April
Lachitatu, April 1
[Yesu anauza] Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! . . . Zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”—Mat. 16:23.
Nanga bwanji ifeyo? Kodi timayendera maganizo a Mulungu kapena a m’dzikoli? N’zoona kuti ambirife tinasintha khalidwe lathu n’kumatsatira zimene Mulungu amafuna. Koma kodi tinasinthanso maganizo athu? Kodi timayesetsa kuti tiziyendera maganizo a Yehova? Kuti zimenezi zitheke pamafunika khama ndithu. Koma munthu safunika kuchita khama kuti ayambe kuyendera maganizo a m’dzikoli. Zili choncho chifukwa chakuti mzimu wadziko uli paliponse m’dzikoli. (Aef. 2:2) Vuto lina ndi lakuti mtima wathu wodzikonda umafulumira kukopeka ndi maganizo a m’dzikoli. Mwachidule tingati pamafunika khama kuti tiziyendera maganizo a Yehova koma kuyendera maganizo a m’dzikoli n’kosavuta ngakhale pang’ono. Munthu akamayendera maganizo a m’dzikoli amakhala wodzikonda komanso safuna kuuzidwa zochita ndi Mulungu. (Maliko 7:21, 22) Choncho ndi bwino kuyesetsa kukhala ndi “maganizo a Mulungu” osati “maganizo a anthu.” w18.11 18 ¶1; 19 ¶3-4
Lachinayi, April 2
Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.—Mat. 3:17.
Yesu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri Yehova atalankhula kuchokera kumwamba maulendo atatu posonyeza kuti amayamikira Mwana wakeyu. Yesu atangobatizidwa mumtsinje wa Yorodano, Yehova ananena mawu ali pamwambawa. N’kutheka kuti Yohane M’batizi yekha ndi amene anamva mawuwa. Kutatsalanso chaka chimodzi kuti Yesu aphedwe, ophunzira ake atatu anamva Yehova akunena za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.” (Mat. 17:5) Yehova analankhulanso ndi Mwana wake kuchokera kumwamba kutatsala masiku ochepa kuti Mwanayo aphedwe. (Yoh. 12:28) Yesu ankadziwa kuti adzafa imfa yochititsa manyazi ndipo anthu adzamunena kuti ndi wonyoza Mulungu. Koma iye anapempherabe kuti zinthu zichitike mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu osati chake. (Mat. 26:39, 42) Baibulo limanena kuti iye ‘anapirira mtengo wozunzikirapo ndipo sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira.’—Aheb. 12:2. w18.07 10-11 ¶15-16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 dzuwa litalowa) Maliko 14:3-9
Lachisanu, April 3
Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi.—Luka 22:42.
Yesu atangoyambitsa mwambo wa Chikumbutso anasonyeza kulimba mtima kwambiri. Iye anavomera kuchita zimene Atate ake ankafuna. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti adzaimbidwa mlandu wochititsa manyazi wakuti wanyoza Mulungu kenako n’kuphedwa. (Mat. 26:65, 66) Yesu anakhalabe wokhulupirika n’cholinga choti alemekeze dzina la Yehova, asonyeze kuti Yehova ndi woyenera kulamulira komanso athandize anthu olapa kuti adzapeze moyo wosatha. Pa nthawi imodzimodziyo, Yesu anathandiza otsatira ake kuti akonzekere zimene adzakumane nazo. Yesu anasonyeza kulimba mtima posiya kuganizira mavuto amene akumane nawo n’kumaganizira zimene atumwi ake okhulupirika ankafunikira. Mwambo wosavuta umene anauyambitsa atatulutsa Yudasi unali woti udzakumbutsa otsatira ake odzozedwa zinthu zabwino zimene zikutheka chifukwa cha magazi a Yesu komanso ubwino wokhala m’pangano latsopano.—1 Akor. 10:16, 17 w19.01 22 ¶7-8
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Maliko 11:1-11
Loweruka, April 4
Atate lemekezani dzina lanu.—Yoh. 12:28.
Yesu atalankhula mawuwa, Atate ake analankhula kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.” Yesu anasautsika mumtima poganizira udindo waukulu umene anali nawo woti akhalebe wokhulupirika kwa Yehova. Iye ankadziwa kuti adzazunzidwa komanso kuphedwa mwankhanza. (Mat. 26:38) Kwa Yesu, chinthu chofunika kwambiri chinali kulemekeza dzina la Atate ake. Koma anthu anamuimba mlandu wonyoza Mulungu ndipo Yesu anada nkhawa kwambiri poona kuti mwina imfa yake idzanyozetsa Mulungu. Nafenso tikhoza kumada nkhawa tikaganizira za kudetsedwa kwa dzina la Yehova. Mwina ifenso sitikuchitiridwa zinthu mwachilungamo. Apo ayi tingamade nkhawa ndi nkhani zabodza zimene adani athu angafalitse. Mwina tingafike poganiza kuti zinthu zimenezi zinyozetsa Yehova. Pa nthawi ngati imeneyi, mawu a Yehovawa akhoza kutilimbikitsa. Yehova sangalephere kulemekeza dzina lake.—Sal. 94:22, 23; Yes. 65:17. w19.03 11-12 ¶14-16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Maliko 11:12-19
Lamlungu, April 5
Yesu Khristu anayamba kuuza ophunzira ake kuti n’koyenera . . . [akazunzidwe] kwambiri . . . Ndiyeno akaphedwa.—Mat. 16:21.
Ophunzira a Yesu anadabwa kwambiri Yesu atawauza kuti pasanapite nthawi yaitali iye azunzidwa kenako aphedwa. Iwo anadabwa chifukwa ankayembekezera kuti Yesuyo ndi amene adzabwezeretse ufumu kwa Aisiraeli. Ndiyeno Petulo anauza Yesu kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” Koma iye anamuyankha kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” (Mat. 16:22, 23; Mac. 1:6) Zimene Yesu ananenazi zikusonyeza kuti pali kusiyana pakati pa maganizo a Mulungu ndi maganizo a anthu m’dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Mtumwi Petulo anafotokoza maganizo ofuna kudzikomera mtima amene afala m’dzikoli. Koma Yesu ankadziwa kuti maganizo a Atate wake ndi osiyana ndi maganizo a anthu. Zimene Yesu anauza Petulo zinasonyeza kuti anakana kuyendera maganizo a anthu koma a Yehova. w18.11 18 ¶1-2
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Maliko 11:20-33; 12:1-27, 41-44
Lolemba, April 6
Mukulengezabe imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.—1 Akor. 11:26.
Tikakhala pamwambo wa Chikumbutso, sikuti Yehova amangotiona m’chigulugulu. Iye amaona munthu aliyense payekha. Mwachitsanzo, amaona aliyense amene amapezeka pamwambowu chaka chilichonse. Ena mwa anthu amenewa amapezekabe pamwambowu ngakhale kuti akuzunzidwa kwambiri. Palinso ena amene sapezeka pamisonkhano nthawi zonse komabe safuna kuphonya mwambo wa Chikumbutso. Yehova amaonanso anthu amene apezeka koyamba pamwambowu kuti aone zimene zimachitika. N’zosakayikitsa kuti Yehova amasangalala kuona anthu ambiri atapezeka pa Chikumbutso. (Luka 22:19) Koma iye amasangalala kwambiri akaona zolinga za anthu amene apezekawo. Kodi ifeyo timafuna kuphunzitsidwa ndi Yehova komanso gulu lake?—Yes. 30:20; Yoh. 6:45. w19.01 26 ¶1-3
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Maliko 14:1, 2, 10, 11; Mateyu 26:1-5, 14-16
Tsiku la Chikumbutso
Dzuwa Litalowa
Lachiwiri, April 7
Khristu anatifera.—Aroma 5:8.
Sikuti Yesu anangofera ophunzira ake, koma tsiku lililonse ankaikanso patsogolo zofuna zawo osati zake. Mwachitsanzo, ankayesetsa kuti akumane nawo ngakhale pamene watopa kapena kupanikizika ndi nkhawa. (Luka 22:39-46) Iye ankaganizira kwambiri zimene angachitire anthu osati zimene anthu angamuchitire. (Mat. 20:28) Timasangalala kwambiri kukhala m’gulu la Akhristu oona ndipo timafuna kuchita zonse zimene tingathe poitanira anthu ena m’gululi. Koma tiyenera kuyesetsa kuthandiza makamaka “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro” amene panopa afooka. (Agal. 6:10) Tingasonyeze kuti timawakonda powaitanira kumisonkhano makamaka kumwambo wa Chikumbutso. Mofanana ndi Yehova ndi Yesu, timasangalala kwambiri munthu wofooka akabwerera kwa Yehova.—Mat. 18:14. w19.01 29 ¶12, 14; 30 ¶15-16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Maliko 14:12-16; Mateyu 26:17-19 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Maliko 14:17-72
Lachitatu, April 8
Mkate uwu ukuimira thupi langa. . . . Vinyoyu akuimira ‘magazi anga a pangano.’—Mat. 26:26-28.
Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake pongogwiritsa ntchito mkate komanso vinyo zimene zinatsala pamwambo wa Pasika. Yesu anauza atumwi ake kuti zinthu ziwirizi zikuimira thupi lake lopanda uchimo komanso magazi ake. Iye anali atatsala pang’ono kupereka zinthuzi nsembe. N’kutheka kuti atumwi sanadabwe kuona kuti mwambo watsopanowu unali wosavuta. Tikutero chifukwa miyezi ingapo Yesu asanayambitse mwambowu, anapita kwa anzake omwe anali Lazaro, Marita ndi Mariya. Iye anayamba kuwaphunzitsa. Marita analipo koma anatanganidwa ndi kukonza chakudya chambiri kuti mlendo wake wapaderayu adye. Yesu ataona zimenezi anamufotokozera mokoma mtima kuti sankayenera kuphika zambiri. (Luka 10:40-42) Ndiyeno Yesu atatsala pang’ono kupereka moyo wake nsembe, anatsatira malangizo amene anapatsa Marita aja. Iye anagwiritsa ntchito zinthu zochepa poyambitsa mwambo wokumbukira imfa yake. w19.01 20-21 ¶3-4
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Maliko 15:1-47
Lachinayi, April 9
Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo.—Yoh. 17:5.
Yehova analemekeza Yesu m’njira imene sankayembekezera chifukwa Baibulo limanena kuti anamupatsa “malo apamwamba” komanso anali woyamba kulandira “moyo wosakhoza kufa.” (Afil. 2:9; 1 Tim. 6:16) Apatu Yehova anasonyeza kuti ankadziwa komanso kuyamikira utumiki umene Yesu anauchita mokhulupirika. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamafune kukhala odziwika m’dzikoli? Tizikumbukira kuti nthawi zonse, Yehova amadalitsa atumiki ake okhulupirika ndipo nthawi zambiri amachita zimenezi m’njira imene sankayembekezera. Panopa palibe amene akudziwa madalitso osayembekezereka amene Yehova adzatipatse m’tsogolomu. Chongofunika panopa n’kupirira mavuto amene tingakumane nawo m’dzikoli, n’kumakumbukira kuti dzikoli litha posachedwapa. (1 Yoh. 2:17) Koma Atate wathu Yehova ‘si wosalungama woti angaiwale ntchito yathu ndi chikondi chimene timachisonyeza pa dzina lake.’—Aheb. 6:10. w18.07 11 ¶17-18
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66 (Zochitika pa Nisani 16 dzuwa litalowa) Maliko 16:1
Lachisanu, April 10
[Ndikupemphera] kuti onsewa akhale amodzi.—Yoh. 17:20, 21.
Yesu ankaganizira kwambiri za mgwirizano pamene ankadya chakudya chamadzulo chomaliza ndi atumwi ake. Popemphera nawo, ananena kuti ankafunitsitsa kuti ophunzira ake akhale ogwirizana ngati mmene iye ndi Atate wake alili. Mgwirizano wa ophunzirawo ukanapereka umboni wamphamvu wakuti Yehova ndi amene anatuma Yesu padzikoli kuti adzachite chifuniro cha Mulungu. Chikondi chinathandiza anthu kuzindikira ophunzira enieni a Yesu ndipo chinathandizanso ophunzirawo kuti akhale ogwirizana. (Yoh. 13:34, 35) M’pomveka kuti Yesu anatsindika kwambiri za mgwirizano chifukwa anaona kuti nthawi zina atumwi ake zinkawavuta kukhala mogwirizana. Ndipotu pa nthawi ya chakudya chamadzulo chomaliza chija, atumwiwo anakangananso za “amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.” (Luka 22:24-27; Maliko 9:33, 34) Pa nthawi ina, Yakobo ndi Yohane anapempha Yesu kuti awapatse malo apamwamba kwambiri okhala pafupi naye mu Ufumu wake.—Maliko 10:35-40. w18.06 8 ¶1-2
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Maliko 16:2-8
Loweruka, April 11
Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.—Gen. 2:24.
Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azikondana kwa moyo wawo wonse. (Mat. 19:3-6) Munthu akachita chigololo amasonyeza kuti alibiretu chikondi. M’pomveka kuti lamulo la nambala 7 pa Malamulo 10 linali loletsa chigololo. (Deut. 5:18) Munthu akachita chigololo amakhala kuti ‘wachimwira Mulungu’ komanso kuchitira nkhanza mkazi kapena mwamuna wake. (Gen. 39:7-9) Munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wachita chigololo zikhoza kumupweteka kwa zaka zambiri. Yehova amakondanso kwambiri ana. Yehova analamula kuti makolo azisamalira ana awo mwakuthupi komanso mwauzimu. Makolo ankafunika kuyesetsa kuthandiza ana awo kuti azidziwa bwino Chilamulo cha Yehova komanso azimukonda kwambiri. (Deut. 6:6-9; 7:13) Makolo ankayenera kuona ana awo ngati cholowa kapena kuti mphatso yochokera kwa Yehova ndipo ankayenera kuwakonda kwambiri.—Sal. 127:3. w19.02 21 ¶5, 7
Lamlungu, April 12
Mulungu adzadziwa kuti ndili ndi mtima wosagawanika.—Yobu 31:6.
Yobu ankayembekezera kuti Mulungu adzamudalitsa ndipo izi zinamuthandiza kukhalabe ndi mtima wosagawanika. Iye ankadziwa kuti Mulungu ankayamikira kuti anali ndi mtima wosagawanika. Ngakhale kuti anakumana ndi mayesero, Yobu sankakayikira kuti Yehova adzamudalitsa. N’zosachita kufunsa kuti zimenezi zinamuthandiza kukhalabe wokhulupirika. Yehova anasangalala kwambiri kuti Yobu anali ndi mtima wosagawanika moti anamudalitsa. (Yobu 42:12-17; Yak. 5:11) Ndipo m’tsogolomu adzamudalitsanso kwambiri. Mulungu wathu sanasinthe. (Mal. 3:6) Choncho kudziwa kuti Mulungu amasangalala tikakhala ndi mtima wosagawanika, kungatithandize kuti tisamakayikire kuti adzatidalitsa m’tsogolomu. (1 Ates. 5:8, 9) Tiyeni tiziyesetsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika. Nthawi zina mungamve ngati ndinu nokha amene mukuyesetsa kuchita zimenezi. Koma simuli nokha. Pali anthu mamiliyoni ambiri amene akukhalabe okhulupirika kwa Mulungu. Mukhoza kukhalanso m’gulu la amuna ndi akazi akale amene anakhalabe ndi mtima wosagawanika ngakhale pamene moyo wawo unali pa ngozi.—Aheb. 11:36-38; 12:1. w19.02 7 ¶15-16
Lolemba, April 13
Mukhale amaganizo amodzi, omverana chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu, ndiponso amaganizo odzichepetsa.—1 Pet. 3:8.
Pamene nyengo ya Chikumbutso ikudutsa, tingachite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ndingatani kuti ndizitsanzira kwambiri Yesu pa nkhani yosonyeza chikondi? Nanga kodi ndimaganizira kwambiri zofuna za Akhristu anzanga kuposa zofuna zanga? Kodi ndimayembekezera zambiri kwa abale ndi alongo anga kuposa zimene angakwanitse?’ Tiyeni nthawi zonse tizitsanzira Yesu posonyeza kuti ‘timamvera chisoni’ anzathu. Nthawi ina m’tsogolomu tidzasiya kuchita mwambo wokumbukira imfa ya Khristu. Paja Yesu akadzabwera pa chisautso chachikulu, adzasonkhanitsa odzozedwa amene adzakhale adakali padzikoli kuti apite kumwamba. Apa m’pamene tidzasiyire kuchita Chikumbutso. (1 Akor. 11:26; Mat. 24:31) Koma ngakhale titadzasiya kuchita mwambowu, tizidzakumbukirabe mfundo yakuti mwambo wosavutawu unkasonyeza kuti Yesu anali wodzichepetsa, wolimba mtima komanso wachikondi kuposa munthu wina aliyense. w19.01 25 ¶17-19
Lachiwiri, April 14
Taonani! Mumakondwera ndi choonadi chochokera pansi pa mtima. Ndipo mundidziwitse nzeru mumtima mwanga.—Sal. 51:6.
Kuti timvetse za munthu wathu wamkati, tiyeni tikambirane za thupi lathu lenileni. Choyamba, kuti tikhale athanzi timafunika kudya chakudya chabwino komanso kuchita masewera olimbitsa thupi. N’chimodzimodzinso ndi munthu wathu wamkati. Kuti tikhale athanzi timafunika chakudya chauzimu komanso kuchita zinthu zosonyeza kuti timakhulupirira Yehova. Mwachitsanzo, tiyenera kutsatira zimene timaphunzira komanso kuuza anthu ena zimene timakhulupirira. (Aroma 10:8-10; Yak. 2:26) Chachiwiri, munthu akhoza kuoneka kuti ndi wathanzi koma mkati mwa thupi lake ali ndi matenda. Mofanana ndi zimenezi, tingaganize kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa choti timachita zinthu zokhudza kulambira koma mumtima mwathu titayamba kulakalaka zinthu zoipa. (1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15) Tiyenera kukumbukira kuti Satana amafuna kutisokoneza kuti tiziyendera maganizo ake. w19.01 15 ¶4-5
Lachitatu, April 15
Pita, iwenso uzikachita zomwezo.—Luka 10:37.
Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimachita zinthu ngati mmene anachitira Msamariya wachifundo uja?’ (Luka 10:30-35) ‘Kodi pali zinthu zinanso zimene ndingachite pothandiza anthu amene akuvutika? Nanga ndingathandize bwanji Akhristu achikulire, amasiye komanso amene makolo awo si Mboni? Kodi ndingamayesetse kulankhula “molimbikitsa kwa amtima wachisoni”?’ (1 Ates. 5:14; Yak. 1:27) Tikamachitira anthu chifundo timapeza chimwemwe chomwe chimabwera chifukwa chopatsa. Komanso timadziwa kuti zimene tikuchitazo zimasangalatsa Yehova. (Mac. 20:35; Aheb. 13:16) Ponena za munthu amene amaganizira anzake, Mfumu Davide ananena kuti: “Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo. Adzatchedwa wodala padziko lapansi.” (Sal. 41:1, 2) Tikamachitira anthu chifundo, Yehova adzatichitiranso chifundo ndipo zimenezi zidzatithandiza kukhala osangalala mpaka muyaya.—Yak. 2:13. w18.09 19-20 ¶11-12
Lachinayi, April 16
Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.—Yes. 41:10.
Mlongo wina wokhulupirika dzina lake Yoshiko anauzidwa ndi dokotala kuti wangotsala ndi miyezi yochepa kuti amwalire. Kodi mlongoyu anatani? Iye anakumbukira lemba limene ankalikonda kwambiri, lomwe ndi la lero. Kenako anauza dokotalayo mtima uli m’malo kuti sakuopa chilichonse chifukwa Yehova anali atagwira dzanja lake. Mawu olimbikitsa amulembali anathandiza mlongoyu kuti azidalira kwambiri Yehova. Vesili lingatithandizenso ifeyo kuti tisamade nkhawa tikakumana ndi mavuto aakulu. Poyamba, Yehova anauza Yesaya kuti alembe mawu amenewa n’cholinga choti alimbikitse Ayuda amene anadzatengedwa kupita ku ukapolo wa ku Babulo. Koma Yehova analola kuti mawuwa asungidwebe kuti azilimbikitsanso anthu ake ena mpaka masiku ano. (Yes. 40:8; Aroma 15:4) Panopa tikukhala ‘m’nthawi yovuta’ ndipo kuposa kale lonse, tikufunika kulimbikitsidwa ndi mawu a m’buku la Yesaya.—2 Tim. 3:1. w19.01 2 ¶1-2
Lachisanu, April 17
Ngati wosakhulupirirayo wachoka, achoke.—1 Akor. 7:15.
Anthu akapatukana amakhalabe kuti ali pa banja. Choncho akakhala kosiyana amakumana ndi mavuto. Mtumwi Paulo anatchula chifukwa chimenechi kuti n’chimene chimachititsa kuti anthu ena azikhalabe m’banja lamavuto. Iye anati: “Mwamuna wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wake, ndiponso mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha m’baleyo, apo ayi, ana anu akanakhala osayera, koma tsopano ndi oyera.” (1 Akor. 7:14) Akhristu ambiri okhulupirika anasankha kuti asapatukane ndi amuna kapena akazi awo ngakhale kuti m’banja mwawo munali mavuto aakulu. Iwo anasangalala kwambiri kuti anachita zimenezi chifukwa zinathandiza kuti mnzawoyo asinthe n’kukhala wa Mboni. (1 Akor. 7:16; 1 Pet. 3:1, 2) M’mipingo yapadziko lonse, muli mabanja ambiri amene akuyenda bwino. N’zosachita kufunsa kuti mumpingo wanunso muli mabanja ambiri osangalala. M’mabanja oterewa muli abale okhulupirika amene amakonda akazi awo komanso akazi achikondi amene amalemekeza amuna awo. Ndipo onsewa amasonyeza kuti amalemekeza ukwati.—Aheb. 13:4. w18.12 14 ¶18-19
Loweruka, April 18
Yehova Mulungu anakonza munda ku Edeni, ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumbayo.—Gen. 2:8.
Mawu oti Edeni amatanthauza “Chisangalalo” ndipo n’zoona kuti mundawo unali wosangalatsa. Munali chakudya cha mwanaalirenji, malo okongola kwambiri komanso nyama zambiri zoti munthu akhoza kusangalala nazo. (Gen. 1:29-31) Mawu achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito pomasulira mawu achiheberi akuti munda ndi akuti pa·raʹdei·sos. Buku lina lofotokoza zinthu za m’Baibulo lolembedwa ndi M’Clintock komanso Strong limanena za mawu amenewa kuti: “Ndi malo aakulu otetezeka, okongola komanso osawonongedwa. Amakhala ndi mitengo yam’tchire ndipo mitengo yambiri imakhala ya zipatso. Mumakhala mitsinje yabwino ndipo m’mbali mwa mitsinjeyo mumapezeka agwape kapena nkhosa zambiri. Izi n’zimene munthu wachigiriki angaganize akamva za paradaiso.” (Gen. 2:15, 16) Mulungu anaika Adamu ndi Hava m’paradaiso koma iwo anathamangitsidwamo chifukwa chosamvera. Izi zinachititsa kuti iwo ndi ana awo onse asakhalenso m’paradaiso. (Gen. 3:23, 24) Ngakhale kuti mu Edeni simunkakhala anthu, mundawu unali ulipobe mpaka m’masiku a Nowa, pamene chigumula chinafika. w18.12 3-4 ¶3-5
Lamlungu, April 19
Ine Yehova ndine . . . amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.—Yes. 48:17.
Makolo amayesetsa kuthandiza ana awo kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Anawo akatsatira mfundo zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo, akhoza kumasankha komanso kuchita zinthu zimene sanganong’oneze nazo bondo. Izi zingawathandize kuti apewe mavuto komanso zinthu zodetsa nkhawa. Yehova ali ngati kholo labwino chifukwa amafuna kuti ana akefe tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. (Yes. 48:18) Choncho amatiphunzitsa kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso tiziganizira anzathu. Ndiye amafuna kuti tiziyendera maganizo ake pa nkhani imeneyi. Zimenezi sizitipanikiza ayi, koma zimangotithandiza kuti tikhale ndi maganizo abwino komanso apamwamba. (Sal. 92:5; Miy. 2:1-5; Yes. 55:9) Zimatithandiza kusankha zinthu zimene tingasangalale nazo koma pa nthawi imodzimodziyo tikugwiritsa ntchito ufulu wathu. (Sal. 1:2, 3) Kunena zoona, kuyendera maganizo a Yehova n’kwabwino komanso kothandiza. w18.11 19-20 ¶7-8
Lolemba, April 20
Amakunyozani.—1 Pet. 4:4.
Kuti tipitirize kuyenda m’choonadi tiyenera kupewa kumangotengera zochita za anzathu. Titangophunzira kumene choonadi, kachezedwe kathu ndi anzathu komanso achibale omwe si Mboni kanasintha. Anzathu ena anazivomereza mosavuta koma ena ankatitsutsa kwambiri. Achibale athu, anzathu akuntchito kapena akusukulu angafune kuti tichite nawo miyambo ina. Kodi tingapewe bwanji kuchita nawo miyambo ndi zikhalidwe zimene Mulungu amadana nazo? Chimene chingatithandize ndi kukumbukira mmene Yehova amaonera zinthuzo. Ndi bwino kuonanso nkhani za m’mabuku athu zofotokoza mmene maholide osiyanasiyana anayambira. Kukumbukira zifukwa za m’Malemba zimene zingatithandize kuti tizipewa maholidewa kumatithandiza kutsimikiza mumtima mwathu kuti tikuchita zinthu ‘zovomerezeka kwa Ambuye.’ (Aef. 5:10) Kukhulupirira Yehova ndiponso Mawu ake kumatithandiza kuti tisamaope anthu.—Miy. 29:25. w18.11 11 ¶10, 12
Lachiwiri, April 21
Yehova anali ndi Yosefe, ndipo chilichonse chimene iye anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.—Gen. 39:23.
Zinthu zikasintha mwadzidzidzi pa moyo wathu, tikhoza kudera nkhawa kwambiri zam’tsogolo mpaka kufika pongogwa ulesi. Zimenezi zikanatha kuchitikira Yosefe. Koma iye anayesetsa kuchita zimene akanatha kuti asangalatse Yehova ndipo anadalitsidwa. Ngakhale pamene anali kundende, Yosefe ankagwira mwakhama ntchito iliyonse imene anapatsidwa ndi mkulu wa ndende, ngati mmene ankachitira ali kwa Potifara. (Gen. 39:21-22) Mofanana ndi Yosefe, tikhoza kukumana ndi mavuto amene sitingawathetse. Koma ngati tingakhale oleza mtima n’kumachita zimene tingathe posangalatsa Yehova, iye adzatidalitsa. (Sal. 37:5) N’zoona kuti nthawi zina tikhoza kusokonezeka maganizo n’kumada nkhawa, koma mogwirizana ndi mawu a Paulo, ‘sitingasoweretu pothawira.’ (2 Akor. 4:8) Zimene Paulo ananenazi zikhoza kutichitikira, makamaka ngati timachita khama mu utumiki. w18.10 29 ¶11, 13
Lachitatu, April 22
Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.—Aheb. 6:10.
Kodi mumamva bwanji ngati munthu amene mumamudziwa komanso kumulemekeza waiwala dzina lanu kapena sakukuzindikirani n’komwe? Zimenezi zingakhale zokhumudwitsa. Tikutero chifukwa chakuti mwachibadwa anthufe timafuna kuti tizikondedwa. Timafuna kuti anthu azitizindikira komanso kukumbukira zimene tachita pa moyo wathu. (Num. 11:16; Yobu 31:6) Koma mofanana ndi zinthu zina zimene timafuna mwachibadwa, n’zotheka kukhala ndi maganizo olakwika pa nkhani yofuna kudziwika kapena kuyamikiridwa ndi anthu ena. Popeza si ife angwiro, tingafune kudziwika m’njira yolakwika. Dziko la Satanali limalimbikitsa mtima wofuna kudziwika kwambiri umene umalepheretsa anthu kulemekeza komanso kulambira Atate wathu Yehova Mulungu.—Chiv. 4:11. w18.07 7 ¶1-2
Lachinayi, April 23
Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.—1 Yoh. 5:19.
N’chifukwa chake sitidabwa kuti Satana ndi ziwanda amachititsa anthu amene ali ndi maudindo m’dzikoli kuti ‘azilankhula mabodza.’ (1 Tim. 4:1, 2) Atsogoleri achipembedzo amene amalankhula mabodza ali ndi mlandu waukulu chifukwa amawononga tsogolo la anthu amene amawakhulupirira. Zili choncho chifukwa munthu akakhulupirira mabodza awo n’kumachita zinthu zimene Mulungu amadana nazo, sadzalandira moyo wosatha. (Hos. 4:9) Yesu ankadziwa kuti atsogoleri a munthawi yake ankanamiza anthu. Paja anawauza kuti: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumatha mitunda kuti mukatembenuze munthu mmodzi, koma akatembenuka mumam’sandutsa woyenera kuponyedwa m’Gehena [kapena kuti kuwonongedweratu] kuposa inuyo.” (Mat. 23:15, mawu am’munsi) Apatu Yesu anadzudzula atsogoleriwo mwamphamvu kwambiri. Iwo anachokeradi ‘kwa atate wawo Mdyerekezi, yemwe ndi wopha anthu.’—Yoh. 8:44. w18.10 7 ¶5-6
Lachisanu, April 24
Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani . . . chifukwa cha ine.—Mat. 5:11.
Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Iye anapitiriza kuti: “Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:12) Atumwi atamenyedwa komanso kulamulidwa kuti asiye kulalikira, “anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala.” N’zoona kuti kumenyedwa sikunawasangalatse. Koma anasangalala “chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” (Mac. 5:41) Masiku anonso anthu a Yehova amakhalabe osangalala akamazunzidwa chifukwa cha dzina la Yesu kapena akamakumana ndi mayesero aakulu kwambiri. (Yak. 1:2-4) Sikuti timasangalala ndi mavuto. Koma tikakhalabe okhulupirika kwa Mulungu pa nthawi ya mavuto, Yehova amatithandiza kuti tipirire mosangalala. Tikamasangalatsa “Mulungu wachimwemwe,” timakhalabe osangalala ngakhale kuti tikuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chathu kapena kutsutsidwa ndi anthu a m’banja lathu.—1 Tim. 1:11. w18.09 21 ¶18-20
Loweruka, April 25
Amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.—Sal. 90:10.
Popeza moyo wa masiku ano ndi ‘wodzaza ndi mavuto ndi zopweteka,’ anthu ambiri amakhala ndi nkhawa ndipo ambiri amaganiza kuti bola kungofa. (2 Tim. 3:1-5) Kafukufuku amasonyeza kuti anthu oposa 800,000 amadzipha chaka chilichonse. Choncho tingati munthu mmodzi amadzipha pa masekondi 40 alionse. N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale Akhristu ena amadzipha chifukwa chopanikizika ndi mavuto. Ngakhale abale ndi alongo amene sakufuna kufa amafunikirabe kulimbikitsidwa mwachikondi chifukwa cha mavuto awo. Zili choncho chifukwa ena amazunzidwa komanso kunyozedwa. Pomwe ena amavutika kuntchito chifukwa choti anzawo amawatsutsa kapena kuwajeda. Apo ayi, amakhala otopa chifukwa chogwira ntchito kwa maola ambiri kapena mopanikizika. Komanso ena amakumana ndi mavuto a m’banja monga kutsutsidwa ndi mwamuna kapena mkazi wawo amene si Mboni. Mavuto ngati amenewa amachititsa anthu ambiri mumpingo kuti azikhala otopa komanso ankhawa. w18.09 13 ¶3, 5
Lamlungu, April 26
Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.—3 Yoh. 4.
Makolo amagwiranso ntchito ndi Yehova akamathandiza ana awo kuti akhale ndi zolinga zofuna kumutumikira. Ana ambiri amene makolo awo anachita zimenezi anasamukira kutali ndi kwawo. Ena mwa iwo ndi amishonale, ena akuchita upainiya m’gawo limene kukufunika ofalitsa ambiri ndipo ena akutumikira pa Beteli. N’kutheka kuti ana amene akutumikira kutali ndi makolo awo sangamacheze nawo pafupipafupi ngati mmene angafunire. Komabe, makolo amene amaika kutumikira Yehova pamalo oyamba amalimbikitsa ana awo kuti asasiye utumiki wawo. Zili choncho chifukwa chakuti amasangalala kwambiri podziwa kuti ana awowo akuika za Ufumu pamalo oyamba. Mwina ambiri mwa makolowa amamva ngati mmene Hana ankamvera. Iye ankaona kuti ‘anapereka’ mwana wake, Samueli, kwa Yehova. Choncho makolowo amaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kulola kuti ana awo azitumikira Yehova ndipo sangafune kuti asiye utumiki wawowo.—1 Sam. 1:28. w18.08 24 ¶4
Lolemba, April 27
Zidzakhalatu zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu ufumu wakumwamba.—Mat. 19:23.
Yesu sananene kuti n’zosatheka. Iye ananenanso kuti: “Odala ndinu osaukanu, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.” (Luka 6:20) Koma sankatanthauza kuti anthu onse osauka anali odala ndipo ankamvetsera uthenga wake. Osauka ambiri anakana kumvetsera uthenga wa Yesu. Apatu mfundo ndi yakuti, Sitinganene kuti munthu ali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kapena ayi potengera zinthu zimene ali nazo. Chosangalatsa n’chakuti m’gulu lathu muli abale ndi alongo ambiri, olemera komanso osauka, omwe amatumikira Yehova ndi mtima wonse. Malemba amauza anthu olemera kuti “asamadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu.” (1 Tim. 6:17-19) Baibulo limalimbikitsanso anthu a Mulungu, kaya akhale olemera kapena osauka, kuti asamakonde ndalama. (1 Tim. 6:9, 10) Kunena zoona tikamayesetsa kuona abale athu ngati mmene Yehova amawaonera, sitingayambe kuweruza anthu potengera kusauka kapena kulemera kwawo. w18.08 10-11 ¶11-12
Lachiwiri, April 28
Gonjerani Mulungu.—Yak. 4:7.
Tiyenera kuyesetsa kusonyeza kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa mwayi wokhala anthu ake. Tiyeneranso kuona kuti popeza ndife anthu ake, ndi nzeru kudzipereka kwa iye. Komanso tiyenera kukaniratu kuchita zinthu zoipa. Tiyeneranso kukonda ndiponso kulemekeza Akhristu anzathu podziwa kuti nawonso ndi anthu a Yehova. (Aroma 12:10) Baibulo limalonjeza kuti: “Yehova sadzataya anthu ake.” (Sal. 94:14) Lonjezoli lidzakwaniritsidwa ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Ngakhale imfa singatisiyanitse ndi chikondi cha Yehova. (Aroma 8:38, 39) Paja Baibulo limanena kuti: “Kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Tonsefe timalakalaka nthawi imene Yehova adzaukitse anthu onse amene anamwalira omwe anali anzake okhulupirika. (Mat. 22:32) Koma ngakhale panopa timapeza madalitso ambiri. Baibulo limanena kuti: “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.”—Sal. 33:12. w18.07 26 ¶18-19
Lachitatu, April 29
Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu. Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zolimbikitsa.—1 Akor. 10:23.
Anthu ena amaganiza kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha pa nkhani ngati maphunziro ndi ntchito malinga ngati chikumbumtima chake chikumulola. Mwina amaona kuti nkhaniyi ikufanana ndi nkhani ya chakudya imene Paulo anauza Akhristu a ku Korinto. Paja ananena kuti: “N’chifukwa chiyani ufulu wanga ukulamulidwa ndi chikumbumtima cha munthu wina?” (1 Akor. 10:29) N’zoona kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha pa nkhani zimenezi. Koma kumbukirani kuti ufulu umene timapatsidwa uli ndi malire ake ndipo chilichonse chimene timasankha chimakhala ndi zotsatira zake. N’chifukwa chake Paulo anayamba mawu akewa ndi mawu amulemba la lero. Mfundo imeneyi ingatithandize kuona kuti munthu asanasankhe zochita pa nkhani ngati zimenezi ayenera kuganizira kaye zinthu zina zofunika kwambiri. w18.04 10 ¶10
Lachinayi, April 30
Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu.—Mal. 3:7.
Masiku ano Mkhristu akhoza kumanena kuti amalambira Yehova koma kwinaku akuyenda panjira yolakwika. (Yuda 11) Mwachitsanzo, akhoza kukhala ndi mtima wadyera, wolakalaka chiwerewere kapena wokwiyira Mkhristu mnzake. (1 Yoh. 2:15-17; 3:15) Mtimawu ukhoza kuchititsa kuti tsiku lina adzachite tchimo. Zimenezi zikhoza kuchitika ngakhale kuti munthuyo amachita bwinobwino zinthu monga kulalikira ndi kupezeka pamisonkhano nthawi zonse. N’zoona kuti anthu ena sangadziwe zimene zili mumtima mwathu koma Yehova amadziwa zonse ndipo sangalephere kudziwa ngati sitili kumbali yake ndi mtima wonse. (Yer. 17:9, 10) Chosangalatsa n’chakuti Yehova safulumira kutiona kuti ndife okanika. Anthu akayamba kuyenda panjira yolakwika, Yehova amawauza kuti: “Bwererani kwa ine.” Tikakhala ndi vuto linalake, Yehova amafuna kuti tizichita khama poyesetsa kupewa zoipa. (Yes. 55:7) Tikamatero, iye amatithandiza kuti tikhale olimba mwauzimu, tisasokonezeke maganizo komanso tipeze mphamvu zotithandiza kugonjetsa maganizo ofuna kuchita zoipa.—Gen. 4:7. w18.07 18 ¶5-6