Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • es20 98-108
  • October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
  • Timitu
  • Lachinayi, October 1
  • Lachisanu, October 2
  • Loweruka, October 3
  • Lamlungu, October 4
  • Lolemba, October 5
  • Lachiwiri, October 6
  • Lachitatu, October 7
  • Lachinayi, October 8
  • Lachisanu, October 9
  • Loweruka, October 10
  • Lamlungu, October 11
  • Lolemba, October 12
  • Lachiwiri, October 13
  • Lachitatu, October 14
  • Lachinayi, October 15
  • Lachisanu, October 16
  • Loweruka, October 17
  • Lamlungu, October 18
  • Lolemba, October 19
  • Lachiwiri, October 20
  • Lachitatu, October 21
  • Lachinayi, October 22
  • Lachisanu, October 23
  • Loweruka, October 24
  • Lamlungu, October 25
  • Lolemba, October 26
  • Lachiwiri, October 27
  • Lachitatu, October 28
  • Lachinayi, October 29
  • Lachisanu, October 30
  • Loweruka, October 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
es20 98-108

October

Lachinayi, October 1

Lirani ndi anthu amene akulira.​—Aroma 12:15.

N’zoona kuti ifeyo sitingadziwe zimene zili mumtima mwa anthu ngati Yehova ndi Yesu. Koma tikhoza kuzindikira mmene akumvera komanso zimene akufunikira. (2 Akor. 11:29) Mosiyana ndi anthu odzikonda am’dzikoli, ifeyo timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” (Afil. 2:4) Akulu mumpingo ndi amene ayenera kuyesetsa kwambiri kuti azichita zinthu moganizira ena. Iwo amadziwa kuti adzayankha mlandu pa zimene amachitira nkhosa zimene akuziyang’anira. (Aheb. 13:17) Kuti akulu athandize bwino Akhristu anzawo, amafunika kukhala omvetsa. Ndiye kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amaganizira ena? Mkulu woganizira ena amapeza nthawi yoti acheze ndi abale ndi alongo. Iye amafunsa mafunso n’kumamvetsera mwatcheru zimene munthu akulankhula. Zimenezi zimathandiza ngati m’bale kapena mlongo akufuna kufotokoza zimene zili mumtima mwake koma akusowa mawu oti anene. (Miy. 20:5) Mkulu akamapeza nthawi yocheza ndi abale ndi alongo amayamba kuwakonda komanso kugwirizana nawo.​—Mac. 20:37. w19.03 17 ¶14-17

Lachisanu, October 2

Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.—Miy. 25:11.

Kuyamikira kuli ngati chakudya chabwino chimene chimasangalatsa ukamadya ndi anzako. Munthu akatiyamikira timamva bwino ndipo ifeyo tikayamikira munthu timamuthandiza kuti nayenso amve bwino. Amazindikira kuti zimene anatichitira zinali zothandiza. Zimenezi zimachititsa kuti tizigwirizana naye kwambiri. Mawu athu oyamikira amakhala amtengo wapatali. Taona zimenezi mulemba la lero. Tangoganizani mmene maapozi agolide angakongolere ataikidwa m’mbale zasiliva. Nanga mungawagule ndalama zingati? Ndiye inuyo mungamve bwanji munthu atakupatsani? Mawu amene munganene poyamikira munthu amakhalanso amtengo wapatali. Maapozi agolide sangawonongekenso. N’chimodzimodzi ndi mawu athu oyamikira. N’kutheka kuti munthu amene tamuyamikirayo sangaiwale kwa moyo wake wonse. w19.02 15 ¶5-6

Loweruka, October 3

Munthu wakhala wodziwa zabwino ndi zoipa ngati ife.—Gen. 3:22.

Pamene Adamu ndi Hava anadya chipatso cha mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa, anasonyeza kuti sankakhulupirira Yehova komanso mfundo zake. Iwo anaona kuti angathe kumasankha okha kuti izi n’zabwino, izi n’zoipa. Koma zotsatira zake zinali zoipa kwambiri. Iwo anataya ubwenzi wawo ndi Yehova, mwayi wokhala ndi moyo wosatha ndipo anapatsira ana awo uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Zimene Adamu ndi Hava anachita n’zosiyana ndi zimene nduna ya ku Itiyopiya inachita italalikiridwa ndi Filipo. Ndunayi inayamikira kwambiri zimene Yehova ndi Yesu anaichitira ndipo sinachedwe kubatizidwa. (Mac. 8:34-38) Tikadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, ngati munthu wa ku Itiyopiyayu, timasonyezanso kuti timayamikira zimene Yehova ndi Yesu atichitira. Timasonyezanso kuti timadalira Yehova ndipo timazindikira mfundo yoti iye ndi woyenera kutiuza kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika. w19.03 2 ¶1-2

Lamlungu, October 4

Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.​—Yobu 27:5.

Atumiki a Mulungufe timasonyeza kuti tili ndi mtima wosagawanika tikamakonda Mulungu ndi mtima wonse komanso tikamaika zofuna zake pamalo oyamba posankha zochita. Mawu amene anamasuliridwa m’Baibulo kuti “mtima wosagawanika” angatanthauze chinthu chathunthu kapena chopanda vuto lililonse. Mwachitsanzo, nyama zimene zinkaperekedwa kwa Yehova zinkayenera kukhala zopanda chilema chilichonse. (Lev. 22:21, 22) Sankayenera kupereka nyama yopanda mwendo, khutu kapena diso. Komanso nyamayo inkayenera kukhala yopanda matenda. Yehova ankafuna kuti nyamayo ikhale yabwinobwino, yathunthu komanso yopanda vuto lililonse. (Mal. 1:6-9) Zimenezi ndi zomveka. Paja anthufe tikamagula chinthu, kaya chikhale chipatso, buku kapena chida chinachake, timafuna kuti chikhale ndi mbali zake zonse komanso chisakhale ndi vuto lililonse. Timafuna kuti chikhale chabwinobwino komanso chathunthu. Izi n’zimene Yehova amafunanso pa nkhani ya mtima wathu. Iye amafuna kuti tizimukonda ndi mtima wathunthu kapena kuti wosagawanika. w19.02 3 ¶3

Lolemba, October 5

Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.​—Sal. 119:97.

Kuti titeteze mtima wathu, tiyenera kuutsegula kuti mulowe zinthu zabwino. Mlonda wamumzinda wakale ankatseka geti ngati kukubwera adani koma nthawi zina ankatsegula kuti anthu alowetse chakudya ndi zinthu zina zofunika. Mageti akanati azikhala otseka nthawi zonse ndiye kuti anthu amumzindawo akanafa ndi njala. Nafenso tiyenera kutsegula mtima wathu kuti muzilowa maganizo a Yehova omwe tingawapeze m’Baibulo. Choncho tikamaliwerenga timalola maganizo akewo kusintha maganizo athu, mtima wathu komanso zochita zathu. Ndiye kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri powerenga Baibulo? Kupemphera kumatithandiza kuzindikira ‘zinthu zodabwitsa’ za m’Mawu” a Mulungu. (Sal. 119:18) Tiyeneranso kusinkhasinkha zimene tikuwerenga. Tikamapemphera, kuwerenga Mawu a Mulungu ndiponso kuwasinkhasinkha, mawuwo amafika “mkati mwa mtima” wathu ndipo timayamba kukonda maganizo a Yehova.​—Miy. 4:20-22. w19.01 18 ¶14-15

Lachiwiri, October 6

Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu.​—Aheb. 13:15.

Yehova amadziwa kuti timasiyana maluso komanso zinthu zina. Choncho amayamikira nsembe zimene aliyense amatha kupereka. Taganizirani za nsembe zochokera kwa Aisiraeli zimene iye ankalandira. Aisiraeli ena ankakwanitsa kupereka nkhosa kapena mbuzi. Koma Aisiraeli osauka sankakwanitsa kuchita zimenezi ndipo ankaloledwa kuti apereke “njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.” Ndipo ngati anali osauka kwambiri moti sangathe kupereka zimenezi ankaloledwa kupereka “ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.” (Lev. 5:7, 11) Ufawu sunali wodula koma Yehova ankayamikira nsembe imeneyi ngati unali “ufa wosalala.” Maganizo a Mulungu wathu wokoma mtima sanasinthe pa nkhaniyi. Iye sayembekezera kuti tonsefe tikamapereka ndemanga tizilankhula mwaluso ngati Apolo kapena mokopa ngati Paulo. (Mac. 18:24; 26:28) Koma amangofuna kuti tiziyesetsa kupereka ndemanga zabwino mmene tingathere. Kumbukirani chitsanzo cha mkazi wamasiye amene anapereka tindalama tiwiri tokha. Yehova anayamikira kwambiri mayiyu chifukwa anapereka zimene akanatha.​—Luka 21:1-4. w19.01 8-9 ¶3-5

Lachitatu, October 7

Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.​—Mat. 10:22.

Akhristufe timayembekezera kuti anthu azidana nafe. Paja Yesu ananeneratu kuti ophunzira ake adzazunzidwa m’masiku otsiriza. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20) Chachiwiri, ulosi wa Yesaya unasonyeza kuti adani athu sadzangodana nafe koma adzagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana polimbana nafe. Amagwiritsa ntchito zida monga chinyengo, mabodza ankunkhuniza komanso kuzunza mwankhanza. (Mat. 5:11) Yehova saletsa adani athu kugwiritsa ntchito zida zimenezi polimbana nafe. (Aef. 6:12; Chiv. 12:17) Koma sitiyenera kuchita mantha chifukwa Yehova ananena kuti “chida chilichonse” chimene anthu angagwiritse ntchito polimbana nafe “sichidzapambana.” (Yes. 54:17) Mofanana ndi mmene khoma limatitetezera ku mphepo yamkuntho, Yehova amatitetezanso pamene “anthu ankhanza akuwomba” ngati mphepo. (Yes. 25:4, 5) Adani athu sangathe kutiwonongeratu. (Yes. 65:17) Adani onse a anthu a Mulungu “sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.”​—Yes. 41:11, 12. w19.01 6-7 ¶13-16

Lachinayi, October 8

Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.​—2 Akor. 3:17.

Achinyamatanu muyenera kudziwa kuti Yehova amakonda ufulu ndipo anakupatsani mtima wofuna ufuluwo. Koma amafuna kuti muzigwiritsa ntchito ufuluwo mwanzeru kuti mukhale otetezeka. Mwina mukudziwa anthu ena amene amaonera zolaula, kuchita chiwerewere, kuchita masewera oika moyo pa ngozi, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kuledzera. N’zoona kuti kwakanthawi angaoneke kuti akusangalala. Koma zotsatira zake zimakhala zoopsa, mwina kutenga matenda, kukhala chidakwa kapena kufa kumene. (Agal. 6:7, 8) Amaona kuti ali pa ufulu koma amakhala akungodzinamiza. (Tito 3:3) Ndiye mudzifunse kuti, kodi ndi anthu angati amene anadwala chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo? Apa zikuonekeratu kuti kumvera Yehova n’kothandiza komanso kumatipatsa ufulu. (Sal. 19:7-11) Ndipotu mukamagwiritsa ntchito ufulu wanu motsatira mfundo za Mulungu, mumasonyeza Mulunguyo komanso makolo anu kuti mutapatsidwa ufulu wina mungaugwiritse ntchito bwino.​—Aroma 8:21. w18.12 22-23 ¶16-17

Lachisanu, October 9

Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.​—Gen. 2:24.

Adamu atachimwa, zinthu zinasintha. Anthu anayamba kufa ndipo zimenezi zinakhudza mabanja. Tingatsimikizire zimenezi tikaganizira zimene Paulo ananena posonyeza kuti Akhristu sayendera Chilamulo cha Mose. Iye ananena kuti imfa imathetsa banja ndipo wotsalayo akhoza kukwatira kapena kukwatiwanso. (Aroma 7:1-3) M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli munalinso malamulo okhudza banja. Chilamulochi chinkalola mwamuna kukwatira mitala koma izi zinali zitayamba kale kuchitika Chilamulocho chisanaperekedwe. Komabe panali malamulo oyenera kutsatira pa nkhani ya mitala n’cholinga choti akazi ndi ana asamachitiridwe nkhanza. Mwachitsanzo, ngati mwamuna wakwatira mkazi wachiwiri, sankayenera kusintha zimene ankachita posamalira mkazi woyambayo pa nkhani ya chakudya, zovala komanso kugonana. Mulungu ankafuna kuti mwamunayo azisamalirabe mkazi woyambayo komanso kumuteteza. (Eks. 21:9, 10) N’zoona kuti masiku ano sitiyendera Chilamulo, koma chimasonyeza kuti Yehova amaona kuti ukwati ndi wamtengo wapatali. Zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kuti tizilemekeza ukwati. w18.12 10 ¶3; 11 ¶5-6

Loweruka, October 10

Simungakhulupirire ngakhale wina atakufotokozerani.​—Hab. 1:5.

Habakuku atafotokozera Yehova nkhawa zake, ayenera kuti ankayembekezera kuti aone mmene Yehova angamuyankhire. Popeza Yehova ndi wachifundo komanso womvetsa zinthu, sanakalipire Habakuku chifukwa chomudandaulira. Iye ankadziwa kuti mneneri wakeyo wachita zimenezo chifukwa chopanikizika ndi mavuto. Choncho anamuuza mawu opita kwa Ayuda osamvera ofotokoza zimene zichitike pasanapite nthawi yaitali. N’kutheka kuti Habakuku anali woyamba kuuzidwa ndi Yehova kuti mapeto a zinthu zoipazo ali pafupi kwambiri. Yehova anasonyeza Habakuku kuti anali wokonzeka kuthetsa zoipa. Anali atangotsala pang’ono kulanga anthu oipa komanso ankhanza. Ponena kuti “m’masiku anu” Yehova ankatanthauza kuti apereka chiweruzocho Habakukuyo kapena Aisiraeli anzake a pa nthawiyo ali moyo. Zimene Yehova ananenazi si zimene Habakuku ankayembekezera. Kodi zimenezi zinayankha mafunso ake odandaula aja? Mawu amene Yehova anamuuza anasonyeza kuti Ayuda adzavutika kwambiri. w18.11 14-15 ¶7-8

Lamlungu, October 11

Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.​—1 Tim. 2:4.

Kodi mumaona bwanji anthu osiyanasiyana amene panopa sanaphunzire choonadi? Mtumwi Paulo ankalalikira Ayuda omwe ankadziwa zinthu zina zokhudza Mulungu. Koma ankathandizanso anthu amitundu ina amene ankalambira milungu yonyenga. Zimene anthu olambira milungu yonyengawo anachita zikanatha kumulepheretsa kukhala wodzichepetsa. Mwachitsanzo, pa ulendo wake woyamba waumishonale, anthu a ku Lukaoniya anaganiza kuti Paulo ndi Baranaba anali Zeu ndi Heme, yomwe inali milungu yawo yonyenga. Kodi Paulo ndi Baranaba anasangalala kulemekezedwa chonchi? Kodi anaganiza kuti zimenezi zinali zosangalatsa chifukwa chakuti anali atazunzidwa m’mizinda imene ankachokera? Kapena kodi ankaganiza kuti kutchuka kwawo kungathandize kuti anthu ambiri amvetsere uthenga wabwino? Ayi, sankaganiza choncho. M’malomwake, nthawi yomweyo anang’amba malaya awo n’kukalowa m’gulu la anthuwo ndipo anati: “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.”​—Mac. 14:8-15. w18.09 5 ¶8-9

Lolemba, October 12

Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu? . . . Ndipo ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera, . . . mwayesedwa olungama.​—1 Akor. 6:9, 11.

Kuti tiphunzire choonadi n’kumatsatira mfundo za m’Baibulo, tiyenera kulolera kusintha maganizo ndi makhalidwe athu. Paja Petulo analemba kuti: “Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. Koma . . . khalani oyera m’makhalidwe anu onse.” (1 Pet. 1:14, 15) Anthu ambiri a ku Korinto anali ndi makhalidwe oipa choncho munthu anafunika kusintha moyo wake kuti agule choonadi. Masiku anonso, anthu ambiri amene akuphunzira choonadi amasintha makhalidwe awo. Paja Petulo anakumbutsanso Akhristu a nthawi yake kuti: “Nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”​—1 Pet. 4:3. w18.11 6 ¶13

Lachiwiri, October 13

Onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.​—Mac. 13:48.

Kodi tingazindikire bwanji anthu omwe ali ‘ndi maganizo abwino amene angawathandize kudzapeza moyo wosatha’? Mofanana ndi mmene zinalili munthawi ya atumwi, tingapeze anthu ngati amenewa tikamalalikira. Choncho tiyenera kutsatira malangizo a Yesu akuti: “Mukalowa mumzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera.” (Mat. 10:11) Sitingayembekezere kuti anthu amene alibe chidwi, amene sakonda zinthu zokhudza Mulungu kapena anthu onyada angamvetsere uthenga wabwino. Koma tiyenera kufufuza anthu oona mtima, odzichepetsa komanso amene akufunitsitsa kuphunzira choonadi. Tingayerekezere kufufuza kumeneku ndi zimene Yesu ayenera kuti ankachita pa ntchito ya ukalipentala. Iye ayenera kuti ankafufuza mtengo umene unali woyenera kuti apangire mipando, zitseko, magoli kapena zinthu zina. Akapeza mtengo woyenera ankatenga zipangizo zake n’kupangira mwaluso zimene ankafunazo. Tiyenera kuchitanso zimenezi tikamayesetsa kuphunzitsa munthu woona mtima kuti akhale wophunzira wa Yesu.​—Mat. 28:19, 20. w18.10 12 ¶3-4

Lachitatu, October 14

Filipo anapita kumzinda wa Samariya ndi kuyamba kulalikira za Khristu kwa anthu akumeneko.​—Mac. 8:5.

Filipo ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yochita khama polalikira. Atangopatsidwa kumene utumiki watsopano, Akhristu anayamba kuzunzidwa ku Yerusalemu pambuyo poti Sitefano waphedwa. (Mac. 6:1-6) Koma pamene Akhristu anabalalitsidwa, Filipo sanangokhala. Iye anapita kukalalikira mumzinda wa Samariya, womwe munali anthu amene anali asanamvepo uthenga wabwino. (Mat. 10:5; Mac. 8:1) Filipo anali ndi mtima wofunitsitsa kupita kulikonse kumene mzimu wa Mulungu ungamutsogolere. Choncho Yehova anamugwiritsa ntchito kupita kumalo kumene kunali kusanalalikiridwepo. Popeza Asamariya ankanyozedwa ndi Ayuda, ayenera kuti anasangalala kuona kuti Filipo analibe tsankho. N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri ankakonda kumvetsera uthenga wake. (Mac. 8:6-8) Filipo sanasiye kulalikira mwakhama ndipo iye ndi banja lake anadalitsidwa kwambiri ndi Yehova.​—Mac. 21:8, 9. w18.10 30 ¶14-16

Lachinayi, October 15

Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.​—Aheb. 10:24.

Pa nthawi ina pamene Yesu anali m’zigawo za Dekapole, anthu “anam’bweretsera munthu wogontha komanso wovutika kulankhula.” (Maliko 7:31-35) M’malo momuchiritsira pa gulu, Yesu ‘anapita naye pambali.’ Anachita zimenezi chifukwa chakuti mwina vuto la munthuyu linkachititsa kuti asamamasuke pa gulu. Ndiye mwina Yesu atazindikira zimenezi anaona kuti ndi bwino kumuchiritsira pambali. N’zoona kuti ifeyo sitingachiritse munthu. Koma tikhoza kuchita zinthu moganizira mavuto amene anthu akukumana nawo komanso mmene akumvera. Yesu anazindikira mmene munthu uja ankamvera ndipo anachita zinthu momuganizira. Tizichitanso zinthu moganizira achikulire komanso odwala. Akhristu amadziwika kuti amachita zinthu mwadongosolo komanso mwachikondi. (Yoh. 13:34, 35) Chikondi chimenechi chimatilimbikitsa kuti tiziyesetsa mmene tingathere kuti tithandize achikulire kapena olumala kuti azipezeka pamisonkhano komanso azilalikira. Timachita zimenezi ngakhale kuti zimene iwo angakwanitse n’zochepa.​—Mat. 13:23. w18.09 29-30 ¶7-8

Lachisanu, October 16

Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa.​—Aroma 15:2.

Mtumiki wa Yehova aliyense ndi wofunika kwambiri kwa iye komanso kwa Yesu amene anapereka moyo wake monga dipo. (Agal. 2:20) Tonse timakonda abale ndi alongo athu ndipo timafuna kuwathandiza mwachikondi komanso mwachifundo. Koma kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuyesetsa kutsatira “zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.” (Aroma 14:19) Tonsefe tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene tizidzakhala popanda chokhumudwitsa m’Paradaiso. Sipadzakhalanso zinthu zokhumudwitsa monga matenda, nkhondo, kuzunzidwa, mavuto a m’banja komanso imfa. Pamene zaka 1,000 zizidzatha, anthu onse adzakhala ali angwiro. Anthu amene adzapambane mayesero omaliza ndi amene Yehova Mulungu adzawalola kukhala ana ake padziko lapansi ndipo adzapeza “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Tiyeni tonse tiziyesetsa kulimbikitsana mwachikondi komanso kuthandizana kuti tidzalandire madalitso amenewa. w18.09 14 ¶10; 16 ¶18

Loweruka, October 17

Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.​—Sal. 119:97.

Kuphunzira Mawu a Mulungu kumatanthauza zambiri osati kungowerenga nkhani kapena kungopeza mayankho a mafunso. Tikamaphunzira tiyenera kudzifunsa kuti, Kodi nkhaniyi ikundiuza chiyani za makhalidwe a Yehova, njira zake komanso maganizo ake? Tizidzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani Mulungu amatilamula kuti tizichita zakutizakuti n’kumatiletsa kuchita zakutizakuti? Ndi bwinonso kuganizira zimene tiyenera kusintha pa moyo wathu komanso kaganizidwe kathu. N’zoona kuti sitingachite zonsezi pa nkhani iliyonse imene tikuphunzira. Koma tiyenera kupatula nthawi, mwina hafu ya nthawi yonse imene tikufuna kuphunzirayo, kuti tiganizire mwakuya zimene tawerengazo. (1 Tim. 4:15) Tikamasinkhasinkha Mawu a Mulungu timayamba kupeza umboni wotsimikizira kuti maganizo a Yehova pa nkhani iliyonse amakhala olondola. Timayamba kuona zinthu mmene Yehova amazionera n’kumagwirizana ndi maganizo ake. (Aroma 12:2) Ndiyeno kaganizidwe kathu kamasintha moti timayamba kukhala ndi maganizo a Yehova. w18.11 24 ¶5-6

Lamlungu, October 18

Ndife antchito anzake a Mulungu.​—1 Akor. 3:9.

Paulo ananena kuti iye ndi anzake anali “antchito anzake a Mulungu” chifukwa chakuti ankagwira ntchito yodzala komanso kuthirira mbewu za Ufumu. (1 Akor. 3:6) Ifenso tingakhale “antchito anzake a Mulungu” tikamagwiritsa ntchito nthawi yathu, zinthu zathu komanso mphamvu zathu pa ntchito yolalikira imene Mulungu watipatsa. Kunena zoona umenewu ndi mwayi waukulu kwambiri. Timasangalala tikamagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu polalikira ndi kuphunzitsa anthu. Abale ndi alongo amene akhala akuphunzitsa anthu n’kumawaona akusintha akhoza kukuuzani zinthu zosangalatsa zimene zimachitika pogwira ntchitoyi. Zimakhala zosangalatsa kuona anthu akumvetsa mfundo za m’Baibulo, kuzikhulupirira, kusintha moyo wawo komanso kuyamba kuuza ena zimene amaphunzira. Yesu anasangalala kwambiri ataona kuti anthu 70 amene anawatumiza kukalalikira abwera “ali osangalala” chifukwa choti ntchito yawo inayenda bwino.​—Luka 10:17-21. w18.08 20 ¶11-12

Lolemba, October 19

Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa.​—Miy. 28:26.

Kudalira kwambiri luso lathu lomvetsa zinthu kungakhale msampha. Tingayambe kuganiza kuti tikangoona pang’ono zinthu zina tingadziwiretu nkhani yonse. Ngati sitigwirizana ndi Mkhristu mnzathu, tikhozanso kulephera kuona zinthu moyenera. Tikamangoganizira zinthu zokhudza Mkhristuyo zimene sizitisangalatsa, tingayambe kumukayikira. Ndiye tikangomva nkhani yoipa yokhudza iyeyo tikhoza kuikhulupirira nthawi yomweyo. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kusagwirizana ndi abale athu kungachititse kuti tiziwaganizira zoipa tilibe umboni wokwanira. (1 Tim. 6:4, 5) Kuti tipewe zimenezi, tiyenera kuyesetsa kuti tisakhale ndi nsanje kapena kaduka mumtima mwathu. M’malomwake tiziyesetsa kukonda abale athu komanso kuwakhululukira ndi mtima wonse.​—Akol. 3:12-14. w18.08 6 ¶15; 7 ¶18

Lachiwiri, October 20

Kumwamba ndi kwa Yehova . . . dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi zake zonsezo.—Deut. 10:14.

Munthu aliyense ndi wa Yehova chifukwa iye ndi amene anatilenga. (Sal. 100:3; Chiv. 4:11) Koma kuyambira kale, Mulungu wakhala akusankha magulu osiyanasiyana a anthu kuti akhale anthu ake apadera. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 135 limanena kuti Aisiraeli amene ankatumikira Yehova mokhulupirika anali “chuma chake chapadera.” (Sal. 135:4) Buku la Hoseya linaloseranso kuti anthu ena omwe si Aisiraeli adzakhala anthu a Yehova. (Hos. 2:23) Ulosi wa Hoseya unakwaniritsidwa pamene Yehova analola kuti anthu omwe sanali Ayuda akhale m’gulu la anthu amene akalamulire ndi Khristu. (Mac. 10:45; Aroma 9:23-26) Gululi limatchedwa “mtundu woyera” komanso “chuma chapadera” cha Yehova chifukwa choti amadzozedwa ndi mzimu woyera komanso amasankhidwa kukakhala ndi moyo kumwamba. (1 Pet. 2:9, 10) Nanga bwanji za Akhristu ambirimbiri okhulupirika amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli? Yehova amanenanso kuti amenewa ndi ‘anthu ake osankhidwa mwapadera.’​—Yes. 65:22. w18.07 22 ¶1-2

Lachitatu, October 21

Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo. . . . Anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo.​—Afil. 2:5, 7.

Akhristu enieni amatsanzira Khristu yemwe anatipatsa chitsanzo chabwino pa nkhani yopatsa. (Mat. 20:28) Tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizitsanzira kwambiri Yesu?’ (1 Pet. 2:21) Yehova amasangalala nafe tikamatsatira chitsanzo chake komanso cha Khristu pokhala ndi mtima woganizira anthu ena ndiponso wofunitsitsa kuwathandiza. Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la Msamariya wachifundo posonyeza kuti otsatira ake ayenera kudzipereka pothandiza anthu ena, ngakhale amene amasiyana nawo mtundu. (Luka 10:29-37) Kodi mukukumbukira funso limene linachititsa Yesu kuti afotokoze fanizoli? Myuda wina anamufunsa kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?” Yankho la Yesu limasonyeza kuti tiyenera kukhala ofunitsitsa kuthandiza anthu ngati mmene anachitira Msamariyayo kuti Mulungu azisangalala nafe. w18.08 19 ¶5-6

Lachinayi, October 22

Mngelo . . . anati: “Mtendere ukhale nawe, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova ali nawe.”​—Luka 1:28.

Kodi Yehova anamuyamikira Mariya chifukwa cha kulera komanso kusamalira mokhulupirika Yesu ali mwana? Inde. Mulungu anachititsa kuti zimene Mariya anachita komanso kulankhula zilembedwe m’Baibulo. Zikuoneka kuti Mariya analibe mwayi woyenda ndi Yesu pa zaka zitatu ndi hafu zimene anachita utumiki wake padzikoli. Mwina anafunika kukhalabe ku Nazareti pambuyo poti mwamuna wake wamwalira. Koma ngakhale kuti analibe mwayi woona zinthu zambiri zimene Yesu anachita, iye analipo pamene Yesu ankaphedwa. (Yoh. 19:26) Pamene tsiku la Pentekosite linkayandikira, Mariya anali limodzi ndi ophunzira a Yesu ku Yerusalemu. (Mac. 1:13, 14) Zikuonekanso kuti iye anali m’gulu la anthu amene anadzozedwa ndi mzimu woyera. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti anali ndi mwayi wokakhala ndi Yesu kumwamba kwamuyaya. Apatu Yehova anasonyeza kuti ankayamikira kwambiri zimene Mariya anachita. w18.07 9 ¶11; 10 ¶14

Lachisanu, October 23

Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.​—1 Akor. 10:31.

Pa utumiki wake wonse, Yesu ankaphunzitsa mfundo zimene zikanathandiza ophunzira ake kuti adziwe mavuto amene angakumane nawo ngati ali ndi maganizo enaake kapena ngati atachita zinazake. Mwachitsanzo, anawaphunzitsa kuti mkwiyo ungayambitse chiwawa ndipo kusirira kungapangitse munthu kuchita chigololo. (Mat. 5:21, 22, 27, 28) Kuti tikhale ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino, tiyenera kulola kuti mfundo za Mulungu zizititsogolera ndipo tikamatero timalemekeza Mulunguyo. Koma pali nkhani zina zimene Akhristu awiri achikumbumtima chophunzitsidwa bwino akhoza kusankha zochita mosiyana. Nkhani ya mowa ndi imodzi mwa nkhani zimenezi. Baibulo sililetsa kumwa mowa mosapitirira malire. Koma limaletsa kumwa kwambiri kapena kuledzera. (Miy. 20:1; 1 Tim. 3:8) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ngati Mkhristu amamwa mosapitirira malire, ndiye kuti palibenso mfundo zina zoyenera kuziganizira pa nkhaniyi? Ayi. Mkhristu ayenera kuganiziranso chikumbumtima cha anthu ena ngakhale pa nkhani zimene chikumbumtima chake sichikumutsutsa. w18.06 18 ¶10-11

Loweruka, October 24

Chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.—Maliko 8:15.

Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti azipewa chofufumitsa kapena kuti mfundo zimene Afarisi, Asaduki ndiponso achipani cha Herode ankaphunzitsa. (Mat. 16:6, 12) Chochititsa chidwi n’chakuti Yesu anapereka chenjezoli patangopita nthawi yochepa kuchokera pamene anthu ankafuna kuti iye akhale mfumu yawo. Nthawi zambiri anthu akamasakaniza ndale ndi chipembedzo, ziwawa sizichedwa kuyambika. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti ayenera kupewa zimenezi. Chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kuti ansembe aakulu komanso Afarisi akonze zoti aphe Yesu chinali chakuti ankaona kuti iye akhoza kuchititsa kuti achotsedwe pa udindo wawo wachipembedzo komanso wandale. Paja iwo anati: “Ngati timulekerera, onse adzakhulupirira mwa iye, ndipo Aroma adzabwera kudzatenga malo athu ndi mtundu wathu.” (Yoh. 11:48) Choncho Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe, anatsogolera pokonza chiwembu choti Yesu aphedwe.​—Yoh. 11:49-53; 18:14. w18.06 6-7 ¶12-13

Lamlungu, October 25

Chikondi chanu chisakhale cha chiphamaso.​—Aroma 12:9.

Njira imodzi imene Satana amapusitsira anthu ndi kugwiritsa ntchito nkhani zokhudza kukhulupirira mizimu. Amagwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga komanso zinthu zosangalatsa pofuna kuti anthu azichita chidwi ndi ziwanda. Zinthu monga mafilimu ndi masewera apakompyuta zimachititsa kuti anthu azisangalala ndi zamatsenga. Kodi tingapewe bwanji msampha umenewu? Sitingayembekezere kuti gulu la Yehova lizitipatsa mndandanda wa zosangalatsa zoyenera ndi zosayenera. Aliyense ayenera kuphunzitsa chikumbumtima chake kuti azisankha zinthu mogwirizana ndi mfundo za Mulungu. (Aheb. 5:14) Tikhoza kusankha zinthu mwanzeru tikamatsatira malangizo a mtumwi Paulo amene ali pamwambawa. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda zingandichititse kukhala munthu wachinyengo? Ngati anthu amene ndimawalalikira ataona zinthu zimene ndimasangalala nazo, kodi angaganize kuti ndimatsatira zimene ndimaphunzitsa?’ Zochita zathu zikamagwirizana ndi zolankhula zathu tikhoza kupewa misampha ya Satana.​—1 Yoh. 3:18. w18.05 25 ¶13

Lolemba, October 26

Chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzero langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe.​—Aroma 10:1.

Kodi tingatsanzire bwanji Paulo? Choyamba, tiyenera kukhalabe ndi mtima wofuna kupeza anthu amene ali ndi “maganizo abwino.” Chachiwiri, tiyenera kuchonderera Yehova m’pemphero kuti atsegule mitima ya anthu oterewa. (Mac. 13:48; 16:14) Silvana, yemwe wachita upainiya kwa zaka pafupifupi 30, ananena kuti, “Ndisanapite kunyumba iliyonse mu utumiki, ndimapempha Yehova kuti andithandize kuona anthuwo moyenera.” Tiyeneranso kupempha Mulungu kuti angelo azititsogolera kwa anthu ofuna kumva uthenga wabwino. (Mat. 10:11-13; Chiv. 14:6) M’bale wina dzina lake Robert, yemwe wachita upainiya kwa zaka zoposa 30, anati, “Kugwira ntchito limodzi ndi angelo omwe amadziwa zimene zikuchitikira anthu n’kosangalatsa kwambiri.” Chachitatu, tiyenera kuyesetsa kuona zabwino mwa anthu amene timawalalikira. M’bale wina dzina lake Carl, yemwe ndi mkulu, ananena kuti: “Ndimayesetsa kuona zabwino mwa munthu aliyense ngakhale zitakhala zochepa. Ndimaona ngati munthuyo akumwetulira, ngati akuoneka wokoma mtima kapena ngati wafunsa funso labwino.” Mofanana ndi Paulo, nafenso tikhoza kupirira n’kumabereka zipatso. w18.05 15 ¶13; 16 ¶15

Lachiwiri, October 27

Tiyeni tiganizirane . . . tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.—Aheb. 10:24, 25.

Anthufe timalimbikitsidwa tikamva kuti anthu amene tinawathandiza m’mbuyomu akupitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika. Umu ndi mmene anamveranso mtumwi Yohane pamene analemba kuti: “Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.” (3 Yoh. 4) Apainiya ambiri akhoza kuvomereza kuti amasangalala akamva kuti anthu amene anawaphunzitsa choonadi adakali okhulupirika ndipo mwinanso ayamba upainiya. Choncho kukumbutsa mpainiya amene wakhumudwa zinthu zosangalatsa zimene anachita m’mbuyomo, kungamulimbikitse kwambiri. Oyang’anira madera ndi akazi awo amayamikiranso akalandira kakalata kowayamikira pambuyo pochezera mpingo. Ndi mmenenso amamvera akulu, amishonale, apainiya komanso atumiki a pa Beteli akalandira uthenga woyamikira zimene akuchita potumikira Mulungu. w18.04 23 ¶14-15

Lachitatu, October 28

[Mfumu isachulukitsenso] akazi kuti mtima wake ungapatuke.—Deut. 17:17.

Solomo sanamvere lamuloli moti anakwatira akazi 700 komanso anali ndi akazi ena apambali okwana 300. (1 Maf. 11:3) Ambiri mwa akaziwa sanali Aisiraeli ndipo ankalambira milungu yonyenga. Choncho Solomo sanamverenso lamulo la Mulungu loletsa kukwatira akazi amitundu ina. (Deut. 7:3, 4) Solomo ankapatuka pang’onopang’ono panjira ya Yehova ndipo izi zinamuchititsa kuti achite machimo akuluakulu. Iye anamanga guwa la mulungu wonyenga dzina lake Asitoreti komanso la mulungu wina dzina lake Kemosi. Ndipo ankapita kumeneko ndi akazi ake n’kumakalambira milungu yonyengayo. Ndiye tangoganizani, malo amene anamanga maguwa amenewa anali paphiri loyang’anizana ndi Yerusalemu kumene anamanga kachisi wa Yehova. (1 Maf. 11:5-8; 2 Maf. 23:13) N’kutheka kuti Solomo ankadzinamiza kuti Yehova sangakhumudwe ndi kusamvera kwakeko chifukwa ankaperekanso nsembe kukachisi. Koma Yehova salekerera machimo. w18.07 18-19 ¶7-9

Lachinayi, October 29

Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro, chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.—Aef. 6:16.

‘Mivi ina yoyaka moto’ imene Satana amagwiritsa ntchito imakhala mabodza okhudza Yehova. Mwachitsanzo, angakuchititseni kukhulupirira kuti Yehova sakuganizirani ndipo sangakukondeni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Ida, yemwe nthawi zambiri amadziona kuti ndi wachabechabe. Iye anati: “Nthawi zambiri ndimaona kuti sindili pa ubwenzi ndi Yehova ndipo Yehovayo sakufuna kukhala Mnzanga.” Ndiye kodi amalimbana bwanji ndi maganizo amenewa? Ida anati: “Misonkhano ndi imene imandithandiza kwambiri. Poyamba ndinkangopita kumisonkhano koma sindinkayankha poganiza kuti palibe angafune kumva zimene ndinganene. Koma panopa ndimakonzekera bwino ndipo ndimayesetsa kuyankha kawiri kapena katatu.” Nkhani ya Ida ikutithandiza kuzindikira mfundo yofunika kwambiri. Chishango cha msilikali chinkakhala cha saizi imodzi koma chikhulupiriro cha munthu chikhoza kukula kapena kuchepa malinga ndi zimene munthuyo amasankha kuchita. (Mat. 14:31; 2 Ates. 1:3) Choncho aliyense ayenera kuyesetsa kukulitsa chikhulupiriro chake. w18.05 29-30 ¶12-14

Lachisanu, October 30

Ndichite chiyani kuti ndipulumuke?​—Mac. 16:30.

Pambuyo poti chivomezi chachitika, m’pamene woyang’anira ndende anasintha maganizo n’kupempha kuti amuthandize. (Mac. 16:25-34) Masiku anonso, anthu ena amene samvetsera uthenga wa m’Baibulo amasintha pambuyo pokumana ndi mavuto aakulu ndipo amafuna kuthandizidwa. Mwachitsanzo, anthu ena akhoza kuchotsedwa ntchito mwadzidzidzi ndipo amasowa mtengo wogwira. Pomwe ena akuvutika kwambiri chifukwa chopezeka ndi matenda aakulu kapena chifukwa mnzawo wamwalira. Anthu ngati amenewa akhoza kufunsa mafunso okhudza cholinga cha moyo omwe m’mbuyomo sankawaganizira. Mwina akhoza kumafunsa kuti, ‘Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?’ Tikakumana nawo, mwina angayambe kumvetsera uthenga wathu wolimbikitsa. Choncho chifukwa chopitiriza kulalikira, timatha kulimbikitsa anthu pa nthawi imene akufuna thandizo.​—Yes. 61:1. w18.05 19-20 ¶10-12

Loweruka, October 31

Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino.​—Luka 4:18.

Masiku ano, anthu ambiri achititsidwa khungu ndi mulungu wa nthawi ino ndipo ali mu ukapolo pa nkhani ya chipembedzo, zachuma komanso moyo wa tsiku ndi tsiku. (2 Akor. 4:4) Koma ifeyo tili ndi mwayi wotsanzira Yesu pothandiza anthu kuti adziwe Mulungu n’kuyamba kumulambira mwaufulu. (Mat. 28:19, 20) Ntchito imeneyi si yophweka ndipo pali mavuto ambiri amene tingakumane nawo. M’mayiko ena anthu amadana ndi ntchitoyi ndipo amatilusira. Koma funso limene aliyense ayenera kudzifunsa ndi lakuti: ‘Kodi n’zotheka kuti ineyo ndigwiritse ntchito ufulu umene ndili nawo panopa kuti ndizichita zambiri popititsa patsogolo ntchito za Ufumu?’ N’zolimbikitsa kuona kuti anthu ambiri masiku ano azindikira zoti nthawi yotsalayi yafupika ndipo ayamba moyo wosalira zambiri n’cholinga choti azilalikira kwambiri. (1 Akor. 9:19, 23) Ena amalalikira m’gawo lawo, pomwe ena amasamukira kumene kukufunika anthu ambiri olalikira. Uwutu ndi umboni wakuti anthu akugwiritsa ntchito ufulu wawo kuti azitumikira Yehova.​—Sal. 110:3. w18.04 11-12 ¶13-14

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani