August
Loweruka, August 1
Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.—Aroma 5:8.
Kumisonkhano timakumbutsidwa zimene Yehova ndi Yesu atichitira. Poyamikira, timayesetsa kutsanzira Yesu pa moyo wathu. (2 Akor. 5:14, 15) Timalimbikitsidwanso kutamanda Yehova chifukwa chopereka dipoli. Njira ina imene tingamutamandire ndi kuyankha pamisonkhano ya mpingo. Tingasonyeze kuti timakonda Yehova ndi Yesu pololera kuti tisachite zinthu zina n’cholinga choti tiziwatumikira. Kunena zoona, pamafunika kudzimana zinthu zina kuti tizipezeka pamisonkhano. M’mipingo yambiri, misonkhano ina imachitika mkati mwa mlungu ndipo anthu ambiri amakhala atatopa pambuyo poweruka kuntchito. Ina imachitika kumapeto kwa mlungu pa nthawi imene anthu ena amakhala akupuma. Yehova amadziwa zoti timalolera kupita kumisonkhano ngakhale titatopa. Ndipo tikamayesetsa kuti tipezeke pamisonkhano ngakhale zinthu zitavuta m’pamenenso Yehova amayamikira kwambiri.—Maliko 12:41-44. w19.01 29 ¶12-13
Lamlungu, August 2
Pamene Ambuye anaona mayiwo, anawamvera chifundo.—Luka 7:13.
Yesu anakumanaponso ndi mavuto. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Yesu analeredwa m’banja losauka. Iye anaphunzira kugwira ntchito mwakhama limodzi ndi Yosefe, yemwe anali bambo ake omulera. (Mat. 13:55; Maliko 6:3) Zikuonekanso kuti Yosefe anamwalira Yesu asanamalize utumiki wake padzikoli. Choncho amadziwa mmene zimapwetekera munthu amene umamukonda akamwalira. Yesu anakuliranso m’banja limene munali anthu osiyana zikhulupiriro. (Yoh. 7:5) Zinthu zimenezi komanso mavuto ena, zinathandiza Yesu kumvetsa mavuto a anthu. Umboni wakuti Yesu anali ndi mtima woganizira ena unkaonekera akamachita zozizwitsa. Sikuti ankangochita zozizwitsa pongofuna kuthana ndi mavuto a anthuwo. Iye ankachitira chifundo anthu amene ankavutika. (Mat. 20:29-34; Maliko 1:40-42) Yesu anamvera anthuwo chisoni ndipo anali ndi mtima wofuna kuwathandiza.—Maliko 7:32-35; Luka 7:12-15. w19.03 16 ¶10-11
Lolemba, August 3
Pitirizani kulolerana.—Akol. 3:13.
Tangoganizirani mmene Yesu ankamvera usiku woti aphedwa mawa lake. Mwina ankadera nkhawa ngati angakhalebe wokhulupirika mpaka imfa. Ankadziwanso kuti ngati sangakhale wokhulupirika anthu mabiliyoni ambiri sadzakhala ndi mwayi wopeza moyo wosatha. (Aroma 5:18, 19) Koma chofunika kwambiri n’chakuti zimene akanachita zikanakhudza dzina la Atate wake. (Yobu 2:4) Ndiye usikuwo pa nthawi ya chakudya cha madzulo, atumwi ake anayamba kukangana “pakati pawo za amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.” Koma chochititsa chidwi n’chakuti Yesu sanapse mtima. M’malomwake anakambirana nawo modekha. Yesu anawafotokozeranso mokoma mtima koma mosapita m’mbali maganizo amene ayenera kukhala nawo. Kenako iye anawayamikira chifukwa chokhala anzake okhulupirika. (Luka 22:24-28; Yoh. 13:1-5, 12-15) Tingachite bwino kutsanzira Yesu n’kumakhalabe ofatsa ngakhale pamene tikuda nkhawa. Tingachite zimenezi tikamakumbukira kuti tonsefe timanena komanso kuchita zinthu zimene sizisangalatsa anthu ena. (Miy. 12:18; Yak. 3:2, 5) Tiyeneranso kuyamikira anthu ena pa zabwino zimene amachita.—Aef. 4:29. w19.02 11-12 ¶16-17
Lachiwiri, August 4
Yehova [wakhazikitsa] mpando wake wachifumu kuti aweruze.—Sal. 9:7.
Chilamulo cha Mose chinkathandiza kuti munthu asamanamiziridwe mlandu. Munthu woimbidwa mlandu anali ndi ufulu wodziwa munthu amene akumuimba mlanduwo. (Deut. 19:16-19; 25:1) Pankafunikanso anthu awiri kuti apereke umboni munthuyo asanaweruzidwe. (Deut. 17:6; 19:15) Ndiye kodi chinkachitika n’chiyani ngati panali mboni imodzi yokha pa mlandu winawake? Wopalamulayo sankayenera kuganiza kuti basi wapulumuka. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anaona zimene wachita. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri chifukwa chilichonse chimene amachita chimakhala chachilungamo. Iye amadalitsa anthu amene amatsatira mfundo zake mokhulupirika koma amalanga anthu amene amapondereza anzawo. (2 Sam. 22:21-23; Ezek. 9:9, 10) Anthu ena akachita zoipa zimaoneka ngati azemba chilango koma Yehova akaona kuti nthawi yabwino yafika amawalanga mwachilungamo. (Miy. 28:13) Ndipo ngati salapa, amadzazindikira kuti “kulandira chilango chochokera kwa Mulungu wamoyo n’chinthu choopsa.”—Aheb. 10:30, 31. w19.02 23-24 ¶20-21
Lachitatu, August 5
Mu Isiraeli simunakhalebe mneneri aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova anali kumudziwa pamasom’pamaso.—Deut. 34:10.
Mose ankayang’ana kwa Yehova kuti amupatse malangizo. Paja Baibulo limati iye “anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Aheb. 11:24-27) Pasanathe miyezi iwiri kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, anakumana ndi vuto lalikulu. Asanafike n’komwe kuphiri la Sinai, anayamba kudandaula za kusowa kwa madzi. Iwo anayamba kung’ung’udzira Mose ndipo zinafika povuta moti Mose anadandaulira Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pang’ono kundiponya miyala!” (Eks. 17:4) Yehova atamva, anauza Mose zoyenera kuchita. Anamuuza kuti atenge ndodo yake n’kumenya mwala ku Horebe kuti madzi atuluke. Baibulo limati: “Mose anachitadi zomwezo, pamaso pa akulu a Isiraeli.” Zitatero Aisiraeli anayamba kumwa moti ludzu lawo linatheratu.—Eks. 17:5, 6. w18.07 13 ¶4-5
Lachinayi, August 6
Chikondi chimamangirira.— 1 Akor. 8:1.
Yehova amatisonyezanso chikondi kudzera mumpingo wachikhristu. Tingasonyeze kuti timayamikira chikondi chake tikamakonda abale ndi alongo athu komanso kuwalimbikitsa. (1 Yoh. 4:19-21) Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.” (1 Ates. 5:11) Izi zikusonyeza kuti Mkhristu aliyense mumpingo, osati akulu okha, angatsanzire Yehova ndi Yesu potonthoza komanso kulimbikitsa abale ndi alongo. (Aroma 15:1, 2) Koma abale ndi alongo amene akudwala matenda amaganizo angafunike thandizo la kuchipatala. (Luka 5:31) Akulu komanso anthu ena mumpingo ayenera kukumbukira kuti iwo si madokotala a matenda ngati amenewa. Ngakhale zili choncho, pali zinthu zina zofunika zimene aliyense mumpingo akhoza kuchita. Tonsefe tiyenera ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wachisoni, kuthandiza ofooka komanso kukhala oleza mtima kwa onse.’—1 Ates. 5:14. w18.09 14 ¶10-11
Lachisanu, August 7
Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.—Yes. 41:10.
Tikamamudziwa bwino Yehova m’pamene timayamba kumudalira kwambiri. Njira imodzi yokha yotithandiza kumudziwa bwino ndi kuwerenga Baibulo mosamala kenako n’kuganizira kwambiri zimene tawerengazo. M’Baibulo muli nkhani zosonyeza mmene Yehova anatetezera anthu ake m’mbuyomu. Nkhani zoterezi zimatitsimikizira kuti ifenso sangatisiye. Yesaya anagwiritsa ntchito mawu abwino kwambiri pofotokoza mmene Yehova amatitetezera. Iye anayerekezera Yehova ndi m’busa ndipo atumiki ake anawayerekezera ndi ana a nkhosa. Pofotokoza za Yehova, Yesaya analemba kuti: “Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” (Yes. 40:11) Tikazindikira kuti dzanja lamphamvu la Yehova likutiteteza sitichita mantha ngakhale pang’ono. Kuti musamade nkhawa ndi mavuto amene mungakumane nawo, muyenera kuganizira mawu olimbikitsa amulemba la leroli. Mawu amenewa adzakuthandizani kwambiri mukadzakumana ndi mavuto m’tsogolomu. w19.01 7 ¶17-18
Loweruka, August 8
Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.—Sal. 40:8.
Kodi muli ndi zolinga zauzimu zimene mukuyesetsa kuti mukwaniritse? N’kutheka kuti mukuyesetsa kuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse. Apo ayi mwina mukuchita khama kuti mukhale ndi luso lokamba nkhani kapena lophunzitsa. Mukayamba kukwaniritsa zolinga zanu kapena anthu ena akakuyamikirani pa zimene mukuchitazo, kodi mumamva bwanji? Muyenera kuti mumasangalala kwambiri. Izi ndi zomveka chifukwa mukuika zimene Mulungu amafuna pamalo oyamba ndipo mukutsatira chitsanzo cha Yesu. (Miy. 27:11) Mukamaika kutumikira Yehova pamalo oyamba, ndiye kuti mukuchita zimene zingakuthandizeni kukhala ndi cholinga chabwino pa moyo komanso kukhala osangalala. Paja mtumwi Paulo analemba kuti: “Khalani olimba, osasunthika, okhala ndi zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye, podziwa kuti zonse zimene mukuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.” (1 Akor. 15:58) Koma anthu amene amayesetsa kuti alemere kapena akhale otchuka m’dzikoli, ngakhale amene angaoneke kuti zinthu zikuwayendera bwino, sakhala osangalala.—Luka 9:25. w18.12 22 ¶12-13
Lamlungu, August 9
Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.—Sal. 37:29.
Davide ankanena za nthawi imene anthu onse padzikoli azidzayendera mfundo za Mulungu zachilungamo. (2 Pet. 3:13) Ndipo ulosi wa pa Yesaya 65:22 umanena kuti: “Masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo.” Izi zikutanthauza kuti anthu azidzakhala zaka masauzande. Malinga ndi lemba la Chivumbulutso 21:1-4, Mulungu adzadalitsa anthu ndipo lonjezo lina ndi lakuti “imfa sidzakhalaponso.” Adamu ndi Hava anataya mwayi wokhala m’paradaiso mu Edeni koma mwayiwu sunatheretu. Mulungu walonjeza kuti anthu adzadalitsidwanso padzikoli. Davide anauziridwa kulemba kuti ofatsa komanso olungama adzakhala padzikoli kwamuyaya. (Sal. 37:11) Ulosi wa Yesaya uyenera kutichititsa mtima dyokodyoko kuti tidzaone madalitso amene Yehova walonjeza. (Yes. 11:6-9; 35:5-10; 65:21-23) Zonsezi zidzachitika m’paradaiso amene Yesu analonjeza chigawenga chija. (Luka 23:43) Ndipo inunso mukhoza kudzakhala m’paradaisoyu. w18.12 7 ¶22-23
Lolemba, August 10
Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa.—Miy. 4:23.
Kodi n’zotheka kupeweratu maganizo a m’dzikoli? Ayi, chifukwa tidakali m’dziko lomweli. Nthawi zina maganizo a m’dzikoli amakhala osapeweka. (1 Akor. 5:9, 10) Paja tikamalalikira timakumana ndi anthu amene ali ndi maganizo olakwika. Koma ngati tamva maganizo osemphana ndi a Yehova, tiyenera kuyesetsa kuti tisayambe kutengera maganizowo. Tiyenera kutsanzira Yesu amene ankakana mwamsanga maganizo amene akanamuchititsa kukhala kumbali ya Satana. Ndipo tiyenera kudziteteza kuti tisamachite dala zinthu zimene zingachititse kuti tisokonezedwe ndi maganizo olakwika. Mwachitsanzo, tiyenera kusamala posankha anthu ocheza nawo. Baibulo limatichenjeza kuti tikamacheza kwambiri ndi anthu amene salambira Mulungu, tikhoza kutengera maganizo awo. (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:12, 32, 33) Tikamapewanso zinthu zolimbikitsa chiwerewere, chiwawa kapena maganizo oti zamoyo sizinachite kulengedwa, sitidzasokonezedwa ndi “chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu.”—2 Akor. 10:5. w18.11 21 ¶16-17
Lachiwiri, August 11
Ndidzayenda m’choonadi chanu.—Sal. 86:11.
Kodi tingatani kuti titsimikize mumtima mwathu zoyendabe m’choonadi? Njira ina ndi kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira. Tikamachita zimenezi timakhala ngati tikugwira mwamphamvu lupanga la mzimu lomwe ndi “mawu a Mulungu.” (Aef. 6:17) Tonsefe tikhoza kuwonjezera luso lathu ‘pophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ (2 Tim. 2:15) Tikamagwiritsa ntchito Baibulo pothandiza anthu kugula choonadi n’kusiya zikhulupiriro zabodza, timakhala tikukhomerezanso mawu a Mulungu m’maganizo ndi m’mitima yathu. Tikamatero sitidzasiya kuyenda m’choonadi. Choonadi ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa. Chimatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova womwe ndi wamtengo wapatali kwambiri. Koma zimene Yehova wakhala akutiphunzitsazi n’zochepa tikaziyerekezera ndi zimene adzatiphunzitse tikadzalandira moyo wosatha. Choncho tiziyamikira choonadi ngati ngale yamtengo wapatali. Tiyeni tipitirize ‘kugula choonadi ndipo tisachigulitse.’—Miy. 23:23. w18.11 8 ¶2; 12 ¶15-17
Lachitatu, August 12
Nowa [anali] mlaliki wa chilungamo.—2 Pet. 2:5.
Chigumula chisanachitike, Nowa ankalalikira ndipo zikuoneka kuti uthenga wake wina unali wochenjeza anthu. Tikutero chifukwa Yesu ananena kuti: “M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mat. 24:38, 39) Ngakhale kuti anthu sankamumvera, Nowa anapitiriza kuwauza uthengawo mokhulupirika. Masiku anonso, timalalikira uthenga wa Ufumu kuti tithandize anthu kudziwa cholinga cha Mulungu chokhudza anthufe. Mofanana ndi Yehova, timafunitsitsa kuti anthu amvere uthengawo n’cholinga choti ‘akhalebe ndi moyo.’ (Ezek. 18:23) Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba kapena m’malo opezeka anthu ambiri, timachenjezanso anthu kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera ndipo udzawononga dziko loipali.—Ezek. 3:18, 19; Dan. 2:44; Chiv. 14:6, 7. w18.05 19 ¶8-9
Lachinayi, August 13
Wotulutsa mawu okhulupirika amanena zolungama.—Miy. 12:17.
Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati ntchito yathu yaletsedwa m’dziko limene tikukhala ndipo akuluakulu a boma akutifunsa za Akhristu anzathu? Kodi tiyenera kuwauza zonse zimene tikudziwa? Chitsanzo chabwino ndi zimene Yesu anachita pamene bwanamkubwa wa Aroma ankamufunsa mafunso. Mogwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula,” pa nthawi ina, Yesu sankayankha chilichonse. (Mlal. 3:1, 7; Mat. 27:11-14) Choncho zimenezi zikatichitikira, tiyenera kukhala osamala kuti tisabweretsere mavuto abale ndi alongo athu. (Miy. 10:19; 11:12) Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mnzanu kapena wachibale wanu wachita tchimo lalikulu ndipo mukudziwa zimene zinachitika? Muyenera kunena zoona. Muli ndi udindo wouza akulu zinthu zonse zimene mukudziwa ndipo simu yenera kusintha mfundo zina. Iwo ayenera kudziwa nkhani yonse n’cholinga choti adziwe njira yabwino yothandizira munthuyo kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova.—Yak. 5:14, 15. w18.10 10 ¶17-18
Lachisanu, August 14
Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.—1 Ates. 5:11.
Kodi tingatani kuti tilimbikitse anthu mwachikondi? Chinthu china chimene tingachite ndi kuwamvetsera bwino. (Yak. 1:19) Munthu wachikondi amamvetsera kuti adziwe mmene mnzake akumvera. Ndi bwino kufunsa mafunso mwanzeru kuti mudziwe zimene zili mumtima mwa munthu amene akuvutika. Mukatero mudzatha kumumvetsa komanso kumulimbikitsa. Nkhope yanu iyenera kusonyeza kuti mukumudera nkhawa ndipo mukufuna kumuthandiza. Ngati akufuna kufotokoza zinthu zina, tingachite bwino kumumvetsera moleza mtima popanda kumudula mawu. Mukamamumvetsera moleza mtima mudzazindikira zimene zikumudetsa nkhawa. Mukatero, munthuyo amayamba kukukhulupirirani ndipo zingakhale zosavuta kuti akumvetsereni mukamamuuza mfundo zolimbikitsa. Mukamasonyeza kuti mumamuganizira komanso kumukonda mudzatha kumulimbikitsa kwambiri. w18.09 14 ¶10; 15 ¶13
Loweruka, August 15
Gula choonadi.—Miy. 23:23.
Pamafunika nthawi kuti munthu apeze choonadi. Mwachitsanzo, munthu ayenera kupeza nthawi yoti amve uthenga wa Ufumu, awerenge Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo, aziphunzira payekha, azikonzekera misonkhano komanso azipezeka pamisonkhanopo. Kuti zimenezi zitheke, munthu amafunika ‘kugula’ nthawi kapena kugwiritsa ntchito nthawi imene akanachitira zinthu zina zosafunika kwenikweni. (Aef. 5:15, 16) Kodi pamafunika nthawi yaitali bwanji kuti munthu aphunzire mfundo zoyambirira za m’Baibulo? Zimadalira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthuyo. Palibe malire ophunzirira nzeru za Yehova, njira zake komanso ntchito zake. (Aroma 11:33) Magazini yoyambirira ya Nsanja ya Olonda inayerekezera kupeza choonadi ndi kupeza kaduwa kokongola. Magaziniyo inati: “Zikanakhala kuti kaduwa kamodziko n’kokwanira si bwenzi pali enanso. Choncho tisamangokhutira ndi mfundo imodzi yokha ya choonadi. Nthawi zonse tizifufuza mfundo zina.” Ngakhale titalandira moyo wamuyaya padzakhalabe mfundo zambiri zokhudza Yehova zimene tingaphunzire. Chofunika panopa ndi kugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi yathu kuti tiziphunzira mfundo zambiri za choonadi. w18.11 5 ¶7
Lamlungu, August 16
Pitirizani kukonda akazi anu.—Aef. 5:25.
Baibulo limanena kuti amuna ayenera kukhala ndi akazi awo “mowadziwa bwino.” Mawu oti “mowadziwa bwino” akhoza kumasuliridwanso kuti “mowaganizira” kapena “mowamvetsa.” (1 Pet. 3:7) Kuti munthu achite zinthu moganizira wina, choyamba amafunika kumumvetsa. Mwachitsanzo, mwamuna womvetsa amadziwa kuti mkazi wake ndi womuthandiza choncho kusiyana naye mu zinthu zina sikuchititsa kuti akhale wotsika. (Gen. 2:18) Izi zimamuthandiza kuti aziganizira mmene akumvera mumtima mwake n’kumachita naye zinthu mwaulemu. Mwamuna amene amaganizira mkazi wake amakhalanso wosamala pochita zinthu ndi akazi ena. Amapewa kukopana kapena kucheza nawo mopitirira malire. Amachitanso zinthu mosamala akamacheza ndi anthu pa intaneti kapena kuonera zinthu pa intanetipo. (Yobu 31:1) Iye amakhala wokhulupirika kwa mkazi wake chifukwa choti amamukonda, amakonda Mulungu komanso amadana ndi zoipa.—Sal. 19:14; 97:10. w18.09 29 ¶3-4
Lolemba, August 17
Aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.—Luka 9:48.
N’chifukwa chiyani zimativuta kutsatira zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu? Chifukwa chimodzi n’chakuti pamafunika kudzichepetsa kuti tizichita zoyenera, koma kukhala odzichepetsa n’kovuta kwambiri m’masiku otsiriza ano. Zili choncho chifukwa masiku ano, anthu ambiri ndi “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza” komanso “osadziletsa.” (2 Tim. 3:1-3) Atumiki a Mulungufe sitisangalala anthu akamachita zinthu modzikonda, koma nthawi zina tikhoza kusirira zimene anthu oterewa amapeza chifukwa cha kudzikondako. (Sal. 37:1; 73:3) Mwina tikhoza kufika podzifunsa kuti: ‘Kodi kuchita zinthu moganizira anthu ena kuli ndi ubwino uliwonse? Kodi anthu sangasiye kundilemekeza ndikamachita zinthu “ngati wamng’ono”?’ Ngati tingatengere khalidwe lodzikonda, tingasiye kugwirizana ndi Akhristu anzathu komanso anthu ena sangadziwe kuti ndife Akhristu. Koma tikamaphunzira za anthu otchulidwa m’Baibulo n’kumatsatira chitsanzo chawo chabwino, timadalitsidwa.w18.09 3 ¶1
Lachiwiri, August 18
Kupatsa kumabweretsa chimwemwe.—Mac. 20:35.
Yehova asanayambe kulenga zinthu anali yekhayekha. Koma sikuti ankangoganiza za iye yekha basi. Tikutero chifukwa anapereka mphatso ya moyo kwa angelo komanso anthu. Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe,” amakonda kupatsa ena zinthu zabwino. (1 Tim. 1:11; Yak. 1:17) Iye amafuna kuti tizisangalala, choncho amatiphunzitsa kuti tizikhala opatsa. (Aroma 1:20) Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake. (Gen. 1:27) Izi zikutanthauza kuti iye anatilenga m’njira yoti tizitha kusonyeza makhalidwe ake. Choncho kuti tizikhala osangalala, tikuyenera kutsatira chitsanzo cha Yehova poganizira za anthu ena komanso kukhala opatsa. (Afil. 2:3, 4; Yak. 1:5) Zili choncho chifukwa umu ndi mmene Yehova anatilengera. Ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kutsanzira Yehova pa nkhani yopatsa.—Aef. 5:1. w18.08 18 ¶1-2; 19 ¶4
Lachitatu, August 19
Nkhosa zanga zimamva mawu anga.—Yoh. 10:27.
Otsatira a Khristu amasonyeza kuti amamva mawu ake osati pongomvetsera koma potsatira zimene watiuzazo. Iwo salola kusokonezeka ndi “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) Ngakhale zinthu zitavuta kwambiri, iwo amaona kuti chofunika kwambiri ndi kutsatira mawu a Yesu. Abale athu amakhalabe okhulupirika kwa Yehova zivute zitani. Njira ina imene tingasonyezere kuti timamvera Yesu ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi anthu amene asankhidwa kuti azititsogolera. (Aheb. 13:7, 17) Posachedwapa, gulu la Yehova lasintha zinthu zambiri. Mwachitsanzo, pali zinthu zatsopano zogwiritsa ntchito mu utumiki, njira zatsopano zolalikirira, njira yochitira misonkhano ya mkati mwa mlungu ndiponso njira zomangira Nyumba za Ufumu komanso kuzikonza. Malangizo amene timalandirawa amasonyeza kuti Yehova amatikonda. Sitikayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova adzatidalitsa tikamatsatira malangizo apanthawi yake amene gulu lake limatipatsa. w19.03 10-11 ¶11-12
Lachinayi, August 20
Tisakhalenso . . . otengeka kupita uku ndi uku ndi . . . chiphunzitso chonyenga cha anthu.—Aef. 4:14.
Nkhani ya ziganizo 10 imene ili ndi chiganizo chimodzi chokha cholakwika ikhoza kusokonezeratu munthu. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Aisiraeli amene ankakhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano m’masiku a Yoswa. (Yos. 22:9-34) Iwo anamva kuti Aisiraeli amene ankakhala kum’mawa anamanga guwa lalikulu. Zimene anamvazi zinali zoona. Koma popeza sankadziwa zonse zokhudza nkhaniyi, anaganiza kuti abale awowo asiya kulambira Yehova. (Yos. 22:9-12) Koma mwamwayi, anaganiza zotumiza kaye anthu odalirika kuti akafufuze zoona zake. Kodi anapeza zotani? Abale awowo sanamange guwalo kuti aziperekapo nsembe koma kuti chingokhala chikumbutso. Ankafuna kuti anthu odzabadwa m’tsogolo adzazindikire kuti nawonso anali atumiki a Yehova okhulupirika. Aisiraeli akumadzulowo ayenera kuti anasangalala kuti sanapupulume n’kupha abale awo koma anafufuza kaye n’kudziwa zoona zenizeni. w18.08 5 ¶9-10
Lachisanu, August 21
Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.—1 Akor. 10:12.
Mawu a Paulowa akusonyeza kuti ngakhale anthu amene amalambira Yehova akhoza kuchita zinthu zolakwika. Anthu amene amagonja pa mayesero akhoza kuganiza kuti Yehova akuwakondabe. Koma kungofuna kapena kungonena kuti ndife okhulupirika kwa Yehova sikutanthauza kuti tili naye pa ubwenzi wabwino. (1 Akor. 10:1-5) Mofanana ndi Aisiraeli amene anayamba kuda nkhawa Mose atachedwa kuphiri la Sinai, Akhristu masiku ano akhoza kuda nkhawa poganiza kuti tsiku la Yehova komanso dziko latsopano zikuchedwa. Mwina angayambe kuganiza kuti zinthuzi zili kutali kwambiri kapena sizichitika n’komwe. Kupanda kusamala, maganizo amenewa akhoza kuchititsa munthu kuti aziika zinthu zakuthupi pamalo oyamba m’malo mwa zimene Mulungu amafuna. Mapeto ake tikhoza kuchita zinthu zimene poyamba sitinkaganiza n’komwe kuti tingazichite. w18.07 21 ¶17-18
Loweruka, August 22
Ndidzachita izinso zimene wanena, chifukwa ndakukomera mtima ndipo ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe.—Eks. 33:17.
Tingapeze madalitso ambiri ngati Yehova atatidziwa bwino. Kuti tikhale odziwika kwa Yehova, tiyenera kumukonda komanso kudzipereka kwa iye. (1 Akor. 8:3) Koma tiyenera kuyesetsa kuti tipitirize kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Tikufunika kutsatira malangizo amene Paulo analembera Akhristu a ku Galatiya akuti azipewa kukhala akapolo a “mfundo zachibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake” za m’dzikoli monga kufuna kudziwika kwa anthu. (Agal. 4:9) Akhristu akalewo anali atafika podziwidwa ndi Mulungu. Koma Paulo ananena kuti Akhristuwa anayamba ‘kubwereranso’ ku zinthu zopanda pake. Zinali ngati akuwauza kuti: “Inu mwasintha zambiri kuti mufike pamenepa, ndiye n’chifukwa chiyani mukubwereranso ku zinthu zopusa komanso zopanda phindu zomwe munazisiya?” w18.07 8 ¶5-6
Lamlungu, August 23
Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.—Miy. 1:5.
Sikuti tiyenera kuphunzira nkhwangwa ili m’mutu kuti tione ubwino wotsatira malamulo a Mulungu. Koma tiziphunzirapo kanthu pa zimene anthu ena otchulidwa m’Baibulo analakwitsa. Tikamawerenga komanso kuganizira mozama nkhani za m’Baibulo zimene zinachitikadi timapeza malangizo abwino ochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Davide zinamupwetekera ataphwanya lamulo la Mulungu n’kuchita chigololo ndi Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Mukamawerenga nkhaniyi mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Davide akanapewa bwanji mavuto amene anakumana nawo chifukwa chochita chigololo ndi Bati-seba? Kodi ineyo nditakumana ndi mayesero ngati amenewo ndingalimbe? Kodi ndidzathawa ngati Yosefe kapena ndidzakopeka ngati Davide?’ (Gen. 39:11-15) Tikamaganizira mavuto amene tingakumane nawo chifukwa chochita tchimo, tikhoza kutsimikiza mumtima mwathu kuti ‘tizidana ndi zoipa.’—Amosi 5:15. w18.06 17 ¶5, 7
Lolemba, August 24
Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.—Mat. 22:21.
Nthawi zambiri, zinthu zopanda chilungamo zikachitika anthu amayamba kukangana pa nkhani zandale. Mwachitsanzo, m’nthawi ya Yesu anthu ankakangana pa nkhani ya msonkho. Anthu amene ankalamuliridwa ndi Aroma, kuphatikizapo amene Yesu ankawalalikira, ankapereka msonkho pa zinthu zambiri monga katundu, malo ndi nyumba. Okhometsa misonkho ankachita zachinyengo ndipo zimenezi zinkapangitsa operekawo kuona kuti akuponderezedwa. Okhometsa misonkho ena ankachita kugula udindo wawowo n’cholinga choti azipeza ndalama zambiri. Mwachitsanzo, Zakeyu anali mkulu wa okhometsa misonkho ku Yeriko ndipo analemera chifukwa choti ankabera anthu. (Luka 19:2, 8) N’kutheka kuti panali anthu ambiri amene ankachita zinthu ngati zimenezi. Adani a Yesu anamufunsa zokhudza msonkho pofuna kuti akhale kumbali inayake pa nkhani zandale. Msonkho umene ankamufunsa unali wa dinari imodzi ndipo nzika iliyonse ya mu ufumu wa Aroma inkafunika kupereka. (Mat. 22:16-18) Ayuda sankafuna kupereka msonkhowu chifukwa munthu akapereka ankasonyeza kuti akugonjera ulamuliro wa Aroma. w18.06 5-6 ¶8-10
Lachiwiri, August 25
Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.—Agal. 6:7.
Mavuto amene munthu angakumane nawo akakhala kumbali ya Satana, nthawi zonse amakhala aakulu kwambiri kuposa mapindu amene angapeze. (Yobu 21:7-17; Agal. 6:8) Kodi kudziwa mphamvu zimene Satana ali nazo kumatithandiza bwanji? Kumatithandiza kuona moyenera olamulira a m’dzikoli komanso kumatilimbikitsa kugwira mwakhama ntchito yolalikira. Timadziwa kuti Yehova amafuna kuti tizilemekeza maboma. (1 Pet. 2:17) Amafunanso kuti tizimvera malamulo a mabomawa kupatulapo ngati akusemphana ndi malamulo a Mulungu. (Aroma 13:1-4) Koma timadziwa kuti sitiyenera kuchita nawo zandale. Si bwino kukondera chipani chinachake kapena wolamulira winawake. (Yoh. 17:15, 16; 18:36) Popeza timaona kuti Satana akuyesetsa kuipitsa kwambiri dzina la Yehova, timafunitsitsa kuphunzitsa anthu mfundo zoona zokhudza Mulungu wathu. Timanyadira kudziwika ndi dzina lake komanso kuligwiritsa ntchito. Timadziwanso kuti kukonda Mulungu n’kothandiza kwambiri kuposa kukonda ndalama kapena chuma.—Yes. 43:10; 1 Tim. 6:6-10. w18.05 24 ¶8-9
Lachitatu, August 26
Mkazi asasiye mwamuna wake.—1 Akor. 7:10.
Kodi Mkhristu akakumana ndi mavuto m’banja lawo, akhoza kungopatukana? Malemba amanena kuti munthu akhoza kuthetsa banja ngati mnzake wachita dama, koma safotokoza zifukwa zochititsa kuti anthu apatukane. Paulo analemba kuti: “Mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupirira, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye mwamuna wakeyo.” (1 Akor. 7:12, 13) Masiku anonso tiyenera kutsatira malangizo amenewa. N’zoona kuti nthawi zina mwamuna “wosakhulupirira” amasonyeza kuti sakufuna kuti akhalebe ndi mkazi wake. Mwina amamuchitira nkhanza moti mkaziyo amaona kuti moyo wake uli pa ngozi. Apo ayi mwina amakaniratu kusamalira iyeyo ndi ana ake. Kapenanso amamulepheretsa kulambira Yehova. Zimenezi zikachitika akazi ena angasankhe kupatukana ndi mwamunayo chifukwa choona kuti ‘sakulola kukhala naye’ ngakhale kuti sananene zimenezi. Koma Akhristu ena amene akumana ndi mavuto oterewa amasankha kungopirira n’kumayesetsa kuti banja lawo liziyenda bwino. w18.12 13 ¶14; 14 ¶16-17
Lachinayi, August 27
Ndi anthu amene . . . [amabereka] zipatso mwa kupirira.—Luka 8:15.
Mufanizo la wofesa mbewu lopezeka pa Luka 8:5-8, 11-15, mbewu zikuimira “mawu a Mulungu” kapena kuti uthenga wa Ufumu. Nthaka ikuimira mtima wophiphiritsa wa munthu. Mbewu zimene zimagwera panthaka yabwino zimazika mizu kenako n’kukula ndipo zimabereka “zipatso kuwirikiza maulendo 100.” Mofanana ndi nthaka yabwino ya mufanizoli, tinalandira uthengawo n’kuugwiritsitsa. Ndiye tinganene kuti uthengawo unazika mizu n’kukula ndipo linakhala phesi la tirigu lomwe likhoza kubereka zipatso. Mofanana ndi phesi la tirigu lomwe limabereka tinjere osati mapesi ena, ifenso zipatso zimene timabereka sizikhala ophunzira atsopano koma mbewu zatsopano za Ufumu. Ndiye kodi timabereka bwanji mbewu zatsopano za Ufumu? Nthawi iliyonse imene timauza anthu uthenga wa Ufumu, timakhala ngati tikuchulukitsa ndiponso kumwaza mbewu imene inafesedwa mumtima mwathu. (Luka 6:45; 8:1) Choncho fanizoli limasonyeza kuti tikamapitiriza kuuza anthu uthenga wa Ufumu, timakhala ‘tikubereka zipatso mopirira.’ w18.05 14 ¶10-11
Lachisanu, August 28
Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.—Chiv. 3:19.
Paulo ankalimbikitsa abale ake koma ankayesetsanso ‘kugwiritsa ntchito zinthu zake zonse ndiponso kudzipereka ndi moyo wake wonse’ pofuna kuwathandiza. (2 Akor. 12:15) Nawonso akulu ayenera kulimbikitsa abale ndi alongo ndiponso kupeza njira zodziwira mavuto awo n’kumawathandiza. (1 Akor. 14:3) Kupereka malangizo ndi njira inanso imene akulu angalimbikitsire anthu. Koma pochita zimenezi, akulu ayenera kutsatira zitsanzo zabwino za m’Baibulo n’cholinga choti malangizo awo akhale olimbikitsa. Chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi ndi Yesu. Iye ataukitsidwa anafunika kupereka malangizo amphamvu kumipingo ina ya ku Asia Minor. Koma asanapereke malangizo aliwonse anayamba ndi kuyamikira mpingo wa Efeso, Pegamo ndi Tiyatira. (Chiv. 2:1-5, 12, 13, 18, 19) Akulu ayenera kutengera chitsanzo cha Yesu popereka malangizo. w18.04 22 ¶8-9
Loweruka, August 29
Abambo, . . . muwalere [ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.—Aef. 6:4.
N’zosachita kufunsa kuti ngati ndinu makolo, mumateteza ana anu kuti asadwale matenda alionse. Mwachitsanzo, mumaonetsetsa kuti pakhomo panu m’paukhondo komanso mumataya chilichonse chimene chingadwalitse inuyo kapena ana anu. Mofanana ndi zimenezi, muyenera kuteteza ana anu ku mafilimu, mapulogalamu a pa TV, masewera a pa kompyuta komanso mawebusaiti amene akhoza kuwachititsa kuti atengere maganizo a Satana. Yehova wakupatsani udindo wosamalira ana anu mwauzimu. (Miy. 1:8) Choncho musamaope kuika malamulo m’banja lanu omwe akugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Muziuza ana anu zinthu zoyenera kuonera ndi zosayenera kuonera ndipo muziwathandiza kuzindikira zifukwa zake. (Mat. 5:37) Ndiyeno anawo akamakula, muziwathandiza kuti azigwiritsa ntchito mfundo za Yehova kuti azitha kuzindikira paokha zoyenera ndi zolakwika. (Aheb. 5:14) Muzikumbukiranso kuti ana amatsatira kwambiri zochita zanu.—Deut. 6:6, 7; Aroma 2:21. w19.01 16 ¶8
Lamlungu, August 30
Okalamba pamodzi ndi ana . . . atamande dzina la Yehova.—Sal. 148:12, 13.
Ngati ndinu wachinyamata, mungachite bwino kumacheza ndi achikulire. Mukhoza kuwapempha mwaulemu kuti afotokoze zinthu zimene akumana nazo potumikira Yehova. Zimenezi zingalimbikitse achikulirewo komanso inuyo kuti muzionetsa kwambiri kuwala kwanu. Tonsefe tiyeneranso kulandira bwino anthu amene abwera kudzasonkhana nafe ku Nyumba ya Ufumu. Munthu amene wapemphedwa kuti achititse msonkhano wokonzekera utumiki angathandizenso kwambiri abale ndi alongo achikulire. Angawapatse gawo lomwe angakwanitse kukalalikira. Nthawi zina pangafunike kuwagawa ndi munthu wamphamvuko amene angamawathandize poyenda. Angachitenso bwino kuganizira anthu amene sangakwanitse kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena mavuto ena. Abalewa akamachita zinthu moganizira anthu, kaya achinyamata kapena achikulire, angawathandize kuti azilalikira uthenga wabwino mwakhama.—Lev. 19:32. w18.06 23-24 ¶10-12
Lolemba, August 31
Ufulu wanu usakhale ngati chophimbira zoipa, koma monga akapolo a Mulungu.—1 Pet. 2:16.
Tisamapeputse zimene Mulungu wachita potimasula ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Dipo limatithandiza kuti tizitumikira Mulungu mosangalala tili ndi chikumbumtima chabwino. (Sal. 40:8) Kuwonjezera pa kuyamikira ufulu wathu, tiyenera kupewa kuugwiritsa ntchito molakwika. Mtumwi Petulo ananena kuti si bwino kugwiritsa ntchito ufuluwu kuti tikwaniritse zimene thupi lathu limalakalaka. Chenjezo limeneli liyenera kutikumbutsa zimene zinachitikira Aisiraeli m’chipululu. Choncho nafenso tiyenera kukhala osamala chifukwa n’zosavuta kuti tikodwe mumsamphawu. Satana ndi dziko lakeli amafuna kuti tizikopeka ndi kavalidwe, njira zodzikongoletsera, chakudya, zakumwa, zosangalatsa komanso zinthu zosiyanasiyana. Makampani amatsatsa malonda pogwiritsa ntchito anthu ooneka bwino n’cholinga choti tizilakalaka kukhala ndi zinthu zambiri zosafunika kwenikweni. Choncho n’zosavuta kukopeka n’kuyamba kugwiritsa ntchito ufulu wathu m’njira yolakwika. w18.04 9-10 ¶7-8