo mfundo za m’Baibulo zimene ifeyo timazidziwa bwino. Ndipo ambiri amakonda kwambiri mfundo zimene amakhulupirira. Mwina amaona kuti mfundo zimene amakhulupirirazo zimawathandiza kuti azigwirizana ndi achibale awo, anthu am’dera lawo kapena achikhalidwe chawo. Tisanawauze kuti asiye kukhulupirira mfundo zawo tiyenera kuwathandiza kuti amvetse bwino mfundo zatsopano zimene sakuzidziwa bwino. Akamvetsa zatsopanozo m’pamene angathe kusiya zimene ankakhulupirira poyamba. Ndiye kuti zimenezi zichitike pangadutse nthawi yambiri.—Aroma 12:2. w19.03 23 ¶10, 12; 24 ¶13
Lachiwiri, March 3
Ndimakondwera nawe.—Maliko 1:11.
Zimene Yehova anachita polimbikitsa Mwana wake komanso kusonyeza kuti amamukonda, zikutikumbutsa kuti nafenso tizilimbikitsa anzathu. (Yoh. 5:20) Anthufe timamva bwino kwambiri anthu amene timawakonda akatisonyeza chikondi komanso kuyamikira zabwino zimene tachita. Abale ndi alongo komanso anthu a m’banja lathu amafunanso kuti tiziwakonda komanso kuwalimbikitsa. Tikamayamikira anzathu timawathandiza kuti chikhulupiriro chawo chilimbe komanso azitumikira Yehova mokhulupirika. Makolo makamaka amafunika kulimbikitsa ana awo. Ana amakula bwino akamayamikiridwa ndi makolo awo komanso kusonyezedwa chikondi. Mawu akuti: “Ndimakondwera nawe” anasonyeza kuti Yehova sankakayikira zoti Yesu adzachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Atate ake. Ngati Yehova amakhulupirira Mwana wake chonchi, nafenso sitiyenera kukayikira zoti Yesu adzakwaniritsa zinthu zonse zimene Yehova walonjeza. (2 Akor. 1:20) Kuganizira chitsanzo cha Yesu kungatithandize kuti tizichita zonse zimene tingathe pophunzira za iye komanso kutengera chitsanzo chake. Yehova sakayikiranso kuti anthu ake, monga gulu, adzapitiriza kuphunzira zinthu kwa Mwana wakeyu.—1 Pet. 2:21. w19.03 8 ¶3; 9 ¶5-6
Lachitatu, March 4
Chilamulo cha mzimu umene umapatsa moyo mwa Khristu Yesu chakumasulani ku chilamulo cha uchimo ndi cha imfa.—Aroma 8:2.
Munthu amayamikira kwambiri mphatso imene walandira akazindikira kuti ndi yamtengo wapatali. Aisiraeli sankaona kuti kumasulidwa ku ukapolo ku Iguputo ndi mwayi wamtengo wapatali. Pasanapite miyezi yambiri, anayamba kulakalaka zakudya ndi zakumwa zimene anazisiya ku Iguputo ndipo ankadandaula kuti zinthu zimene Yehova akuwapatsa si zabwino. Anafika mpaka pofuna kubwerera ku Iguputo. Tangoganizani, eti ankaona kuti ‘nsomba, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi’ zinali zabwino kuposa ufulu wolambira umene Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, anawapatsa. M’pake kuti Yehova anakwiya nawo kwambiri. (Num. 11:5, 6, 10; 14:3, 4) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mtumwi Paulo anauza Akhristu onse kuti asamapeputse ufulu umene Yehova watipatsa kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu.—2 Akor. 6:1. w18.04 9-10 ¶6-7
Lachinayi, March 5
Iye amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera. Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.—Sal. 33:5.
Tonsefe timafuna kukondedwa komanso kuchitiridwa zinthu mwachilungamo. Ngati zimenezi sizikuchitika, timayamba kudziona kuti ndife achabechabe ndipo timataya mtima. Yehova amadziwa kuti anthufe timafuna chikondi ndi chilungamo. (Sal. 33:5) Tisamakayikire kuti Yehova amatikonda kwambiri ndipo amafuna kuti tizichitiridwa zinthu mwachilungamo. Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli chimatsimikizira mfundo imeneyi. Tikamaphunzira Chilamulo cha Mose timatha kuzindikira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi kwambiri. (Aroma 13:8-10) Tinganene kuti Mulungu anasonyeza chikondi popereka Chilamulo cha Mose chifukwa chilichonse chimene amachita, amachichita chifukwa cha chikondi. (1 Yoh. 4:8) Malamulo onse amene Mulungu anapereka anachokera pa mfundo ziwiri. Mfundo zake ndi zakuti uzikonda Mulungu komanso uzikonda mnzako. (Lev. 19:18; Deut. 6:5; Mat. 22:36-40) Malamulo oposa 600 amene Mulungu anapereka amasonyeza chikondi chake. w19.02 20-21 ¶1-4
Lachisanu, March 6
Kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.—Mat. 6:21.
Yobu ankasamala pochita zinthu ndi atsikana kapena azimayi. (Yobu 31:1) Iye ankadziwa kuti sayenera kukopana ndi akazi ena. Masiku ano, anthu ambiri m’dzikoli amalimbikitsa chiwerewere. Mofanana ndi Yobu, kodi timakana kukopana ndi munthu amene sitili naye pa banja? Nanga kodi timapewa kuona zithunzi zilizonse zolaula? (Mat. 5:28) Tikamayesetsa kukhala odziletsa pa nkhaniyi tidzakwanitsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika. Yobu ankamveranso Yehova pa nkhani ya chuma. Iye ankaona kuti akamadalira chuma chake, ndiye kuti akuchita cholakwa chofunika kupita nacho kwa oweruza. (Yobu 31:24, 25, 28) Anthu ambiri masiku ano ali ndi mtima wokonda chuma. Koma tikamatsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza mmene tiyenera kuonera ndalama komanso chuma, tidzakhala ofunitsitsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika.—Miy. 30:8, 9; Mat. 6:19, 20. w19.02 6-7 ¶13-14
Loweruka, March 7
Monga Atate wakondera ine, inenso [Ndakukondani] inu, inunso khalanibe m’chikondi changa.—Yoh. 15:9.
Zonse zimene Yesu ankachita zimasonyeza mmene Yehova amatikondera. (1 Yoh. 4:8-10) Yesu analolera kupereka moyo wake m’malo mwa ife chifukwa ali ndi mtima wachikondi kwambiri. Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” timapindula ndi chikondi chimene Yehova ndi Mwana wake anatisonyeza popereka dipo. (Yoh. 10:16; 1 Yoh. 2:2) Zinthu zimene Yesu anagwiritsa ntchito poyambitsa mwambo wa Chikumbutso zimasonyeza kuti iye amakonda kwambiri ophunzira ake. N’chifukwa chiyani tikutero? Yesu anasonyeza chikondi kwa otsatira ake odzozedwa poyambitsa mwambo wosavuta kuti azichita. Mwambowu unali woti ophunzira odzozedwa aziuchita chaka chilichonse ngakhale pamene akukumana ndi mavuto monga kukhala mundende. (Chiv. 2:10) Ndipo ophunzirawo akhala akukwanitsa kuchita zimenezi chaka chilichonse. Akhristu onse akhala akuyesetsa kuti azichita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu mpaka pano. w19.01 24 ¶13-15
Lamlungu, March 8
Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.—Yoh. 8:32.
Munthu akapeza ufulu umenewu, amamasulidwa ku chipembedzo chonyenga, zikhulupiriro zabodza komanso kuti asakhale osazindikira. Komanso pa mapeto pake adzapeza “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Ngakhale panopa, tikhoza kulawa ufuluwu ‘tikamasunga mawu a Khristu.’ Tikamachita zimenezi ‘tidzadziwa choonadi’ osati chifukwa chongochiphunzira koma chifukwa chochitsatira. (Yoh. 8:31) M’dziko lakaleli moyo umene anthu ambiri amati ndi wabwino umakhala wosadalirika komanso wakanthawi. Paja sitidziwa zimene zingachitike mawa. (Yak. 4:13, 14) Choncho ndi nzeru kukhalabe pa njira yopita ku ‘moyo weniweni,’ womwe ndi moyo wosatha. (1 Tim. 6:19) Koma Mulungu satikakamiza kuyenda pa njirayo. Tiyenera kusankha tokha. Choncho muziyesetsa kuti Yehova akhale “gawo” lanu. (Sal. 16:5) Muziyamikira kwambiri “zinthu zabwino” zimene wakupatsani. (Sal. 103:5) Muzikhulupiriranso kuti iye angakuthandizeni kuti muzisangalala kwambiri komanso kuti mukhale ndi “chimwemwe mpaka muyaya.”—Sal. 16:11. w18.12 28 ¶19, 21
Lolemba, March 9
Mwamunanso asasiye mkazi wake.—1 Akor. 7:11.
Akhristu onse ayenera kuyesetsa kuti azilemekeza ukwati ngati mmene Yesu ndi Yehova amachitira. Komabe ena angalephere kuchita zimenezi chifukwa anthufe si angwiro. (Aroma 7:18-23) Choncho sitiyenera kudabwa kuti Akhristu ena akale ankakumana ndi mavuto m’mabanja awo. Nthawi zina ankapatukana ngakhale kuti Paulo analemba kuti “mkazi asasiye mwamuna wake.” (1 Akor. 7:10) Paulo sanafotokoze chimene chinkachititsa kuti ena apatukane. Koma vuto silinali lakuti mwamuna anachita dama chifukwa zimenezi zikanapatsa mkaziyo chifukwa chomveka choti athetsere banja n’kukwatiwanso. Paulo analemba kuti mkazi amene anapatukana ndi mwamuna wake “akhale choncho wosakwatiwa. Apo ayi, abwererane ndi mwamuna wakeyo.” Izi zikusonyeza kuti pamaso pa Mulungu anthu awiriwo anali adakali pa banja. Paulo anafotokoza kuti mwamuna ndi mkazi amene akumana ndi mavuto, koma wina sanachite chigololo, ayenera kukhala ndi cholinga choti akonze zinthu m’banja mwawo. Iwo akhoza kupempha akulu mumpingo kuti awathandize kuchita zimenezi. w18.12 13 ¶14-15
Lachiwiri, March 10
Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake.—Mat. 6:33.
Yehova amafuna kuti anthu ake akhale naye pa ubwenzi wabwino komanso azigwira mwakhama ntchito yolalikira. (Mat. 28:19, 20; Yak. 4:8) Anthu ena omwe mwina angakhale ndi zolinga zabwino angatilimbikitse kuti tisiye kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, kodi tingatani ngati bwana wathu akufuna kutikweza udindo komanso kutiwonjezera malipiro, koma zimenezo zichititsa kuti tiziphonya zinthu zina zauzimu? Nanga mungatani ena atakupatsani mwayi woti muchoke kunyumba n’kukachita maphunziro owonjezera? Kodi mungafunike kupemphera, kufufuza m’mabuku athu, kukambirana ndi anthu ena kenako n’kusankha zochita? Koma kodi sizingakhale zothandiza kuoneratu maganizo a Yehova pa nkhani zimenezi panopa n’cholinga choti tiziyendera maganizo akewo? Tikatero sitingasowe chochita ngati zoterezi zitadzatichitikira ndipo sitingazionenso ngati mayesero. Zimakhala ngati uli kale ndi zolinga zako zauzimu, watsimikiza kale mumtima ndipo kwatsala n’kungochita zimene wasankha kalezo. w18.11 27 ¶18
Lachitatu, March 11
Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa.—Miy. 4:23.
Solomo anakhala mfumu ya Aisiraeli ali mnyamata. Atangoyamba kulamulira, Yehova anaonekera kwa iye m’maloto ndipo anamuuza kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikupatse.” Solomo anayankha kuti: “Ndine mwana ndipo sindikudziwa zinthu zambiri. . . . Mupatse mtumiki wanune mtima womvera kuti ndiweruze anthu anu.” (1 Maf. 3:5-10) Solomo anapempha “mtima womvera” ndipo zimenezi zimasonyeza kuti anali wodzichepetsa. M’pake kuti Yehova ankamukonda kwambiri. (2 Sam. 12:24) Mulungu anasangalala kwambiri ndi zimene Solomo anapempha moti anamupatsa “mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu.” (1 Maf. 3:12) Pamene Solomo anali wokhulupirika kwa Yehova, ankadalitsidwa kwambiri. Iye anapatsidwa mwayi womanga kachisi wodziwika ndi “dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (1 Maf. 8:20) Solomo anatchuka kwambiri chifukwa cha nzeru zimene Mulungu anamupatsa. Ndipo mfundo zimene ananena atauziridwa ndi Mulungu zinalembedwa m’mabuku atatu a m’Baibulo. Buku la Miyambo ndi limodzi mwa mabuku amenewa. w19.01 14 ¶1-2
Lachinayi, March 12
Musamatengere nzeru za nthawi ino.—Aroma 12:2.
Anthu ambiri amadana ndi zoti aziyendera maganizo a winawake. Iwo amaona kuti palibe angawauze zochita. Koma mwina izi zimatanthauza kuti amasankha okha zochita ndipo amaona kuti zimenezi n’zoyenera. Iwo amafuna ufulu wosankha zochita popanda kugonjera aliyense. Koma kuyendera maganizo a Yehova sikutanthauza kuti munthu sakhala ndi ufulu uliwonse woganiza kapena wosankha yekha zochita. Malinga ndi lemba la 2 Akorinto 3:17, “pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” Munthu amakhala ndi ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi mmene iyeyo alili. Angasankhe yekha zochita pa zinthu zimene zimamusangalatsa. Ndipo Yehova anatilenga m’njira yoti tizigwiritsa ntchito ufuluwu. Chimene amangofuna n’chakuti tizidziwa malire athu pougwiritsa ntchito. (1 Pet. 2:16) Posankha kuti ichi n’choyenera ichi n’cholakwika, Yehova amafuna kuti tiziyendera maganizo ake. w18.11 19 ¶5-6
Lachisanu, March 13
Dema wandisiya chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi ino.—2 Tim. 4:10.
Titaphunzira choonadi tinaona kuti zinthu zauzimu ziyenera kukhala pamalo oyamba. Tinkaona kuti ndi bwino kulolera kuti tisakhale ndi zinthu zina n’cholinga choti tiziyendabe m’choonadi. Koma nthawi ikamadutsa tikhoza kumaona anzathu akugula zipangizo zamakono kapena akupeza ndalama zambiri. Ndiye mwina tingayambe kuganiza kuti tikumanidwa zambiri. Kenako tingayambe mtima wosakhutira ndi zinthu zofunika zomwe tili nazo moti tingalolere kusiya zinthu zokhudza kulambira n’cholinga choti tipeze zinthu zinazake. Zoterezi zinachitikiranso Mkhristu wina dzina lake Dema. Mtima wokonda “zinthu za m’nthawi ino” unamuchititsa kuti asiye kutumikira limodzi ndi Paulo. Kodi n’chifukwa chiyani Dema anachita zimenezi? Kaya ankakonda kwambiri zinthu zakuthupi kuposa zauzimu, kapena ankaona kuti akumanidwa zinthu zina akamayenda ndi Paulo, Baibulo silinena. Koma mfundo ndi yakuti si bwino kulola mtima wolakalaka chuma kutichititsa kusiya kukonda choonadi. w18.11 10 ¶9
Loweruka, March 14
Kufa simudzafa ayi.—Gen. 3:4.
Bodza la Satanali linali loipa kwambiri chifukwa ankadziwa kuti Hava akakhulupirira zimene amuuze n’kudya chipatsocho adzafa. Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo patapita nthawi anafa. (Gen. 3:6; 5:5) Koma kuwonjezera pamenepo, uchimo wawo unachititsa kuti ‘imfa ifalikire kwa anthu onse.’ Ndipo Baibulo limanena kuti: “Imfa inalamulira monga mfumu . . . , ngakhalenso kwa anthu amene sanachimwe monga mmene anachimwira Adamu.” (Aroma 5:12, 14) Choncho m’malo mokhala ndi moyo wosatha ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba, anthufe timangokhala ‘zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera zimakwana zaka 80.’ Chomvetsa chisoni n’chakuti masiku onsewa “amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.” (Sal. 90:10) Mavuto onsewatu anayamba chifukwa cha bodza la Satana. Yesu ananena kuti Mdyerekezi “sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi.” (Yoh. 8:44) Satana sanasinthe chifukwa akupitirizabe ‘kusocheretsa dziko lonse lapansi’ ndi mabodza ake. (Chiv. 12:9) Koma ife sitifuna kupusitsidwa ndi Mdyerekezi. w18.10 6-7 ¶1-4
Lamlungu, March 15
Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’—Mat. 5:9.
Anthu amene amayesetsa kukhazikitsa mtendere amakhala osangalala. Paja Yakobo analemba kuti: “Chilungamo ndicho chipatso cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.” (Yak. 3:18) Tikasemphana maganizo ndi munthu wina mumpingo kapena m’banja tiyenera kuchonderera Mulungu kuti atithandize kukhazikitsa mtendere. Zimenezi zingathandize kuti mzimu woyera uzigwira bwino ntchito, tizichita zinthu mwachilungamo komanso tikhale osangalala. Pofotokoza kufunika kokhazikitsa mtendere, Yesu ananena kuti: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.”—Mat. 5:23, 24. w18.09 21 ¶17
Lolemba, March 16
Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana.—Yoh. 13:34.
Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anatchula za chikondi maulendo 30. Iye anatsindika mfundo yoti ophunzira ake ayenera kukondana. (Yoh. 15:12, 17) Chikondi chawo chinayenera kukhala chapamwamba kwambiri mpaka kufika pokhala chizindikiro choti ndi Akhristu enieni. (Yoh. 13:35) Chikondi choterechi si chimene munthu amachisonyeza chifukwa chongotengeka basi. Apa Yesu ankanena za chikondi chololera kuvutikira anthu ena. Paja ananena kuti: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake. Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.” (Yoh. 15:13, 14) Chikondi chimene atumiki a Yehova ali nacho masiku ano komanso mgwirizano wawo zimatsimikizira kuti ndi anthu a Mulungu. (1 Yoh. 3:10, 11) Chosangalatsa kwambiri n’chakuti atumiki a Yehova amasonyezana chikondi ngakhale kuti amasiyana mitundu, zilankhulo komanso kochokera. w18.09 12 ¶1-2
Lachiwiri, March 17
Ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.—1 Tim. 5:8.
Yehova amafuna kuti atumiki ake azisamalira mabanja awo. Mwachitsanzo, mwina muyenera kugwira ntchito kuti muzipezera banja lanu zofunika pa moyo. Azimayi ambiri amafunika kukhala pakhomo n’cholinga choti azisamalira ana awo aang’ono. Ndipo anthu ena amafunika kusamalira makolo awo amene akudwala. Ntchito zonsezi ndi zofunika kwambiri. Ngati muli ndi udindo wosamalira banja lanu, mwina simungakhale ndi nthawi yambiri yochita zonse zimene mungafune m’gulu la Yehova. Koma musadandaule. Yehova amasangalala mukamasamalira banja lanu. (1 Akor. 10:31) Ngati mulibe udindo waukulu wosamalira banja, kodi mungathandize Akhristu anzanu amene ndi achikulire, odwala, ali ndi mavuto ena kapena amasamalira anthu ena? Mungachite bwino kuona ngati mumpingo wanu muli anthu amene amafunika kuthandizidwa. Mukamachita zimenezi mungakhale kuti mukugwira ntchito ndi Yehova pothandiza kuyankha pemphero la munthu wina.—1 Akor. 10:24. w18.08 24 ¶3, 5
Lachitatu, March 18
Mulungu anali naye, ndipo anamulanditsa m’masautso ake onse.—Mac. 7:9, 10.
Yosefe ndi zaka 17, abale ake anamugulitsa chifukwa chomuchitira nsanje. Izi zisanachitike, iye anali mwana wokondedwa ndi bambo ake. (Gen. 37:2-4, 23-28) Kwa zaka 13, Yosefe anakhala kapolo komanso mkaidi ku Iguputo ndipo anali kutali ndi bambo ake omwe ankawakonda kwambiri. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asataye mtima kapena kukwiya? Pa nthawi imene Yosefe ankazunzika m’ndende, ayenera kuti ankaganizira kwambiri mmene Yehova ankamuthandizira. (Gen. 39:21; Sal. 105:17-19) Maloto ochokera kwa Mulungu amene Yosefe analota ali mwana ayeneranso kuti ankamutsimikizira kuti Mulungu akusangalala naye. (Gen. 37:5-11) N’zosakayikitsa kuti iye ankauza Yehova zimene zinkamupweteka. (Sal. 145:18) Ndiyeno Yehova anayankha mapemphero ake ochokera mumtimawo n’kumuthandiza kudziwa kuti “anali naye” pa mavuto ake onse. w18.10 28 ¶3-4
Lachinayi, March 19
Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake, koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.—Miy. 14:20.
Tiyenera kupewa kuweruza anthu potengera kusauka kapena kulemera kwawo. Kodi zingatheke bwanji kuweruza munthu potengera zinthu zimenezi? Mzimu woyera unathandiza Solomo kuti alembe mfundo yamulemba la lero yokhudza anthu ochimwafe yomwe ndi yoona koma yomvetsa chisoni. Kodi tikuphunzirapo chiyani palemba limeneli? Tikapanda kusamala, tingayambe kumangogwirizana ndi anthu olemera n’kumapewa osauka. Koma n’chifukwa chiyani kuona kuti munthu ndi wofunika potengera chuma chake n’koopsa kwambiri? Chifukwa chakuti tikamachita zimenezi tingasokoneze mgwirizano mumpingo. Yakobo ananena kuti vuto limeneli linkagawanitsa anthu m’mipingo ya mu nthawi yake. (Yak. 2:1-4) Choncho tiyenera kusamala kuti vutoli lisasokoneze mpingo wathu masiku ano. Tiyeneranso kuyesetsa kuti tizipewa kuweruza anthu poona maonekedwe akunja. w18.08 10 ¶8-10
Lachisanu, March 20
Khalani okondana kwambiri.—1 Pet. 4:8.
Zimene timachitira abale ndi alongo athu zingasonyeze ngati timayamikira ubwenzi wathu ndi Yehova kapena ayi. Tizikumbukira kuti anzathuwo ndi a Yehovanso. Tikamakumbukira mfundo imeneyi, nthawi zonse tidzakhala okoma mtima komanso achikondi kwa abale ndi alongo athu. (1 Ates. 5:15) Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Chochititsa chidwi n’chakuti Malaki ananena kuti Yehova ‘amatchera khutu n’kumamvetsera’ zimene anthu ake akukambirana. (Mal. 3:16) Izi zikusonyezeratu kuti Yehova “amadziwa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Iye amadziwa chinthu chilichonse chimene timachita komanso kulankhula. (Aheb. 4:13) Tikamachita kapena kulankhula zinthu zopweteka kwa Akhristu anzathu, Yehova ‘amatchera khutu n’kumamvetsera.’ Koma tikamachereza alendo, kupereka zinthu mowolowa manja, kukhululukira anthu komanso kuwakomera mtima, Yehova amaonanso.—Aheb. 13:16. w18.07 26 ¶15, 17
Loweruka, March 21
Muzim’tumikira [Yehova] ndi kum’mamatira.—Deut. 10:20.
Yehova Mulungu wathu ndi wamphamvu, wanzeru komanso wachikondi kuposa aliyense. Choncho n’zomveka kuti timafuna kukhala kumbali yake nthawi zonse. (Sal. 96:4-6) Koma atumiki a Yehova ena amasiya kukhala kumbali yake akapanikizika ndi mavuto. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Kaini. Iye ankanena kuti amalambira Yehova osati milungu ina. Koma Yehova sankasangalala ndi zimene ankachita pomulambira. Zinali choncho chifukwa chakuti maganizo oipa anayamba kukula mumtima mwake. (1 Yoh. 3:12) Yehova analankhula ndi Kaini n’kumuuza kuti: “Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti uchite chabwino, uchimo wamyata pakhomo kukudikirira, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Apa tingati Yehova ankauza Kaini kuti: “Tangolapa n’kukhala kumbali yanga ndipo inenso ndikhala kumbali yako.” Koma Kaini sanamvere. w18.07 17-18 ¶1, 3-4
Lamlungu, March 22
Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu.—Mat. 5:16.
Njira imodzi imene timaonetsera kuwala kwathu ndi kulalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa anthu. (Mat. 28:19, 20) Koma timalemekezanso Yehova tikakhala ndi khalidwe labwino. Paja anthu amene timawalalikira kapena kukumana nawo mu utumiki amaona zochita zathu. Tikamamwetulira komanso kupereka moni mwansangala timathandiza anthu kuti akhale ndi maganizo oyenera okhudza ifeyo komanso Mulungu wathu. Paja Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pamene mukulowa m’nyumba, perekani moni kwa a m’banja limenelo.” (Mat. 10:12) M’dera limene Yesu ndi ophunzira ake ankalalikira, anthu ankakonda kuitanira anthu achilendo m’nyumba zawo. Koma zimenezi sizichitikachitika m’madera ambiri masiku ano. Komabe tikakhala aubwenzi tikhoza kuthandiza munthu amene tamupeza kuti asakhale ndi maganizo olakwika. Nthawi zambiri, kumwetulira kumathandiza kuti muyambe kukambirana naye. Zimenezi zimathandizanso tikamalalikira pogwiritsa ntchito kashelefu m’malo opezeka anthu ambiri. Nthawi zambiri anthu amachita chidwi akaona kuti tikumwetulira komanso kuwapatsa moni mwansangala. w18.06 22 ¶4-5
Lolemba, March 23
Mulungu alibe tsankho.—Mac. 10:34.
Mtumwi Petulo anali atazolowera kuchita zinthu ndi Ayuda okhaokha. Koma Mulungu atamuthandiza kuzindikira kuti Akhristu ayenera kuchita zinthu mopanda tsankho, Petulo analalikira msilikali wachiroma dzina lake Koneliyo. (Mac. 10:28, 35) Kenako anayamba kudya komanso kucheza ndi Akhristu amitundu ina. Koma patapita zaka zingapo, Petulo anasiya kudya ndi Akhristu omwe sanali Ayuda mumzinda wa Antiokeya. (Agal. 2:11-14) Zimenezi zitachitika, Paulo anamudzudzula ndipo zikuoneka kuti Petulo anamvera. Pamene Petulo analemba kalata yoyamba yopita kwa Akhristu achiyuda komanso amitundu ina ku Asia Minor anawalimbikitsa kuti azikonda gulu lonse la abale. (1 Pet. 1:1; 2:17) Apa zikuonekeratu kuti atumwi anaphunzira kwa Yesu mtima wokonda “anthu osiyanasiyana.” (Yoh. 12:32; 1 Tim. 4:10) Iwo anasintha maganizo awo ngakhale kuti zinawatengera nthawi yaitali. Akhristuwo anavala “umunthu watsopano” womwe unawathandiza kuzindikira kuti anthu onse ndi ofanana pamaso pa Mulungu.—Akol. 3:10, 11. w18.06 11 ¶15-16
Lachiwiri, March 24
Khalani olimba, . . . mutavalanso chodzitetezera pachifuwa chachilungamo.—Aef. 6:14.
Chodzitetezera pachifuwa chimene asilikali achiroma ankavala chinkakhala ndi zitsulo zolimba zomwe sizinkasiya mpata woti munthu n’kubayidwa. Msilikali akavala zimenezi ankafunika kuona pafupipafupi ngati chitsulo chilichonse chidakali pamalo ake bwinobwino n’cholinga choti mtima wake kapena ziwalo zina zofunika kwambiri zisabayidwe. Fanizo limeneli likusonyeza bwino mmene mfundo zachilungamo za Yehova zingatetezere mtima wathu wophiphiritsa. (Miy. 4:23) Msilikali wanzeru sangavule chodzitetezera chachitsulo cholimba n’kuvala chachitsulo chosalimba. Nafenso, sitingayerekeze kusiya kutsatira mfundo za Yehova n’kumayendera zathu. Paja nzeru zathu n’zoperewera ndipo sizingatiteteze bwinobwino. (Miy. 3:5, 6) Choncho ndi bwino kumadzifufuza pafupipafupi kuti tione ngati mtima wathu wophiphiritsa ndi wotetezeka bwino ndi mfundo za Yehova. Ngati timakonda kwambiri mfundo za Mulungu sitingavutike kuvala “chodzitetezera pachifuwa,” kapena kuti kutsatira mfundo zake zachilungamo.—Sal. 111:7, 8; 1 Yoh. 5:3. w18.05 28 ¶3-4, 6-7
Lachitatu, March 25
Anthuwo anayamba kukangana ndi Mose.—Num. 20:3.
Anthuwa anayamba kudandaula ngakhale kuti Mose anali atasonyeza kwa nthawi yaitali kuti ndi mtsogoleri woganizira anthu osati wodzikonda. Anthuwo sankangonena za madzi okha koma ankatsutsanso Mose ngati kuti iye ndi amene anawachititsa kumva ludzu. (Num. 20:1-5, 9-11) Zitatero, Mose analephera kukhala wofatsa ndipo anapsa mtima. M’malo mosonyeza chikhulupiriro n’kulankhula ndi mwala mogwirizana ndi malangizo a Yehova, Mose anakwiya n’kukalipira anthuwo komanso kusonyeza kuti iye ndi amene angawapatse madzi. Kenako anamenya mwalawo kawiri moti madzi ambiri anayamba kutuluka. Kudzikuza komanso mkwiyo zinamuchititsa kuti alakwitse kwambiri zinthu. (Sal. 106:32, 33) Zimene anachizi zinachititsa kuti asaloledwe kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:12) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Choyamba, tiyenera kuyesetsa nthawi zonse kuti tikhalebe ofatsa. Tikangodzilekerera, ngakhale pang’ono pokha, tikhoza kuyamba kudzikuza n’kulankhula kapena kuchita zinthu mopanda nzeru. Chachiwiri, munthu akakhala ndi nkhawa amafooka choncho tiziyesetsa kukhalabe ofatsa ngakhale pamene tapanikizika. w19.02 12-13 ¶19-21
Lachinayi, March 26
Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.—Mat. 24:14.
Kodi kumvera lamulo la Yesu loti tizilalikira n’kovuta kwambiri? Ayi. Tikutero chifuwa chakuti Yesu atafotokoza fanizo la mtengo wa mpesa ananena kuti olalikira za Ufumu adzapeza chimwemwe. (Yoh. 15:11) Iye anatitsimikizira kuti chimwemwe chake chidzakhalanso chathu. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Yesu ananena kuti ali ngati mtengo wa mpesa ndipo ophunzira ake ali ngati nthambi. (Yoh. 15:5) Mtengo ndi umene umathandiza nthambi kuti zizikhala ndi moyo. Nthambi zikakhala zolumikizidwabe ndi mtengo zimalandira madzi ndi chakudya. Ifenso tikakhalabe ogwirizana ndi Khristu potsatira mapazi ake, timakhala osangalala ngati mmene iye amasangalalira chifukwa chochita zofuna za Atate wake. (Yoh. 4:34; 17:13; 1 Pet. 2:21) Mlongo wina dzina lake Hanne, yemwe wachita upainiya kwa zaka zoposa 40, ananena kuti: “Ndimakhala wosangalala kwambiri ndikaweruka mu utumiki moti ndimafunitsitsa kugwirabe ntchito ya Yehova.” Kunena zoona, chimwemwe chimene timakhala nacho chimatithandiza kupitiriza kulalikira ngakhale m’magawo ovuta.—Mat. 5:10-12. w18.05 17 ¶2; 20 ¶14
Lachisanu, March 27
Ndinasankhidwa kuti ndikhale mphunzitsi wophunzitsa anthu a mitundu ina za chikhulupiriro ndi choonadi.—1 Tim. 2:7.
Paulo anachita zambiri polimbikitsa Akhristu anzake. Mzimu woyera unamuthandiza kuti akalalikire kwa anthu a m’madera olamulidwa ndi Agiriki ndi Aroma, omwe ankakhulupirira milungu yambirimbiri. (Agal. 2:7-9) Paulo anayenda m’madera ambiri a anthu a mitundu ina n’kumakhazikitsa mipingo moti anafika ku Greece, ku Italy komanso kudziko limene panopa limatchedwa Turkey. Akhristu atsopano m’maderawa ankazunzidwa ndi anthu akwawo ndipo ankafunika kulimbikitsidwa. (1 Ates. 2:14) Cha mu 50 C.E., Paulo analembera Akhristu atsopano ku Tesalonika kuti: “Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamatchula za inu nonse m’mapemphero athu. Timatero pakuti timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro, ndi ntchito zanu zachikondi. Timateronso pokumbukira mmene munapiririra.” (1 Ates. 1:2, 3) Iye anawauzanso kuti azilimbikitsana. Anati: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.”—1 Ates. 5:11. w18.04 19 ¶16-17
Loweruka, March 28
Uthenga wabwino uyenera ulalikidwe choyamba.—Maliko 13:10.
Wachinyamata amene amafunitsitsa kusangalatsa Yehova amaganizira kwambiri za utumiki. Popeza ntchito yolalikira ndi yofunika kugwiridwa mwamsanga, tiyenera kuiika pamalo oyamba. Ndiye kodi inuyo mungayesetse kuwonjezera nthawi imene mumalalikira? Nanga kodi mungachite upainiya? Kodi mungatani ngati panopa simusangalala kwenikweni ndi ntchito yolalikira? Kodi mungatani kuti muzilalikira mogwira mtima? Pali zinthu ziwiri zimene mungachite. Choyamba, muyenera kukonzekera bwino ndipo musamagwe ulesi pa nkhani yophunzitsa anthu mfundo zachoonadi zimene mukudziwa. Mukhoza kudabwa kuona mmene mungasangalalire polalikira. Mwina poyambira pabwino pangakhale kukonzekera yankho la funso limene anzanu ambiri kusukulu amakonda kufunsa, monga lakuti, “N’chifukwa chiyani umakhulupirira zoti kuli Mulungu?” Pa webusaiti yathu pali nkhani zothandiza achinyamata kuti asamavutike kuyankha funso ngati limeneli. Mukapita pamenepa mudzapeza zochita pa nkhani yakuti “N’chifukwa chiyani ndimakhulupirira zoti kuli Mulungu?” Mfundo zimene zili pamenepo zingakuthandizeni kukonzekera zimene mungayankhe. w18.04 27 ¶10-11
Lamlungu, March 29
Muberekane, muchuluke.—Gen. 1:28.
Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anali ndi ufulu wambiri, panali mfundo zina zimene ankafunika kuyendera. Ndipo zina ndi zoti ankazitsatira mwachibadwa. Mwachitsanzo, ankafunika kupuma, kudya, kugona komanso kuchita zinthu zina kuti akhalebe ndi moyo. Ndipo akamachita zinthu zimenezi sankaona kuti akuphwanyiridwa ufulu. Zili choncho chifukwa chakuti Yehova anakonza zinthu m’njira yakuti anthuwo akamachita zinthu za tsiku ndi tsiku ngati zimenezi azisangalala. (Sal. 104:14, 15; Mlal. 3:12, 13) Yehova analamulanso Adamu ndi Hava kuti adzaze dziko lapansi komanso kuliyang’anira. Kodi lamulo limeneli linali lowaphwanyira ufulu? Ayi. Mulungu analipereka n’cholinga choti anthuwo athandize nawo pokwaniritsa cholinga chake choti dziko lonse likhale paradaiso wodzaza ndi anthu angwiro. (Sal. 127:3; Yes. 45:18) Adamu ndi Hava anali ndi mwayi wokhala m’banja n’kumasangalala ndi ana awo mpaka muyaya. w18.04 4-5 ¶7-8
Lolemba, March 30
Onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.—Mac. 13:48.
Ngati ndife oleza mtima, sitidzayembekezera kuti anthu amvetse komanso kuvomereza mfundo za m’Baibulo pa ulendo woyamba. Tiyerekeze kuti tikukambirana ndi munthu za moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akafa zonse zimathera pomwepo. Apo ayi amakhulupirira kuti anthu abwino onse amapita kumwamba. M’bale wina anafotokoza zimene zimamuthandiza. Choyamba, amawerengera munthu lemba la Genesis 1:28. Kenako amamufunsa kuti, “Kodi Mulungu ankafuna kuti anthu azikhala kuti, nanga azikhala motani?” Ambiri amayankha kuti, “Padziko lapansi mosangalala.” Kenako m’baleyo amawerenga Yesaya 55:11 n’kufunsa munthuyo ngati cholinga cha Mulungu chinasintha. Ambiri amayankha kuti sichinasinthe. Pomaliza, m’baleyo amawerenga Salimo 37:10, 11 n’kufunsa munthuyo kuti, “Malinga ndi vesili, kodi n’chiyani chidzachitike m’tsogolo?” Malemba ngati amenewa amathandiza anthu kumvetsa mfundo yoti Mulungu akufunabe kuti anthu akhale m’Paradaiso padziko lapansi. w19.03 24 ¶14-15; 25 ¶19
Lachiwiri, March 31
Muzimumvera.—Mat. 17:5.
Yehova anasonyeza kuti amafuna kuti tizimvera mawu a Mwana wake. Yesu anaphunzitsa bwino ophunzira ake ntchito yolalikira uthenga wabwino ndipo anawauza mobwerezabwereza kuti ayenera kukhala maso. (Mat. 24:42; 28:19, 20) Iye anawauzanso kuti azichita zinthu mwamphamvu komanso kuti asafooke. (Luka 13:24) Yesu anauzanso ophunzira ake kuti ayenera kukondana, kukhala ogwirizana komanso kutsatira malamulo ake. (Yoh. 15:10, 12, 13) Malangizo amenewa ndi othandizanso masiku ano. Yesu ananena kuti: “Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvera mawu anga.” (Yoh. 18:37) Ndiye timasonyeza kuti tikumvera mawu ake tikamapitiriza “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akol. 3:13; Luka 17:3, 4) Timasonyezanso kumvera mawu ake tikamalalikira uthenga wabwino mwakhama “m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.”—2 Tim. 4:2. w19.03 10 ¶9-10