Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • es20 118-128
  • December

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
  • Timitu
  • Lachiwiri, December 1
  • Lachitatu, December 2
  • Lachinayi, December 3
  • Lachisanu, December 4
  • Loweruka, December 5
  • Lamlungu, December 6
  • Lolemba, December 7
  • Lachiwiri, December 8
  • Lachitatu, December 9
  • Lachinayi, December 10
  • Lachisanu, December 11
  • Loweruka, December 12
  • Lamlungu, December 13
  • Lolemba, December 14
  • Lachiwiri, December 15
  • Lachitatu, December 16
  • Lachinayi, December 17
  • Lachisanu, December 18
  • Loweruka, December 19
  • Lamlungu, December 20
  • Lolemba, December 21
  • Lachiwiri, December 22
  • Lachitatu, December 23
  • Lachinayi, December 24
  • Lachisanu, December 25
  • Loweruka, December 26
  • Lamlungu, December 27
  • Lolemba, December 28
  • Lachiwiri, December 29
  • Lachitatu, December 30
  • Lachinayi, December 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
es20 118-128

December

Lachiwiri, December 1

Anawamvera chifundo.—Maliko 6:34.

N’zosangalatsa kuti Yesu amamvetsa mavuto amene anthu amakumana nawo. Yesu ali padzikoli, ‘ankasangalala ndi anthu amene akusangalala komanso kulira ndi anthu amene akulira.’ (Aroma 12:15) Mwachitsanzo, ophunzira ake 70 atabwera mosangalala chifukwa chakuti zinthu zawayendera bwino kokalalikira, Yesu “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera.” (Luka 10:17-21) Koma ataona anthu ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya Lazaro, Yesu “anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.” (Yoh. 11:33) Yesu anali wangwiro koma pochita zinthu ndi anthu ochimwa ankakhala wokoma mtima komanso wachifundo. Kodi n’chiyani chinkamuthandiza kuchita zimenezi? Choyamba, Yesu ankakonda anthu. (Miy. 8:31) Kukonda anthu n’kumene kunamuthandiza kuti azimvetsa maganizo awo. Paja mtumwi Yohane anati Yesu “anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.”​—Yoh. 2:25. w19.03 20 ¶1-2

Lachitatu, December 2

[Khudzani] zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!—Yobu 1:11.

Satana anawononga chuma cha Yobu, kuipitsa mbiri yake komanso kupha atumiki ake ndi ana ake onse 10. Kenako anamudwalitsa pochititsa kuti atuluke zilonda thupi lonse. Mkazi wa Yobu anasokonezeka maganizo moti anamuuza kuti atukwane Mulungu kuti afe. Nayenso Yobu ankalakalaka atangofa koma anakhalabe wokhulupirika. Kenako Satana anapeza njira ina yomuyesera pogwiritsa ntchito anzake atatu. Anthuwa anabwera kudzaona Yobu ndipo anakhala naye masiku angapo koma sanamulimbikitse. M’malomwake, ankangolankhula mopanda chifundo ndiponso kumudzudzula. Iwo ananena kuti Mulungu ndi amene ankamubweretsera mavutowo ndipo kukhulupirika kwake analibe nako ntchito. Iwo anafika posonyeza kuti Yobu ndi munthu woipa moti m’pomveka kuti akukumana ndi mavuto.​—Yobu 1:13-22; 2:7-11; 15:4, 5; 22:3-6; 25:4-6. w19.02 4 ¶7-8

Lachinayi, December 3

Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.​—Sal. 111:10.

Mantha ena ndi abwino. Mwachitsanzo, ndi bwino kuopa kukhumudwitsa Yehova. Adamu ndi Hava akanakhala ndi mantha amenewa si bwenzi atachimwa. Iwo atachita zimene Mulungu anawaletsa, maso awo anatseguka, kutanthauza kuti anazindikira kuti ndi ochimwa. Kuyambira pamenepo, chimene akanapatsira ana awo ndi uchimo ndi imfa basi. Chifukwa chozindikira vuto lawoli, anayamba kuchita manyazi kuti sanavale ndipo anasoka masamba n’kuvala. (Gen. 3:7, 21) Taona kuti tiyenera kuopa Yehova moyenera koma sitiyenera kuopa kwambiri imfa. Yehova wakonza kale njira yotithandiza kuti tidzapeze moyo wosatha. Ngati tachimwa n’kulapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova amaiwala nkhaniyo. Iye amatikhululukira chifukwa choti timakhulupirira nsembe ya Mwana wake. Njira yaikulu imene timasonyezera kuti tili ndi chikhulupiriro ndi kudzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa.​—1 Pet. 3:21. w19.03 5-6 ¶12-13

Lachisanu, December 4

Sipanatsale ndi mmodzi yemwe kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.—Num. 26:65.

Aisiraeli nawonso anali ndi zifukwa zambiri zowachititsa kuyamikira Yehova. Paja Yehova anawapulumutsa ku ukapolo pobweretsa miliri 10 ku Iguputo. Kenako anawapulumutsanso powononga asilikali onse a ku Iguputo pa Nyanja Yofiira. Aisiraeliwo anayamikira kwambiri ndipo anaimba nyimbo yotamanda Yehova. Koma kodi mtima woyamikirawu unapitirira? Aisiraeli atangokumana ndi mavuto ena anaiwaliratu zinthu zabwino zimene Yehova anawachitira. Kenako anachita zinthu zosonyeza kuti analibe mtima woyamikira. (Sal. 106:7) Baibulo limanena kuti “khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udzira Mose ndi Aroni” koma zoona zake n’zakuti ankang’ung’udzira Yehova. (Eks. 16:2, 8) Yehova anakhumudwa kwambiri ndi mtima wosayamika umene Aisiraeli anasonyeza. Kenako ananena kuti m’badwo wonse wa Aisiraeliwo udzathera m’chipululu, kupatulapo Yoswa ndi Kalebe.​—Num. 14:22-24. w19.02 17 ¶12-13

Loweruka, December 5

Ndine wofatsa ndi wodzichepetsa.​—Mat. 11:29.

Yesu sankafuna kudzionetsera polamula anthu kuti azichita zambiri pokumbukira imfa yake. M’malomwake, anauza ophunzira ake kuti azichita mwambo wosavuta pokumbukira imfa yake kamodzi pa chaka. (Yoh. 13:15; 1 Akor. 11:23-25) Mwambowu ndi wosavuta koma woyenerera ndipo umasonyeza kuti Yesu si wodzikuza. Timasangalala kwambiri kuti Mfumu yathu yakumwamba ili ndi makhalidwe abwino monga kudzichepetsa. (Afil. 2:5-8) Kodi tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Yesu? Tingachite zimenezi tikamaika zofuna za ena patsogolo osati zathu. (Afil. 2:3, 4) Taganiziraninso zimene zinachitika usiku woti Yesu aphedwa mawa lake. Iye ankadziwa kuti afa imfa yopweteka koma ankadera nkhawa atumwi ake chifukwa chodziwa kuti adzakhala ndi chisoni kwambiri. Choncho usikuwo anawaphunzitsa komanso kuwalimbikitsa. (Yoh. 14:25-31) Iye ankaganizira zofuna za anthu ena osati zofuna zake. Apatu anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. w19.01 21 ¶5-6

Lamlungu, December 6

Inu Yehova, chonde kondwerani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga.​—Sal. 119:108.

Kodi inuyo mumachita mantha mukangoganiza zokweza dzanja lanu kuti muyankhe? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Ambirife timakhala ndi mantha tikafuna kuyankha. Kunena zoona, kuopa kungasonyeze kuti ndinu wodzichepetsa komanso mumaona kuti anthu ena ndi okuposani. Yehova amakonda anthu odzichepetsa chonchi. (Sal. 138:6; Afil. 2:3) Koma iye amafunabe kuti muzimutamanda ndiponso kulimbikitsa abale ndi alongo anu kumisonkhano. (1 Ates. 5:11) Iye amakukondani ndipo angakuthandizeni kuti muzilimba mtima n’kumayankha. Pali mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize. Baibulo limanena kuti tonsefe timalakwitsa nthawi zina polankhula. (Yak. 3:2) Yehova komanso abale ndi alongo athu sayembekezera kuti tizichita zabwino zokhazokha popanda kulakwitsa chilichonse. (Sal. 103:12-14) Abale ndi alongowa ali ngati achibale athu ndipo amatikonda kwambiri. (Maliko 10:29, 30; Yoh. 13:35) Amadziwanso kuti nthawi zina sitingafotokoze mfundo mmene timafunira. w19.01 8 ¶3; 10-11 ¶10-11

Lolemba, December 7

Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.—Mlal. 12:1.

N’zoona kuti kuchita zimenezi masiku ano si kophweka koma n’zotheka. Yehova amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino komanso muzisangalala. Iye angakuthandizeni kuti muzisangalala panopa komanso kwa moyo wanu wonse. Kuti timvetse nkhaniyi, tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira pa zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankagonjetsa adani awo m’Dziko Lolonjezedwa. Aisiraeli atayandikira Dziko Lolonjezedwa, Yehova sanawauze kuti ayambe kukonzekera nkhondo. (Deut. 28:1, 2) M’malomwake, anangowauza kuti azitsatira malamulo ake komanso kumukhulupirira. (Yos. 1:7-9) Munthu akhoza kuona kuti malangizowa anali osathandiza. Koma zoona zake n’zakuti anali othandiza kwambiri chifukwa Yehova anathandiza anthu ake kuti azigonjetsa asilikali a ku Kanani. (Yos. 24:11-13) Munthu amafunika kukhala ndi chikhulupiriro kuti amvere Yehova ndipo nthawi zonse chikhulupirirocho chimamuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino. Mfundoyi sinasinthe ndipo ndi yoona mpaka pano. w18.12 25 ¶3-4

Lachiwiri, December 8

Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.​—Yoh. 6:68.

Anthu ena anakhumudwa chifukwa chakuti kafotokozedwe ka malemba ena a m’Baibulo kanasinthidwa. Apo ayi, anasiya choonadi chifukwa chogwirizana ndi ampatuko kapena anthu otsutsa omwe amapotoza mfundo zachoonadi. Zimenezi zapangitsa kuti ena ayambe ‘kuchoka’ mwadala kwa Yehova komanso mumpingo. (Aheb. 3:12-14) Anthu otere zinthu zikanawayendera bwino kwambiri akanasungabe chikhulupiriro chawo komanso kukhulupirira Yesu ngati mmene mtumwi Petulo anachitira. Ena anasiya choonadi pang’onopang’ono mwinanso asakuzindikira. Munthu amene amasiya choonadi pang’onopang’ono amafanana ndi bwato limene likutengeka pang’onopang’ono kupita pakatikati pa mtsinje. Baibulo limati anthu otere ‘amatengeka pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro. (Aheb. 2:1) Mosiyana ndi munthu amene amachoka m’choonadi mwadala, munthu amene amatengeka pang’onopang’ono amachita zimenezi mosazindikira. Koma munthu akayamba kuchita zimenezi ubwenzi wake ndi Yehova umayamba kusokonekera ndipo akapanda kusamala ukhoza kutheratu. w18.11 9 ¶5-6

Lachitatu, December 9

Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa.​—Sal. 110:3.

Kodi mungafune kuphunzira zinthu zina zimene zingakuthandizeni kutumikira bwino Yehova? Ngati zili choncho, mwina mukhoza kupita ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Sukuluyi imathandiza abale ndi alongo amene akuchita utumiki wa nthawi zonse kuti awonjezere utumiki wawo. Anthu amene amapita ku sukuluyi ayenera kukhala okonzeka kutumizidwa kulikonse akamaliza maphunzirowo. Kodi mungakonde kupita kusukulu imeneyi kuti muwonjezere utumiki wanu? (1 Akor. 9:23) Atumiki a Yehovafe timayesetsa tsiku lililonse kukhala opatsa. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti ndife abwino, okoma mtima komanso achikondi. Ndiye tikamasonyeza makhalidwe amenewa timakhala mosangalala komanso mwamtendere. (Agal. 5:22, 23) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, mukhoza kukhalabe osangalala mukamatsanzira mtima wopatsa wa Yehova komanso mukamagwira ntchito limodzi naye.​—Miy. 3:9, 10. w18.08 27 ¶16-18

Lachinayi, December 10

Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.​—Mat. 19:6.

Mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi pangakhale chifukwa choti Mkhristu athetsere banja n’kukwatira kapena kukwatiwanso?’ Yesu anafotokoza maganizo ake pa nkhaniyi. Iye anati: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo molakwira mkaziyo. Ndipo ngati mkazi wasiya mwamuna wake, ndiyeno n’kukwatiwa ndi wina, wachita chigololo.” (Maliko 10:11, 12; Luka 16:18) Apa zikuonekeratu kuti Yesu amalemekeza ukwati ndipo amafuna kuti ifenso tizichita zimenezi. Mwamuna akasiya mkazi wake wokhulupirika (kapena mkazi akasiya mwamuna wake wokhulupirika) pa zifukwa zina n’kukwatira wina ndiye kuti akuchita chigololo. Kwa Mulungu, anthu awiriwo amakhala adakali “thupi limodzi.” Yesu ananenanso kuti munthu akasiya mkazi wake wosalakwa amamuchititsa chigololo. Zili choncho chifukwa pa nthawiyo mkazi amene banja lake latha mwina ankakakamizika kuti akwatiwenso n’cholinga choti azisamaliridwa. Koma akakwatiwanso ankakhala kuti wachita chigololo. w18.12 11 ¶8-9

Lachisanu, December 11

Ine ndidzaimabe pamalo a mlonda.​—Hab. 2:1.

Zimene Habakuku anakambirana ndi Yehova zinamuthandiza kuti mtima wake ukhale m’malo. Choncho anaona kuti azingoyembekezera popanda kukayikira kuti Yehova adzathandizapo. Sikuti maganizowa anangokhala nawo kwa kanthawi kochepa. Paja iye nthawi ina ananenanso kuti: “Ndidzayembekezera mofatsa tsiku la nsautso.” (Hab. 3:16) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Habakuku anachita? Choyamba, kaya mavuto atipanikize chotani, sitiyenera kusiya kupemphera kwa Yehova. Chachiwiri, tiyenera kumamvetsera zimene Yehova amatiuza kudzera m’Mawu ake komanso gulu lake. Chachitatu, tiyenera kuyembekeza Yehova moleza mtima ndipo tisamakayikire kuti adzathetsa mavuto athu pa nthawi yake. Tikamatsanzira Habakuku pa nkhani yolankhula ndi Yehova kuchokera mumtima, kumvetsera mawu ake komanso kumuyembekezera moleza mtima, maganizo athu adzakhala m’malo ndipo tidzatha kupirira mavuto athu. Chiyembekezo chathu chidzatithandiza kukhala oleza mtima ndipo izi zingachititse kuti tizikhalabe osangalala ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Chiyembekezo chathu chimatithandiza kuti tisamakayikire zoti Atate wathu wakumwamba adzathetsa mavuto athu.​—Aroma 12:12. w18.11 15-16 ¶11-12

Loweruka, December 12

Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru.​—1 Tim. 2:9.

Kodi maganizo a Yehova pa nkhani yokhumudwitsa anthu ena ndi otani? Yesu anati: “Aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana tokhulupirirati, zingakhale bwino kwambiri kuti amumangirire chimwala champhero m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kumuponya m’nyanja.” (Maliko 9:42) Mawu amenewatu ndi amphamvu. Popeza Yesu anatengera Yehova ndendende, n’zosachita kufunsa kuti Yehova amanyansidwa ndi anthu amene amakhumudwitsa otsatira a Yesu. (Yoh. 14:9) Kodi ifeyo timayenderanso maganizo a Yehova ndi Yesu pa nkhaniyi? Nanga zochita zathu zimasonyeza chiyani? Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti timakonda kuvala kapena kudzikongoletsa m’njira imene ikhoza kukhumudwitsa anthu ena mumpingo, kapena kuchititsa ena kuganizira zachiwerewere. Kodi tidzalolera kusiya n’cholinga choti tisawakhumudwitse? w18.11 25 ¶9-10

Lamlungu, December 13

Satana anamuyankha Yehova kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe? . . . Tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”​—Yobu 1:9, 11.

Tonsefe tiyenera kukhala ndi mtima wosagawanika chifukwa chakuti Satana amatsutsa Yehova komanso ifeyo. Mngelo woipayu anayesetsa kuipitsa mbiri yabwino ya Yehova ponena zinthu zosonyeza kuti Mulungu ndi woipa, wodzikonda komanso wabodza. N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kumvera Satana osati Yehova. (Gen. 3:1-6) Mu Edeni anali ndi zinthu zambiri zimene zikanawathandiza kukonda kwambiri Yehova. Koma pamene Satana anawayesa, anasonyeza kuti sankakonda Yehova ndi mtima wathunthu kapena kuti ndi mtima wonse. Patapita nthawi, Satana anatsutsanso zoti anthu angakhalebe okhulupirika kwa Yehova chifukwa chomukonda. Tingati anakayikira zoti anthu angapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. Satana anayambitsa nkhaniyi munthawi ya Yobu. (Yobu 1:8-11) Yobu sanali wangwiro ndipo ankalakwitsa zinthu zina ngati ifeyo. Koma Yehova ankamukonda kwambiri chifukwa anali ndi mtima wosagawanika. w19.02 4 ¶6-7

Lolemba, December 14

Anapita . . . n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo.​—Mat. 13:46.

Pofuna kusonyeza kuti choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu ndi chofunika kwambiri kwa anthu amene achipeza, Yesu anafotokoza zimene munthu wina wamalonda anachita atapeza ngale yabwino imene ankaifufuza. Ngaleyo inali yamtengo wapatali moti anapita “mwamsanga” n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo kuti akagule ngaleyo. (Mat. 13:45, 46) Ifenso titadziwa choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu komanso mfundo zina zomwe tinaziphunzira m’Mawu a Mulungu, tinaona kuti ndi zamtengo wapatali. Tinalolera kusintha zinthu zambiri mwamsanga kuti tikhale m’choonadi. Ndiye tikamachiona kuti ndi chamtengo wapatali, ‘sitingachigulitse.’ (Miy. 23:23) Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu a Mulungu ena asiya kuona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali ndipo afika pochigulitsa. Ifeyo tisalole kuti zimenezi zitichitikire. Kuti tisonyeze kuti timaona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali komanso kuti sitingachigulitse, tiyenera kumvera malangizo a m’Baibulo akuti tipitirizebe “kuyenda m’choonadi.” (3 Yoh. 2-4) Kuti tiziyendabe m’choonadi, tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene timaphunzira komanso kuika zinthu zokhudza choonadi pamalo oyamba. w18.11 9 ¶3

Lachiwiri, December 15

Mwa chikhulupiriro, makoma a Yeriko anagwa, atawazungulira masiku 7.​—Aheb. 11:30.

Aisiraeli analangizidwa kuti asaukire mzinda wa Yeriko koma azingouzungulira kamodzi pa tsiku kwa masiku 6 ndipo tsiku la 7 auzungulire maulendo 7. Asilikali ena ayenera kuti ankaganiza kuti, ‘Uku ndiye n’kungotaya nthawi chabe komanso kungodzitopetsatu.’ Koma Mtsogoleri wosaoneka wa Aisiraeli ankadziwa zimene akuchita. Kutsatira malangizo a Mulunguwa kunawathandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti asamenyane ndi asilikali amphamvu a ku Yeriko. (Yos. 6:2-5) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Nthawi zina tingamvetse chifukwa chimene gulu likuchitira zinthu zinazake. Mwachitsanzo, mwina poyamba tinkadabwa kuti n’chifukwa chiyani gulu likulimbikitsa kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kumisonkhano, mu utumiki komanso pophunzira patokha. Koma panopa ambirife tazindikira ubwino wake. Tikaona ubwino wa zinthu zimene poyamba sitinkazimvetsa, chikhulupiriro chathu chimalimba ndipo timakhala ogwirizana. w18.10 23 ¶8-9

Lachitatu, December 16

Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?—Mac. 1:6.

N’zosakayikitsa kuti zimene anthu, ngakhalenso ophunzira a Yesu, ankayembekezera zokhudza Mesiya n’zimene zinachititsa anthu a ku Galileya kufuna kuti Yesu akhale mfumu yawo. Ayenera kuti ankaganiza kuti Yesu akhala mfumu yabwino kwambiri chifukwa chakuti ankatha kuchiritsa odwala, kudyetsa anthu anjala komanso ankaphunzitsa bwino. Yesu atadyetsa amuna pafupifupi 5,000 anazindikira zimene anthuwo ankaganiza. Baibulo limati: “Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kumugwira kuti amuveke ufumu, anachoka ndi kupitanso kuphiri yekhayekha.” (Yoh. 6:10-15) Tsiku lotsatira, Yesu ali kutsidya lina la nyanja ya Galileya, anaona kuti ndi nthawi yabwino yowafotokozera za cholinga cha ntchito yake. Iye anawafotokozera kuti anabwera kudzathandiza anthu mwauzimu osati kungowapatsa zinthu monga chakudya. Yesu anawauza kuti: “Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha.”​—Yoh. 6:25-27. w18.06 4 ¶4-5

Lachinayi, December 17

Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima sadzachizimitsa.​—Yes. 42:3.

Yesu ankamvetsa anthu amene anali ngati bango lophwanyika kapena chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima. Chifukwa cha zimenezi, ankachita nawo zinthu mowaganizira, mokoma mtima komanso moleza mtima. (Maliko 10:14) N’zoona kuti sitingafanane ndi Yesu pa nkhani ya nzeru komanso kuphunzitsa bwino. Koma tiyenera kuchita zinthu moganizira anthu amene timawapeza mu utumiki. Tiyenera kuganizira mmene tingawalankhulire, nthawi imene tiyenera kuwapeza komanso kutalika kwa nthawi imene tingakambirane nawo. Masiku ano anthu ambiri ndi “onyukanyuka ndi otayika” chifukwa choponderezedwa ndi anthu amalonda, andale komanso achipembedzo. (Mat. 9:36) Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri alibe chiyembekezo ndipo sakhulupirira anthu. Choncho tiyenera kusankha bwino mawu n’kuwalankhula mokoma mtima komanso mwachifundo. Anthu ambiri amakopeka ndi uthenga wathu osati chifukwa choti timadziwa Baibulo kapena timafotokoza bwino mfundo basi, koma chifukwa choti timachita zinthu mowaganizira. w18.09 31-32 ¶13-14

Lachisanu, December 18

Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.​—Mat. 5:3.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timazindikira zosowa zathu zauzimu? Timachita zimenezi tikamaphunzira Mawu a Mulungu, kuyamikira mfundo zochokera kwa Yehova komanso kuika kutumikira Mulungu pamalo oyamba. Tikamachita zonsezi tidzakhala osangalala. Tidzayambanso kukhulupirira kwambiri kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. (Tito 2:13) Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale wosangalala. Pa nkhaniyi, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye [Yehova]. Ndibwerezanso, Kondwerani.” (Afil. 4:4) Kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova, tiyenera kukhala ndi nzeru yochokera kwa Mulungu. (Miy. 3:13, 18) Koma kuti tizisangalalabe sitiyenera kungowerenga Mawu a Mulungu koma tizitsatira zimene taphunzirazo. Potsindika kufunika kotsatira zimene taphunzira, Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.” (Yoh. 13:17; Yak. 1:25) Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri kuti munthu apeze zinthu zimene akusowa mwauzimu komanso kuti akhale wosangalala. w18.09 18 ¶4-6

Loweruka, December 19

[Epafura] amakupemphererani mwakhama nthawi zonse.—Akol. 4:12.

Epafura ankawadziwa bwino abale ndipo ankawakonda kwambiri. Ngakhale kuti anamangidwa limodzi ndi Paulo, iye ankaganizira za anthu ena ndipo ankawathandiza. (Filim. 23) Apatu anasonyeza kuti sanali wodzikonda. Kupempherera Akhristu anzathu n’kothandiza kwambiri makamaka tikamatchula mayina awo m’mapemphero athu. (2 Akor. 1:11; Yak. 5:16) Kodi ndi anthu ati amene mungawatchule m’mapemphero anu? Mofanana ndi Epafura, abale ndi alongo amapempherera anthu ena mumpingo wawo. Mwachitsanzo, amapempherera mabanja amene ali ndi maudindo akuluakulu, amene ayenera kusankha zochita pa nkhani zovuta kapena amene akukumana ndi mayesero. Ndi bwinonso kuganizira anthu amene aferedwa, akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi kapena nkhondo komanso amene akumana ndi mavuto azachuma. Pali abale ndi alongo ambiri amene tifunika kuwapempherera ndipo kuchita zimenezi kungawathandize kwambiri. w18.09 5-6 ¶12-13

Lamlungu, December 20

Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.—Mac. 20:35.

Kuwonjezera pa kupatsa anthu zinthu, Paulo ankatanthauzanso kupereka malangizo, kuthandiza anthu amene akuvutika komanso kuwalimbikitsa. (Mac. 20:31-35) Zolankhula komanso zochita za Paulo zimatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita pa nkhaniyi. Tiyenera kukonda anthu, kuwaganizira komanso kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu kuti tiwathandize. Anthu ochita kafukufuku apezanso kuti anthu opatsa amakhala osangalala. Nkhani ina imanena kuti “anthu akathandiza anzawo amayamba kumva bwino kwambiri komanso kusangalala.” Ochita kafukufukuwo ananena kuti munthu akamathandiza ena “amaona kuti moyo wake uli ndi cholinga.” Zili choncho chifukwa chakuti tinalengedwa m’njira yoti tizisangalala tikamathandiza ena. Chifukwa cha zimenezi, akatswiri amalimbikitsa anthu kuti azidzipereka kugwira ntchito zothandiza ena n’cholinga choti azimva bwino komanso azikhala osangalala. Zimenezi n’zosadabwitsa kwa anthu amene amaona kuti Baibulo ndi mphatso imene Mlengi wathu Yehova anatipatsa.​—2 Tim. 3:16, 17. w18.08 22 ¶17-18

Lolemba, December 21

Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.​—Yoh. 7:24.

Zimene Yesaya analosera zokhudza Yesu Khristu ndi zolimbikitsa kwambiri. Iye ananena kuti Yesu “sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake.” Ananenanso kuti Yesu “adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka.” (Yes. 11:3, 4) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimenezi ndi zolimbikitsa? Chifukwa chakuti m’dzikoli anthu ambiri ndi okondera ndiponso atsankho. Tonsefe timafuna kukhala ndi woweruza wabwino yemwe sangatiweruze potengera maonekedwe akunja. Tsiku lililonse timaweruza anthu. Koma popeza si ife angwiro, sitiweruza molondola ngati mmene Yesu amachitira. Nthawi zambiri timaweruza potengera zimene timaona. Koma Yesu ali padzikoli, anatilamula kuti tisamaweruze “poona maonekedwe akunja” koma kuweruza “ndi chiweruzo cholungama.” Apa n’zodziwikiratu kuti Yesu amafuna kuti tizimutsanzira n’kumapewa kuweruza anthu potengera maonekedwe awo. w18.08 8 ¶1-2

Lachiwiri, December 22

[Udzamva] mawu kumbuyo kwako, akuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.”​—Yes. 30:21.

N’zoona kuti sitichita kumva mawu akewo kuchokera kumwamba. Koma iye watipatsa Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, kuti tizipezamo malangizo. Mzimu woyera umathandizanso “mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika” kuti azipereka chakudya kwa atumiki ake. (Luka 12:42) Panopa timalandira chakudya chauzimu chambiri kudzera m’mabuku, zinthu za pa intaneti, mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera. Tiyeni tizikumbukira nthawi zonse mawu amene Yehova ananena pamene Yesu anali padzikoli. Tizichita zonse zimene tingathe kuti tilimbikitsidwe ndi mawu ake omwe ali m’Baibulo. Tizidziwa kuti Yehova akuona zonse zimene zikuchitika ndipo adzakonza mavuto onse amene anayamba chifukwa cha Satana ndi dziko loipali. Ndiye tiyeni tiziyesetsa kumvera mawu onse a Yehova. Tikatero tidzatha kupirira mavuto onse amene tingakumane nawo panopa kapena m’tsogolomu. Paja Baibulo limatiuza kuti: “Mukufunika kupirira, kuti mutachita chifuniro cha Mulungu, mudzalandire zimene Mulungu walonjeza.”​—Aheb. 10:36. w19.03 13 ¶17-18

Lachitatu, December 23

Yehova analankhula ndi Yoswa . . . kuti: “Mose mtumiki wanga wamwalira. Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodanoyu.”​—Yos. 1:1, 2.

Popeza Mose anatsogolera Aisiraeli kwa zaka zambiri, Yoswa ayenera kuti ankadzifunsa ngati anthuwo angamamumvere monga mtsogoleri wawo. (Deut. 34:8, 10-12) Ponena za Yoswa 1:1, 2, buku lina lofotokoza za Baibulo limanena kuti kuyambira kale komanso masiku ano, mtsogoleri akasintha zinthu zimasokonekera pa nkhani ya chitetezo cha dziko. Yoswa anali ndi zifukwa zomveka zomuchititsa kukhala ndi mantha. Koma patangopita masiku ochepa, anachita zinthu molimba mtima. (Yos. 1:9-11) Iye ankakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo sanagwiritsidwe mwala. Baibulo limasonyeza kuti Yehova anatsogolera Yoswa ndi mtundu wa Aisiraeli pogwiritsa ntchito mngelo. Pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti mngeloyu anali Mawu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu woyamba kubadwa. (Eks. 23:20-23; Yoh. 1:1) Yehova anathandiza Aisiraeli kuti azolowere kutsogoleredwa ndi Yoswa m’malo mwa Mose. w18.10 22-23 ¶1-4

Lachinayi, December 24

Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova​—Mal. 3:16.

Yehova amazindikira anthu amene amamutumikira ndi mtima wonse ndipo amalemba mayina awo ‘m’buku la chikumbutso.’ Komabe anthu amene mayina awo alembedwa ‘m’buku la chikumbutso’ la Yehova amayenera kuchita zinthu zina. Paja Malaki anasonyeza kuti tiyenera ‘kuopa Yehova komanso kuganizira za dzina lake.’ Ngati titayamba kudzipereka kwa munthu wina kapena chinthu china ndiye kuti dzina lathu likhoza kuchotsedwa m’buku la moyo lophiphiritsali. (Eks. 32:33; Sal. 69:28) Choncho pamafunika zambiri kuti munthu adzipereke kwa Yehova osati kungolonjeza kuti achita zimene Yehovayo amafuna ndiponso kubatizidwa basi. Tikutero chifukwa chakuti kulonjeza ndiponso kubatizidwa sizitenga nthawi yaitali ndipo zikhoza kuiwalika. Koma munthu amafunika kusonyeza kuti amamvera Yehova ndipo ali kumbali ya ulamuliro wake kwa moyo wake wonse.​—1 Pet. 4:1, 2. w18.07 23-24 ¶7-9

Lachisanu, December 25

Pamene tasiya chiphunzitso choyambirira cha Khristu tsopano, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.​—Aheb. 6:1.

Zimenezi sizingachitike pazokha. Tiyenera ‘kuyesetsa mwakhama’ ndipo sitiyenera kusiya. Kuti munthu akhale wolimba mwauzimu, ayenera kuwonjezera zimene amadziwa komanso kuzimvetsa bwino. N’chifukwa chake timakumbutsidwa pafupipafupi kuti tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse. (Sal. 1:1-3) Kodi mumayesetsa kuchita zimenezi? Tikamawerenga Baibulo tsiku lililonse tingayambe kulimvetsa bwino komanso kumvetsa malamulo ndi mfundo za Yehova. Lamulo lalikulu kwambiri la Akhristu ndi lonena za chikondi. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Yakobo, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, analemba kuti lamulo lonena za chikondi ndi “lamulo lachifumu.” (Yak. 2:8) Nayenso Paulo anati: “Chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.” (Aroma 13:10) N’zosadabwitsa kuti anthuwa anatsindika za chikondi chifukwa Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.”​—1 Yoh. 4:8. w18.06 19 ¶14-15

Loweruka, December 26

Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.​—Sal. 106:33.

Aisiraeli anaputa mkwiyo wa Yehova, koma Mose ndi amene anakwiya. Kusadziletsa kwake kunachititsa kuti alankhule mosaganizira mavuto amene angakumane nawo. Mose analola kuti zochita za anthu ena zimulepheretse kuyang’anabe kwa Yehova. Iye atakumana ndi vutoli pa ulendo woyamba anachita zinthu bwinobwino. (Eks. 7:6) Koma n’kutheka kuti atakhala zaka zambiri ndi Aisiraeli, omwe nthawi zambiri sankamvera, iye anakhumudwa komanso kutopa nawo. Mwina Mose ankaganizira kwambiri mmene Aisiraeliwo ankamukhumudwitsira m’malo moganizira mmene iyeyo angalemekezere Yehova. Ngati Mose, yemwe anali mneneri wokhulupirika, analephera kuyang’anabe kwa Yehova, ndiye kuti ifenso zikhoza kutichitikira. Nafenso tangotsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano limene Yehova watilonjeza. (2 Pet. 3:13) Palibe amene angafune kutaya mwayi umenewu. Koma kuti zimenezi zitheke, tonsefe tiyenera kuyang’anabe kwa Yehova kuti tidziwe zimene akufuna n’kumachita zomwezo.​—1 Yoh. 2:17. w18.07 15 ¶14-16

Lamlungu, December 27

Mwagonjetsa woipayo.​—1 Yoh. 2:14.

Satana sangatikakamize kuchita zimene sitikufuna. (Yak. 1:14) M’dzikoli anthu ambiri amachita zofuna za Satana mosazindikira. Koma akaphunzira mfundo za m’Baibulo, amasankha amene akufuna kumutumikira, kaya ndi Yehova kapena Satana. (Mac. 3:17; 17:30) Ngati tatsimikiza mumtima kuti tizimvera Yehova, palibe zimene Satana angachite kuti atilepheretse. (Yobu 2:3; 27:5) Koma pali zinthu zinanso zimene Satana ndi ziwanda zake sangathe kuchita. Mwachitsanzo, palibe paliponse m’Malemba pamene pamasonyeza kuti iwo angathe kuzindikira zimene zili m’maganizo kapena mumtima mwa munthu. Koma Malemba amasonyeza kuti Yehova ndi Yesu ndi amene angathe kuchita zimenezi. (1 Sam. 16:7; Maliko 2:8) Tikamayesetsa kulankhula komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna, tizidziwa kuti Yehova sangalole kuti Satana atibweretsere mavuto amene sangathetsedwe. (Sal. 34:7) Ndi zoona kuti tiyenera kudziwa bwino mdani wathu koma sitiyenera kumuopa. Ngakhale anthu amene si angwiro akhoza kugonjetsa Satana akamathandizidwa ndi Yehova. Tikamatsutsa Mdyerekezi, adzatithawa.​—Yak. 4:7; 1 Pet. 5:9. w18.05 26 ¶15-17

Lolemba, December 28

Pereka ntchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.​—Miy. 16:3.

Tiyerekeze kuti muli pa ulendo wokachita zinthu zina zofunika m’tauni ina yakutali. Ulendowo ndi wa pa basi ndipo ukutengerani nthawi yaitali. Kumalo okwerera basi kuli mabasi ambiri ndipo mumafunika kukwera basi yoyenera. Koma ngati mungakwere basi ina iliyonse, mukhoza kupita kumalo kolakwika. Achinyamata ali ngati munthu wa pa ulendo. Ulendo wake si wongoyenda pa basi, koma ndi wa moyo wawo wonse. Nthawi zina amavutika kuti asankhe bwino zochita ndipo anthu ambiri amawauza zinthu zosiyanasiyana zoti achite pa moyo. Koma ngati ali kale ndi cholinga pa moyo wawo, savutika kusankha zochita. Ndiye kodi muli ndi cholinga chosangalatsa Yehova? Izi zikutanthauza kuti muyenera kuganizira zimene Yehova amafuna mukamasankha zinthu pa nkhani zokhudza maphunziro, ntchito, banja komanso zinthu zina. M’mawu ena tingati ndi bwino kukhala ndi zolinga zauzimu n’kumayesetsa kuzikwaniritsa. Achinyamata amene amayesetsa kuti akwaniritse zolinga zawo pa nkhani yotumikira Yehova amadalitsidwa kwambiri. w18.04 25 ¶1-3

Lachiwiri, December 29

Kalanga ine mwana wanga! Wandiweramitsa ndi chisoni ndipo ine ndikukupitikitsa.​—Ower. 11:35.

Yefita anasunga lonjezo lake ndipo anatumiza mwana wakeyo, yemwe anali namwali, kuti azikatumikira kuchihema cha Mulungu ku Silo kwa moyo wake wonse. (Ower. 11:30-35) Zimene zinachitikazi zinamupweteka Yefita, koma mwana wakeyo ayeneranso kuti anapwetekedwa mtima. Koma chosangalatsa n’chakuti anavomereza zimene bambo ake analonjeza. (Ower. 11:36, 37) Apa tingati analolera kuti asadzakwatiwe n’kukhala ndi ana ndipo analibe mwayi wopitiriza dzina la banja lake kapena kulandira cholowa. Pamenepa titha kuoneratu kuti iye ankafunika kulimbikitsidwa. Baibulo limati: “Mu Isiraeli munakhala chizolowezi chakuti, chaka ndi chaka ana aakazi a mu Isiraeli anali kupita kukayamikira mwana wamkazi wa Yefita wa ku Giliyadi, maulendo anayi pa chaka.” (Ower. 11:39, 40) Masiku anonso, abale ndi alongo omwe sanalowe m’banja n’cholinga choti ‘akondweretse Ambuye’ ayenera kuyamikiridwa komanso kulimbikitsidwa.​—1 Akor. 7:32-35. w18.04 17 ¶10-11

Lachitatu, December 30

Angelo . . . sanasunge maloawo oyambirira koma anasiya malo awo okhala.​—Yuda 6.

Angelo ambiri anakhala kumbali ya Satana poukira Mulungu. Chigumula chisanafike, Satana anakopa angelo ena kuti agone ndi akazi padzikoli. Baibulo limatsimikizira zimenezi pofotokoza Satana monga chinjoka chimene chinakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba. (Gen. 6:1-4; Chiv. 12:3, 4) Pamene angelowo anachoka m’banja la Mulungu, anayamba kulamuliridwa ndi Satana. Koma sikuti angelowa amangokhala ngati gulu la anthu osokoneza basi. Tikutero chifukwa chakuti Satana wakhazikitsa ufumu motsanzira Ufumu wa Mulungu, ndipo iye ndi mfumu yake. Mu ufumu wake wosaonekawu, wakhazikitsanso maboma ndipo waika ziwanda zake kuti zizilamulira. (Aef. 6:12) Satana amagwiritsa ntchito ufumu wake kuti azilamulira maboma a anthu. w18.05 23 ¶5-6

Lachinayi, December 31

Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.—Sal. 16:7.

Nthawi zina Mulungu amatisonyeza chikondi potipatsa malangizo ngati mmene bambo angachitire ndi mwana wake. Davide atapatsidwa malangizo anawalandira bwino. Iye ankaganizira kwambiri mfundo za Yehova, kuzikonda komanso kulola kuti zisinthe maganizo ake. Inunso mukamachita zimenezi mudzayamba kukonda kwambiri Yehova komanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumumvera. Mudzakhalanso Mkhristu wolimba mwauzimu. Mlongo wina dzina lake Christin anati: “Ndikamafufuza mfundo za m’Baibulo komanso kuziganizira kwambiri ndimamva ngati mfundozi Yehova analembera ineyo.” Kukhala munthu wauzimu kumathandizanso munthu kukhala wozindikira komanso wanzeru. Zili choncho chifukwa amatha kuona zinthu za m’dzikoli komanso zam’tsogolo ngati mmene Mulungu amazionera. Koma kodi n’chifukwa chiyani Yehova amakupatsani nzeru zimenezi komanso kuzindikira? Iye amafuna kuti muziika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba, muzisankha zochita mwanzeru komanso musamaope zimene zichitike m’tsogolo.—Yes. 26:3. w18.12 26 ¶9-10

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani