June
Lolemba, June 1
Chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa [akupatsani].—Yoh. 15:16.
Lonjezo limeneli liyenera kuti linalimbikitsa kwambiri atumwi. N’zoona kuti atumwiwo sanamvetse bwinobwino zimene zichitike. Pa nthawiyo, Mtsogoleri wawo anali atatsala pang’ono kuphedwa koma iwo sakanasiyidwa popanda thandizo. Yehova ankafunitsitsa kuyankha mapemphero awo opempha kuti aziwathandiza kumvera lamulo loti azilalikira uthenga wa Ufumu. Ndiyeno patangopita nthawi yochepa, anaonadi Yehova akuyankha mapemphero awo. (Mac. 4:29, 31) Ndi mmene zililinso masiku ano. Tikamapirira pobereka zipatso timakhala anzake a Yesu. Ndipo sitiyenera kukayikira kuti Yehova amafunitsitsa kuyankha mapemphero athu n’kumatithandiza kuthetsa vuto lililonse lomwe tingakumane nalo polalikira. (Afil. 4:13) Timayamikira kwambiri kuti mapemphero athu amayankhidwa komanso kuti ndife anzake a Yesu. Mphatso zochokera kwa Mulungu zimenezi zimatithandiza kupitiriza kubereka zipatso.—Yak. 1:17. w18.05 21 ¶17-18
Lachiwiri, June 2
Tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.—Aheb. 10:24, 25.
Pasanathe zaka 5 kuchokera pamene Paulo anapereka malangizowa, Akhristu achiyuda anazindikira kuti tsiku la Yehova layandikira. Anaona chizindikiro chimene Yesu ananena kuti akadzachiona adzathawe mumzindawo. (Mac. 2:19, 20; Luka 21:20-22) Tsikuli linafika mu 70 C.E. pamene Yehova anawononga mzinda wa Yerusalemu pogwiritsa ntchito Aroma. Masiku anonso, umboni wakuti ‘tsiku la Yehova lalikulu komanso lochititsa mantha’ layandikira uli paliponse. (Yow. 2:11) Mneneri Zefaniya analemba kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.” (Zef. 1:14) Chenjezo limene anaperekali ndi lothandizanso masiku ano. Popeza tsikuli lili pafupi kwambiri, mtumwi Paulo akutiuza kuti: “Tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Choncho tiyenera kuganizira za abale ndi alongo athu n’cholinga choti tiziwalimbikitsa pa nthawi iliyonse yoyenera. w18.04 20 ¶1-2
Lachitatu, June 3
Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.—Yos. 1:9.
Mawu amenewa ndi amene Yehova anauza Yoswa asanathandize anthu ake kuti akhazikike m’Dziko Lolonjezedwa ndipo anali olimbikitsa kwambiri. Nthawi zina Yehova ankalimbikitsanso anthu ake monga gulu. Ayuda ali ku ukapolo ku Babulo, Mulungu anapereka ulosi wolimbikitsa wakuti: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” (Yes. 41:10) Mulungu ankalimbikitsanso Akhristu oyambirira ndipo amachitanso zomwezo masiku ano. (2 Akor. 1:3, 4) Ngakhale Yesu analimbikitsidwapo ndi Atate ake. Pa nthawi ya ubatizo wake, anamva mawu ochokera kumwamba akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mat. 3:17) Mawu amenewa ayenera kuti analimbikitsa Yesu pa nthawi yonse ya utumiki wake wapadziko lapansili. w18.04 16 ¶3-5
Lachinayi, June 4
Usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.—Gen. 2:17.
Anthu ena akawerenga lamulo limene Mulungu anapatsa Adamu amanena kuti ankamuphera ufulu. Vuto la anthuwo ndi lakuti satha kusiyanitsa pakati pa ufulu wosankha ndi udindo wonena kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika. Adamu ndi Hava anali ndi ufulu wosankha kumvera Mulungu kapena kusamumvera. Koma Yehova ndi amene anali ndi udindo wonena kuti izi n’zabwino izi n’zoipa ndipo chizindikiro cha udindowu chinali “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa” umene unali m’munda wa Edeni. (Gen. 2:9) Lamulo limene Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava linali lowathandiza kuzindikira njira yabwino yogwiritsira ntchito ufulu wawo. N’zomvetsa chisoni kuti makolo athu oyambirira anasankha kusamvera Mulungu. Kodi zimene Adamu ndi Hava anasankha zinawathandiza kukhala ndi ufulu wambiri? Ayi. Mtima wofuna ufulu wambiri unawatayitsa ufulu weniweni umene anapatsidwa. w18.04 5-6 ¶9-12
Lachisanu, June 5
Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.—Yes. 63:9.
Sikuti Yehova amangomva chisoni akaona atumiki ake akuvutika. Iye amawathandiza. Mwachitsanzo, Aisiraeli atazunzika ku ukapolo ku Iguputo, Yehova anamvetsa mavuto awo ndipo anawathandiza. Yehova anauza Mose kuti: “Ndaona nsautso ya anthu anga . . . ndipo ndamva kulira kwawo . . . ndikudziwa bwino zowawa zawo. Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo.” (Eks. 3:7, 8) Yehova anamva chisoni ndi mavuto a anthu ake, choncho anawamasula ku ukapolo. Aisiraeli atakhala m’Dziko Lolonjezedwa kwa zaka zambiri, anaukiridwanso ndi mitundu ina ya anthu. Kodi Yehova anatani? Baibulo limati iye “anali kuwamvera chisoni akamva kubuula kwawo chifukwa cha owapondereza ndi owakankhakankha.” Mtima woganizira ena ndi umene unachititsa Yehova kuti athandize anthu ake. Iye anatumiza oweruza kuti apulumutse Aisiraeli kwa adani awo.—Ower. 2:16, 18. w19.03 15 ¶4-5
Loweruka, June 6
Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa, osamvera chisoni mwana wochokera m’mimba mwake? Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala, koma ine sindidzakuiwala.—Yes. 49:15.
Malamulo awiri oyambirira ankalimbikitsa Aisiraeli kuti azilambira Yehova yekha osati mafano. (Eks. 20:3-6) Malamulo amenewa anali othandiza anthuwo osati Yehova. Aisiraeliwo akakhala okhulupirika kwa Yehova zinthu zinkawayendera bwino. Koma akayamba kulambira milungu ya mitundu ina ankavutika kwambiri. Koma Yehova ankadalitsa kwambiri anthu ake akakhala okhulupirika komanso akamachitirana zinthu mwachilungamo. (1 Maf. 10:4-9) Sitiyenera kuimba mlandu Yehova ngati anthu asiya kutsatira mfundo zake n’kumazunza anzawo. Yehova amatikonda kwambiri ndipo amadziwa ngati sitikuchitiridwa zinthu mwachilungamo. Iye amazindikira mavuto athu kuposa mmene mayi amachitira ndi mwana wake wakhanda. Ngakhale kuti mwina sangathetse mavuto athuwo panopa, pa nthawi yoyenera adzalanga anthu osalapa amene amachitira nkhanza anzawo. w19.02 22 ¶13-15
Lamlungu, June 7
Chifuniro chanu chichitike, osati changa.—Luka 22:42.
Kukatsala milungu yochepa kuti tichite Chikumbutso, timakambirana kumisonkhano chitsanzo cha Yesu pa khalidwe la kudzichepetsa limene anasonyeza pololera kupereka moyo wake monga nsembe. Zimatithandizanso kuti tizitsanzira kudzichepetsa kwake komanso kuti tizichita zofuna za Yehova ngakhale pa nthawi imene takumana ndi mavuto. Taganizirani mmene anasonyezera kulimba mtima kutatsala masiku ochepa kuti aphedwe. Iye ankadziwa kuti posachedwa adani ake amunyoza, kumumenya kenako n’kumupha. (Mat. 20:17-19) Komabe iye analolera kuti zimenezi zimuchitikire. Atatsala pang’ono kugwidwa, anauza ophunzira ake amene anali naye ku Getsemane kuti: “Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.” (Mat. 26:36, 46) Ndipo gulu la anthu onyamula zida litafika, iye anawayandikira n’kuwauza kuti amene mukumufunayo ndine. Atatero anauza asilikali kuti awasiye ophunzira ake azipita. (Yoh. 18:3-8) Apatu Yesu anasonyeza kulimba mtima kwambiri. Masiku ano, Akhristu odzozedwa komanso a nkhosa zina amayesetsa kukhala olimba mtima ngati Yesu. w19.01 27-28 ¶7-8
Lolemba, June 8
Yesetsani kukhala ofatsa.—Zef. 2:3.
Munthu wojambula amasakaniza penti yosiyanasiyana kuti akongoletse chithunzi. Ifenso timafunika kukhala ndi makhalidwe osiyanasiyana kuti tikhale ofatsa. Ena mwa makhalidwe amenewa ndi kudzichepetsa, kugonjera, kudekha komanso kulimba mtima. Anthu odzichepetsa okha ndi amene amagonjera zimene Mulungu amafuna. Chinthu chimodzi chimene Mulungu amafuna n’chakuti tizikhala odekha. (Miy. 29:11; 2 Tim. 2:24) Tikamachita zimene Mulungu amafuna, Satana amakwiya kwambiri. Choncho anthu ambiri m’dziko la Satanali amadana nafe ngakhale kuti ndife ofatsa komanso odzichepetsa. (Yoh. 15:18, 19) N’chifukwa chake timafunika kukhala olimba mtima kuti tilimbane ndi Satana. Koma munthu amene si wofatsa amakhala wodzikuza, sachedwa kukwiya komanso samvera Yehova. Umu ndi mmene Satana alili. Ndipo m’pake kuti amadana ndi anthu ofatsa. Popeza anthuwo amakhala ndi makhalidwe amene iye alibe, amasonyeza kuti iyeyo ndi woipa kwambiri. Anthu ofatsa amasonyezanso kuti Satana ndi wabodza. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale iye atayesetsa bwanji, sangalepheretse anthu ofatsa kuti azitumikira Yehova.—Yobu 2:3-5. w19.02 8-9 ¶3-5
Lachiwiri, June 9
Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.—Yes. 41:10.
Yehova ankadziwa kuti anthu a ku Babulo adzachita mantha. Koma kodi n’chiyani chikanawachititsa mantha? Chakumapeto kwa zaka 70 za ukapolo uja, asilikali a Mediya ndi Perisiya anaukira Babulo. Yehova anagwiritsa ntchito asilikali amenewa kuti amasule anthu ake ku ukapolo. (Yes. 41:2-4) Ababulo ndi anthu ena ataona kuti adani akuyandikira, anayamba kulimbikitsana pouzana kuti: “Limba mtima.” Iwo anapanganso mafano ena ambiri poganiza kuti awateteza. (Yes. 41:5-7) Koma Yehova analimbikitsa Ayuda powauza kuti: “Iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga [mosiyana ndi mitundu inayo] . . . Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” (Yes. 41:8-10) Onani kuti Yehova ananena kuti “Ine ndine Mulungu wako.” Apa Yehova ankatsimikizira atumiki ake okhulupirika kuti sanawaiwale ndipo iwo anali adakali anthu ake. Anawauzanso kuti ‘awanyamula ndiponso kuwapulumutsa.’ Ayudawo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu amenewa.—Yes. 46:3, 4. w19.01 4 ¶8
Lachitatu, June 10
Panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”—Maliko 1:11.
Yehova analankhula kuchokera kumwamba katatu ndipo lemba la Maliko 1:9-11 limafotokoza zimene zinachitika pa nthawi yoyamba. Yehova anati: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.” Yesu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kumva Atate ake akulankhula mawu olimbikitsa komanso osonyeza kuti amamukonda. Mawuwa anatsimikizira mfundo zitatu zofunika zokhudza Yesu. Yoyamba ndi yakuti Yesu ndi Mwana wake. Yachiwiri ndi yakuti Yehova amakonda Mwana wakeyo. Ndipo yachitatu ndi yakuti Yehova amakondwera ndi Mwana wake. Ponena kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga,” Yehova anasonyeza kuti ubwenzi wapadera unali utayambika pakati pa iye ndi Yesu. Yesu ali kumwamba anali mwana wauzimu wa Mulungu. Koma pa ubatizo wake, iye anadzozedwa ndi mzimu woyera. Pa nthawiyi Mulungu anasonyeza kuti Yesu, yemwe anadzozedwa, tsopano ankayembekezera kubwerera kumwamba n’kukakhala Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe wosankhidwa ndi Mulungu. (Luka 1:31-33; Aheb. 1:8, 9; 2:17) Choncho m’pomveka kuti pa nthawi ya ubatizoyi, Yehova anauza Yesu kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga.”—Luka 3:22. w19.03 8 ¶3-4
Lachinayi, June 11
Palibe nzeru . . . kapena malangizo alionse otsutsana ndi Yehova.—Miy. 21:30.
Malangizo opanda nzeru anayamba kalekale pamene Satana analankhula ndi Hava. Anauza Hava kuti iye ndi mwamuna wake angakhale osangalala kwambiri akamasankha okha zochita. (Gen. 3:1-6) Koma Satana anali ndi zolinga zadyera. Iye ankafuna kuti Adamu ndi Hava komanso ana awo azilambira iyeyo osati Yehova. Koma Satana anali asanawachitire chilichonse chabwino. Yehova ndi amene anali atawapatsa zinthu zonse monga banja losangalala, malo okongola, matupi angwiro komanso mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo anasokoneza ubwenzi wawo ndi iye. Zotsatira zake zinali zoopsa kwambiri. Mofanana ndi duwa limene limayamba kufota likathyoledwa, iwo anayamba kufooka mwapang’onopang’ono mpaka kufa. Ana awonso anakumana ndi mavuto chifukwa cha uchimo. (Aroma 5:12) Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amasankhabe kuti asamamvere Mulungu. Iwo amafuna kuti azingochita chilichonse chimene akufuna. (Aef. 2:1-3) Zotsatira zake zimasonyezeratu kuti mawu amulemba la leroli ndi oona. w18.12 20 ¶3-4
Lachisanu, June 12
[Timalankhula] osati ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mawu amene mzimu watiphunzitsa, pamene tikuphatikiza zochitika zauzimu ndi mawu auzimu.—1 Akor. 2:13.
Mtumwi Paulo anali wanzeru, wophunzira komanso ankadziwa zilankhulo ziwiri kapena kuposerapo. (Mac. 5:34; 21:37, 39; 22:2, 3) Koma sanalole kuti aziyendera maganizo a m’dzikoli pa nkhani yoti izi ndi zoyenera izi ndi zosayenera. M’malomwake, ankayendera maganizo a Yehova. (Mac. 17:2; 1 Akor. 2:6, 7) Zotsatira zake n’zakuti zinthu zinkamuyendera bwino pa utumiki wake ndipo ankayembekezera mphoto yamuyaya. (2 Tim. 4:8) Zikuonekeratu kuti maganizo a Yehova ndi apamwamba kwambiri kuposa a anthu. Munthu akamayendera maganizo a Mulungu amakhala wosangalala ndipo zinthu zimamuyendera bwino. Koma Yehova satikakamiza kuti tiziyendera maganizo ake. Akulu komanso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” salamulira maganizo a anthu. (Mat. 24:45; 2 Akor. 1:24) M’malomwake, Mkhristu aliyense ali ndi udindo wosintha kuti aziyendera maganizo a Yehova. w18.11 20-21 ¶12-13
Loweruka, June 13
Chisoni ndi kubuula zidzachoka.—Yes. 35:10.
Mulungu anagwiritsa ntchito Yesaya polosera kuti anthu ake akadzabwerera kudziko lawo sadzavutika ndi nyengo zoipa, zilombo zolusa kapena anthu oopsa. Aliyense adzakhala wotetezeka, kaya wamkulu kapena wamng’ono. (Yes. 11:6-9; 35:5-10; 51:3) Ulosi womwewu unanenanso kuti dziko lonse, osati la Isiraeli lokha, “lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” Yesaya analoseranso kuti anthu obwerera kwawo sadzaopa zilombo kapena anthu. Dziko lawo lidzabereka zipatso zambiri chifukwa choti mudzakhala madzi okwanira ngati mmene zinalili m’munda wa Edeni. (Gen. 2:10-14; Yer. 31:12) Kodi zonsezi zinakwaniritsidwa mu nthawi ya Aisiraeli? Palibe umboni wakuti anthu amene anachoka ku ukapolo anachiritsidwa mozizwitsa. Mwachitsanzo, akhungu sanayambe kuona. Choncho Mulungu ayenera kuti ankatanthauza kuti zoterezi zidzachitika m’tsogolo. w18.12 5 ¶11-12
Lamlungu, June 14
[Pitirizani kuyenda] m’choonadi.—3 Yoh. 3.
Nkhani yoyenda m’choonadi ilibe malire chifukwa tikuyembekezera kuchita zimenezi mpaka kalekale. Ndiye kodi tingatani kuti titsimikize mumtima mwathu zoyendabe m’choonadi? Tiyenera kupitiriza kuphunzira mfundo zamtengo wapatali za m’Baibulo komanso kuzisinkhasinkha. Tikamapeza nthawi yophunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu timakhala tikugula choonadi. Zimenezi zimathandiza kuti tiziyamikira kwambiri choonadicho komanso tikhale osamala kuti tisachigulitse. Lemba la Miyambo 23:23 limanenanso kuti tiyenera kugula “nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.” Choncho kungodziwa zinthu si kokwanira. Tiyenera kutsatira mfundo zachoonadi pa moyo wathu. Kumvetsa zinthu n’kumene kungatithandize kuona kuti mfundo zonse zimene Yehova amatiuza n’zogwirizana. Pomwe nzeru zingatithandize kuchita zinthu zoyenera mogwirizana ndi zimene tikudziwa. Nthawi zina, mfundo zachoonadi zimakhala malangizo otiuza zimene tiyenera kusintha. Tikalandira malangizo oterewa tiyenera kuwatsatira mwamsanga chifukwa ndi amtengo wapatali kuposa siliva.—Miy. 8:10. w18.11 9 ¶3; 11 ¶13-14
Lolemba, June 15
Gula choonadi ndipo usachigulitse.—Miy. 23:23.
Kodi chinthu chamtengo wapatali kwambiri kwa inuyo ndi chiyani? Kodi mungalolere kuchisinthanitsa ndi chinthu chotchipa? Mafunsowa si ovuta kwa atumiki a Yehova okhulupirika. Chinthu chamtengo wapatali kwambiri kwa ife ndi ubwenzi wathu ndi Yehova ndipo sitingausinthanitse ndi chilichonse. Timayamikiranso kwambiri choonadi cha m’Baibulo chimene chatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba. (Akol. 1:9, 10) Tangoganizirani mfundo zambirimbiri zimene Yehova watiphunzitsa kuchokera m’Baibulo. Iye watiuza za dzina lake, tanthauzo la dzinali komanso makhalidwe ake abwino. Iye watiphunzitsanso zoti anatisonyeza chikondi chosaneneka potumiza Mwana wake kuti akhale dipo lotiwombola. Yehova watiuzanso za Ufumu wa Mesiya, zoti odzozedwa adzapita kumwamba ndiponso zoti a “nkhosa zina” adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi. Amatiphunzitsanso kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Timayamikira kwambiri zonsezi chifukwa zimatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino. Zimatithandizanso kuti tiziona kuti moyo wathu uli ndi cholinga. w18.11 3 ¶1-2
Lachiwiri, June 16
Musamanamizane.—Akol. 3:9.
Anthu achinyengo sangabisire kanthu Yehova chifukwa “kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino.” (Aheb. 4:13) Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza kuti munthawi ya atumwi, Satana ‘analimbitsa mtima’ banja lina kuti linamize Mulungu. Hananiya ndi Safira anapangana kuti anamize atumwi. Iwo anagulitsa munda wawo koma sanapereke kwa atumwi ndalama zonse zimene anapeza. Pofuna kuoneka banja labwino banjali linanama kuti lapereka ndalama zonse. Koma Yehova anaona zimene anachita ndipo anawapatsa chilango choyenerera. (Mac. 5:1-10) Kodi Yehova amakuona bwanji kunama? Satana komanso anthu onse amene amamutsanzira ponena mabodza koma osalapa, “adzaponyedwa m’nyanja ya moto.” (Chiv. 20:10; 21:8; Sal. 5:6) Timadziwa kuti Yehova “si munthu, woti anganene mabodza” moti “n’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Num. 23:19; Aheb. 6:18) Baibulo limanena kuti ‘Yehova amadana ndi lilime lonama.’ (Miy. 6:16, 17) Choncho kuti timusangalatse, tiyenera kuyendera mfundo zake pa nkhani yonena zoona. w18.10 8 ¶10-13
Lachitatu, June 17
Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama.—1 Tim. 4:15.
Tiyerekeze kuti bwana wanu akukuuzani kuti musonkhe nawo ndalama zinazake zodzagwiritsa ntchito pa chikondwerero chinachake chokhudza kulambira konyenga. Kodi mungatani? M’malo modikira kuti zidzakuchitikireni kenako muziganiza zochita, ndi bwino kuoneratu panopa maganizo a Yehova pa nkhani ngati zimenezi. Ndiyeno zikadzakuchitikirani simudzasowa zochita kapena zolankhula. Kudziwiratu zochita kuti tikhale okhulupirika n’kofunikanso pa nkhani zachipatala. N’zoona kuti tonse tinatsimikiza mumtima mwathu kuti sitingalandire magazi kapena zigawo zikuluzikulu za magazi. Koma pali njira zina zimene madokotala amagwiritsira ntchito magazi zomwe aliyense ayenera kusankha yekha mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo zimene zimasonyeza maganizo a Yehova. (Mac. 15:28, 29) Nthawi yabwino kusankha zochita pa nkhani zimenezi ndi inoyo osati pamene tagonekedwa m’chipatala, tikumva ululu ndipo anthu akutipanikiza kuti tisankhe msangamsanga. Ndi bwino panopa kufufuza m’mabuku athu, kulemberatu bwinobwino zimene tingakonde komanso kulankhulana ndi dokotala wathu. w18.11 24 ¶5; 26 ¶15-16
Lachinayi, June 18
Munthu wondimvera adzakhala mwabata.—Miy. 1:33.
Yehova ndi m’busa wabwino amene amasamalira anthu ake. Iye amawateteza mwachikondi kwa adani awo. Mfundo zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri pamene tikuyandikira mapeto a dzikoli. Yehova apitiriza kusamalira anthu ake mpaka pa chisautso chachikulu chimene chikubwera posachedwapa. (Chiv. 7:9, 10) Choncho kaya ndife aang’ono kapena achikulire, athanzi kapena olumala, sitidzafunika kuopa pa nthawi ya chisautso chachikulu. M’malomwake, tidzangokumbukira mawu a Yesu akuti: “Mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.” (Luka 21:28) Tidzapitiriza kudalira Yehova ngakhale pa nthawi imene tidzaukiridwe ndi Gogi, yemwe akuimira mgwirizano wa mitundu yamphamvu ya anthu. (Ezek. 38:2, 14-16) Koma kodi n’chiyani chidzathandize anthu a Mulungu kuti asachite mantha? Iwo amadziwa kuti Yehova sasintha ndipo nthawi zonse azichita zinthu mowaganizira n’kuwapulumutsa.—Yes. 26:20. w18.09 26 ¶15-16
Lachisanu, June 19
Ndiwe wamtengo wapatali kwa ine . . . ndipo ndimakukonda.—Yes. 43:4.
Aisiraeli okhulupirika ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri pamene anamva mawu a Yehova omwe ali pamwambawa. Nafenso tisamakayikire kuti Yehova amatikonda kwambiri chifukwa timamutumikira. Mawu a Mulungu amalonjeza munthu aliyense amene amalambira Yehova kuti: “Adzakupulumutsa chifukwa ndi wamphamvu. Iye adzakondwera nawe.” (Zef. 3:16, 17) Yehova analonjeza atumiki ake kuti aziwathandiza komanso kuwalimbikitsa pa mayesero alionse amene angakumane nawo. Iye anati: ‘Inu mudzayamwadi. Mudzanyamulidwa m’manja ndipo mudzasisitidwa mwachikondi mutaikidwa pamwendo. Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.’ (Yes. 66:12, 13) Zimasangalatsa kuona mmene mayi amatonthozera mwana wake pomunyamula kapena kumusisita. N’chifukwa chake Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzochi posonyeza mmene amakondera anthu amene amamulambira. Musamakayikire kuti Yehova amakuonani kuti ndinu ofunika ndipo amakukondani.—Yer. 31:3. w18.09 13 ¶6-7.
Loweruka, June 20
Ndani lero ali wokonzeka kupereka mphatso kwa Yehova?—1 Mbiri 29:5.
Kale ku Isiraeli, pankafunika anthu odzipereka kuti athandize pa zinthu zosiyanasiyana. (Eks. 36:2; Neh. 11:2) Masiku ano palinso njira zambiri zimene tingathandizire abale ndi alongo athu pogwiritsa ntchito nthawi, chuma komanso maluso athu. Mukatero mudzakhala osangalala komanso mudzadalitsidwa kwambiri. Anthu amene amadzipereka kuti agwire ntchito zosiyanasiyana m’gulu la Yehova amakhala ndi mwayi wopeza anzawo atsopano. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Margie, yemwe wakhala akugwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu kwa zaka 18. Pa zaka zimenezi, iye ankathandiza alongo achitsikana kuti adziwe zinthu zosiyanasiyana. Mlongoyu amaona kuti kudzipereka kugwira ntchitoyi kunamupatsa mwayi wolimbikitsana ndi Akhristu anzake. (Aroma 1:12) Margie akakumana ndi mavuto, anzake amene anawapeza pogwira ntchito zomangamanga akhala akumulimbikitsa. Kodi munayamba mwadzipereka kugwira nawo ntchito zomangamanga? w18.08 25 ¶9; 26 ¶11
Lamlungu, June 21
Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono. M’malomwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.—1 Tim. 4:12.
Pamene Paulo ankalemba mawuwa, Timoteyo ayenera kuti anali ndi zaka za m’ma 30. Komabe Paulo anamupatsa udindo waukulu. Kaya anamulembera malangizowa chifukwa chiyani, mfundo yake ndi yomveka bwino. Sitiyenera kuweruza abale achinyamata pongotengera msinkhu wawo. Tizikumbukiranso kuti ngakhale Ambuye wathu Yesu anachita utumiki wake padzikoli ali ndi zaka za m’ma 30 zokha. Mwina m’chikhalidwe chathu anthu amaderera amuna achinyamata. Ngati zili choncho, akulu mumpingo mwina sangafune kuti abale achinyamata omwe ndi oyenerera akhale atumiki othandiza kapena akulu. Akulu onse ayenera kukumbukira kuti Malemba sanena kuti munthu angakhale mtumiki wothandiza kapena mkulu akakwanitsa zaka zinazake.—1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9. w18.08 11-12 ¶15-16
Lolemba, June 22
[Pewa] zimene ena monama amati ndiye “kudziwa zinthu.”—1 Tim. 6:20.
Kuti tisankhe zochita mwanzeru pa nkhani inayake, timayenera kudziwa mfundo zoona. Choncho tiyenera kusankha bwino zimene timawerenga. (Afil. 4:8, 9) Tisamawononge nthawi powerenga zinthu zokayikitsa pa intaneti kapena nkhani zopanda umboni zimene timalandira m’maimelo. Koma chofunika kwambiri ndi kupewa mawebusaiti a anthu ampatuko. Tikutero chifukwa chakuti cholinga cha anthuwo ndi kusokoneza anthu a Mulungu komanso kupotoza choonadi. Ngati mfundo zimene tikudziwa pa nkhani inayake ndi zokayikitsa, sitingasankhe bwino zochita. Komanso musaiwale kuti ngati nkhani ili ndi mfundo zina zabodza ikhoza kusokoneza kwambiri maganizo komanso mtima wanu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika mu nthawi ya Mose. Pa anthu 12 amene anakaona Dziko Lolonjezedwa, anthu 10 anafotokoza zinthu zoipa. (Num. 13:25-33) Iwo anakokomeza zinthu moti anthu a Yehova anakhala ndi mantha komanso anataya mtima. (Num. 14:1-4, 6-10) Aisiraeliwo anasankha kukhulupirira zinthu zabodzazo m’malo moyesetsa kudziwa nkhani yonse komanso kukhulupirira Yehova. w18.08 4 ¶4-5
Lachiwiri, June 23
Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.—1 Akor. 15:33.
Anthu ambiri amakhala ndi makhalidwe abwino ndipo ena amene si a Mboni sachita zinthu zoipa kwambiri. Ngati umu ndi mmene zilili ndi anzanu, kodi zikutanthauza kuti palibe vuto kugwirizana nawo kwambiri? Ndi bwino kudzifunsa kuti, Kodi kugwirizana kwambiri ndi anthu amenewa kungakhudze bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova? Kodi ubwenziwo ukula kapena uchepa? Kodi anthuwo ali ndi mtima wotani? Mwachitsanzo, kodi amakonda kulankhula za mafashoni, ndalama, zipangizo zamakono, zosangalatsa kapena zinthu zina zakuthupi? Kodi amakonda kulankhula zonyoza ena kapena zotukwana? Pajatu Yesu ananena kuti: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Ngati mukuona kuti anzanu akhoza kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova, ndi bwino kuti muchepetse kucheza nawo kapena kungosiyiratu ndipo muchite zimenezo mwamsanga.—Miy. 13:20. w18.07 19 ¶11
Lachitatu, June 24
Moseyo anali munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse.—Num. 12:3.
Mose ali ndi zaka 80, Mulungu anamupatsa ntchito yokapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo. (Eks. 3:10) Mose anapereka zifukwa zosonyeza kuti sangakwanitse ntchitoyo koma Yehova anamulezera mtima. Ndipo anamupatsa mphamvu yochitira zozizwitsa (Eks. 4:2-9, 21) Iye akanatha kuopseza Mose kuti amvere msangamsanga. Koma m’malomwake, anamumvetsera moleza mtima ndipo anayesetsa kulimbikitsa Mose yemwe anali wodzichepetsa kwambiri. Kodi zimene Mulungu anachitazi zinathandiza? Inde. Mose anadzakhala mtsogoleri wabwino komanso wofatsa ndipo ankachita zinthu moganizira ena ngati mmene Yehova anachitira. Ngati muli ndi udindo woyang’anira ena, muyenera kutsanzira Yehova pa nkhani yochita zinthu mokoma mtima, moleza mtima komanso moganizira anthuwo. (Akol. 3:19-21; 1 Pet. 5:1-3) Mukamayesetsa kutsanzira Yehova komanso Yesu Khristu, yemwe ndi Mose Wamkulu, anthu azimasuka nanu ndipo mukhoza kuwalimbikitsa.—Mat. 11:28, 29. w18.09 24-25 ¶7-10
Lachinayi, June 25
Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!—Sal. 133:1.
Tiyeni tiziyesetsa kulimbikitsa mgwirizano pakati pa abale ndi alongo athu. Ngati mumachita kale zimenezi mukuchita bwino kwambiri. Koma mwina mukhoza ‘kufutukula mtima wanu’ powonjezera zimene mukuchitazo. (2 Akor. 6:11-13) Kodi mungawonjezere zimene mumachita poonetsa kuwala kwanu m’dera limene mumakhala? Mawu ndi zochita zanu zingathandize anthu amene mumakhala nawo pafupi kuti ayambe kuphunzira Baibulo. Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amene ndimakhala nawo pafupi amandiona bwanji? Kodi pakhomo panga ndi paukhondo? Kodi ndimayesetsa kuthandiza anthu ena? Mukamacheza ndi abale ndi alongo mungachite bwino kuwapempha kufotokoza mmene kukoma mtima kwawo ndi khalidwe lawo labwino zathandizira achibale awo, anthu okhala nawo pafupi, anzawo akuntchito kapena akusukulu. N’kutheka kuti angafotokoze zinthu zosangalatsa kwambiri.—Aef. 5:9. w18.06 24 ¶13-14
Lachisanu, June 26
Nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu.—Yoh. 16:2.
Izi n’zimene zinachitika pamene anthu anapha Sitefano komanso atumiki ena a Mulungu. (Mac. 6:8, 12; 7:54-60) N’zodabwitsa kuti anthu amene amati ndi opembedza amachita zoipa ngati zimenezi n’kumaphwanya malamulo a Mulungu amene amanena kuti amamupembedzayo. (Eks. 20:13) Apa zikuonekeratu kuti chikumbumtima chingathe kusocheretsa munthu. Kodi tingatani kuti chikumbumtima chathu chisamatisocheretse? Malamulo komanso mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu n’zothandiza “pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.” (2 Tim. 3:16) Choncho tiyenera kuphunzira Baibulo mwakhama, kuganizira mozama zimene taphunzira komanso kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu. Tikatero chikumbumtima chathu chimayendera maganizo a Mulungu ndipo chimatithandiza kuchita zinthu zabwino. Tsopano tiyeni tikambirane mmene malamulo komanso mfundo za Yehova zingatithandizire kuti tiziphunzitsa chikumbumtima chathu. w18.06 17 ¶3-4
Loweruka, June 27
Landirani . . . lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu.—Aef. 6:17.
Lupanga limene asilikali achiroma ankagwiritsa ntchito pa nthawi imene Paulo analemba kalata yake yopita kwa Aefeso linkakhala lalitali masentimita 50. Linkapangidwa m’njira yoti msilikali akhoza kuligwiritsa ntchito bwino pomenyana pafupi ndi msilikali wina. Asilikali achiroma ankatha kugwiritsa ntchito lupanga lawo mwaluso chifukwa ankayeserera tsiku lililonse. Paulo anayerekezera Mawu a Mulungu ndi lupanga. Koma tiyenera kuphunzira Mawuwo kuti tiziwagwiritsa ntchito mwaluso pofotokoza zimene timakhulupirira kapena kuti atithandize kusintha maganizo athu. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 2:15) Sitiyenera kuopa Satana kapena ziwanda zake. N’zoona kuti ndi amphamvu koma sikuti ndi osagonjetseka. Komanso iwo sadzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Posachedwapa, mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, adzamangidwa ndipo kenako adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 7-10) Timadziwa bwino mdani wathu, njira zimene amagwiritsa ntchito komanso zolinga zake. Koma Yehova akhoza kutithandiza kuti tisasunthike polimbana naye. w18.05 30 ¶15; 31 ¶19-21
Lamlungu, June 28
Njokayo inauza mkaziyo kuti: “Kufa simudzafa ayi.”—Gen. 3:4.
N’zosakayikitsa kuti Adamu ankadziwa zoti njoka sizilankhula. Choncho ayenera kuti anazindikira kuti pali winawake wauzimu amene anagwiritsa ntchito njokayo polankhula ndi Hava. (Gen. 3:1-6) Adamu ndi Hava sankadziwa chilichonse chokhudza mdani ameneyu. Ngakhale zinali choncho, Adamu anasankha kusamvera Atate wake wachikondi ndipo anagwirizana ndi mdani wosadziwikayo pochita zinthu zosemphana ndi cholinga cha Mulungu. (1 Tim. 2:14) Nthawi yomweyo, Yehova anayamba kuulula za mdani amene anasokoneza Adamu ndi Havayu ndipo analonjeza kuti adzawonongedwa. Koma Yehova anasonyezanso kuti kwa kanthawi ndithu, mdaniyo adzakhala ndi mphamvu zolimbana ndi anthu amene amakonda Mulungu. (Gen. 3:15) Popeza Yehova ndi wanzeru, sanatiuze dzina lenileni la mngelo amene anamugalukirayu. Ndipo Mulungu sanatchulenso dzina limene anapatsidwa loti Satana mpaka panadutsa zaka pafupifupi 2,500 kuchokera pamene anapusitsa anthu oyambirira.—Yobu 1:6. w18.05 22 ¶1-2
Lolemba, June 29
Ndi anthu amene . . . [amabereka] zipatso mwa kupirira.—Luka 8:15.
Ngati munakhumudwapo chifukwa cholalikira m’dera limene anthu ambiri safuna kumvetsera, mungamvetse bwino zimene mtumwi Paulo ananena. Pa zaka pafupifupi 30 zimene ankalalikira, anathandiza anthu ambiri kuti akhale Akhristu. (Mac. 14:21; 2 Akor. 3:2, 3) Komabe sanathe kuthandiza Ayuda ambiri kuti ayambe kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Ayuda ambiri sankamumvera ndipo ena ankamuzunza. (Mac. 14:19; 17:1, 4, 5, 13) Kodi zimenezi zinamukhudza bwanji Paulo? Iye ananena kuti: “Ndikunena zoona mwa Khristu . . . kuti ndili ndi chisoni chachikulu ndiponso mtima ukundipweteka nthawi zonse.” (Aroma 9:1-3) N’chifukwa chiyani Paulo ankamva chonchi? Iye ankalalikira ndi mtima wonse ndipo ankalalikira Ayuda chifukwa chowakonda. Choncho zinkamupweteka kwambiri chifukwa Ayuda ankakana kulandira chifundo cha Mulungu. Mofanana ndi Paulo, timalalikira anthu chifukwa chowakonda.—Mat. 22:39; 1 Akor. 11:1. w18.05 13 ¶4-5
Lachiwiri, June 30
Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.—Miy. 12:25.
Paulo anasonyeza kuti ngakhale abale amene ali ndi udindo wolimbikitsa ena amafunikanso kulimbikitsidwa. Mwachitsanzo, m’kalata yake yopita kwa Aroma, analemba kuti: “Ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugawireni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba, kapena kuti tidzalimbikitsane mwa chikhulupiriro, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Ngakhale kuti Paulo ankalimbikitsa kwambiri anthu ena, nayenso nthawi zina ankafunika kulimbikitsidwa. (Aroma 15:30-32) Abale ndi alongo amene amadzimana zinthu zina kuti atumikire Yehova ayenera kuyamikiridwa. Tilinso ndi abale ndi alongo amene sali m’banja chifukwa choti sanapeze munthu woti angakwatirane naye “mwa Ambuye.” Anthu oterewa amafunika kuwalimbikitsa. (1 Akor. 7:39) Akazi achikhristu amene amagwira ntchito zapakhomo mwakhama amafunika kulimbikitsidwanso ndi amuna awo. (Miy. 31:28, 31) Akhristu amene amakhalabe okhulupirika pamene akuzunzidwa kapena kudwala amafunikanso kulimbikitsidwa.—2 Ates. 1:3-5. w18.04 21 ¶3-5