December 18-24
ZEKARIYA 9-14
Nyimbo Na. 49 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musachoke ‘M’chigwa cha Pakati pa Mapiri’”: (10 min.)
Zek. 14:3, 4—“Chigwa chachikulu kwambiri” chikuimira chitetezo chochokera kwa Mulungu (w13 2/15 19 ¶10)
Zek. 14:5—Anthu amene ‘angathawire m’chigwachi’ adzatetezedwa (w13 2/15 20 ¶13)
Zek. 14:6, 7, 12, 15—Anthu amene ali kunja kwa chigwa cha Yehova cha chitetezo adzawonongedwa (w13 2/15 20 ¶15)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Zek. 12:3—Kodi Yehova anasandutsa bwanji Yerusalemu kukhala “mwala wotopetsa”? (w07 12/15 22-23 ¶9-10)
Zek. 12:7—N’chifukwa chiyani Yehova adzayambirire kupulumutsa “mahema a Yuda”? (w07 12/15 25 ¶13)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Zek. 12:1-14
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) g17.6 14-15—Muitanireni kumisonkhano yathu.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) g17.6—tsamba 14 ndi 15. Sonyezani mmene mungapangire ulendo wobwereza pogwiritsa ntchito magazini imene munamusiyira pa ulendo woyamba. Kenako muitanireni kumisonkhano yathu.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) jl phunziro 5—Muitanireni kumisonkhano yathu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Gulu Lathu Lachita: (7 min.) Onetsani vidiyo yakuti Zimene Gulu Lathu Lachita ya December.
“Mbali Yatsopano pa Misonkhano ya Mkati mwa Mlungu”: (8 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo ya Betefage, Phiri la Maolivi ndi Yerusalemu.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 11 ¶22-28 komanso tsamba 117
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero