Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • es20 47-57
  • May

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • May
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
  • Timitu
  • Lachisanu, May 1
  • Loweruka, May 2
  • Lamlungu, May 3
  • Lolemba, May 4
  • Lachiwiri, May 5
  • Lachitatu, May 6
  • Lachinayi, May 7
  • Lachisanu, May 8
  • Loweruka, May 9
  • Lamlungu, May 10
  • Lolemba, May 11
  • Lachiwiri, May 12
  • Lachitatu, May 13
  • Lachinayi, May 14
  • Lachisanu, May 15
  • Loweruka, May 16
  • Lamlungu, May 17
  • Lolemba, May 18
  • Lachiwiri, May 19
  • Lachitatu, May 20
  • Lachinayi, May 21
  • Lachisanu, May 22
  • Loweruka, May 23
  • Lamlungu, May 24
  • Lolemba, May 25
  • Lachiwiri, May 26
  • Lachitatu, May 27
  • Lachinayi, May 28
  • Lachisanu, May 29
  • Loweruka, May 30
  • Lamlungu, May 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
es20 47-57

May

Lachisanu, May 1

Muzikonda mlendo wokhala pakati panu.—Deut. 10:19.

Masiku ano, anthu ambiri amathawa kwawo n’kusamukira m’mayiko ena. Mwina mungayambe ndi kuphunzira moni wa chilankhulo cha anthu amene asamukira m’dera lanu. Mwinanso mungaphunzire mawu ena amene angathandize kuti muyambe kucheza nawo. Kenako mungawasonyeze mavidiyo ndi mabuku achilankhulo chawo pa jw.org. Chifukwa chotikonda, Yehova watipatsa msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu kuti uzitithandiza kulalikira mogwira mtima. Zimene timaphunzira pamisonkhanoyi zimatithandiza kuti tisamadzikayikire pochita maulendo obwereza kapena pophunzitsa anthu Baibulo. Makolo angachite bwino kuthandiza ana kuti azipereka ndemanga m’mawu awoawo. Anthu ena anayamba kuphunzira choonadi chifukwa chomva ana akuyankha mwachidule koma kuchokera mumtima.​—1 Akor. 14:25. w18.06 22-23 ¶7-9

Loweruka, May 2

Landiranani, monga mmene Khristu anatilandirira.—Aroma 15:7.

Ndi bwino kukumbukira kuti pa nthawi ina tonsefe tinali ngati “alendo osadziwika” kwa Mulungu. (Aef. 2:12) Koma Yehova anatisonyeza chikondi ‘potikokera’ kwa iye. (Hos. 11:4; Yoh. 6:44) Ndipotu Khristu anatilandira bwino. Zili ngati iye anatitsegulira chitseko kuti tilowe m’banja la Mulungu. Popeza Yesu watilandira ngakhale kuti si ife angwiro, si nzeru kukana kulandira anthu ena. Pamene mapeto akuyandikira, tsankho ndi chidani ziziwonjezereka m’dzikoli. (Agal. 5:19-21; 2 Tim. 3:13) Koma atumiki a Yehovafe timayendera nzeru yochokera kumwamba yomwe ndi yopanda tsankho komanso yolimbikitsa mtendere. (Yak. 3:17, 18) Timasangalala kukhala ndi anzathu ochokera kumayiko ena ngakhale kuti ndife osiyana chikhalidwe. Nthawi zina timayesetsanso kuphunzira zilankhulo zawo. Tikamachita zimenezi mtendere wathu umakhala ngati mtsinje ndipo chilungamo chathu chimakhala ngati mafunde a m’nyanja.​—Yes. 48:17, 18. w18.06 12 ¶18-19

Lamlungu, May 3

Mapazi anu [muwaveke] nsapato zokonzekera uthenga wabwino wamtendere.​—Aef. 6:15.

Ngati msilikali wachiroma sanavale nsapato zake, sankakhala wokonzeka kupita kunkhondo. Popanga nsapatozi, ankaphatikiza zikopa zitatu. Zimenezi zinkathandiza kuti zizikhala zolimba komanso kuti zisamapweteke akamayenda nazo. Nsapato zimene asilikaliwa ankavala zinkawathandiza kuti akhale okonzeka kukamenya nkhondo. Nazonso nsapato zophiphiritsa zimene Akhristu amavala zimawathandiza kuti azikhala okonzeka kulengeza uthenga wamtendere. (Yes. 52:7; Aroma 10:15) Ngakhale zili choncho, timafunika kulimba mtima kuti tilalikire. Mnyamata wina wazaka 20 dzina lake Bo anati: “Ndinkachita mantha kuti ndizilalikira anzanga kusukulu. Ndikuona kuti vuto langa linali manyazi. Sindikudziwa chifukwa chake ndinkamva choncho. Koma panopa ndimasangalala kulalikira anzanga.” Achinyamata ambiri amaona kuti sizimawavuta kulalikira ngati akonzekera bwino. w18.05 29 ¶9-11

Lolemba, May 4

[Pitirizani] kubala zipatso zambiri.​—Yoh. 15:8.

Yesu anauza atumwi ake kuti: “Ndikupatsani mtendere wanga.” (Yoh. 14:27) Kodi mtenderewo umatithandiza bwanji kubereka zipatso? Tikamapirira, timamva mtendere wamumtima chifukwa chodziwa kuti tikusangalatsa Yehova ndiponso Yesu. (Sal. 149:4; Aroma 5:3, 4; Akol. 3:15) Yesu atauza atumwi ake kuti akufuna kuti ‘chimwemwe chawo chisefukire,’ anawafotokozera kufunika kosonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. (Yoh. 15:11-13) Kenako ananena kuti: “Ndakutchani mabwenzi.” Kukhala anzake a Yesu ndi mphatso yamtengo wapatali. Koma kodi atumwi ankayenera kuchita chiyani kuti akhalebe anzake? Iwo ankayenera ‘kupitiriza kubala zipatso.’ (Yoh. 15:14-16) Zaka pafupifupi ziwiri asananene zimenezi, Yesu anauza atumwi ake kuti: “Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’” (Mat. 10:7) Choncho usiku woti aphedwa mawa lake anawalimbikitsa kuti apirire pochita ntchito imene anali atayamba kale.​—Mat. 24:13; Maliko 3:14. w18.05 20-21 ¶15-16

Lachiwiri, May 5

Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.​—Agal. 6:7.

Ngati ndinu achinyamata, muyenera kukhala ndi cholinga chosangalatsa Yehova nthawi zonse. Taona kuti izi zingatheke ngati mutakhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa. Mwina mumaona achinyamata ena amene amangoganizira zonjoya basi ndipo nthawi zina amafuna kuti muzichita nawo zimene amachita. Choncho mungafunike kusonyeza kuti muli ndi zolinga zanu zimene mukufunitsitsa kuzikwaniritsa. Musalole kuti anzanu akusokonezeni. Pali zinthu zingapo zimene zingakuthandizeni kuti musasokonezedwe ndi anzanu. Choyamba, muzipewa kupezeka pamalo amene mungayesedwe. (Miy. 22:3) Muzikumbukiranso mavuto amene mungakumane nawo chifukwa chongotengera makhalidwe oipa a anzanu. Chinthu china chimene chingakuthandizeni n’kuzindikira kuti mumafunika malangizo. Ngati ndinu odzichepetsa mudzalola kuti makolo anu kapena abale ndi alongo odziwa zambiri akupatseni malangizo. (1 Pet. 5:5, 6) Kodi inuyo muli ndi mtima wodzichepetsa moti mungamvere malangizo abwino? w18.04 28-29 ¶14-16

Lachitatu, May 6

Gwirani mwamphamvu . . . , zimene muli nazo, mpaka nditabwera. Ndipo amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu.​—Chiv. 2:25, 26.

Yesu anayamikiranso zimene otsatira ake ankachita m’mipingo ya ku Asia Minor. Mwachitsanzo, anayamba uthenga wake wopita kumpingo wa ku Tiyatira ndi mawu akuti: “Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.” (Chiv. 2:19) Yesu anayamikira ntchito zawo komanso makhalidwe amene anawachititsa kuti agwire ntchitozo. Ngakhale kuti iye ankafunika kuwapatsa malangizo, anayamba ndiponso kumaliza uthenga wake ndi mawu olimbikitsa. (Chiv. 2:27, 28) Yesu ali ndi udindo waukulu chifukwa ndi mutu wa mipingo yonse. Choncho sikuti amafunika kutithokoza chifukwa cha ntchito imene timagwira. Ngakhale zili choncho, amayesetsa kutiyamikira. Kunena zoona, iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa akulu. w19.02 16 ¶10

Lachinayi, May 7

Yudasi ndi Sila . . . analimbikitsa abalewo ndi mawu ambiri ndipo anawapatsa mphamvu.​—Mac. 15:32.

M’nthawi ya atumwi, bungwe lolamulira linkalimbikitsa oyang’anira komanso Akhristu ena onse. Mwachitsanzo, pamene Filipo ankalalikira za Khristu kwa Asamariya, abale a m’bungwe lolamulira anamuthandiza kwambiri. Anatumiza Petulo ndi Yohane kuti apite kukapempherera Akhristu atsopano kuti alandire mzimu woyera. (Mac. 8:5, 14-17) Filipo komanso Akhristu atsopanowo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kuona zimene bungwe lolamulira linachitazo. Masiku anonso, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limalimbikitsa atumiki a pa Beteli, atumiki apadera ena komanso abale ndi alongo padziko lonse. Mofanana ndi nthawi ya atumwi, abale ndi alongo amasangalala kwambiri akalimbikitsidwa chonchi. Mu 2015, Bungwe Lolamulira linatulutsanso kabuku kakuti Bwererani kwa Yehova, komwe kalimbikitsa anthu ambiri padziko lonse. w18.04 19 ¶18-20

Lachisanu, May 8

Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.​—Yoh. 8:32.

Anthu ambiri amaganiza kuti munthu amasangalala ngati wapatsidwa ufulu wambiri. Koma zoona zake ndi zakuti munthu akakhala ndi ufulu wopanda malire amakhala ngati ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse. Kodi mukuganiza kuti dzikoli likanafika pati zikanakhala kuti aliyense ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna? Pa nkhaniyi, buku lina linati: “Malo alionse amakhala ndi malamulo amitundumitundu omwe amathandiza kuti anthu azikhala ndi ufulu wochita zinazake komanso aziletsedwa kuchita zinthu zina.” (The World Book Encyclopedia) M’pake kuti bukuli linati pali malamulo amitundumitundu chifukwa kunja kuno anthu alemba mabuku ambirimbiri a malamulo. Amalembanso ntchito maloya ndi oweruza milandu ankhaninkhani n’cholinga choti azithandiza anthu kumvetsa komanso kutsatira malamulowo. Yesu anasonyeza kuti pali zinthu ziwiri zofunika kuti munthu apeze ufulu weniweni. Choyamba, munthuyo ayenera kutsatira mfundo zachoonadi zimene Yesu ankaphunzitsa. Chachiwiri, ayenera kukhala wophunzira wake. Munthu akachita zimenezi amakhaladi pa ufulu weniweni. Koma kodi ufulu wake umakhala wotani? Yesu anapitiriza kuti: “Aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimo. . . . Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.”​—Yoh. 8:34, 36. w18.04 6-7 ¶13-14

Loweruka, May 9

Nonsenu mukhale . . . omverana chisoni.​—1 Pet. 3:8.

Anthufe timasangalala tikakhala ndi anthu amene amatiganizira. Anthuwo amaganizira mmene iwowo akanamvera zikanakhala kuti vuto lathulo akumana nalo ndi iwowo, n’kuzindikira zimene tikuganiza komanso mmene tikumvera. Iwo amazindikira zimene tingafunikire ndipo amatithandiza ngakhale tisanawapemphe. Mwachidule, tingati timayamikira kukhala ndi anthu amene amachita zinthu moganizira ena kapena kuti mowamvera chisoni. Akhristufe timafunika kuchita zinthu moganizira ena. Koma kuti tichite zimenezi pamafunika khama. Tikutero chifukwa chakuti anthufe si angwiro. (Aroma 3:23) Choncho timafunika kulimbana ndi mtima womangoganizira zofuna zathu. Enafe tingavutike kuchita zinthu moganizira ena chifukwa cha mmene tinakulira kapena chifukwa cha mavuto amene tinakumana nawo. Tingalepherenso kuchita zimenezi chifukwa choti tili m’dziko limene anthu ambiri saganizira anzawo. M’masiku otsiriza ano, anthu ambiri ndi “odzikonda” ndipo amangoganiza za iwo okha basi. (2 Tim. 3:1, 2) Tikhoza kuchita zinthu moganizira ena tikamatsanzira Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. w19.03 14 ¶1-3

Lamlungu, May 10

Uteteze mtima wako.​—Miy. 4:23.

Lamulo lomaliza pa Malamulo 10 linali loletsa kusirira, kapena kulakalaka zinthu za munthu wina. (Deut. 5:21; Aroma 7:7) Yehova anapereka lamuloli pofuna kuphunzitsa anthu kuti ayenera kuteteza mitima yawo kapena maganizo awo. Iye amadziwa kuti zoipa zimene anthu amachita zimayambira mumtima. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Davide. Nthawi zambiri iye ankachita zabwino. Koma nthawi ina anayamba kusirira mkazi wa munthu wina ndipo kenako anachimwa. (Yak. 1:14, 15) Paja Davide anachita chigololo, anayesetsa kupusitsa mwamuna wa mkaziyo kenako anakonza zoti mwamunayo aphedwe. (2 Sam. 11:2-4; 12:7-11) Yehova samangoona maonekedwe athu koma amaonanso zimene zili mumtima mwathu. (1 Sam. 16:7) Sitingabisire Yehova chilichonse chimene tikuganiza, kulakalaka kapena kuchita. Iye amayang’ana zabwino zimene timachita ndipo amatilimbikitsa kuchita zabwinozo. Koma amafunanso kuti tizindikire zinthu zoipa zimene tayamba kuganizira n’kusiya kuziganizira tisanafike pochita zoipazo.​—2 Mbiri 16:9; Mat. 5:27-30. w19.02 21 ¶9; 22 ¶11

Lolemba, May 11

Bwerani kwa Yehova, inu nonse ofatsa a padziko lapansi . . . Yesetsani kukhala ofatsa.​—Zef. 2:3.

Baibulo limanena kuti Mose “anali munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anali munthu wopepera, wamantha komanso wovutika kusankha zochita? Ena amaganiza kuti munthu wofatsa amakhala wotero koma si zoona. Mose ankachita zinthu mwamphamvu potumikira Mulungu ndipo anali wolimba mtima komanso wodziwa zoyenera kuchita. Yehova anamuthandiza kuti alimbe mtima n’kukakumana ndi Farao, kutsogolera anthu pafupifupi 3 miliyoni kudutsa m’chipululu komanso kuthandiza Aisiraeli kugonjetsa adani awo. N’zoona kuti sitingakumane ndi zimene Mose anakumana nazo, koma tsiku lililonse timakumana ndi anthu kapena zinthu zimene zingatilepheretse kukhala ofatsa. Ngakhale zili choncho, pali chifukwa chomveka chotichititsa kuyesetsa kuti tikhale ofatsa. Paja Yehova walonjeza kuti “anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi.” (Sal. 37:11) Ndiye kodi inuyo mumaona kuti ndinu munthu wofatsa? Nanga anthu ena anganene kuti ndinu ofatsa? w19.02 8 ¶1-2

Lachiwiri, May 12

Tsoka kwa amene akunena kuti . . . choipa n’chabwino.​—Yes. 5:20.

Anthu akhala ali ndi chikumbumtima kungoyambira pamene analengedwa. Mwachitsanzo, Adamu ndi Hava ataphwanya lamulo la Yehova anabisala. Zimenezi zikusonyeza kuti chikumbumtima chawo chinkawavutitsa. Anthu amene chikumbumtima chawo sichinaphunzitsidwe bwino amakhala ngati munthu woyendetsa sitima yapamadzi amene kampasi yake sikugwira bwino ntchito. Ndipo munthu akhoza kusochera ngati akuyenda panyanja opanda kampasi yolondola. Mphepo komanso mafunde zingachititse kuti sitimayo iyambe kulowera kolakwika. Koma kampasi yomwe ikugwira bwino ntchito ingathandize woyendetsa sitima kuti asasochere. Chikumbumtima chathu chilinso ngati kampasi yothandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Chimakhala ngati munthu wathu wamkati amene amatiuza kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika ndipo chingatithandize kuti tizichita zinthu zoyenera. Koma kuti chikumbumtimacho chizitithandiza, tiyenera kuchiphunzitsa bwino. Ngati munthu sanaphunzitse bwino chikumbumtima chake, sichingamuletse kuchita zoipa. (1 Tim. 4:1, 2) Zikatero, munthuyo akhoza kuyamba kuona kuti ‘zoipa ndi zabwino.’ w18.06 16 ¶1-3

Lachitatu, May 13

Musamatengere nzeru za nthawi ino.​—Aroma 12:2.

Tiyenera kukhalanso osamala kuti tisayambe kutengera maganizo olakwika m’njira zovuta kuzizindikira. Mwachitsanzo, nkhani za pa wailesi kapena munyuzi zingafotokozedwe m’njira yokomera maganizo enaake pa nkhani ya ndale. Nkhani zina zimatilimbikitsa kuchita zimene anthu a m’dzikoli amaona kuti n’zabwino. Mabuku ndi mafilimu ena amalimbikitsa mtima wongodziganizira kapena woganizira kwambiri za banja lako kuposa chilichonse. Zimenezi ndi zosiyana ndi mfundo ya m’Malemba yakuti munthu komanso mabanja amakhala osangalala ngati amakonda Yehova kuposa chilichonse. (Mat. 22:36-39) Apatu sitikunena kuti zosangalatsa n’zolakwika. Koma ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi timatha kuzindikira maganizo a m’dzikoli ngakhale atabwera m’njira yosaonekera kwambiri? Kodi timakhala ndi malire pa nkhani ya zosangalatsa zimene ana athu kapena ifeyo timakonda? Kodi timayesetsa kuchotsa maganizo olakwika amene ana athu akumana nawo n’kuwasinthanitsa ndi maganizo a Mulungu?’ w18.11 22 ¶18-19

Lachinayi, May 14

Usachite mantha, pakuti ndili nawe.​—Yes. 41:10.

Yehova amasonyeza kuti ali nafe chifukwa amatiganizira komanso amatikonda kwambiri. Paja anati: “Ndiwe wamtengo wapatali kwa ine, ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.” (Yes. 43:4) Palibe chilichonse m’chilengedwe chimene chingachititse kuti Yehova asiye kukonda anthu amene amamutumikira. Iye ndi wokhulupirika kwambiri kwa ife. (Yes. 54:10) Yehova salonjeza kuti athetsa mavuto athu onse panopa. Koma sadzalola kuti mavuto okhala ngati “mitsinje” atimize kapena mayesero okhala ngati “moto” atiwonongeretu. Iye amatitsimikizira kuti adzakhala nafe ndipo adzatithandiza “kudutsa” bwinobwino pa mavuto athu. Adzatithandiza kuti tisamachite mantha n’cholinga choti tikhalebe okhulupirika kwa iye ngakhale titatsala pang’ono kufa. (Yes. 41:13; 43:2) Tikamakhulupirira lonjezo la Mulungu loti adzakhala nafe, tidzakhalanso olimba mtima pokumana ndi mavuto. w19.01 3 ¶4-6

Lachisanu, May 15

Mumtima mwa munthu mumakhala zolinga zambiri, koma zolinga za Yehova n’zimene zidzakwaniritsidwe.​—Miy. 19:21.

Ngati ndinu wachinyamata, muyenera kuti mwalimbikitsidwapo ndi aphunzitsi, alangizi komanso anthu ena kuti muphunzire kwambiri n’cholinga choti mudzapeze ntchito yapamwamba. Koma izi si zimene Yehova amakuuzani kuti muchite. N’zoona kuti amafuna kuti muzilimbikira sukulu n’cholinga choti muzidzapeza zofunika pa moyo. (Akol. 3:23) Koma amafuna kuti muzitsatira mfundo zake posankha zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu. Amafunanso kuti muziganizira cholinga chake komanso zimene amatipempha kuti tizichita m’masiku otsirizawa. (Mat. 24:14) Yehova akudziwa zonse zimene zichitike padzikoli komanso nthawi imene lidzathe. (Yes. 46:10; Mat. 24:3, 36) Iye amatidziwanso bwino ndipo amadziwa zimene zingatithandize kukhala osangalala ndi zimene zingatichititse kukhala osasangalala. Choncho ngakhale malangizo a munthu atamveka abwino chotani, ngati sakugwirizana ndi Mawu a Mulungu ndiye kuti si anzeru. w18.12 19 ¶1-2

Loweruka, May 16

Woipa sadzakhalakonso.​—Sal. 37:10.

Koma “anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Mulungu anathandizanso Davide kulosera kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:11, 29; 2 Sam. 23:2) Kodi mukuganiza kuti malonjezowa anakhudza bwanji anthu amene ankafuna kuchita zimene Mulungu amafuna? Ayenera kuti anaganiza kuti ngati padzikoli padzakhala anthu olungama okhaokha, ndiye kuti moyo udzakhala ngati wa m’munda wa Edeni. Koma patapita zaka, Aisiraeli ambiri amene ankanena kuti amatumikira Yehova anakhala osakhulupirika. Choncho Mulungu analola kuti Ababulo abwere n’kudzawagonjetsa, kuwononga dziko lawo komanso kutenga anthu ambiri kupita nawo ku ukapolo. (2 Mbiri 36:15-21; Yer. 4:22-27) Komabe aneneri a Mulungu analosera kuti pakatha zaka 70, anthuwo adzabwerera kwawo. N’zoona kuti maulosiwa anakwaniritsidwa koma akutikhudzanso ifeyo. Tiyeni tikambirane ena mwa maulosiwa n’kuona kuti akugwirizana bwanji ndi nkhani ya paradaiso padziko lapansi. w18.12 4 ¶9-10

Lamlungu, May 17

Monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi, momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.—Yes. 55:9.

Malangizo ambiri a m’dzikoli ndi osemphana kwambiri ndi Malemba. Kodi inuyo mukuona kuti malangizo ena amene anthu amaperekawa ndi othandiza? Yesu ananena kuti: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mat. 11:19) Anthu m’dzikoli apita patsogolo kwambiri pa nkhani ya zipangizo zamakono koma akulephera kuthetsa mavuto amene amatisowetsa mtendere monga nkhondo, kusankhana mitundu ndi ziwawa. Nanga kodi mtima wolekerera makhalidwe oipa wabweretsa mavuto otani? Ambiri amavomereza kuti mtima umenewu ndi umene ukuchititsa kuti mabanja azisokonekera, matenda azifala komanso kuti pakhale mavuto ena. Koma Akhristu amene amayendera maganizo a Mulungu amasangalala m’banja, amakhala ndi moyo wathanzi chifukwa chopewa makhalidwe oipa komanso amagwirizana ndi Akhristu anzawo padziko lonse. (Yes. 2:4; Mac. 10:34, 35; 1 Akor. 6:9-11) Kodi umenewu si umboni wakuti maganizo a Yehova ndi apamwamba kuposa a m’dzikoli? w18.11 20 ¶8-10

Lolemba, May 18

Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.​—1 Akor. 15:33.

N’zoona kuti timafuna kugwirizana ndi achibale athu komanso kuwakomera mtima. Koma si bwino kulolera kuphwanya mfundo zachoonadi pongofuna kuwasangalatsa. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tizigwirizana nawo. Koma tizigwirizana kwambiri ndi anthu amene amakonda Yehova. Anthu onse amene akuyenda m’choonadi ayenera kukhala oyera. (Yes. 35:8; 1 Pet. 1:14-16) Pamene tinkaphunzira choonadi, tonsefe tinasintha zinthu zina kuti tiziyendera mfundo za m’Baibulo. Ena anafunika kusintha kwambiri kuti zimenezi zitheke. Kaya tinasintha zambiri kapena zochepa, si bwino kugulitsa choonadi pochisinthanitsa ndi makhalidwe onyansa a m’dzikoli. Ndiye kodi tingatani kuti tisakopeke ndi makhalidwe oipa? Ndi bwino kuganizira mtengo umene Yehova analipira potithandiza kuti tikhale oyera. Pajatu anatigula ndi magazi amtengo wapatali a Mwana wake Yesu Khristu. (1 Pet. 1:18, 19) Ndiye kuti tikhalebe oyera pamaso pa Yehova, tiyenera kukumbukira nthawi zonse zoti tinagulidwa ndi nsembe ya dipo la Yesu. w18.11 11 ¶10-11

Lachiwiri, May 19

Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa. Mulungu wanga adzandimvera.​—Mika 7:7.

Anthu ambiri amene amachita utumiki wa nthawi zonse amaona kuti zinthu zikasintha pa moyo wawo, kupitiriza kulalikira mwakhama kumawathandiza kuti akhalebe ndi maganizo oyenera. Zitsanzo za anthuwa zikusonyeza kuti tikamayesetsa kuchita zimene zimasangalatsa Yehova n’kumamuyembekezera ndi mtima wonse, tikhoza kukhalabe ndi mtendere wamumtima. N’kutheka kuti zinthu zimene zasintha pa moyo wathu zingatithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu chifukwa cha matenda, udindo watsopano m’banja kapena ngati utumiki wathu wasintha. Zikatero, musamakayikire kuti Yehova amakuganizirani ndipo adzakuthandizani. (Aheb. 4:16; 1 Pet. 5:6, 7) Komanso muziyesetsa kuchita zimene mungathe kuti muzisangalatsa Yehova. Muzipemphera kwa iye ndiponso kusiya zinthu m’manja mwake. Mukamachita zimenezi, mudzakhalabe ndi mtendere wamumtima ngakhale kuti zinthu zasintha pa moyo wanu. w18.10 30 ¶17; 31 ¶19, 22

Lachitatu, May 20

[Yehova] akudziwa bwino mmene anatiumbira, Amakumbukira kuti ndife fumbi.​—Sal. 103:14.

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza mmene Yehova anachitira zinthu moganizira atumiki ake. Mwachitsanzo taganizirani mmene Yehova anathandizira Samueli ali mwana kuti apereke uthenga wachiweruzo kwa Eli yemwe anali mkulu wa ansembe. Nkhaniyi imapezeka pa 1 Samueli 3:1-18. Yehova analamula ana kuti azilemekeza achikulire, makamaka amene akutsogolera. (Eks. 22:28; Lev. 19:32) Ndiye kodi mukuganiza kuti Samueli akanakwanitsa kungodzuka m’mawa n’kupita kwa Eli kukamuuza uthenga woopsa wochokera kwa Mulungu? Ayi. Baibulo limanena kuti Samueli “anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.” Koma Mulungu anathandiza Eli kudziwa kuti ndi iyeyo amene ankamuitana Samueli. Choncho Eli ndi amene anauza Samueliyo kuti afotokoze zonse osabisa “ngakhale mawu amodzi.” Samueli anamvera ndipo “anamuuza mawu onse” ndipo uthengawu unali wofanana ndi uthenga umene Eli anauzidwa nthawi ina. (1 Sam. 2:27-36) Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova ndi wanzeru komanso amaganizira anthu ake. w18.09 23 ¶2; 24 ¶4-5

Lachinayi, May 21

Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’chihema chanu? . . . Ndi amene . . . [akulankhula] zoona mumtima mwake.​—Sal. 15:1, 2.

Anthu masiku ano amakonda kufalitsa mabodza. Munkhani ina yofotokoza chifukwa chake anthu amakonda kunama, munthu wina (Y. Bhattacharjee) analemba kuti “bodza linalowerera m’mitima ya anthu.” Anthu amakonda kunama pofuna kudziteteza kapena kudzitchukitsa. Amanama pofuna kuti anthu asadziwe zimene alakwitsa kapena pofuna kuti apeze kenakake. Munkhani imene tanena ija, analembanso kuti anthu ena “amanama mosavuta pa nkhani zikuluzikulu komanso zing’onozing’ono kwa anthu achilendo, anzawo akuntchito, anzawo apamtima ngakhalenso kwa anthu a m’banja lawo.” Zotsatira zake n’zakuti anthu amasiya kukhulupirirana komanso kugwirizana. Davide anapemphera kwa Yehova kuti: “Mumakondwera ndi choonadi chochokera pansi pa mtima.” (Sal. 51:6) Davide ankadziwa kuti kukhala wopanda chinyengo kumayambira mumtima. Nthawi zonse Akhristu oona ‘amalankhula zoona zokhazokha.’​—Zek. 8:16. w18.10 7 ¶4; 8 ¶9-10; 10 ¶19

Lachisanu, May 22

Anapitiriza kuwatsogolera ndi kuwateteza ndipo iwo sanachite mantha.​—Sal. 78:53.

Aisiraeli amene anapulumutsidwa ku Iguputo mu 1513 B.C.E. ayenera kuti anali oposa 3 miliyoni. Pa gululi panali ana, achikulire komanso mwina anthu odwala kapena olumala. Kuti munthu atsogolere bwinobwino gulu lalikulu chonchi, anafunika kukhala womvetsa komanso woganizira ena. Yehova anali mtsogoleri wotereyu ndipo anagwiritsa ntchito Mose. Izi zinathandiza kuti Aisiraeli asachite mantha pochoka ku Iguputo kumene anabadwira. (Sal. 78:52) Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu ake kuti asamachite mantha pa ulendowu? Choyamba, anawauza kuti aziyenda “mwa dongosolo lomenyera nkhondo.” (Eks. 13:18) Dongosolo limeneli linathandiza Aisiraeliwo kudziwa kuti Yehova awayendetsa bwino. Yehova anawathandizanso kudziwa kuti ali nawo chifukwa ankawatsogolera ndi “mtambo masana” ndipo usiku ankawatsogolera ndi “kuwala kwa moto.” (Sal. 78:14) Apa zinali ngati Yehova akuwauza kuti: “Musaope. Ndili nanu. Ndizikutsogolerani komanso kukutetezani.” w18.09 26 ¶11-12

Loweruka, May 23

Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda, . . . mukanati mundiikire nthawi n’kudzandikumbukira.—Yobu 14:13.

Atumiki ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo anapanikizikapo ndi mavuto moti ankafuna atangofa. Mwachitsanzo, Yobu atavutika kwambiri ananena kuti: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Yobu 7:16) Nayenso Yona anakhumudwa kwambiri chifukwa cha zimene zinachitika pa utumiki wake moti ananena kuti: “Tsopano inu Yehova, chotsani moyo wanga, pakuti kuli bwino kuti ndife kusiyana n’kukhala ndi moyo.” (Yona 4:3) Pa nthawi ina Eliya anadandaula kwambiri ndipo anapemphanso kuti afe. Iye anati: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga Yehova.” (1 Maf. 19:4) Koma Yehova ankaona kuti anthuwo anali amtengo wapatali ndipo ankafuna kuti akhalebe ndi moyo. Iye sanawadzudzule chifukwa choti ankafuna kufa. M’malomwake anawathandiza kusintha maganizo awo ndipo anawalimbikitsa mwachikondi kuti apitirize kumutumikira mokhulupirika. w18.09 13 ¶4

Lamlungu, May 24

Ndife antchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.

Antchito anzake a Yehova amadziwika kuti ndi ochereza. M’Malemba Achigiriki, mawu amene anamasuliridwa kuti “kuchereza” amatanthauza “kukomera mtima alendo.” (Aheb. 13:2) M’Mawu a Mulungu muli nkhani zambiri zotsimikizira kuti kusonyeza chikondi n’kofunika. (Gen. 18:1-5) Choncho tiziyesetsa kuthandiza anthu ena, kaya ndi “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro” kapena ayi. (Agal. 6:10) Kodi mungagwire ntchito ndi Mulungu pochereza anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse omwe abwera mumpingo wanu? (3 Yoh. 5, 8) Tikamachita zimenezi ‘timalimbikitsana.’ (Aroma 1:11, 12) Mawu a Mulungu amalimbikitsa abale kuti azigwira ntchito ndi Yehova poyesetsa kuti ayenerere udindo mumpingo. (1 Tim. 3:1, 8, 9; 1 Pet. 5:2, 3) Abale amene amachita zimenezi amafunitsitsa kuti azithandiza anthu m’njira zosiyanasiyana. (Mac. 6:1-4) Abale amene amathandiza pa zinthu zofunika mumpingo angavomereze kuti amasangalala kwambiri chifukwa chothandiza anthu ena. w18.08 24 ¶6-7; 25 ¶10

Lolemba, May 25

Usadzudzule mwamuna wachikulire mokalipa, koma umudandaulire ngati bambo ako.​—1 Tim. 5:1.

Ngakhale kuti Timoteyo anali ndi udindo woyang’anira, ankayenera kuchita zinthu mwachifundo komanso mwaulemu ndi abale achikulire. Koma kodi malangizo okhudza anthu achikulirewa tiyenera kuwatsatira bwanji? Mwachitsanzo, kodi tiyenera kumverabe munthu wachikulire ngakhale pamene akuchita machimo mwadala kapena akulimbikitsa zinthu zimene Yehova sasangalala nazo? Yehova saweruza potengera maonekedwe ndipo sangalekerere munthu wochimwa chifukwa choti ndi wachikulire. Taganizirani mfundo yopezeka pa Yesaya 65:20 imene imati: “Wochimwa, ngakhale ali ndi zaka 100, temberero lidzamugwera.” M’masomphenya amene Ezekieli anaona muli mfundo yofanananso. (Ezek. 9:5-7) Choncho chofunika kwambiri ndi kulemekeza “Wamasiku Ambiri,” yemwe ndi Yehova Mulungu. (Dan. 7:9, 10, 13, 14) Tikamachita zimenezi sitingaope kupereka malangizo kwa munthu wachikulire.​—Agal. 6:1. w18.08 11 ¶13-14

Lachiwiri, May 26

Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.—Miy. 14:15.

Akhristufe tiyenera kukhala ndi luso loganizira bwino nkhani iliyonse n’cholinga choti tizindikire zoona zake. (Miy. 3:21-23; 8:4, 5) Ngati tilibe luso limeneli, zingakhale zosavuta kuti tisokonezedwe ndi Satana komanso anthu a m’dzikoli. (Aef. 5:6; Akol. 2:8) Choncho kuti tidziwe zoona zake pa nkhani inayake, tiyenera kudziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. Masiku ano, timawerenga kapena kumva nkhani zambirimbiri. Tikhoza kupeza mfundo zankhaninkhani pa zinthu monga intaneti ndi TV. Anthu amalandiranso maimelo, mameseji kapena nkhani zambirimbiri kuchokera kwa anzawo. Popeza anthu ena amakonda kufalitsa nkhani zabodza kapena kupotoza mfundo zina, tiyenera kukhala osamala kwambiri. w18.08 3 ¶1, 3

Lachitatu, May 27

Mulungu wakukomera mtima.—Luka 1:30.

Nthawi yoti Yesu abadwe padzikoli itakwana, Yehova anasankha Mariya kuti akhale mayi wa mwana wapaderayu. Mariya anali namwali wodzichepetsa ndipo ankakhala mumzinda wa Nazareti. Mzindawu unali wosatchuka ndipo unali kutali ndi Yerusalemu komanso kachisi wake wokongola. (Luka 1:26-33) Zimene Mariya analankhula kwa Elizabeti zimasonyeza kuti ankadziwa bwino Mulungu komanso kumukonda. (Luka 1:46-55) Yehova ankaona kukhulupirika kwa Mariya ndipo anamudalitsa m’njira imene sankaiganizira. Yesu atabadwa, Yehova sanaulule nkhaniyi kwa anthu otchuka kapena olamulira a ku Yerusalemu ndi ku Betelehemu. M’malomwake anatumiza angelo kuti akauze abusa amene ankagona kubusa n’kumayang’anira nkhosa. (Luka 2:8-14) Abusawa atamva zimenezi anapita kukaona mwanayo. (Luka 2:15-17) Mariya ndi Yosefe ayenera kuti anadabwa kuona kuti Yesu akulemekezedwa m’njira imeneyi. w18.07 9-10 ¶11-12

Lachinayi, May 28

Yehova anamukwiyira kwambiri Solomo.​—1 Maf. 11:9.

N’chifukwa chiyani Yehova anamukwiyira Solomo? Baibulo limanena kuti: “Chifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova . . . , amene anamuonekera kawiri konse. Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatire milungu ina, koma iye sanasunge zimene Yehova analamula.” Zochita za Solomo zinachititsa kuti Yehova asiye kumukonda komanso kumuthandiza. Ana ake anataya mwayi wolamulira mtundu wonse wa Isiraeli chifukwa ufumuwo unagawikana ndipo anakumana ndi mavuto ambiri. (1 Maf. 11:9-13) Nafenso ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kusokonekera mosavuta ngati timacheza kwambiri ndi anthu amene sadziwa kapena kulemekeza mfundo za Yehova. Anthu ena amatha kukhala m’gulu la Yehova koma ali ofooka mwauzimu ndipo angatisokoneze. Tingasokonezedwenso ndi achibale athu, anthu amene timakhala nawo pafupi ndiponso anzathu akuntchito kapena kusukulu omwe salambira Yehova. Mwachidule tingati tikamagwirizana kwambiri ndi munthu aliyense amene salemekeza mfundo za Yehova, pakapita nthawi munthuyo akhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. w18.07 19 ¶9-10

Lachisanu, May 29

Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.​—1 Yoh. 5:19.

Satana amagwiritsa ntchito mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV pofuna kuti anthu azitengera maganizo ake. Iye amadziwa kuti nkhani zopeka zimasangalatsa komanso zimachititsa kuti munthu asinthe maganizo ndi zochita zake. Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuphunzitsa anthu m’njira yowafika pamtima. Mwachitsanzo, anafotokoza fanizo la Msamariya wachifundo komanso la mwana wolowerera amene anawononga cholowa chake. (Mat. 13:34; Luka 10:29-37; 15:11-32) Koma nkhani zopekedwa ndi anthu amene akuyendera maganizo a Satana zikhoza kutisokoneza. Choncho tiyenera kukhala oganiza bwino. N’zoona kuti tikhoza kusangalala ndi mafilimu komanso mapulogalamu ena a pa TV popanda kusokoneza maganizo athu. Koma tiyenera kukhala osamala. Tikamasankha zosangalatsa tizidzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuphunzira chiyani pa zimene ndikuonerazi? Kodi sizingandichititse kuganiza kuti palibe vuto kumangochita zofuna za thupi langa?’ (Agal. 5:19-21; Aef. 2:1-3) Kodi muyenera kuchita chiyani mukazindikira kuti pulogalamu inayake ikulimbikitsa maganizo a Satana? Muyenera kuipeweratu ngati mmene mungapewere matenda oopsa. w19.01 15-16 ¶6-7

Loweruka, May 30

Landirani chisoti cholimba chachipulumutso.​—Aef. 6:17.

Mofanana ndi chisoti chimene chinkateteza ubongo wa msilikali, “chiyembekezo chachipulumutso” chimateteza maganizo athu. (1 Ates. 5:8; Miy. 3:21) Kodi Satana angatinyengerere bwanji kuti tivule chisoti chathu? Taganizirani zimene anachita poyesa Yesu. N’zosakayikitsa kuti Satana ankadziwa zoti Yesu akuyembekezera kudzalamulira anthu. Koma Yesu ankafunika kuyembekezera nthawi imene Mulungu ankafuna kuti ayambe kulamulirako. Ndipo anafunika kuvutika komanso kufa asanayambe kulamulira. Ndiyeno Satana anapatsa Yesu mwayi woti ayambe kulamulira mwamsanga. Anamuuza kuti akangomulambira kamodzi kokha, adzamupatsa ulamulirowo pompopompo. (Luka 4:5-7) Satana amadziwanso kuti Yehova adzatipatsa zinthu zimene timafuna m’dziko latsopano. Koma panopa tiyenera kudikira komanso kukumana ndi mavuto ena. Ndiyeno Satana amatipatsa mwayi woti tikhaliretu ndi moyo wofewa panopa. Iye amatinyengerera kuti tikhale ndi mtima wofunitsitsa kupeza zomwe timafuna pompopompo. Cholinga chake n’choti tiziika Ufumu pamalo achiwiri.​—Mat. 6:31-33. w18.05 30-31 ¶15-17

Lamlungu, May 31

Mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako.​—Mlal. 11:9.

Yehova amafuna kuti achinyamata azisangalala. Ndi bwino kukhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa ndiponso kuika Yehova patsogolo posankha zochita. Mukachita zimenezi mwamsanga, mudzaonanso mwamsanga kuti Yehova akukutsogolerani, akukutetezani komanso akukudalitsani. Ndi bwino kuganizira malangizo onse amene timapeza m’Mawu a Mulungu n’kumatsatira mfundo yakuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” (Mlal. 12:1) Achinyamata amene tili nawo mumpingo ayenera kuyamikiridwa kwambiri chifukwa chokhala ndi mtima wofuna kutumikira Yehova ndi moyo wawo wonse. Achinyamata amakwanitsa kuchita zimenezi ngati ali ndi zolinga zauzimu komanso ngati amaika patsogolo ntchito yolalikira. Amayesetsanso kuti asamasokonezedwe ndi dzikoli. Achinyamata oterewa sayenera kukayikira zoti Yehova sadzaiwala zimene akuchita. Azikumbukira kuti pali abale ndi alongo amene ali kumbali yawo ndipo akamaika Yehova patsogolo, zolinga zawo zonse zidzakwaniritsidwa. w18.04 29 ¶17, 19

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani