Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MARCH 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 3
Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Yehova
ijwbv nkhani na. 14 ¶4-5
Miyambo 3:5, 6—“Usamadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
“Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” Timasonyeza kuti timadalira Mulungu tikamachita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake. Timafunika kumakhulupirira Mulungu ndi mtima wathu wonse. Nthawi zambiri Baibulo likamanena za mtima, limanena zokhudza mmene munthuwe ulili mumtima mwako, zomwe zikuphatikizapo mmene umamvera, zolinga zako, maganizo ako komanso mmene umaonera zinthu. Choncho, kukhulupirira Mulungu ndi mtima wathu wonse kumaphatikizapo zinthu zambiri osangoti mmene timamvera. Ndi zimene timasankha chifukwa chokhulupirira kwambiri kuti Mlengi wathu amadziwa zinthu zomwe ndi zothandiza kwambiri kwa ife.—Aroma 12:1.
“Usamadalire luso lako lomvetsa zinthu.” Popeza si ife angwiro, timafunika kudalira Mulungu osati luso lathu la kuganiza. Tikamadzidalira kapena kumangochita zinthu chifukwa cha mmene tikumvera, tikhoza kusankha zinthu zomwe poyamba zingaoneke zabwino koma zotsatira zake zingakhale zoipa. (Miyambo 14:12; Yeremiya 17:9) Nzeru za Mulungu ndi zapamwamba kwambiri kuposa zathu. (Yesaya 55:8, 9) Tikamatsogoleredwa ndi maganizo ake, zinthu zimatiyendera bwino.—Salimo 1:1-3; Miyambo 2:6-9; 16:20.
ijwbv nkhani na 14 ¶6-7
Miyambo 3:5, 6—“Usamadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
“Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse.” Timafunika kuyendera maganizo a Mulungu pa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu komanso tikamasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Timachita zimenezi tikamapemphera kwa iye kuti azititsogolera ndiponso tikamatsatira zimene amatiuza m’Mawu ake, Baibulo.—Salimo 25:4; 2 Timoteyo 3:16, 17.
“Iye adzawongola njira zako.” Mulungu amawongola njira zathu potithandiza kuti tizitsatira mfundo zake zolungama pa moyo wathu. (Miyambo 11:5) Zimenezi zimatithandiza kuti tisamakumane ndi mavuto opeweka ndipo timakhala moyo wosangalala kwambiri.—Salimo 19:7, 8; Yesaya 48:17, 18.
be 76 ¶4
Khalani Womapitabe Patsogolo
Munthu akaona zambiri m’moyo, angalingalire kuti: ‘Zimenezi sizachilendo kwa ine. Ndikudziwa zochita.’ Kodi imeneyi ingakhale nzeru? Miyambo 3:7 imachenjeza kuti: “Usadziyese wekha wanzeru.” Inde, kudziwa zambiri kuyeneradi kutithandiza kuona mbali zosiyanasiyana pochita ndi mikhalidwe ina m’moyo. Koma ngati tikupita patsogolo mwauzimu, kudziwa kwathu zambiri kuyenera kuthandizanso maganizo athu ndi mitima yathu kudziwa kuti tifunikira thandizo la Yehova kuti tipambane. Choncho, taona kuti kupita kwathu patsogolo kumaonekera osati mwa kudzidalira tokha pochita ndi mikhalidwe, koma mwa kutembenukira kwa Yehova mwachangu kuti atitsogolere m’miyoyo yathu. Kumaonekera mwa kukhala ndi chidaliro chakuti palibe chingatheke popanda chilolezo chake. Kumaonekeranso mwa kusunga unansi wathu wokhulupirira Atate wathu wakumwamba ndi kumukonda.
Mfundo Zothandiza
w06 9/15 17 ¶7
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
3:3. Tiyenera kuona kuti kukhala wokoma mtima mwachikondi ndi wachoonadi ndi makhalidwe amtengo wapatali, ndipo tiyenera kuwasonyeza ngati mmene tingachitire ndi mkanda wa pakhosi womwe uli wokwera mtengo. Tikufunikiranso kukhomereza makhalidwe amenewa pamtima pathu, kuwachititsa kukhala mbali yaikulu ya moyo wathu.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
w11 3/15 14 ¶7-10
Muzidalira Yehova Pamene Mapeto Akuyandikira
7 Abale athu ambiri amatumikira m’madera amene amafunika kupirira kwambiri. Mneneri Yeremiya anatumikiranso m’dera lotereli. Iye ankalalikira mu ufumu wa Yuda utatsala pang’ono kuwonongedwa ndipo iyi inali nthawi yovuta kwambiri. Tsiku lililonse chikhulupiriro cha Yeremiya chinkayesedwa chifukwa chomvera Mulungu pogwira ntchito yolalikira uthenga wa chiweruzo Chake. Pa nthawi ina ngakhale Baruki, yemwe anali mlembi wake wokhulupirika, anadandaula chifukwa chotopa. (Yer. 45:2, 3) Kodi Yeremiya anagwa ulesi chifukwa cha zimenezi? Pa nthawi zina iye ankavutika kwambiri maganizo mpaka anafika ponena kuti: “Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!” Ananenanso kuti: “N’chifukwa chiyani ndinabadwa? Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni, ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?”—Yer. 20:14, 15, 18.
8 Koma Yeremiya sanasiye ntchito yake. Iye anapitiriza kudalira Yehova. Zotsatira zake zinali zakuti mneneriyu anaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yehova olembedwa pa Yeremiya 17:7, 8 akuti: “Wodala ndi munthu aliyense amene amakhulupirira Yehova, amene amadalira Yehova. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi. Kutentha kukadzafika iye sadzadziwa, koma masamba ake adzachuluka ndi kukhala obiriwira. Pa nthawi ya chilala sadzada nkhawa kapena kusiya kubala zipatso.”
9 Mofanana ndi mtengo wa zipatso wobiriwira “wobzalidwa m’mphepete mwa madzi” kapena m’munda wa zipatso wothiriridwa bwino, Yeremiya ‘sanasiye kubala zipatso.’ Iye sanalole kufooketsedwa ndi anthu oipa amene ankamunyoza. M’malomwake, iye nthawi zonse ankadalira Kasupe wa “madzi” opatsa moyo ndipo ankatsatira zonse zimene Yehova anamuuza. (Werengani Salimo 1:1-3; Yer. 20:9) Apatu Yeremiya anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri makamaka ngati tikutumikira Mulungu m’madera ovuta. Ngati mukutumikira m’dera lovuta, pitirizani kudalira kwambiri Yehova amene angakuthandizeni kupirira “polengeza dzina lake kwa anthu ena.”—Aheb. 13:15.
10 Yehova watipatsa paradaiso wauzimu wokhala ndi zinthu zambiri pofuna kutithandiza kuti tipirire mavuto a pa moyo wathu masiku otsiriza ano. Zina mwa zinthu zimene watipatsa ndi Baibulo lonse, lomwe ndi Mawu ake, ndipo likumasuliridwa molondola m’zinenero zambirimbiri. Iye wapereka chakudya chauzimu chambiri ndiponso pa nthawi yake kudzera mwa gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Iye watipatsanso abale ndi alongo amene amatilimbikitsa tikamacheza nawo pa misonkhano yampingo ndi ikuluikulu. Kodi mumagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimene watipatsazi? Anthu onse amene amagwiritsa ntchito mokwanira zinthu zimenezi “adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” Koma amene samvera Mulungu ‘adzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo adzafuula chifukwa chosweka mtima.’—Yes. 65:13, 14.
MARCH 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 6
Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Nyerere?
it-1 115 ¶1-2
Nyerere
‘Nzeru Zachilengedwe.’ Nyerere zimachita zinthu ‘mwanzeru,’ osati chifukwa choti zimaganiza kwambiri, koma chifukwa cha mmene Mlengi anazilengera. Baibulo limanena za nyerere kuti “imakonza chakudya chake m’chilimwe, ndipo imasonkhanitsa chakudya chake pa nthawi yokolola.” (Miy 6:8) Mtundu wina wa nyerere zodziwika bwino zomwe zimapezeka ku Palesitina (Messor semirufus), zimasunga chakudya chochuluka m’nyengo yokolola komanso yotentha ndipo zimagwiritsa ntchito chakudyachi m’nyengo imene chimasowa, kuphatikizapo nyengo yozizira. Nthawi zambiri nyerere zimenezi zimapezeka m’malo opunthira mbewu omwe pamakhala mbewu zambiri. Ngati mvula yachititsa kuti mbewuzi zinyowe, nyererezi zimazitutira panja kukaziyanika padzuwa kuti ziume. Zimadziwikanso kuti zimaluma kamtima ka mbewu zimene zasunga n’cholinga choti zisamere. Pamalo pamene pamakhala nyererezi pamadziwika bwino ndi tinjira take komanso mankhusu a mbewu amapezeka pamene zimalowera.
Zimapereka Chitsanzo Chabwino. Pofotokoza mwachidule zimene nyerere zimachita, Baibulo limanena kuti: “Pita kwa nyerere waulesi iwe, ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.” (Miy 6:6) Nyerere sikuti zimangodziwika bwino ndi kukonzekera zam’tsogolo basi, koma zimadziwikanso kuti zimagwira ntchito mwakhama. Nthawi zambiri zimanyamula zinthu zolemera kuwirikiza kawiri kulemera kwake kapena kuposa ndipo zimayesetsa mmene zingathere kuti zimalize ntchito zimene zikugwira. Sizifooka ngakhale zitagwa, kuterereka kapena kugubuduka zikamayenda malo ovuta kuyendapo. Chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti, zimachita zinthu mogwirizana poyesetsa kuti malo amene zimakhala azikhala aukhondo komanso zimachita zinthu moganizira zinzawo zimene zavulala kapena zimene zatopa ndipo nthawi zambiri zimazithandiza kuti zibwerere kudzenje.
w00 9/15 26 ¶3-4
Tetezani Dzina Lanu
Mofanana ndi nyerere, kodi nafenso sitifunikira kuchita khama? Kugwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa kuti tichite bwino pantchito yathu n’kwabwino kwa ife kaya pali wotiyang’anira kapena ayi. Inde, kusukulu, kuntchito kwathu, komanso pogwira ntchito zauzimu ndi anzathu, tiyenera kuchita bwino koposa. Monga momwe nyerere zimapindulira ndi khama lawo, momwemonso Mulungu akufuna kuti ‘tione zabwino m’ntchito zathu zonse.’ (Mlaliki 3:13, 22; 5:18) Chikumbumtima chabwino ndi chikhutiro ndizo mphoto ya kugwira ntchito molimbika.”—Mlaliki 5:12.
Pogwiritsa ntchito mafunso awiri odzutsa chidwi, Solomo akuyesa kugalamutsa waulesi kuti asachite zala lende, akumati: “Udzagona mpaka liti, waulesi iwe? Udzauka ku tulo tako liti?” Mwa kuyerekezera kulankhula kwa munthu waulesi, mfumuyo ikupitiriza kuti: “Tulo ta pang’ono, kuodzera pang’ono, kungomanga manja pang’ono, ndi kugona; ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala, ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa [“msilikali,” NW].” (Miyambo 6:9-11) Pamene waulesi akadagona, umphawi umam’fikira mofulumira ngati wakuba, ndipo kusauka kumam’kantha ngati munthu wonyamula lupanga. Minda ya munthu waulesi siichedwa kumera thengo ndi khwisa. (Miyambo 24:30, 31) Bizinesi yake imalowa pansi pa kanthawi kochepa. Kodi wolemba anthu ntchito angalekerere waulesi kwautali wotani? Ndipo kodi wophunzira amene n’ngwaulesi n’kuwerenga angayembekezere kuchita bwino kusukulu?
APRIL 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 8
Muzimvetsera Nzeru Yomwe Ikulankhula Ngati Munthu
cf 131 ¶7
“Ndimakonda Atate”
7 Mu vesi 22, nzeru ikunena kuti: “Ine ndinali woyamba kulengedwa ndi Yehova, ndinali woyambirira pa zinthu zonse zimene anapanga kalekale kwambiri.” Lembali silikungonena za nzeru zenizeni chifukwa nzeru sizinachite “kulengedwa.” Nzeru zilibe chiyambi chifukwa Yehova wakhala alipo kuyambira kalekale ndipo nthawi zonse ndi wanzeru. (Salimo 90:2) Koma Mwana wa Mulungu ali ndi chiyambi chifukwa ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” Iye anachita kupangidwa kapena kuti kulengedwa ndipo ndi woyamba pa zonse zimene Yehova analenga. (Akolose 1:15) Mwanayu analipo Mulungu asanalenge dziko lapansi komanso kumwamba ngati mmene buku la Miyambo likufotokozera. Monga Mawu, kapena kuti wolankhula m’malo mwa Mulungu, iye anasonyeza bwino kwambiri nzeru zimene Yehova ali nazo.—Yohane 1:1.
cf 131-132 ¶8-9
“Ndimakonda Atate”
8 Kodi Mwanayu ankachita chiyani pa nthawi yonse imene anali kumwamba asanabwere padziko lapansi? Vesi 30 likusonyeza kuti Yesu anali pambali pa Mulungu monga “mmisiri waluso.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Lemba la Akolose 1:16 limanena kuti: “Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi . . . Analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye ndiponso chifukwa cha iye.” Choncho Yehova, yemwe ndi Mlengi, anagwiritsa ntchito Mwana wake, amene ndi Mmisiri Waluso, polenga zinthu zonse monga angelo kumwamba, zinthu zonse zakuthambo, dziko lapansi ndi zinthu zonse zodabwitsa monga zomera komanso nyama. Analenganso munthu, yemwe ndi wapamwamba kuposa chinthu chilichonse padziko lapansi. Mgwirizano wa Atate ndi Mwana wakeyu tingauyerekezere ndi wa katswiri wolemba mapulani a nyumba ndi mmisiri wake amene amatsatira mapulaniwo pomanga nyumba. Tikamachita chidwi ndi zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, kwenikweni timakhala tikutamanda Yehova, Katswiri Wamkulu Wolemba Mapulani. (Salimo 19:1) Komanso tingakumbukire mgwirizano wabwino umene unalipo kwa nthawi yaitali pakati pa Mlengi ndi ‘mmisiri wake waluso’ ameneyo.
9 Anthu awiri opanda ungwiro akamagwira ntchito limodzi nthawi zina amasemphana maganizo. Koma si mmene zinalili pakati pa Yehova ndi Mwana wake. Mwanayu anagwira ntchito limodzi ndi Atate wake kwa nthawi yaitali kwambiri ndipo iye ananena kuti: “Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (Miyambo 8:30) Iye ankasangalala kukhala ndi Atate wake ndipo ankakondana kwambiri. Mwanayu anayamba kuchita zinthu mofanana kwambiri ndi Atate wake ndipo anatengera makhalidwe ake. Mpake kuti Atate ndi Mwanayu anayamba kukondana kwambiri. Choncho tinganene motsimikiza kuti palibe amene amakondana kwambiri kuposa Atate ndi Mwana wakeyu. Iwo anayamba kukondana kalekale.
w09 4/15 31 ¶14
Kuzindikira Yesu Monga Davide Wamkulu Ndiponso Solomo Wamkulu
14 Ndi munthu mmodzi yekha amene anali ndi nzeru kuposa Solomo. Munthu ameneyu anali Yesu Khristu. Iye anadzitcha kuti “wina woposa Solomo.” (Mat. 12:42) Mawu a Yesu anali “mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:68) Chitsanzo cha zimenezi ndi mfundo zimene iye ananena mu ulaliki wapaphiri. Mfundo zimenezi zimafotokoza bwino lomwe zinthu zimene Solomo ananena m’miyambi yake ndipo zimatithandiza kumvetsa miyambiyo. Solomo anafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zingawathandize atumiki a Yehova kukhala osangalala. (Miy. 3:13; 8:32, 33; 14:21; 16:20) Yesu anatsindika mfundo yakuti zimene zimabweretsa chisangalalo chenicheni ndi zinthu zokhudza kulambira Yehova komanso kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake. Iye ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) Anthu amene amagwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsa amakhala pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi “chitsime cha moyo.” (Sal. 36:9; Miy. 22:11; Mat. 5:8) Zoonadi, Khristu ndi “nzeru za Mulungu.” (1 Akor. 1:24, 30) Monga Mfumu Mesiya, Yesu Khristu ali ndi “mzimu wanzeru.”—Yes. 11:2.
APRIL 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 9
Mukhale Anzeru, Osati Onyoza
w01 5/15 30 ¶5
‘Ndi Nzeru Masiku Athu Adzachuluka’
Ndi udindo wa aliyense kuyesetsa kupeza nzeru. Ponenetsa mfundo imeneyi, Solomo anati: “Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo? Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.” (Miyambo 9:12) Munthu wanzeru amapindula nayo yekha, koma wonyoza adzavutika yekha. Ndithudi, timakolola zomwe tinafesa. Tsono tiyenitu ‘titchere makutu athu ku nzeru.’—Miyambo 2:2.
Mfundo Zothandiza
w06 9/15 17 ¶5
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
9:17—Kodi “madzi akuba” n’chiyani ndipo n’chifukwa chiyani ‘amatsekemera’? Popeza kuti Baibulo limayerekezera kusangalala ndi kugonana kumene kumachitika muukwati ndi kumwa madzi otsitsimula otungidwa pachitsime, madzi akuba akuimira kuchita zachiwerewere mobisa. (Miyambo 5:15-17) Maganizo ochita zachiwerewere popanda kugwidwa ndiwo amene amachititsa kuti madzi oterowo azioneka ngati otsekemera.
APRIL 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 10
Kodi N’chiyani Chimathandiza Munthu Kumasangalaladi pa Moyo?
w01 7/15 25 ¶1-3
‘Madalitso Ali pa Wolungama’
Wolungama amapindulanso m’njira ina. “Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa. Wokolola m’malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakututa ndi mwana wochititsa manyazi.”—Miyambo 10:4, 5.
Mawu a mfumuwa akutanthauza zambiri makamaka kwa ogwira ntchito yotuta. Nthawi yotuta si nthawi yogona. Ndi nthawi yogwira ntchito mwakhama kwa maola ochuluka. Ndithudi imeneyi imakhala nthawi yofunika kuchita changu.
Pamene Yesu anali kulingalira za kututa anthu osati zokolola zakumunda, anauza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta [Yehova Mulungu] kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:35-38) M’chaka cha 2000, anthu oposa 14 miliyoni anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu; kuwirikiza kawiri chiwerengero cha Mboni za Yehova. Motero ndani angatsutse kuti ‘m’minda mwayera kufikira kumweta’? (Yohane 4:35) Olambira oona amapempha Mwini ntchito kuti atumize antchito ena. Akamatero amakhalanso akudzipereka zolimba m’ntchito yopanga ophunzira mogwirizana ndi mapemphero awowo. (Mateyu 28:19, 20) Ndipotu Yehova wadalitsa khama lawo mosaneneka! M’chaka chautumiki cha 2000, munabatizidwa anthu atsopano oposa 280,000. Amenewanso amayesetsa kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Tikhaletu achimwemwe ndi okhutira panthawi yotuta ino mwa kugwira nawo mokwanira ntchito yopanga ophunzira.
Mfundo Zothandiza
w06 5/15 30 ¶18
Ubwino Woyenda Mwangwiro
18 “Madalitso a Yehova” ndiwo akuthandiza anthu ake kuti zinthu ziziwayendera bwino mwauzimu. Ndipo akutitsimikizira kuti “sawonjezerapo chisoni.” (Miyambo 10:22) Ndiyeno n’chifukwa chiyani ambiri mwa anthu okhulupirika a Mulungu amakumana ndi mavuto ndiponso mayesero, omwe amachititsa kuti azivutika kwambiri? Timavutika chifukwa cha zinthu zitatu makamaka. (1) Zochita zathu zauchimo. (Genesis 6:5; 8:21; Yakobo 1:14, 15) (2) Satana ndi ziwanda zake. (Aefeso 6:11, 12) (3) Dziko loipa. (Yohane 15:19) Ngakhale kuti Yehova amalola kuti zinthu zoipa zizitichitikira, sikuti iye ndiye amachititsa zinthuzo. Ndipotu, “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko.” (Yakobo 1:17) Madalitso a Yehova sabweretsa mavuto.
APRIL 28–MAY 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 11
Musamalankhule
w02 5/15 26 ¶4
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Kuwongoka mtima kwa olungama ndiponso zimene woipa amachita zimakhudzanso anthu ena. Mfumu ya Israyeli inati: “Wonyoza Mulungu awononga mnzake ndi m’kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.” (Miyambo 11:9) Kodi alipo angatsutse zoti bodza, miseche, mawu otukwana, ndi njerengo zachabe zimavulaza ena? Kusiyana ndi zimenezi, wolungama amalankhula zabwino, amaganiza kaye asanalankhule, ndiponso amaganizira ena. Wolungama amapulumuka mwa zimene akudziwa chifukwa kuwongoka mtima kwake kumam’thandiza kukhala ndi umboni wofunika kusonyeza kuti anthu amene akumuimba mlandu ndi abodza.
w02 5/15 27 ¶3-4
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Anthu amene amachita zinthu zolungama pamudzi amalimbikitsa mtendere ndi moyo wabwino ndiponso amalimbikitsa ena. Motero, amakuza mudzi, zinthu zimayenda bwino pamudzipo. Amene amalankhula zojeda anzawo, zokhumudwitsa, ndiponso zinthu zachabe amayambitsa chisokonezo, chisoni, kusagwirizana ndi mavuto. Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati amene akuchita zimenezo ndi anthu amene ali ndi udindo pamudzipo. Pamudzi wotero pamakhala chisokonezo, katangale, makhalidwe oipa ndiponso mwina mavuto a zachuma.
Mfundo ya pa Miyambo 11:11 imagwiranso ntchito chimodzimodzi kwa anthu a Yehova akamasonkhana pamodzi m’mipingo yawo yonga midzi. Anthu auzimu—amene amatsatira kuwongoka mtima—akamatsogolera mpingo, anthu mumpingomo amakhala achimwemwe, okangalika ndiponso amakhala othandiza. Zimenezi zimalemekeza Mulungu. Yehova amadalitsa mpingowo, ndipo umayenda bwino mwauzimu. Nthawi zina, anthu ochepa odandaula ndi osakondwa, omwe amapeza anzawo zifukwa ndipo amalankhula moipidwa ndi mmene zinthu zikuyendera, ali ngati ‘muzu wowawa’ umene ungafalikire ndi kuipitsa anthu ena amene poyamba analibe maganizo otero. (Ahebri 12:15) Nthawi zambiri anthu oterowo amafuna mpando ndi kutchuka. Amayambitsa mphekesera zakuti mumpingomo kapena akulu sakuchita chilungamo, pali kusankhana mafuko, kapena zinthu zina. Pakamwa pawo pangagawanitsedi mpingo. Kodi si bwino kusamvera zimene akunena ndi kuyesetsa kukhala anthu auzimu amene tingalimbikitse mtendere ndi mgwirizano mumpingo?
Mfundo Zothandiza
g20.1 11, bokosi
Zimene Mungachite Kuti Muchepetse Nkhawa
“GONJETSANI NKHAWA POCHITIRA ENA ZABWINO”
“Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake, koma munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.”—MIYAMBO 11:17.
Buku lina lofotokoza za nkhawa lili ndi mutu wakuti “Gonjetsani Nkhawa Pochitira Ena Zabwino.” (Overcoming Stress) Mlembi wa bukuli dzina lake Dr. Tim Cantopher ananena kuti kuchitira ena zabwino kumathandiza kuti munthu akhale wathanzi komanso azisangalala. Koma munthu amene sachitira ena zabwino kapena wankhanza, sasangalala chifukwa anthu amamupewa.
Tingachepetsenso nkhawa ngati timayesetsa kuchita zinthu modziganizira. Mwachitsanzo, sitiyenera kumadzikhaulitsa kapena kudzipanikiza komanso tisamadzikayikire. Yesu Khristu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”—Maliko 12:31.