Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb17.10 7
  • Muzitumikira Yehova Nthawi Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzitumikira Yehova Nthawi Zonse
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Muzisangalala ndi Utumiki Wanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Achinyamata, Kodi Yehova Ndi Mnzanu Wapamtima?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Muzisangalala ndi Zonse Zomwe Mukuchita Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17.10 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzitumikira Yehova Nthawi Zonse

Moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali. Zimene timachita tsiku ndi tsiku zimasonyeza ngati timayamikira mphatsoyi kapena ayi. Monga Mboni za Yehova, timayesetsa kugwiritsa ntchito mphamvu zathu komanso luso lathu potumikira Yehova, yemwe anatipatsa moyo. (Sal. 36:9; Chiv. 4:11) Komabe nkhawa za tsiku ndi tsiku zimene timakhala nazo zingasokoneze zolinga zathu zofuna kutumikira Yehova. (Maliko 4:18, 19) Choncho tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuyesetsa kuchita zonse zimene ndingathe potumikira Yehova? (Hos. 14:2) Kodi ntchito imene ndimagwira ikundilepheretsa kuchita zambiri? Kodi zolinga zanga n’zotani? Kodi ndingatani kuti ndizichita zambiri mu utumiki?’ Ngati mukuona kuti pali zina zimene mukufunikira kusintha, pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni. Musamakayikire kuti kutumikira Yehova nthawi zonse kudzakuthandizani kukhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala.​—Sal. 61:8.

Edgardo Franco akuimba; Edgardo Franco ali mu utumiki

Kodi inuyo mumapereka luso lanu kwa ndani?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRITSA NTCHITO LUSO LANU KUTUMIKIRA YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani tinganene kuti si nzeru kugwiritsa ntchito luso lathu pa zinthu za m’dziko la Satanali? (1 Yoh. 2:17)

  • Kodi anthu amene amachita zonse zimene angathe potumikira Yehova amapeza madalitso otani?

  • Kodi mungathe kugwiritsa ntchito luso lanu pochita mautumiki osiyanasiyana ati?

ZIMENE MUNGACHITE PA KULAMBIRA KWA PABANJA:

  • Funsani wofalitsa amene watumikira Yehova kwa zaka zambiri, mwina pochita utumiki wa nthawi zonse. Kodi anadzimana zinthu ziti kuti azichita zambiri potumikira Yehova? Nanga Yehova wamudalitsa bwanji?

  • Pitani pa JW Broadcasting, ndipo onani pamene alemba kuti ZOCHITIKA PA MOYO WA ANTHU ENA > MADALITSO OBWERA CHIFUKWA CHOCHITA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE. Pamenepo muona komanso kumva zosangalatsa zimene zinachitikira anthu ena amene akhala akuchita mautumiki osiyanasiyana kwa nthawi yaitali

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani