July
Lachitatu, July 1
Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.—Aef. 5:17.
Panopa tili m’masiku ovuta kwambiri. Ndipo mavutowa aziwonjezereka pamene nthawi yoti padzikoli pakhalenso mtendere ikuyandikira. (2 Tim. 3:1) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimadalira ndani kuti andithandize ndiponso kundilangiza?’ M’mbuyomo, wolemba masalimo wina anasonyeza kuti tiyenera kuyang’ana kwa Yehova pa nthawi imene tapanikizika ndi mavuto. (Sal. 123:1-4) Iye anayerekezera kuyang’ana kwa Yehova ndi zimene kapolo amachita poyang’ana kwa mbuye wake. Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? N’zoona kuti kapolo amayang’ana kwa mbuye wake kuti amupatse chakudya komanso azimuteteza. Koma amayang’ananso mbuyeyo kuti adziwe zimene akufuna kenako n’kuchita zimene akufunazo. Ifenso tiyenera kufufuza m’Mawu a Mulungu tsiku lililonse kuti tidziwe zimene Yehova akufuna kenako n’kumachita zimene akufunazo. Tikamachita zimenezi sitingakayikire ngakhale pang’ono kuti iye adzatithandiza tikapanikizika ndi mavuto. w18.07 12 ¶1-2
Lachinayi, July 2
Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.—Yoh. 8:36.
Yesu ankatanthauza kumasuka ku ‘ukapolo wa uchimo’ womwe ndi woopsa kwambiri. (Yoh. 8:34) Uchimo sumangotichititsa zoipa koma umatilepheretsanso kuchita zimene tingathe kapena zimene tikudziwa kuti n’zolondola. Izi zikamachitika munthu amakhala pa ukapolo ndipo zotsatira zake zimakhala zakuti amakhala ndi nkhawa, amavutika, amamva ululu kenako n’kufa. (Aroma 6:23) Tikadzamasuka ku uchimo m’pamene tidzakhale pa ufulu weniweni umene Adamu ndi Hava anali nawo poyamba. Mawu a Yesu akuti “mukamasunga mawu anga nthawi zonse” amasonyeza kuti pali zinthu zina zimene tiyenera kutsatira komanso zimene tiyenera kupewa kuti iye atithandize kukhala pa ufulu. (Yoh. 8:31) Popeza tinadzipereka kwa Mulungu, ndiye kuti tinadzikana tokha n’kusankha moyo wotsatira zimene Yesu ankaphunzitsa. (Mat. 16:24) Malinga ndi zimene Yesu analonjeza, tidzakhala pa ufulu weniweni pa nthawi imene mavuto onse adzatha chifukwa cha dipo limene anapereka. w18.04 7 ¶14-16
Lachisanu, July 3
Inu nokha ndiye mumadziwa bwino mtima wa ana a anthu.—2 Mbiri 6:30.
Yehova amachitanso zinthu moganizira atumiki ake ngakhale pamene maganizo awo si abwino kwenikweni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yona. Yehova anamutuma kuti akapereke uthenga wachiweruzo kwa anthu a ku Nineve. Anthuwo atalapa, Mulungu sanawawononge. Ndiye Yona “anakwiya koopsa” poona kuti zimene analosera sizinachitike. Koma Yehova anamulezera mtima kwambiri ndipo anamuthandiza kuti asinthe maganizo ake. (Yona 3:10–4:11) Kenako Yona anamvetsa maganizo a Yehova ndipo anamugwiritsira ntchito kuti alembe nkhani yakeyi n’cholinga choti tiphunzirepo kanthu. (Aroma 15:4) Zimene Yehova wakhala akuchita ndi atumiki ake zimasonyeza kuti ali ndi mtima woganizira ena. Iye amadziwa mavuto amene munthu aliyense akukumana nawo. Iye amadziwa maganizo athu, zimene zili mumtima mwathu komanso zimene sitingathe kuchita. Ndipo ‘sangalole kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapirire.’ (1 Akor. 10:13) Kunena zoona, mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri. w19.03 16 ¶6-7
Loweruka, July 4
Kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.—Aheb. 4:13.
Mu Chilamulo cha Mose akulu ndi oweruza ankafunika kuweruza anthu pa nkhani zokhudza kulambira komanso milandu yosiyanasiyana. Taganizirani zitsanzo zina pa nkhaniyi. Munthu wa ku Isiraeli amene wapha mnzake sankaphedwa nthawi yomweyo. Akulu amumzinda umene ankakhala ankaifufuza nkhaniyo kuti adziwe ngati munthuyo ndi woyenera kuphedwa kapena ayi. (Deut. 19:2-7, 11-13) Akulu ankaweruzanso milandu yosiyanasiyana yokhudza katundu, mavuto a m’banja ndiponso nkhani zina. (Eks. 21:35; Deut. 22:13-19) Akuluwo akamachita zinthu mwachilungamo komanso Aisiraeli akamamvera malamulo, zinthu zinkawayendera bwino ndipo Yehova ankalemekezeka. (Lev. 20:7, 8; Yes. 48:17, 18) Apa zikuonekeratu kuti Yehova amaona chilichonse chimene chikuchitika pa moyo wathu. Iye amafuna kuti tizichita zinthu mwachikondi komanso mwachilungamo. Mulungu amamva zimene timalankhula komanso kuona zimene timachita ngakhale m’banja lathu. w19.02 23 ¶16-18
Lamlungu, July 5
Analola kuti asautsidwe, koma sanatsegule pakamwa pake.—Yes. 53:7.
Tikamada nkhawa zingativute kuti tikhalebe ofatsa. Ndiye tingayambe kulankhula kapena kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. Koma chitsanzo cha Yesu chingakuthandizeni pa nkhaniyi. Pa miyezi yomalizira ya moyo wake padzikoli, Yesu ankada nkhawa kwambiri. Iye ankadziwa kuti azunzika kwambiri komanso kuphedwa. (Yoh. 3:14, 15; Agal. 3:13) Pa nthawi ina, iye ananena kuti akuvutika kwambiri mumtima. (Luka 12:50) Kutatsala masiku ochepa kuti aphedwe, ananena kuti: “Moyo wanga ukusautsika.” Iye anasonyeza kudzichepetsa komanso kugonjera Mulungu pamene anauza Mulungu m’pemphero zamumtima mwake. (Yoh. 12:27, 28) Pa nthawi yake, Yesu analimba mtima n’kudzipereka kwa adani a Mulungu omwe anamupha m’njira yopweteka kwambiri komanso yochititsa manyazi. Ngakhale kuti ankada nkhawa komanso kuzunzika, Yesu anachitabe zimene Mulungu ankafuna. Apa zikuonekeratu kuti Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yokhalabe wofatsa ngakhale pamene ankada nkhawa.—Yes. 53:10. w19.02 11 ¶14-15
Lolemba, July 6
Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.—Aheb. 10:24.
Tingafunike kulimba mtima kuti tizisonkhana nthawi zonse ngakhale pamene zinthu zavuta. Abale ndi alongo ena amasonkhanabe ngakhale atakumana ndi mavuto monga maliro, matenda kapena zinthu zina zokhumudwitsa. Ena amapita kumisonkhano ngakhale kuti amatsutsidwa ndi achibale awo kapena akuluakulu a boma. Kodi mukuganiza kuti chitsanzo chathu chimalimbikitsa bwanji abale amene amangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo? (Aheb. 13:3) Iwo akamva kuti tikutumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto, amapitiriza kukhulupirira Mulungu, kulimba mtima komanso kukhala okhulupirika. Paulo ali kundende, ankasangalala akamva zoti abale akutumikirabe Mulungu mokhulupirika. (Afil. 1:3-5, 12-14) Atatsala pang’ono kumasulidwa kapena atangomasulidwa kumene, analembera kalata Akhristu achiheberi. M’kalatayo analimbikitsa Akhristuwo kuti asaleke kusonkhana.—Aheb. 10:25. w19.01 28 ¶9
Lachiwiri, July 7
Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.—1 Yoh. 5:19.
Satana ndi chigawenga chodzikonda komanso chosamvera Yehova ndipo amafuna kuti nafenso tizichita zomwezo. Iye angagwiritse ntchito anthu a m’dzikoli omwe wawasocheretsa kale n’cholinga choti ‘awononge’ maganizo ndi makhalidwe athu. (1 Akor. 15:33) Satana amafunanso kutisokoneza potichititsa kuganiza kuti nzeru za anthu n’zabwino kusiyana ndi za Mulungu. (Akol. 2:8) Mwachitsanzo, iye amafuna kuti anthu aziganiza kuti chofunika kwambiri pa moyo ndi kupeza chuma. Anthu amene amayendera maganizo amenewa akhoza kupezadi chuma kapena osachipeza. Koma kaya chumacho achipeze kapena ayi, akhoza kukumana ndi mavuto. Tikutero chifukwa chakuti pofunafuna chumacho amatha kuwononga thanzi lawo, mabanja awo mwinanso ubwenzi wawo ndi Mulungu. (1 Tim. 6:10) Timayamikira kwambiri kuti Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wanzeru, amatithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ndalama.—Mlal. 7:12; Luka 12:15. w19.01 15 ¶6; 17 ¶9
Lachitatu, July 8
Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe! Unakhulupirika pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.—Mat. 25:21.
Ngakhale Yesu asanabwere padzikoli, n’kupereka chitsanzo pa nkhani yolimbikitsa anthu, atumiki a Mulungu ena ankalimbikitsa anzawo. Mwachitsanzo, Asuri ataopseza Ayuda, Hezekiya anasonkhanitsa akuluakulu a asilikali komanso Ayuda ena kuti awalimbikitse. Baibulo limanena kuti “anthuwo anayamba kulimba mtima chifukwa cha mawu a Hezekiya.” (2 Mbiri 32:6-8) Pa nthawi imene Yobu anali pa mavuto aakulu anaperekanso chitsanzo chabwino pouza anthu amene anabwera kudzamutonthoza njira yabwino yolimbikitsira anthu. M’malo momulimbikitsa, anzakewo ankangomuimba mlandu. Yobu ananena kuti moyo wa anthuwo ukanakhala ngati moyo wake, iye akanawalimbikitsa ndiponso kuwatonthoza. (Yobu 16:1-5) Kenako Yobuyo analimbikitsidwa ndi Elihu komanso Yehova.—Yobu 33:24, 25; 36:1, 11; 42:7, 10. w18.04 16 ¶6; 17 ¶8-9
Lachinayi, July 9
Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.—Yes. 41:10.
Yesaya anali atafotokoza kale mmene Yehova adzalimbitsire anthu ake ponena kuti: “Adzabwera ngati wamphamvu ndipo dzanja lake lizidzalamulira m’malo mwa iyeyo.” (Yes. 40:10) Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “dzanja” kutanthauza mphamvu. Choncho mawu oti “dzanja lake lizidzalamulira” akutikumbutsa kuti Yehova ndi Mfumu yamphamvu. Iye anagwiritsa ntchito mphamvu zake zosagonjetseka kuti athandize komanso kuteteza atumiki ake m’mbuyomu ndipo akupitiriza kuchita zomwezo kwa anthu amene amamudalira. (Deut. 1:30, 31; Yes. 43:10) Yehova amakwaniritsa mawu ake akuti: “Ndikulimbitsa.” Amachita zimenezi makamaka pa nthawi imene tikuzunzidwa. Kumayiko ena adani athu akuyesetsa kuti aletse ntchito yathu yolalikira kapena athetse gulu lathu. Ngakhale zili choncho, sitichita mantha. Yehova watipatsa lonjezo limene limatipatsa mphamvu komanso kutilimbitsa mtima. Iye watilonjeza kuti: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.”—Yes. 54:17. w19.01 5-6 ¶12-13
Lachisanu, July 10
Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.—Mat. 5:3.
Mosiyana ndi zinyama, anthufe timakhala ndi zosowa zauzimu ndipo amene angatisamalire pa nkhaniyi ndi Mlengi wathu yekha. (Mat. 4:4) Mukamamumvera ndi mtima wonse mumayamba kukhala ozindikira, anzeru komanso osangalala. Mulungu amakusamalirani mwauzimu pogwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso chakudya chambiri chauzimu chimene chimachokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Chakudyachi chimakhala chosiyanasiyana komanso chabwino kwambiri. (Yes. 65:13, 14) Chakudyachi chingakuthandizeni kukhala anzeru komanso oganiza bwino. Zimenezi zingakutetezeni m’njira zosiyanasiyana. (Miy. 2:10-14.) Mwachitsanzo, kuganiza bwino komanso nzeru zingakuthandizeni kuzindikira mfundo zabodza monga yakuti kulibe Mulungu. Zingakutetezeni ku bodza lakuti ndalama ndi chuma n’zimene zingakuthandizeni kukhala osangalala. Zimakuthandizaninso kuzindikira ndi kupewa kulakalaka zinthu zimene zingakupwetekeni. Choncho muziyesetsa kukhala anzeru komanso oganiza bwino ndipo muziona kuti zimenezi ndi chuma chamtengo wapatali. w18. 12 20 ¶6-7
Loweruka, July 11
Masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo.—Yes. 65:22.
Kodi ndi liti pamene masiku a anthufe “adzakhala ngati masiku a mtengo?” Mitengo ina imakhala zaka masauzande angapo. Kuti anthu akhale ndi moyo zaka zonsezi afunika kukhala athanzi. Ndipo zinthu zabwino zonse zimene Yesaya analosera zitati zichitike ndiye kuti paradaiso wafika basi. Komatu ulosi umenewu udzakwaniritsidwa ndithu. Ganizirani mmene malonjezo amulemba la leloli akusonyezera kuti kudzakhala paradaiso. Anthu padziko lonse adzadalitsidwa ndi Mulungu ndipo sadzaopanso zilombo zolusa kapena anthu oopsa. Anthu osaona, okhala ndi vuto la kumva komanso olumala adzachiritsidwa. Anthu adzamanga nyumba zawo komanso kulima mbewu zomwe zizidzabereka bwino. Azidzakhala ndi moyo masiku ambiri kuposa a mitengo. Baibulo limasonyeza kuti zonsezi zidzachitika m’tsogolomu. Koma ena akhoza kuganiza kuti maulosiwa satanthauza kuti paradaiso adzakhala padzikoli. Kodi inuyo mutamva wina akunena zimenezi mungamuyankhe bwanji? Kodi n’chiyani chimakutsimikizirani kuti paradaiso adzabweradi padzikoli? Yesu anapereka zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira zimenezi.—Luka 23:43. w18.12 5 ¶13-15
Lamlungu, July 12
Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.—Aroma 12:2.
Maganizo athu amatha kusintha. Zimene timalola kuti zilowe m’maganizo mwathu n’kumaziganizira zimatha kusintha kaganizidwe kathu. Choncho tikamaganizira kwambiri maganizo a Yehova tingayambe kuona kuti ndi olondola. Tikatero tidzakhala ndi mtima wofuna kumayendera maganizo akewo. Komabe, kuti munthu ayambe kukhala ndi maganizo a Yehova amafunika kusiya ‘kutengera nzeru za nthawi ino.’ Tiyenera kupewa maganizo kapena mfundo zotsutsana ndi maganizo a Mulungu. Zimenezi tingaziyerekezere ndi zakudya. Munthu amene akufuna kukhala wathanzi akhoza kuganiza kuti asinthe n’kumadya zakudya zopatsa thanzi. Koma kodi munthuyo angakhale wathanzi ngati amadyanso zakudya zoipa? Mofanana ndi zimenezi, kuphunzira maganizo a Yehova sikungatithandize kwenikweni ngati timasokonezanso maganizo athu ndi nzeru za m’dzikoli. w18.11 21 ¶14-15
Lolemba, July 13
Khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi m’chiuno mwanu.—Aef. 6:14.
Tiyenera kutsimikiza mumtima mwathu kuti tizitsatira mfundo za choonadi tsiku lililonse. Choonadi chiyenera kukhala ngati lamba amene tamanga m’chiuno mwathu. Kale, lamba wa msilikali ankateteza chiuno ndi ziwalo zina zamkati. Koma kuti lambayo amuteteze bwino ankafunika kumumanga mwamphamvu. Tikutero chifukwa lamba wokhwepa sankathandiza msilikali. Tikamangirira mwamphamvu choonadi ngati lamba, chimatiteteza kuti tipewe maganizo olakwika ndipo chimatithandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Tikamayesedwa kapena kuzunzidwa, mfundo za m’Baibulo zimatithandiza kuti tichite zinthu zoyenera. Msilikali sankapita kunkhondo opanda lamba. Nafenso sitiyenera kuyerekeza ngakhale pang’ono kukhwepetsa kapena kumasuliratu lamba wathu wa choonadi. Koma tizimangirira mwamphamvu lambayu poyesetsa kutsatira mfundo za choonadi pa moyo wathu. w18.11 12 ¶15
Lachiwiri, July 14
Gula choonadi ndipo usachigulitse.—Miy. 23:23.
Munthu sangapeze choonadi cha m’Mawu a Mulungu popanda kuchita khama. Munthu ayenera kulolera kuti asakhale ndi zinthu zina n’cholinga choti apeze choonadichi. Paja wolemba buku la Miyambo ananena kuti tiyenera ‘kugula’ kapena kupeza choonadi n’kumayesetsa kuti ‘tisachigulitse’ kapena kulola kuti chitayike. Munthu amafunika kuchita zinazake kuti apeze chinthu ngakhale chinthucho chitakhala chaulere. Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “gula” pa Miyambo 23:23 angamasuliridwenso kuti “peza.” Mawu onsewa amatanthauza kuchita zinazake, kapena kusiya zinazake kuti upeze chinthu chamtengo wapatali. Kuti timvetse mfundoyi, taganizirani za chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti kumsika winawake alengeza kuti kuli nthochi zaulere. Kodi nthochizo zingafike m’nyumba mwathu popanda kuchita chilichonse? Ayi. Tingafunike kupita kumsikako kuti tikazitenge. Kodi pamenepa tingati nthochizo ndi zaulere? Inde n’zaulere koma tifunika kuchita zinazake komanso kupeza nthawi yokazitengera kumsikako. Ndi mmene zililinso ndi kugula choonadi. N’zoona kuti ndi chaulere koma timafunika kuchita zinthu zina kuti tichipeze. w18.11 4 ¶4-5
Lachitatu, July 15
Nkhope yake inawala ngati dzuwa. Malaya ake akunja anawala kwambiri.—Mat. 17:2.
Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane n’kupita nawo kuphiri lalitali. Ali kuphiriko, ophunzirawo anaona zinthu zodabwitsa. Nkhope ya Yesu inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinawalanso. Ndiyeno panaoneka Mose ndi Eliya akulankhula naye zokhudza imfa yake. (Luka 9:29-32) Kenako mtambo waukulu unawaphimba ndipo panamveka mawu a Mulungu kuchokera mumtambowo. Masomphenyawa ankasonyeza zimene zidzachitike Yesu akadzalandira mphamvu ndi ulemerero monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. N’zosachita kufunsa kuti Yesu analimbikitsidwa kwambiri moti anali wokonzeka kupirira mavuto ndi imfa zimene anali atatsala pang’ono kukumana nazo. Zimene ophunzirawa anaona zinalimbitsanso chikhulupiriro chawo n’kuwapatsa mphamvu kuti adzapirire komanso kugwira ntchito mwakhama m’tsogolo. Patapita zaka 30, mtumwi Petulo anafotokoza za masomphenyawa ndipo izi zikusonyeza kuti ankawakumbukirabe.—2 Pet. 1:16-18. w19.03 10 ¶7-8
Lachinayi, July 16
Tikusonyeza . . . kuti ndife atumiki a Mulungu . . . [tikamalankhula] zoona.—2 Akor. 6:4, 7.
Kodi Akhristu enieni amasiyana ndi anthu azipembedzo zina m’njira iti? Ifeyo timalankhula zoona zokhazokha. (Zek. 8:16, 17) Timalankhula zoona pa nkhani zikuluzikulu komanso zing’onozing’ono kwa anthu achilendo, anzathu akuntchito, anzathu apamtima komanso kwa anthu a m’banja lathu. Ngati ndinu wachinyamata mwina mumafuna kuti anzanu asamakusaleni. Komabe muyenera kuyesetsa kuti musamachite zinthu mwachiphamaso n’kumaoneka abwino mukakhala ndi anthu a m’banja lanu kapena amumpingo koma n’kusintha mukakhala ndi achinyamata a m’dzikoli kapena mukamacheza pa intaneti. Mukamachita zimenezi mumakhala mukuchita chinyengo ndipo mukunamiza makolo anu, Akhristu anzanu komanso Mulungu. (Sal. 26:4, 5) Yehova amadziwa ‘tikamamulemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yathu ili kutali ndi iye.’ (Maliko 7:6) Tingachite bwino kwambiri kutsatira mawu akuti: “Mtima wako usamasirire anthu ochimwa, koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.”—Miy. 23:17. w18.10 9 ¶14-15
Lachisanu, July 17
Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu amene amapitiriza kusonyeza chikondi, amakhalabe wogwirizana ndi Mulungu ndiponso Mulungu amakhala wogwirizana naye.—1 Yoh. 4:16.
Anthu a Mulungu amakhala ngati banja limodzi ndipo amakondana. (1 Yoh. 4:21) Sikuti amangosonyeza chikondi m’zinthu zikuluzikulu zokha koma m’zinthu zing’onozing’ononso zimene amachita ndiponso kunena. Tikamachita zinthu mokoma mtima komanso moganizira ena timakhala kuti ‘tikutsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Yesu ankatsanzira Atate wake pa zonse zimene ankachita. Iye anati: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani . . . , chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28, 29) Tikamatsanzira Khristu pa nkhani yochita zinthu “moganizira munthu wonyozeka” timasangalatsa Atate wathu wakumwamba ndipo nafenso timakhala osangalala. (Sal. 41:1) Choncho tiyeni tizisonyeza chikondi pochita zinthu moganizira anthu a m’banja lathu, mumpingo komanso mu utumiki. w18.09 28 ¶1-2
Loweruka, July 18
Ndife antchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.
Pakachitika ngozi, timakhala ndi mwayi wogwira ntchito ndi Mulungu pothandiza abale ndi alongo athu. Mwachitsanzo, tikhoza kuwathandiza ndi ndalama zathu. (Yoh. 13:34, 35; Mac. 11:27-30) Tingawathandizenso pokonza zinthu zimene zinaonongeka pa ngoziyo. Nyumba ya mlongo wina wa ku Poland dzina lake Gabriela, inawonongeka chifukwa cha kusefukira kwa madzi. Iye anasangalala pamene abale ndi alongo a m’mipingo yapafupi ndi kwawo anabwera kudzamuthandiza. Mlongoyo ananena kuti: “Sindifotokoza za zinthu zimene zinawonongeka chifukwa si zofunika kwenikweni. Koma ndikufuna kufotokoza za madalitso amene ndinapeza. Zimene ndakumana nazozi zandithandiza kuzindikira kuti kukhala mumpingo wachikhristu ndi mwayi waukulu komanso kumakuthandiza kukhala wosangalala.” Anthu ambiri amene anathandizidwa atakumana ndi ngozi amanena kuti analimbikitsidwa kwambiri. Komanso abale ndi alongo amene amagwira ntchito ndi Yehova pothandiza anthuwa amasangalala kwambiri.—Mac. 20:35; 2 Akor. 9:6, 7. w18.08 26 ¶12
Lamlungu, July 19
Uteteze mtima wako.—Miy. 4:23.
Kuti titeteze mtima wathu tiyenera kuzindikira zinthu zimene zingatisokoneze n’kumazipewa mwamsanga. Mawu amene anamasuliridwa kuti ‘kuteteza’ amatikumbutsa za ntchito imene mlonda amagwira. Pa nthawi ya Mfumu Solomo, alonda ankaima pampanda wa mzinda n’kumachenjeza anthu akaona zoopsa. Mfundo imeneyi imatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita kuti Satana asasokoneze maganizo athu. Kale, alonda apampanda ankagwira ntchito mogwirizana ndi alonda apachipata. (2 Sam. 18:24-26) Iwo ankathandizana poteteza mzinda ndipo ankaonetsetsa kuti mageti atsekedwa pamene adani akubwera. (Neh. 7:1-3) Chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo chimakhala ngati mlonda ndipo chimatichenjeza pamene Satana akufuna kuwononga mtima wathu kapena kuti pamene akuyesetsa kusokoneza maganizo athu, zolinga zathu kapena zimene timalakalaka. Chikumbumtima chathu chikatichenjeza tiyenera kumvera n’kuchita zinthu mwamsanga ngati mlonda amene watseka geti. w19.01 17 ¶10-11
Lolemba, July 20
Atumikire monga atumiki, popeza ndi opanda chifukwa chowanenezera.—1 Tim. 3:10.
Abale achinyamata ayenera kuweruzidwa mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, osati potengera chikhalidwe kapena maganizo a anthu. (2 Tim. 3:16, 17) Chikhalidwe kapena maganizo a anthu zingachititse kuti abale oyenera asaikidwe pa udindo. M’dziko lina, mtumiki wothandiza wina yemwe anali woyenerera anapatsidwa maudindo akuluakulu. Ngakhale kuti akulu mumpingowo anaona kuti m’bale wachinyamatayo anali woyenerera mogwirizana ndi Malemba kuti akhale mkulu, sanaikidwe kukhala mkulu. Zinali choncho chifukwa akulu ena achikulire ankaona kuti m’baleyo ankaoneka wamng’ono kwambiri moti sangakhale mkulu. N’zomvetsa chisoni kuti m’bale wachinyamatayo sanaikidwe kukhala mkulu chifukwa choti ankaoneka wamng’ono basi. Malipoti akusonyeza kuti anthu m’mipingo yambiri padziko lonse ali ndi maganizo olakwikawa. Choncho tiyenera kudalira Malemba osati maganizo athu. Tikamatero ndiye kuti tikumvera Yesu n’kumapewa kuweruza anthu poona maonekedwe awo.—Yoh. 7:24. w18.08 12 ¶16-17
Lachiwiri, July 21
Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.—Miy. 18:13.
Kutumiza maimelo ndiponso mameseji mopupuluma ndi koopsa. M’mayiko ena, ntchito yathu ndi yoletsedwa. Ndipo adani athu m’mayikowa akhoza kufalitsa nkhani n’cholinga choti atiopseze kapena kutichititsa kuti tizikayikirana. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika ku Soviet Union. Apolisi amene ankadziwika kuti KGB anafalitsa mabodza okhudza abale ena amene ankatsogolera m’gulu. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri anakhulupirira mabodzawa moti anachoka m’gulu la Yehova. Chosangalatsa n’chakuti ambiri mwa anthuwo anabwerera koma ena sanabwerere ndipo ‘chikhulupiriro chawo chinasweka ngati ngalawa.’ (1 Tim. 1:19) Kodi tingapewe bwanji mavuto ngati amenewa? Tiyenera kupewa kufalitsa nkhani zoipa kapena zimene zilibe umboni. Komanso sitiyenera kukhulupirira nkhani ngati sitikudziwa mfundo zake zonse. w18.08 4 ¶8
Lachitatu, July 22
Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.—Luka 23:43.
M’mipukutu yoyambirira yachigiriki sankagwiritsa ntchito kwambiri zizindikiro za m’kalembedwe. Ndiye kodi Yesu ananena kuti, “Ndithu ndikukuuza, lero iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso?” Kapena ananena kuti, “Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso?” Koma tisaiwale kuti izi zisanachitike, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mwana wa munthu adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, usana ndi usiku.” (Mat. 12:40; 16:21; 17:22, 23; Maliko 10:34; Mac. 10:39, 40) Izi zikusonyeza kuti Yesu sanapite kuparadaiso aliyense pa tsiku limene anaphedwa limodzi ndi chigawenga chija. Iye anali m’manda kwa masiku angapo mpaka pamene Mulungu anamuukitsa. (Mac. 2:31, 32) Chigawenga chija sichinkadziwa kuti Yesu anachita pangano ndi atumwi ake okhulupirika loti akalamulire naye mu Ufumu wakumwamba. (Luka 22:29) Chigawengacho chinalinso chosabatizidwa n’komwe. (Yoh. 3:3-6, 12) Choncho tingati paradaiso amene Yesu analonjeza ndi wapadzikoli. w18.12 6 ¶17-18, 20-21
Lachinayi, July 23
Tipangire mulungu woti atitsogolere, chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose.—Eks. 32:1.
Pasanapite nthawi yaitali, Aisiraeli anayamba kulambira mwana wa ng’ombe wagolide. Ukutu kunali kusamvera, koma Aisiraeliwo ankadzipusitsa n’kumaganiza kuti adakali kumbali ya Yehova. Aroni anafika ponena kuti zimene ankachita polambira mwana wa ng’ombeyo zinali “chikondwerero cha Yehova.” Kodi Yehova anachita chiyani? Zinamupweteka kwambiri poona kuti anthuwo amusiya. Anauza Mose kuti ‘anthuwo achita zinthu zowawonongetsa ndipo apatuka mwamsanga pa njira imene anawalamula kuyendamo.’ Yehova anakwiya moti anaganiza zopha Aisiraeli onsewo. (Eks. 32:5-10) Koma kenako Yehova anasintha maganizo ofuna kuwawonongawo. (Eks. 32:14) Ngakhale kuti Aroni anapanga nawo mwana wa ng’ombeyo, analapa n’kupita kumbali ya Yehova limodzi ndi Alevi enawo. Iwo anachita zinthu mwanzeru chifukwa tsiku limeneli anthu masauzande angapo amene analambira fano anaphedwa. Koma anthu amene anali kumbali ya Yehova analonjezedwa kuti adzadalitsidwa.—Eks. 32:26-29. w18.07 20 ¶13-16
Lachisanu, July 24
Chenjerani ndi alembi. Iwo amakonda . . . kupatsidwa moni m’misika ndi kukhala . . . malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.—Luka 20:46.
Anthu ambiri m’dzikoli amafuna kuti akhale odziwika kwa ena pa nkhani ya maphunziro, zamalonda komanso zosangalatsa. Koma ifeyo timaona kuti pali munthu wofunika kwambiri amene timafuna kuti atidziwe. Pa nkhaniyi, Paulo anafotokoza kuti: “Tsopano pamene mwadziwa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano pamene mwadziwidwa ndi Mulungu, mukubwereranso bwanji ku mfundo zachibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake, n’kumafuna kukhalanso akapolo ake?” (Agal. 4:9) Ndi mwayitu waukulu ‘kudziwidwa ndi Mulungu,’ yemwe ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Iye amatidziwa, amatikonda komanso amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova ndiye kuti takwaniritsa cholinga chimene anatilengera.—Mlal. 12:13, 14. w18.07 8 ¶3-4
Loweruka, July 25
Ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.—Sal. 119:99.
Kuti malamulo a Mulungu azitithandiza, tiyenera kuwakonda komanso kuwalemekeza. (Amosi 5:15) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Chofunika ndi kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Tiyerekeze kuti muli ndi vuto losowa tulo. Kenako dokotala akukuuzani kuti muzichita masewera olimbitsa thupi, muzidya zakudya zabwino komanso musinthe zinthu zina pa moyo wanu. Ndiyeno mutatsatira malangizowo mukuona kuti mwayamba kupeza tulo bwinobwino. Mukhoza kuthokoza kwambiri dokotalayo chifukwa chokuthandizani. Nayenso Mlengi wathu watipatsa malamulo otithandiza kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso tisamakumane ndi mavuto chifukwa cha uchimo. Tangoganizirani mmene timapindulira tikamatsatira malamulo a m’Baibulo pa nkhani ya kunama, chiwembu, kuba, chiwerewere, chiwawa ndiponso kuchita zamizimu. (Miy. 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikazindikira ubwino woyenda m’njira za Yehova, timayamba kumukonda kwambiri komanso kukonda malamulo ake. w18.06 17 ¶5-6
Lamlungu, July 26
Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?—Yoh. 18:33.
Mwina Pilato ankaopa kuti Yesu akhoza kuyambitsa chisokonezo mu ufumu wake. Koma Yesu anamuyankha kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yoh. 18:36) Iye sankafuna kuchita nawo zandale chifukwa Ufumu wake unali wakumwamba. Choncho anauza Pilato kuti anabwera padziko lapansi “kudzachitira umboni choonadi.” (Yoh. 18:37) Tikamamvetsa cholinga cha utumiki wathu ngati Yesu, tidzapeweratu kuchita chilichonse chosonyeza kuti tili mbali inayake pa nkhani zandale. Koma nthawi zina zimenezi zimakhala zovuta. Woyang’anira dera wina ananena kuti: “Masiku ano, anthu a m’dera lathu ali ndi mtima wofunitsitsa kusintha zinthu. Ndipo anthu ochuluka amakonda kwambiri dziko lawo moti amaona kuti zinthu zikhoza kuyamba kuwayendera bwino ngati atamalamuliridwa ndi anthu amtundu wawo. Koma n’zosangalatsa kuti abale ndi alongo amakhalabe ogwirizana chifukwa amaika maganizo awo pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene angathetse zinthu zopanda chilungamo komanso mavuto amene timakumana nawo.” w18.06 4-5 ¶6-7
Lolemba, July 27
Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.—Yak. 4:7.
M’Malemba Achiheberi muli mabuku atatu okha amene amatchula dzina loti Satana, lomwe limatanthauza “Wotsutsa.” Mabuku ake ndi 1 Mbiri, Yobu ndi Zekariya. N’chifukwa chiyani Yehova sanafotokoze kwambiri za mdaniyu Mesiya asanafike? Zikuoneka kuti Yehova sankafuna kutchukitsa Satana polola kuti zinthu zambiri zokhudza iyeyo zilembedwe m’Malemba Achiheberi. Cholinga chachikulu chimene anauzira anthu kuti alembe Malembawo chinali kuthandiza anthu kuzindikira Mesiya ndiponso kutsogolera anthu a Mulungu kwa Mesiyayo. (Luka 24:44; Agal. 3:24) Mesiya atafika, Yehova anamugwiritsa ntchito limodzi ndi ophunzira ake kufotokoza zambiri zokhudza Satana komanso ziwanda. Zimenezi n’zomveka chifukwa Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu limodzi ndi olamulira anzake kuti aphwanye Satana ndi otsatira ake. (Aroma 16:20; Chiv. 17:14; 20:10) Tisaiwale kuti mphamvu za Mdyerekezi zili ndi malire. Ndipo kumbali yathu kuli Yehova, Yesu ndi angelo okhulupirika. Iwo angatithandize kulimbana ndi mdani wathuyu. w18.05 22-23 ¶2-4
Lachiwiri, July 28
Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso amaidula.—Yoh. 15:2.
Yehova amaona kuti ndife atumiki ake enieni tikamabereka zipatso. (Mat. 13:23; 21:43) Mfundoyi ikusonyeza kuti m’fanizo la pa Yohane 15:1-5, zipatso zimene Mkhristu aliyense ayenera kubereka sizingaimire anthu amene tinawathandiza kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mat. 28:19) Zikanakhala choncho, ndiye kuti Akhristu amene sathandiza anthu kukhala ophunzira chifukwa amalalikira m’madera ovuta, akanakhala m’gulu la nthambi zosabereka zipatso. Komatu zimenezo sizingakhale zomveka chifukwa sitingakakamize anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Yehova sangakane atumiki ake chifukwa cholephera kuchita zinthu zimene sangakwanitse. Paja chilichonse chimene Yehova amatipempha kuti tichite chimakhala choti tingachikwanitse. (Deut. 30:11-14) Ndiye zipatsozi zikuimira zinthu zimene aliyense akhoza kukwanitsa. Choncho “kubereka zipatso” kukuimira kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Mat. 24:14. w18.05 14 ¶8-9
Lachitatu, July 29
Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi . . . Iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.—Yoh. 8:44.
Kaya amadziwika kuti abusa, ansembe, arabi kapena ndi mayina ena, atsogoleri achipembedzo chonyenga ali paliponse. Iwo “akupondereza choonadi” chochokera m’Mawu a Mulungu ndipo “anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza.” (Aroma 1:18, 25) Iwo amaphunzitsa mabodza monga akuti munthu akangolandira Khristu ndiye kuti wapulumutsidwa basi, mzimu sufa, munthu akamwalira amabadwanso kwinakwake komanso kuti Mulungu amavomereza kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Nawonso andale amanamiza anthu. Koma iwo adzanena bodza lalikulu kwambiri pamene azidzati “bata ndi mtendere!” Baibulo limanena kuti akadzangonena bodzali “chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” Tisadzapusitsidwe n’kuyamba kuganiza kuti zinthu zayamba kuyenda bwino m’dzikoli. Paja timadziwa kuti “tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.”—1 Ates. 5:1-4. w18.10 7-8 ¶6-8
Lachinayi, July 30
Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Mac. 20:35.
Yesu Khristu amagwiritsa ntchito “akalonga” omwe ndi akulu odzozedwa komanso a nkhosa zina kuti alimbikitse komanso kutsogolera abale ndi alongo amene akusowa mtendere chifukwa cha mavuto. N’chifukwa chake akuluwa amayesetsa kuti ‘asakhale olamulira chikhulupiriro chathu koma antchito anzathu kuti tikhale ndi chimwemwe.’ (Yes. 32:1, 2; 2 Akor. 1:24) Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Pamene Akhristu a ku Tesalonika ankazunzidwa, iye anawalembera kuti: “Popeza timakukondani kwambiri, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeniyeniyo, chifukwa tinakukondani kwambiri.” (1 Ates. 2:8) Pozindikira kuti mawu olimbikitsa okha si okwanira nthawi zina, Paulo anauza Akhristu a ku Efeso mawu amulemba la lero. w18.04 21-22 ¶6-8
Lachisanu, July 31
Yehova ndiye Mzimu, ndipo pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.—2 Akor. 3:17.
Kuti ife tipeze ufulu umenewu, tiyenera ‘kutembenukira kwa Yehova’ kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi. (2 Akor. 3:16) Aisiraeli ali m’chipululu, sankaona moyenera zinthu zimene Yehova ankawachitira. Tingati anali ndi chophimba m’maganizo ndi mumtima moti ankaona kuti ufulu umene analandira potulutsidwa ku Iguputo unali wongowathandiza kuti azipanga zimene akufuna, osati azisangalatsa Yehova. (Aheb. 3:8-10) Ufulu umene munthu amapeza mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu umathandiza m’njira zambiri, osati kungom’masula munthu ku ukapolo weniweni. Mzimu wa Mulungu umathandiza munthu kuti asakhale kapolo wa uchimo, imfa, kulambira konyenga komanso zikhulupiriro zabodza. (Aroma 6:23; 8:2) Kodi umenewu si ufulu weniweni? Munthu akhoza kukhala pa ufulu umenewu ngakhale pamene ali mundende kapena ku ukapolo.—Gen. 39:20-23. w18.04 9 ¶3-5