Malifalensi a Isibuku ya Sonkano wa Utumiki Koma Teto Moywi-u wa Ikristu
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MULUNGU WA SEPTEMBALA 1-7
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 29
Kamupangengana Miyambo na Viro- romelo Vyevyo Kavinamusangalasa Yehova
wp16.06 takuru 6, bokosi
Masompenya Onikami-a Vwechecha Vya Udimu
Anthu ambiri amaopa kwambiri mizimu yoipa. Iwo amatsirika zinthu zawo komanso kugwiritsa ntchito zithumwa pofuna kudziteteza ku ziwandazo. Komatu palibe chifukwa chochitira zimenezi. Zili choncho chifukwa Baibulo limatitsimikizira kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.” (2 Limbili 16:9) Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana ndipo adzakutetezani mukamamudalira.
Kuti Yehova azikutetezani muyenera kuphunzira zimene amafuna n’kumatsatira zimene mwaphunzirazo. Mwachitsanzo, Akhristu akale amumzinda wa Efeso anasonkhanitsa mabuku awo azamatsenga n’kuwatentha. (Vyo. 19:19, 20) Choncho kuti inunso Mulungu azikutetezani muyenera kutaya zithumwa, nsupa, mikuzi, mabuku azamatsenga kapena chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu.
w19.04 takuru 17 ndima 13
Ni-arelenga Makundo a Choonadi Vaireya Malilo
13 Ngati simukudziwa zoyenera kuchita pa miyambo inayake muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akupatseni nzeru. (Welengani Yakobo 1:5.) Kenako mungafufuze m’mabuku athu. Mwinanso tingafunse akulu mumpingo wathu. Iwo sangakusankhireni zochita koma angakukumbutseni mfundo za m’Baibulo ngati zimene tikukambiranazi. Mukamachita zimenezi, mumaphunzitsa ‘mphamvu zanu za kuzindikira’ kuti muzitha “kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.” — Aheb. 5:14.
w18.11 takuru 11 ndima 12
“Ndinoza Ndiyende mu Choonadinyu”
12 Miyambo ndi zikhalidwe zosemphana ndi Malemba. Achibale athu, anzathu akuntchito kapena akusukulu angafune kuti tichite nawo miyambo ina. Kodi tingapewe bwanji kuchita nawo miyambo ndi zikhalidwe zimene Mulungu amadana nazo? Chimene chingatithandize ndi kukumbukira mmene Yehova amaonera zinthuzo. Ndi bwino kuonanso nkhani za m’mabuku athu zofotokoza mmene maholide osiyanasiyana anayambira. Kukumbukira zifukwa za m’Malemba zimene zingatithandize kuti tizipewa maholidewa kumatithandiza kutsimikiza mumtima mwathu kuti tikuchita zinthu ‘zovomerezeka kwa Ambuye.’ (Aif. 5:10) Kukhulupirira Yehova ndiponso Mawu ake kumatithandiza kuti tisamaope anthu.”— Miya. 29:25.
Makundo Okami-a
w17.10 takuru 9 ndima 11
“Nitonyi-edanenga Chikondi Yeniyeni Muvyoira Vi-u”
Tiziyamikira abale athu kuchokera mumtima. Tiyenera kuyesetsa kuyamikira anzathu pamene achita zabwino chifukwa zimenezi zimawalimbikitsa. (Aife. 4:29) Koma tiyenera kuchita zimenezi kuchokera mumtima. Kupanda kutero kuyamikira kwathuko kumakhala kwachinyengo komanso tingakhale tikupewa udindo wathu wopereka malangizo amene munthuyo angafunikire. (Miya. 29:5) Ngati timayamikira munthu pamaso pake koma kenako n’kukanena zoipa kumbali, ndiye kuti ndife achinyengo. Mtumwi Paulo ankapewa chinyengo choterechi ndipo anapereka chitsanzo chabwino poyamikira anthu kuchokera mumtima. Mwachitsanzo, iye anayamikira Akhristu a ku Korinto chifukwa cha zinthu zabwino zimene ankachita. (1 Akor. 11:2) Koma pamene iwo anachita zinthu zolakwika, iye sanawayamikire koma anawalangiza mwachikondi komanso momveka bwino. — 1 Akor. 11:20-22.
MULUNGU WA SEPTEMBALA 8-14
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 30
“Kamundiva-e Uphawi Kapena Chuma”
w18.01 takuru 24-25 ndima 10-12
Kodi Ninafuneya Muomeluwanga Mbaani ira Nikalenga Osangalala?
10 N’zoona kuti tonsefe timafunikira ndalama. Zili choncho chifukwa zimatiteteza m’njira zina. (Nam. 7:12) Koma funso n’lakuti, Kodi n’zotheka munthu amene amangopeza zofunika pa moyo zokha kukhaladi wosangalala? Inde. (Werengani Namalaleya 5:12.) Aguri mwana wa Yake anapempha Mulungu kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma. Mungondipatsa chakudya chokwanira.” M’pomveka kuti sankafuna kukhala mphawi wadzaoneni. Iye anafotokoza kuti sankafuna zimenezi chifukwa zikhoza kumuchititsa kuti abe n’kunyozetsa Mulungu. Koma n’chifukwa chiyani sankafuna kukhala ndi chuma? Iye anapitiriza kuti: “Kuti ndisakhute kwambiri nʼkukukanani kuti: “Kodi Yehova ndi ndani?’” (Miya. 30:8, 9) Mwina inuyo mwaonapo anthu amene amadalira kwambiri chuma chawo m’malo modalira Mulungu.
11 N’zosatheka kuti anthu amene amakonda ndalama asangalatse Mulungu. Paja Yesu ananena kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Ndipo asananene zimenezi ananena kuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma unjikani chuma chanu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba. — Mat. 6:19, 20, 24.
12 Anthu ambiri amaona kuti akamakhala moyo wosalira zambiri amasangalala komanso amakhala ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova. M’bale wina dzina lake Jack, yemwe amakhala ku United States, anagulitsa nyumba ndiponso bizinezi yake n’cholinga choti azichita upainiya limodzi ndi mkazi wake. Iye anati: “Sizinali zophweka kuti tigulitse nyumba ndiponso malo athu okongola kwambiri. Koma kwa zaka zambiri ndinkaweruka kuntchito n’kubwera nditakhumudwa kwambiri chifukwa cha mavuto akuntchitoko. Mkazi wanga, yemwe anali mpainiya wokhazikika, nthawi zonse ankakhala wosangalala. Iye ankakonda kundiuza kuti, ‘Bwana wanga ndi wabwino kuposa mabwana onse.’ Popeza kuti panopa nanenso ndikuchita upainiya, tonse tikugwirira ntchito Yehova.”
w17.05 takuru 26 ndima 15-17
“Kodi Unondiomeluwana Kwaranya vi?”
15 Masiku ano anthu ambiri amangokhalira kuganizira zinthu monga zovala ndiponso zipangizo zamakono zomwe zangotuluka kumene. N’chifukwa chake Mkhristu aliyense ayenera kudzifufuza pa nkhaniyi. Akhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti zinthu za m’dzikoli ndi zofunika kwambiri? Kodi nthawi yambiri ndimakhala ndikufufuza ndiponso kuganizira zinthu monga mafoni kapena zovala kuposa nthawi imene ndimakhala ndikukonzekera misonkhano? Kodi ndimatanganidwa kwambiri ndi zinthu za tsiku ndi tsiku moti sindikhala ndi nthawi yambiri yoti ndizipemphera kapena kuwerenga Baibulo?’ Tikaona kuti tikuyamba kukonda zinthu za m’dzikoli kuposa Khristu, tingachite bwino kuganizira mawu a Yesu akuti: “Chenjerani ndi dyera lamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) N’chifukwa chiyani Yesu anapereka chenjezo limeneli?
16 Yesu ananena kuti “kapolo sangatumikire ambuye awiri.” Iye ananenanso kuti: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Zili choncho chifukwa “ambuye” onse sangafune kuti tizitumikiranso wina. Komanso Yesu ananena kuti tikamatumikira onse awiri ‘tidzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena tidzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo.’ (Mat. 6:24) Tonsefe ndife ochimwa choncho tiyenera kulimbana ndi “zilakolako za thupi lathu,” kuphatikizapo mtima wokonda chuma. — Aife. 2:3.
17 Anthu amene amakonda zinthu za m’dzikoli amavutika kuti azikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma. (Welengani 1 Akorinto 2:14.) Popeza kuti saganiza bwino, zimawavuta kuti asiyanitse choyenera ndi chosayenera. (Aheb. 5:11-14) N’chifukwa chake amangokhalira kufunafuna chuma ndipo sakhutira. (Nam. 5:10) Komabe tikhoza kupewa zimenezi tikamawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse. (1 Pe. 2:2) Yesu anatha kukana mayesero chifukwa choganizira Mawu a Mulungu. Nafenso tikamatsatira mfundo za m’Baibulo tikhoza kupewa mtima wokonda chuma. (Mat. 4:8-10) Tikamachita zimenezi, Yesu amaona kuti timamukonda kwambiri kuposa chuma.
w11 6/1 takuru 10 ndima 4
Kodi Munapange Avi Ira Mugulenga Vyongo Mogwilizana na Ndalama Dedo Munafwanya Nyo?
Muzisunga ndalama pang’onopang’ono musanagule kanthu. Ngakhale kuti zimaoneka ngati zachikale, ndi bwino kumasunga kaye ndalama musanagule chinthu. Imeneyi ndi njira ina yabwino kwambiri imene ingakuthandizeni kupewa kugwera m’mavuto azachuma. Kuchita zimenezi kumathandiza anthu ambiri kupewa kukhala ndi ngongole. Kumathandizanso kuti musamagule zinthu pa mtengo wokwera chifukwa nthawi zambiri mukagula chinthu pangongole, mumachigula modula. Baibulo limanena kuti nyerere “n’zanzeru” chifukwa “zimasonkhanitsa chakudya chawo m’chilimwe” kuti zidzachigwiritse ntchito m’tsogolo. — Miyambo 6:6-8; 30:24, 25.
Pitilizani Kala Alendo a Yehova Mpakana Walewale
18 Vifukeni ira: Kodi thawi detene ndinakeda ganizela vyandalama koma teto vyevyo ndinagule miyo? Kodi ndaboli-a ndalama ndinochedwa weli-a voganizela ira unoyo undiboli-ile ndalamoyo kanadifuna? Kodi kaana ndalama unondipangi-a ira ndivionenga ngati ofuneya koma lepelanga kami-a amo-i? Kodi ndinoona ira abali na arongola amo-iwa kanoomeluwa ndalama chifukwa yoi kokaana ndalamado? Kodi ndinoomweluwa waleda na athu olemela nopewanga athu osauwa?’ Nikaana mwayi ulukulu wokala alendo a Yehova, eno ira nipitilize kala afwae ninafuneya pewa omeluwana ndalama. Napanganga vyevi Yehova kanaza ani-iya. — Welengani Aheberi 13:5.
Makundo Okami-a
w09 4/15 takuru 17 ndima 11-13
Ilengedwe Inotonyi-eda Zelu da Yehova
11 Mbira ndi mtundu wina wa zolengedwa zazing’ono zimene zingatiphunzitse mfundo zofunika kwambiri. (Werengani Miyambo 30:26.) Nyamayi imaoneka ngati kalulu ndipo ili ndi makutu aafupi koma ozungulira, komanso miyendo yake ndi yaifupi. Nyama yaing’ono imeneyi imakhala m’matanthwe. Iyo ili ndi maso akuthwa kwambiri ndipo amaithandiza kuona msanga adani. Komanso m’matanthwe amene imakhala muli maenje ndi mphako zimene zimaiteteza kwa adani. Mwachibadwa, mbira zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, ndipo zimenezi zimapereka chitetezo komanso zimathandiza nyamazi kukhala zofunda m’nyengo yozizira.
12 Kodi tikuphunzira chiyani kwa mbira? Choyamba, onani kuti nyamayi imasamala kuti isagwidwe. Imagwiritsa ntchito maso ake akuthwa kuonera msanga adani ngakhale ali kutali, ndipo imakhala pafupi ndi dzenje kapena mphako, zimene zingathandize kupulumutsa moyo wake. Ifenso tiyenera kukhala ndi maso auzimu akuthwa kuti tizitha kuona zinthu zobisika zangozi zimene zili m’dziko la Satanali. Mtumwi Petulo analangiza Akhristu kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru chifukwa mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.” (1 Pe. 5:8) Yesu ali padziko lapansi, anakhalabe maso, inde watcheru, pamene Satana ankayesetsa kufuna kuswa umphumphu Wake. (Mat. 4:1-11) Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino kwa otsatira ake.
13 Njira imodzi imene tingakhalire maso ndiyo kuyesetsa kugwiritsa ntchito chitetezo chauzimu chimene Yehova wapereka kwa ife. Sitiyenera kunyalanyaza kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kupezeka pamisonkhano yachikhristu. (Luka 4:4; Aheb. 10:24, 25) Ndiponso mofanana ndi mbira zimene zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, tifunikira kukhala pafupi kwambiri ndi Akhristu anzathu kuti ‘tizilimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Tikamagwiritsa ntchito chitetezo chimene Yehova wapereka, timasonyeza kuti tikugwirizana ndi zimene wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova ndi thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso amene amandipulumutsa. Mulungu wanga ndi thanthwe langa limene ndimathawirako, Iye ndi chishango changa, nyanga yanga ya chipulumutso komanso malo anga othawirako otetezeka.”— Sal. 18:2.
FUNJI-A MWALUSO MU UTUMIKI
Fotokoza Vyevyo Munaroromela Nyo
ijwbq khani 102
Kodi Vocha Juga ti Chimo?
Yosomeda ya m’Baibulo
Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane zokhudza juga, mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuzindikira kuti Mulungu amaona kuti khalidweli ndi tchimo.— Aifeso 5:17.
M’Baibulo, kutchova juga kumatchulidwa mwachindunji kamodzi kokha pa nkhani yonena za asilikali a Roma omwe anachita maere, kapena kuti “anatchova juga” pa chovala cha Yesu. — Mateyu 27:35; Yohani 19:23, 24; Contemporary English Version; Good News Translation.
● Anthu amatchova juga chifukwa cha dyera ndipo Mulungu amadana ndi khalidwe limeneli. (1 Akorinto 6:9, 10; Aifeso 5:3, 5) Kuti munthu wotchova juga awine, pamafunika kuti anzake aluze, koma Baibulo limaletsa kusirira zinthu za anthu ena mwansanje.— Ekisodo 20:17; Aroma 7:7; 13:9, 10.
● Kutchova juga, ngakhale pang’ono pokha, kungachititse munthu kuti ayambe kukonda kwambiri ndalama. — 1 Timoteyu 6:9, 10.
Nthawi zambiri anthu otchova juga amadalira matsenga kapena mwayi. Komabe, Mulungu amaona kuti kukhulupirira zimenezi ndi kulambira mafano, komwe sikugwirizana ndi kulambira kumene iye amavomereza. — Yesaya 65:11.
● M’malo molimbikitsa khalidwe lomapeza zinthu zomwe sitinazigwirire ntchito, Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama. (Namalaleya 2:24; Aifeso 4:28) Anthu omwe amatsatira malangizowa ‘amadya chakudya chimene achigwirira ntchito.’ — 2 Atesalonika 3:10, 12.
● Kutchova juga kumalimbikitsa khalidwe la mpikisano, lomwe limaletsedwa m’Baibulo.— Agalatiya 5:26
MULUNGU WA SEPTEMBALA 15-21
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 31
Vyevyo Ninafunjede Iyo va Malangizo Achikondi a Zimai
w11 2/1 takuru 19 ndima 7-8
Mufunji-enga A-iminyu Ira Kakaena Makalelo Apama
Aphunzitseni zinthu zonse zokhudza kugonana. Ndi bwinodi kuti makolo azichenjeza ana awo nkhani zokhudza kugonana. (1 Akorinto 6:18; Yakobo 1:14, 15) Komabe Baibulo limanena kuti kugonana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, osati msampha wa Satana. (Miyambo 5:18, 19; Nyimbo ya Solomo 1:2) Choncho kuuza ana anu achinyamata zoipa zokhazokha zokhudza kugonana kungachititse kuti aziganiza molakwa za nkhaniyi komanso mosagwirizana ndi Malemba. Mtsikana wina wa ku France dzina lake Corrina ananena kuti: “Makolo anga akafuna kunena nkhani zokhudza kugonana, ankangonena za kuipa kwa chiwerewere ndipo zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti kugonana ndi koipa nthawi zonse.”
Onetsetsani kuti mwauza ana anu mbali zonse zokhudza kugonana. Mayi wina wa ku Mexico, dzina lake Nadia, ananena kuti: “Pokambirana ndi ana anga nkhani zokhudza kugonana, nthawi zonse ndimawauza kuti kugonana ndi kwabwino chifukwa ndi mmene tinalengedwera. Yehova Mulungu anakonza zoti anthu azigonana ndiponso azisangalala. Koma ndimawauzanso kuti anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kugonana. Ndimawauza kuti munthu angasangalale ngati akutsatira dongosolo la Yehova pa nkhaniyi kapena akhoza kupeza mavuto ngati sanatsatire dongosolo limeneli.
ijwhf khani 4 ndima 11-13
Mwemo Munaakami-ele Nyo A-iminyu va Khani Yokuza Walwa
Muziyamba ndi inuyo kukambirana ndi mwana wanu zokhudza mowa. Bambo wina wa ku Britain dzina lake Mark ananena kuti: “Mowa umasokoneza kwambiri ana. Tsiku lina ndinafunsa mwana wanga wamwamuna wa zaka 8 kuti afotokozepo maganizo ake ngati kumwa mowa n’kwabwino kapena ayi. Ndinkalankhula naye momasuka ngati kuti tikungocheza ndipo zimenezi zinathandiza kuti nayenso amasuke kunena maganizo ake pa nkhani ya mowa.”
Ngati nthawi zambiri mumakonda kunena za mavuto amene amakhalapo chifukwa cha mowa, zingathandize ana anu kudziwa kuopsa kwa mowa. Choncho potengera msinkhu wa mwana wanu, mukamakambirana nkhani zofunika pa moyo monga kupewa ngozi pamsewu komanso nkhani zokhudza kugonana, mungakambirane nayenso zokhudza kuopsa kwa mowa.
Muzikhala chitsanzo chabwino. Ana ali ngati thonje. Thonje likaviikidwa m’madzi, kaya akuda kapena oyera, limayamwa komanso kutengera mtundu wa madziwo. Ochita kafukufuku anapeza kuti nawonso ana amatengera kwambiri zimene makolo awo amakonda kuchita. Izi zikutanthauza kuti ngati inuyo mumaona kuti kumwa mowa ndi njira yokhayo yabwino yochepetsera nkhawa kapena mavuto anu, mwana wanunso amatengera zomwezo. Choncho muzikhala chitsanzo chabwino. Ndipo ngati mumamwa, muziyesetsa kumwa moyenera.
g17.6 takuru 9 ndima 5
Kodi Munafunji-e Avi A-iminyu Ira Kakale Oviyevi-a?
Muziwalimbikitsa kukhala opatsa. Muzithandiza mwana wanu kudziwa kuti “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.” (Vyoira 20:35) Mungachite zimenezi polemba mayina a anthu amene mungawathandize komanso mmene mungawathandizire monga kuwagulira zinthu, kuwapatsa ndalama ya thiransipoti kapena kuwakonzera zinthu zomwe zawonongeka. Kenako muzipita ndi mwana wanuyo pokathandiza anthuwo. Mwana wanu adzachita chidwi akamaona kuti mukusangalala chifukwa chothandiza ena. Adzaphunziranso kukhala wodzichepetsa poona zimene mumachita. — Lemba lothandiza: Luka 6:38.
Makundo Okami-a
Akristu Achisikana, Kodi Munapange Avi Ira Mukale Olimba Mwauzimu?
12 Mufunjedenga onga pama na athu. Akristu kanafuneya onganga pama na athu. Vakhani inela, Yakobo unoyo ali ofunjeda wa Yesu, oopeleka malangizo oyi: “Muthu uliwetene akalenga okozeya vuruwana, aganizelenga kaye a-anaonge.” (Yak. 1:19) Mwavuruwananga mosamala vevo amo-iwa kanaongaathu, munotonyi-eda ira munoganizela athu amo-iwa koma teto munowavwela chisoni. (1 Pe. 3:8) Akala munakaikela vyoi muvwechecha vyevyo muthu mʼmo-iwa unaonga liye kapena mwemo unavwela liye, munokoza panga pama fuka vyofuka vyofwanelela. Era eno muganizelenga kae mwa-anaonge. (Miya. 15:28, mawu amphedi.) Muvifukenga ira: ‘Kodi vyevyo ndinafuna miyo onga pivyoona koma teto vyolimbikisa? Kodi vinotonyi-eda ulemu koma teto oma murima?’ Mufunjedenga wa arongola olimba mwauzimu anayo kanaongecha pama na athu. (Welengani Miyambo 31:26.) Muonenga mwemo kanaongelaathu. Mwafunjeda onga pama na athu, pavevo teto munagwilizanenga nyo vinjinji na athu.
MULUNGU WA SEPTEMBALA 22-28
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | NAMALALEYA 1-2
Pitilizani Funji-a M’bado Wo-arela
w17.01 takuru 27-28 ndima 3-4
“Muwakami-enga Abali Aizombwe Ira Kafwanelele kala Vaudindo”
3 Ambirife timakonda kutumikira Yehova komanso timakonda udindo umene tili nawo m’gululi. Koma vuto ndi lakuti munthu akamakalamba sakwanitsa kuchita zambiri ngati poyamba. (Nam. 1:4) Masiku ano, zimenezi zimabweretsa mavuto ena kwa Akhristu. Panopa, ntchito m’gulu la Yehova yakula kwambiri ndipo ikufuna zambiri. Ntchito zatsopano zachititsa kuti papezeke njira zatsopano zogwirira ntchitozo ndipo njira zambiri ndi zamakono. Ndiyeno achikulire ena amavutika kuzolowera njira zatsopanozo. (Luka 5:39) Ngakhale zitakhala kuti achikulirewo sakuvutika, achinyamata amakhala ndi mphamvu zambiri kuposa achikulire. (Miya. 20:29) Choncho ndi bwino kuti achikulire aziphunzitsa achinyamata kuti akhale ndi maudindo akuluakulu. — Welengani Salimo 71:18.
4 Akhristu ena amene ali ndi maudindo zimawavuta kuphunzitsa achinyamata. Ena amaopa kuti alandidwa udindo umene amaukonda. Pomwe ena amakayikira achinyamatawo ndipo amaganiza kuti sangachite bwino zinthu. Ndiye pali enanso amene amaganiza kuti alibe nthawi yophunzitsa munthu wina. Koma nawonso abale achinyamata ayenera kukhala odekha akaona kuti sakupatsidwa udindo winawake.
Makundo Okami-a
it “Namalaleya” ndima 1
Namalaleya
Mawu a Chiheberi akuti Qo·heʹleth (omwe amatanthauza “wosonkhanitsa kapena wobweretsa pamodzi”) amafotokoza bwino udindo wa mfumu ya Aisiraeli mu ulamuliro wotsogoleredwa ndi Mulungu. (Nam 1:1, 12) Unali udindo wa wolamulira kuti azibweretsa anthu a Mulungu pamodzi kuti azilambira Mfumu yawo yeniyeni yomwe ndi Mulungu. (1Ma 8:1-5, 41-43, 66) Pa chifukwa chimenechi, anthuwo ankatha kudziwa kuti mfumuyo ndi yabwino kapena yoipa ngati ikuwatsogolera polambira Yehova kapena ayi. (2Ma 16:1-4; 18:1-6) Wosonkhanitsa, yemwe pa nthawiyo anali Solomo anali atagwira kale ntchito yaikulu yosonkhanitsa ku kachisi Aisiraeli komanso anzawo, ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikolo. M’bukuli, ankafuna kuthandiza anthu a Mulungu kuti asamachite zinthu zoipa komanso zosathandiza zam’dzikoli , m’malomwake azichita zinthu zomwe zingasangalatse Mulungu amene anadzipereka kwa iye.
MULUNGU WA SEPTEMBALA 29– OKOTOBALA 5
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | NAMALALEYA 3-4
Mulimbi-enga Go-inyu Omangiwa na Migo-i Miralu
ijwhf khani 10 ndima 2-8
Kodi Munapange Avi Ira Mafoni Katiusokonezengani?
● Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mwanzeru kukhoza kulimbitsa banja lanu. Mwachitsanzo, amuna ena ndi akazi awo, amagwiritsira ntchito zipangizozi polumikizana pa nthawi imene sali limodzi.
“Meseji yachidule yongonena kuti ‘ndimakukonda’ kapena ‘ndakusowa’ ingatanthauze zambiri ndipo imakupangitsa kumva bwino.” — Jonathan.
● Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mopanda nzeru kukhoza kusokoneza banja lanu. Mwachitsanzo, anthu ena amangokhalira kucheza pa foni ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamakhale ndi nthawi yokwanira yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wawo.
“Sindikukayikira kuti pali nthawi zina pamene mwamuna wanga ankafuna atacheza nane, koma ankalephera chifukwa choti ndinkatanganidwa ndi foni.” — Julissa.
● Anthu ena amaona kuti akhoza kumakambirana zinthu zofunika ndi mwamuna kapena mkazi wawo kwinakunso akugwiritsa ntchito chipangizo chawo chamakono. Koma Sherry Turkle, yemwe ndi katswiri wa zachikhalidwe anatsutsa mfundo imeneyi. Iye ananena kuti “n’zosatheka kumachita zinthu ziwiri pa nthawi imodzi, ndipo tikamachita zinthu zingapo pa nthawi imodzi m’pamene zambiri zimawonongeka.”
“Ndimasangalala kwambiri kucheza ndi mwamuna wanga akakhala kuti sakuchita zinthu zina. Koma ndikamacheza naye, iyeyo n’kumatanganidwa ndi foni, zimakhala ngati foniyo ndi yofunika kwambiri kuposa ineyo.” — Sarah.
Mfundo yofunika kwambiri: Mmene mumagwiritsira ntchito zipangizo zamakono zingachititse kuti banja lanu likhale lolimba kapena lisokonezeke.
w23.05 takuru 23-24 ndima 12-14
Kamutimi-e “Lumi la Mulo wa Ya”
12 Kodi athu otelana kanamusazi-ede avi Akula na Purisikila? Kaganizelani vyongo vinjinji vyevyo nyo monga mulombwana kapena mu-iyana, munafuneela nyo panga. Kodi pivyowandeya ira muirelenga limo-i vyongo vyevi monga banja, m’malo moi uliwetene airelenga vaekave? Mwaisazo, Akula na Purisikila kalaleela limo-i. Kodi nyo teto thawi dinjinji munopangecha vyoi mulaleelenga limo-i? Akula na Purisikila ka-indela teto chito limo-i. Mwina nyo na mamuninyu kapena mu-iyaninyu kamuna-inda chito yofwanafwana, koma kodi munokoza indela limo-i chito davande? (Nam. 4:9) Mwakami-ananga chito imo-iwene, munogwilizana vinjinji koma teto munofwanya mpata owaleda. M’bali Robert na mu-iyanae Linda kookala m’banja chaka dokwaranya 50. M’bali Robert aongile ira: “Onga vyoona, kaninafwanya thawi injinji yoirela limo-i vyongo vyosangalasa. Koma nda-uwanga mbale, iyananga dipukutanga kapena ndalimanga vande, liye za ndikami-a, ndinosangalalecha vinjinji. Irela limo-i vyongo unonikami-a ira nikalenga ogwilizana teto chikondi-u inopitiliza ulukula.”
13 Komave, muumbuwelenga ira keda kala limo-i, kunatapulela ira thawi detene munongoira vyongo mogwilizana. Muzimai m’mo-i wavabanja wawu Brazil aongile ira: “Malambwano, vikala vyongo vinjinji vyosokoneza, moi ndiona ira ninokoza morela musampha woganiza ira ninairelecha vyongo limo-i chifukwa yoi ninakala nyumba imo-i. Ndifunjeda ira wonjedela vokala limo-i, ninafuneela panganga chidwi na fwi-uyo.” Konani vyevyo Bruno na iyanae Tays kanairaathu ira uliwetene airenga chidwi na fwae. Liye aongile ira: “Vathawi-u yowaleda, nino-iyecha mafoni-u vandendai iyo kedanga aleda baasi.”
14 Koma bwanji akala nyo na mamuninyu kapena iyaninyu kamunasangalala irela limo-i vyongo? Mwina munoomeluwa vyongo vyo-iyana kapena teto munakalelecha ambana, ndiye kodi munaire avi? Kaganizelani vya mulo, unoyo nauromon’le iyo umaambeelelo ule. Mulola kunakedecha fiyeda kara mwakopolo. Unafuneela utetedela vang’onovang’ono, era eno ku-elangavo khuni dilukulu. Mofwanafwana na vyevi, bwanji muwambeele nofwanya thawi yoyeva dambo lililetene yoirela vyongo limo-i? Muonechechenga ira muirenga vyongo vyevyo etene munasangalalana nyo, m’malo moira vyevyo vinapangi-e ira muwambeele kangana. (Yak. 3:18) Ambeela mwavang’onovang’ono unoukami-ani ira muulukuli-e chikondinyu.
Kamutimi-e “Lumi la Mulo wa Ya”
3 Ira etene, mulombwana na mu-iyana katitimi-e “lumi la mulo wa Ya,” kanafuneela esaesa limbi-a usamwaliwa na Yehova. Kodi vyevi vinakami-a avi banja liwa? Athu otelana kaonanga ira usamwaliwa na Babiwa waudimu kofuneya vinjinji kanokala okozeya arela malangizwae, vyevi vinowakami-a pewa koma teto limbana na mavuto anayo kanapangi-e ira chikondiwa iyeve. (Welengani Namalaleya 4:12.) Athu anayo kali va usamwali na Yehova kanoesaesa musazi-eda teto kanokaana makalelo monga oma murima, leza murima koma teto khululuka. (Aife. 4:32–5:1) Athu otelana anayo kanatonyi-eda makalelo anala kavinaarucha ira kaomeliwanenga vinjinji. Murongola m’mo-iwa zina lae Lena, unoyo ukan’le m’banja wa chaka dokwaranya 25, aongile ira: “Vinakala vyo-orucha muomeluwana koma teto mulemekeza muthu unoyo unamuomeluwana Yehova.”
Makundo Okami-a
w19.07 takuru 11 ndima 14
Nitumikelenga Yehova Ngakale Boma Langaniruni-ile
14 Tizisamala ndi zimene timauza ena. Pamene ntchito yathu yaletsedwa, tiyenera kuzindikira nthawi yoti ‘tikhale chete.’ (Nam. 3:7) Sitiyenera kuulula zinthu zachinsinsi monga mayina a abale ndi alongo athu, malo amene timasonkhana, mmene timalalikirira ndiponso njira zolandirira chakudya chauzimu. Sitiyenera kuuza akuluakulu a boma zinthu ngati zimenezi kapena kuuza anzathu komanso achibale athu, kaya a m’dziko lathu kapena m’mayiko ena. Zili choncho chifukwa tikawauza tikhoza kuika moyo wa abale athu pa ngozi. — Werengani Salimo 39:1.
MULUNGU WA OKOTOBALA 6-12
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | NAMALALEYA 5-6
Kodi Ninatonyi-ede Avi Ira Ninomulemekeza Vinjinji Mulungwi-u Mulukulu?
w08 8/15 takuru 15-16 ndima 17-18
Mulemekezeni Yehova Votonyi-edana Ulemu
17 Tifunikira kusonyeza ulemu wapadera polambira Yehova. Lemba la Namalaleya 5:1 limati: “Uzisamala mmene ukuyendera ukapita kunyumba ya Mulungu woona.” Mose ndi Yoswa analamulidwa kuvula nsapato zawo pamalo opatulika. (Ekis. 3:5; Yos. 5:15) Iwo amafunika kuchita zimenezi posonyeza ulemu. Ansembe a Chiisiraeli analamulidwa kuvala zovala za miyendo kuti ‘abise maliseche.’ (Ekis. 28:42, 43) Zimenezi zinathandiza kuti azivala modzilemekeza akamatumikira pa guwa la nsembe. Aliyense m’banja la wansembe amafunikira kutsatira malamulo a Mulungu okhudza kudzilemekeza.
18 Motero, monga olambira a Yehova tifunikira kusonyeza ulemu m’mbali zonse za moyo wathu. Kuti ena azitipatsa ulemu ifenso tiyenera kuwapatsa ulemu. Tisasonyeze ulemu mwachiphamaso kapena mongodzionetsera chabe. Koma uzikhala ulemu wochokera mu mtima chifukwa Mulungu amaona mumtima. (1 Sam. 16:7; Miya. 21:2) Tiyenera kukhala aulemu nthawi zonse, m’zochita zathu ndi pochita zinthu ndi ena. Ndipo tiyeneranso kumadzilemekeza. Ndithudi, tizisonyeza ulemu polankhula ndi pochita zinthu zina. Pankhani ya khalidwe lathu, kavalidwe ndi kudzikongoletsa, tifunikira kutsatira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti anthu asapezere chifukwa utumiki wathu. Koma tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu” (2 Akor. 6:3, 4) Mwa njira imeneyi ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu, m’zinthu zonse.’— Tito 2:10.
w09 11/15 takuru 11 ndima 21
Funjeda Baibulo Unokoza Ukami-ani Ira Mapempelwinyu Kakalenga Atantauzo
21 Yesu anapemphera mwaulemu ndiponso ndi chikhulupiriro chonse. Mwachitsanzo asanaukitse Lazaro, “Yesu anakweza maso ake kumwamba ndi kunena kuti: ‘Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse.’” (Yoh. 11:41, 42) Kodi mapemphero anu amasonyeza ulemu ndi chikhulupiriro chotero? Mukawerenga bwinobwino pemphero la Yesu lachitsanzo, mudzaona kuti mbali zazikulu zimene anatchula ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova, kubwera kwa Ufumu wake ndi kuchitika kwa chifuniro chake. (Mat. 6:9, 10) Ndiyeno ganizirani za mapemphero anu. Kodi amasonyeza kuti inuyo mumafunadi Ufumu wa Yehova, kuchita chifuniro chake ndiponso mumafuna kuona dzina lake loyera litayeretsedwa? Mapemphero anu ayenera kusonyeza zimenezi.
w17.04 takuru 6 ndima 12
“Ukwakwaneli-edenga Vyevyo Ulonjezile we”
12 Koma kubatizidwa ndi chiyambi chabe. Munthu akabatizidwa ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene analonjeza kwa Mulungu. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji kuyambira pamene ndinabatizidwa? Kodi ndikutumikirabe Yehova ndi mtima wonse? (Akol. 3:23) Kodi ndimapemphera, kuwerenga Mawu a Mulungu, kusonkhana komanso kulalikira nthawi zonse? Kapena kodi ndafooka pang’ono pa zinthu zimenezi? Paja mtumwi Petulo anati tiyenera “kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, pa makhalidwe anu abwino muwonjezerepo kudziwa zinthu, pa kudziwa zinthu kudziletsa, pa kudziletsa kupirira, pa kupirira kudzipereka kwa Mulungu.” (Werengani 2 Petulo 1:5-8.) Makhalidwe amenewa angatithandize kuti tizitumikirabe Mulungu mwakhama. — Welengani 2 Petulo 1:5-8.
Makundo Okami-a
w20.09 takuru 31 ndima 3-5
Vyofuka Vyokumela wa Owelenga
Lemba la Namalaleya 5:8 limanena za olamulira amene amapondereza osauka komanso kuwachitira zopanda chilungamo. Wolamulira ayenera kukumbukira kuti pali munthu winanso amene amamuyang’anira, yemwe ndi waudindo waukulu kuposa iyeyo. Ndiponso pamwamba pa munthu waudindo waukuluyu, pangakhale enanso a maudindo aakulu kwambiri. Chomvetsa chisoni n’chakuti m’maboma a anthu, olamulira onsewa amakhala achinyengo ndipo anthu amavutika ndi katangale komanso zinthu zopanda chilungamo.
Ngakhale zili choncho, sitiyenera kutaya mtima chifukwa tikudziwa kuti Yehova, amaona zimene anthu a maudindo aakulu m’maboma a anthu amachita. Choncho tingapemphe Yehova kuti atithandize komanso tingathe kumutulira nkhawa zathu. (Sal. 55:22; Afil. 4:6, 7) Timadziwa kuti “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” — 2 Limbili 16:9.
Choncho lemba la Namalaleya 5:8 limatikumbutsa zomwe zimachitikadi m’maboma a anthu, kuti nthawi zonse munthu waudindo waukulu, amakhalanso ndi wina waudindo waukulu kuposa iyeyo. Chofunika kwambiri n’chakuti vesili lingatithandize kuganizira mfundo yakuti Yehova ndi amene ali wamkulu kwambiri, iye ndi Wolamulira Wamkulu. Panopa Yehova akulamulira kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Yehova yemwe ndi Wamphamvuyonse amaona zinthu zonse komanso munthu aliyense ndipo iye komanso Mwana wake ndi achilungamo.
MULUNGU WA OKOTOBALA 13-19
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | NAMALALEYA 7-8
“Muwamiyali-enga Athu Anayo Kakhweliwe”
w22.01 takuru 16 ndima 9
“Kodi Ninafunjeda N’ni va Misodi da Yesu?”
9 Mungathe kuthandiza amene aferedwa. Kuwonjezera pa kulira ndi Marita ndi Mariya, Yesu ankawamvetsera komanso kuwatonthoza. Ifenso tingachite zimenezi kwa amene ali ndi chisoni chifukwa choferedwa. Dan, yemwe amakhala ku Australia, ananena kuti: “Mkazi wanga atamwalira, ndinkafunika kuthandizidwa. Mabanja angapo ankakhala nane nthawi zonse ndipo ankandimvetsera ndikamalankhula. Iwo sankandiletsa kusonyeza chisoni changa ndipo sankakhumudwa ndikamalira. Ankandithandizanso m’njira zina monga kunditsukira galimoto, kukandigulira zinthu komanso kundiphikira ngati ndikulephera kuchita zinthu zimenezi ndekha. Ankapempheranso nane pafupipafupi. Iwo anasonyeza kuti anali anzanga enieni ndiponso m’bale amene ‘anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” — Miya. 17:17.
w19.06 takuru 23 ndima 15
Nikami-enga Athu Anayo kan’na Nkhawa
15 M’bale wina dzina lake William, yemwe mkazi wake anamwalira zaka zingapo zapitazo, ananena kuti: “Ndimayamikira kwambiri anthu akafotokoza zinthu zabwino zokhudza mkazi wanga. Zimanditsimikizira kuti anthu ankamukonda komanso kumulemekeza ndipo zimandilimbikitsa kwambiri. Zili choncho chifukwa mkazi wanga anali wamtengo wapatali kwa ine ndipo ndinkamukonda kwambiri.” Mlongo wina wamasiye dzina lake Bianca anati: “Ndimalimbikitsidwa anthu ena akapemphera nane limodzi komanso kundiwerengera malemba. Zimandithandiza anthuwo akanena zinthu zabwino zokhudza mwamuna wanga kapena akamamvetsera ndikamawauza za iyeyo.”
w17.07 takuru 16 ndima16
“Muulenga na Athu Anayo Kanaula”
16 Kupemphera ndi Akhristu anzathu amene aferedwa kapena kuwapempherera kumathandizanso kwambiri. Pa nthawi yovuta ngati imeneyi munthu akhoza kuvutika kuti anene zomveka m’pemphero. Koma ngakhale atapemphera uku akunjenjemera kapena kulira, akhoza kuthandiza kwambiri munthu woferedwayo. Mlongo Dalene, amene tamutchula uja, ananena kuti: “Nthawi zina alongo akabwera kudzandilimbikitsa ndinkawapempha kuti apemphere. Nthawi zambiri akamayamba pempherolo ankavutika koma kenako mawu awo ankayamba kumveka bwinobwino ndipo mapemphero awo ankakhala olimbikitsa kwambiri. Ndimalimbikitsidwa ndikaganizira chikhulupiriro chawo, chikondi chawo komanso mtima wawo woganizira ena.”
w17.07 takuru 16 ndima 17-19
“Muulenga na Athu Anayo Kanaula”
17 Anthu amamva chisoni mosiyanasiyana. Choncho ndi bwino kupitiriza kulimbikitsa munthu ngakhale achibale kapena anzake amene ankamulimbikitsa pa nthawi ya maliro atachoka. Paja “bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miya. 17:17) Abale ndi alongo ayenera kulimbikitsa munthu mpaka nthawi imene chisoni chake chachepa. — Welengani 1 Atesalonika 3:7.
18 Tizikumbukira kuti anthu oferedwa akhoza kumvanso chisoni pa nthawi inayake pa chaka, akamva nyimbo inayake, kuona zithunzi, kuchita zinthu zina komanso akamva fungo kapena phokoso linalake. Munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira angavutike kwambiri akayambiranso kuchita zinthu zina payekha monga kupita kumsonkhano kapena ku Chikumbutso. M’bale wina anati: “Ndinkaona kuti ndidzavutika kwambiri likadzafika tsiku limene tinakwatirana ndipo zinalidi zovuta. Koma abale ndi alongo ena anakonza zoti ndikacheze ndi anzanga apamtima pa tsikulo n’cholinga choti ndisakhale ndekha.”
19 Koma tizikumbukiranso kuti anthu amene aferedwa amafunikira kuwalimbikitsa nthawi zonse, osati pa nthawi zapadera zokha. Junia ananena kuti: “Anthu akacheza nawe ndiponso kukuthandiza, ngakhale pamene palibe zifukwa zapadera, umalimbikitsidwa kwambiri.” N’zoona kuti sitingathetseretu chisoni cha munthu amene waferedwa koma tikhoza kumulimbikitsa m’njira zosiyanasiyana. (1 Yoh. 3:18) Gaby anati: “Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha akulu achikondi amene ankandithandiza kwambiri mwamuna wanga atamwalira. Ndinkamva ngati Yehova wandikumbatira mwachikondi.”
Makundo Okami-a
“Mweranga Eno, Etene Kanoza Kaiziwe Ira Muli Ofunjedanga”
18 Thawi dimo-i ninokoza ona ira pivyofuneya ira nitapanye na Mkiristu fwi-u onoyo unichimwele. Koma yowambeela ninoira pama vifuka vyofuka n’nga vi: ‘Kodi ndinoiziwa makundo etene okuza khanila?’ (Miya. 18:13) ‘Kodi mwina liye kandichimwele mwadala?’ (Nam. 7:20) ‘Kodi miyo teto ndoowambeela lakwi-avo mwandila enela?’ (Nam. 7:21, 22) ‘Akala ndinatapanye na liye, kodi ndinoiri-a ira khanila iulukule vinjinji m’malo moi imale?’ (Welengani Miyambo 26:20.) Vanduli voganizela vyofuka vyevi, ninokoza ona ira chifukwa yomuwomeluwana bali-uyo nikede nyalanyaza khaniyo.
FUNJI-A MWALUSO MU UTUMIKI
Fotokoza Vyevyo Munaroromela Nyo
ijwfq khani 50
Kodi chin’ni Inaireya Vamalilo a Mboni da Yehova?
Malo: Banja loferedwa ndi limene limasankha malo ochitira mwambo wa maliro. Ena angasankhe ku Nyumba ya Ufumu, kunyumba kwawo, malo otenthera mitembo kapena kumanda.
Mwambo wa maliro: Pamwambowu pamakambidwa nkhani yofotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza imfa komanso zoti akufa adzauka. (Yohani 11:25; Aroma 5:12; 2 Petulo 3:13) Wokamba nkhaniyi angafotokozenso makhalidwe abwino amene munthu womwalirayo anali nawo komanso zimene anthu ena angaphunzirepo. — 2 Samuweli 1:17-27.
Pamwambowu pangaimbidwenso nyimbo yochokera M’malemba. (Akolosi 3:16) Mwambowu umatha ndi pemphero lotonthoza. — Afilipi 4:6, 7.
Malipiro: Sitimauza anamfedwa kuti apereke ndalama zolipirira wokamba nkhani ya maliro. Komanso mofanana ndi mmene timachitira pamisonkhano yathu, sitiyendetsa mbale ya zopereka pamwambo wamaliro. — Mateyu 10:8.
Anthu oyenera kupezekapo: Mofanana ndi mmene zimakhalira ndi misonkhano yathu, anthu onse ngakhale omwe si a Mboni ndi olandiridwa pamwambo wa maliro womwe umachitikira ku Nyumba ya Ufumu.
MULUNGU WA OKOTOBALA 20-26
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | NAMALALEYA 9-10
Muonenga Mavuto Anayo Munagumanananyo Mofwanelela
w13 8/15 takuru 14 ndima 20-21
‘Kamumulunduwele Yehova’
20 Dziwani zimene zayambitsa mavuto anu. Kudziwa zimenezi n’kofunika chifukwa chakuti nthawi zina timadzibweretsera tokha mavuto. Ngati izi zitachitika, ndi bwino kungovomereza. (Agal. 6:7) Si bwino kuimba Mulungu mlandu pa mavuto athu. N’chifukwa chiyani si nzeru kuimba Mulungu mlandu? Tiyerekeze kuti munthu wina akuyendetsa galimoto yothamanga kwambiri. Ndiye atafika pakona, sakuchepetsa liwiro ndipo akuchita ngozi. Kodi munthuyo angaimbe mlandu kampani imene inakonza galimotoyo? Ayi. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Potilenga, iye anatipatsa ufulu wosankha. Komanso watipatsa malangizo othandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Choncho, palibe chifukwa choimbira mlandu Mlengi wathu ngati ifeyo talakwitsa zinazake n’kukumana ndi mavuto?
21 Sikuti mavuto onse amabwera chifukwa choti ifeyo talakwitsa zinazake. Mavuto ena amangobwera chifukwa cha “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka.” (Nam. 9:11) Tisamaiwalenso kuti mavuto anayamba chifukwa cha Satana Mdyerekezi. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:9) Mdani wathu ndi Satanayo osati Yehova. — 1 Pe. 5:8.
w19.09 takuru 5 ndima 10
Yehova Unoona Ira Atumikae Oviyevi-a Mbantengo Wavadimu
10 Kudzichepetsa kumathandizanso kuti zinthu zisamatisowetse mtendere. Kunena zoona, anthufe timakumana ndi zinthu zina zimene zimaoneka kuti si zachilungamo. Mwachitsanzo, Solomo yemwe anali mfumu yanzeru ananena kuti: “Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi, koma akalonga akuyenda pansi ngati antchito.” (Nam. 10:7) Nthawi zina anthu aluso kwambiri sayamikiridwa pomwe amene ali ndi luso lochepa ndi amene amalemekezedwa. Koma Solomo ananena kuti ndi nzeru kungovomereza mmene zinthu zilili m’malo molimbana nazo. (Nam. 6:9) Tikakhala odzichepetsa, sitingavutike kuvomereza mmene zinthu zilili m’malo mokakamira kuti zisinthe.
w11 10/15 takuru 8 ndima 1-2
Kodi Vyevyo Munapangecha Nyo va Thawi Yosangalasa Vinakalecha Vyopinduli-a?
M’BAIBULO muli mawu ambiri osonyeza kuti Yehova samangofuna kuti tikhale ndi moyo, koma kuti tizisangalala nawo. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 104:14, 15 limanena kuti Yehova amachititsa “kuti chakudya chituluke m’nthaka, komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu. Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta, komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.” Yehova ndi amene amatipatsa chakudya chimene chimatithandiza kuti tizikhala ndi moyo. Amameretsa mbewu kuti tipeze chakudya, mafuta ndi vinyo. Ngakhale kuti vinyo sali m’gulu la zinthu zofunika kwambiri pa moyo, ‘amachititsa mtima kusangalala.’ (Nam. 9:7; 10:19) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala ndiponso kuti mitima yathu izikhala yodzaza ndi “chimwemwe.” — Vyo. 14:16, 17.
2 Choncho tisamaone ngati talakwitsa ngati nthawi zina timakonza nthawi yosangalala. Mwina timakonza zokaona “mbalame zam’mlengalenga” ndi “maluwa akutchire,” komanso kuchita zinthu zina zimene zimatitsitsimula. (Mat. 6:26, 28; Sal. 8:3, 4) Kukhala ndi moyo wosangalala “ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Nam. 3:12, 13) Kudziwa kuti nthawi yosangalala ndi mphatso, kungatithandize kuti tiziigwiritsa ntchito m’njira yosangalatsa amene anaipereka.
Makundo Okami-a
it “Miseche, Ongela amo-i vyotakala” ndima 4 na 8
Miseche, Ongela amo-i vyotakala
Miseche ikhoza kuchititsa kuti anthu ayambe kunenera ena zoipa ndipo zimenezi zingawononge kwambiri munthu wonenera ena zoipayo. Mawu anzeru amene amapezeka pa lemba la Namalaleya 10:12-14 amatsimikizira kuti zimenezi ndi zoona. Mawuwa amati: “Milomo ya munthu wopusa imamubweretsera mavuto. Mawu oyamba otuluka mʼkamwa mwake amakhala opusa ndipo mawu ake omaliza amakhala misala yobweretsa chiwonongeko. Ngakhale zili choncho, munthu wopusa amangolankhulabe.
Ngakhale kuti nthawi zina miseche singakhale yoipa kwambiri (koma ikhoza kupangitsa kuti anthu ayambe kunenera ena zoipa), nthawi zonse kunenera ena zoipa kungawononge mbiri ya munthu komanso nthawi zonse kumakhumudwitsa komanso kuyambanitsa anthu. Munthu akhoza kukhala ndi zolinga zabwino kapena zoipa pochita zimenezi. Koma kaya ali ndi zolinga zotani, munthu wonenera ena zoipa amadzipangitsa kukhala mdani wa Mulungu, chifukwa “aliyense amene amayambitsa mikangano pakati pa abale,” Mulungu amanyansidwa naye. (Miy 6:16-19) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kunenera ena zoipa” ndi di·aʹbo·los. Mawu amenewa amagwiritsidwanso ntchito m’Baibulo ponena za Satana “Mdyerekezi” yemwe ndi woneneza wamkulu, wa Mulungu. (Yoh 8:44; Chv 12:9, 10; Ge 3:2-5) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene amaneneza anzawo amakhala kuti akutengera Satana.
MULUNGU WA OKOTOBALA 27– NOVEMBALA 2
CHUMA YOFWANYEYA M’MAWU A MULUNGU | NAMALALEYA 11-12
Mukalenga Athanzi Koma Teto Osangalala
g 3/15 takuru 13 ndima 6-7
Lipevo Laeziezi Koma Teto Zuwa, Ngu Mirombwe
Dzuwa nalonso limapha tizilombo toyambitsa matenda. Magazini ina inanena kuti “tizilombo tambiri toyambitsa matenda monga chimfine, timafa tikawombedwa ndi dzuwa.” — Journal of Hospital Infection
Popeza taona kuti kamphepo kayaziyazi komanso dzuwa ndi mankhwala, si bwino kumangobindikira m’nyumba. Muzikonda kukhala panja nthawi zina n’kumaothera dzuwa komanso kupitidwa kamphepo kayaziyazi. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamadwaledwale.
Niyamikelenga Mphaso ya Moyo Ineyo Mulungu Aniva-ile Liye
6 Masiki ira Baibulo kai buku losambaula vya thanzi kapena vya vyodja, linonikami-eda iziwa mwemo Yehova munaganizela liye va khani dedi. Mofwanafwani-a, liye unonilimbikisa ira ‘nitetezenga thuthu li-u’ uvyongo vyevyo vinaliwononge. (Nam. 11:10) Baibulo linoruni-a dja vinjinji koma teto ng’wa vinjinji walwa chifukwa vyevyi vinokoza wononga moyo. (Miya. 23:20) Yehova unoyembekezela ira niviruni-enga va khani yoinjiva wa yodja koma teto walwa. — 1 Akor. 6:12; 9:25.
7 Ninokoza tonyi-eda ira ninoyamikela mphaso ya moyo eneyo Mulungu aniva-ile liye vo-indi-eda chito luso loganiza. (Sal. 119:99, 100; welengani Miyambo 2:11.) Mofwanafwani-a, ninokoza indi-eda chito luso loganiza vakhani ya vyodja vyevyo ninasakula iyo. Akala ninawomeluwana yodja imo-iwene koma ninoiziwa ira nadja inonibuleli-a, ganiza pama unonikami-eda ira niipewenga. Ninokoza tonyi-eda ira nili oganiza pama nagonanga mokwakwanela, panga masika olimbi-a thuthu, kala awuyesa koma teto samalela vande vi-u.
“Mupangenga Vyevyo Mawu Kanaongaathu”
2 Chifukwa n’ni iyo anayo ninalambela Mulungu ninakala osangalala? Vikala vifukwa vinjinji, koma chifukwa imo-i chiyoi ninowelenga Mawu a Mulungu thawi detene ndipo ninoesaesa arela vyevyo ninafunjeda iyo. — Welengani Yakobo 1:22-25.
3 ‘Panga vyevyo Mawu’ a Mulungu kanaongaathu unonikami-a mundila dinjinji. Yowambeela, napanganga vyevyo ninafunjeda iyo ninosangalasa Yehova. Ndipo naiziwa ira ninosangalasa Yehova ninosangalala vinjinji. (Nam. 12:13) Na-indi-edanga chito vyevyo ninafunjeda iyo m’Mawu a Mulungu ninokala na mabanja apama koma teto ninogwilizana na Akiristu afwi-u. Mwina nyo muona wan’le ira vyevi pivyoona. Enjedela vevo, ninopewa mavuto anayo athu anayo katina-arela makundo a Yehova kanagumananaathu. Ninogwilizana na vyevyo Mwene Davide aongile liye. Angaongile vya malamulo na vigamulo vya Yehova, oomari-a nyimbwae na mawu oyi: “Muthu osunga vigamulovyo unofwanya mphoto ilukulu.”— Sal. 19:7-11.
Makundo Okami-a
it “Andeliwa” ¶10
Andeliwa
Maumboni amasonyeza kuti amuna amene Mulungu anawagwiritsa ntchito polemba Baibulo sankachita zinthu ngati maloboti, kumangolemba uthenga umene akuuzidwa. Timawerenga za mtumwi Yohane kuti Mulungu anamuuzira zokhudza Chivumbulutso kudzera mwa mngelo “pogwiritsa ntchito zizindikiro” ndipo kenako Yohaneyo “anachitira umboni mawu amene Mulungu anapereka ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka, kutanthauza zonse zimene anaona.” (Chv 1:1, 2) ‘Atadzazidwa ndi mzimu woyera,’ Yohane anapezeka kuti ali “m’tsiku la Ambuye” ndipo anauzidwa kuti: “Zimene ukuona, uzilembe mumpukutu.” (Chv 1:10, 11) Choncho zikuoneka kuti Mulungu anaona kuti zingakhale bwino kwambiri kuti anthu amene analemba Baibulo azigwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza posankha mawu komanso mmene angafotokozere masomphenya amene ankaona. (Hab 2:2) Kwinaku akuwatsogolera komanso kuwathandiza kuti zimene akulembazo zikhale zolondola, zoona komanso zogwirizana ndi cholinga chake. (Miy 30:5, 6) Wolemba Baibulo aliyense ankafunika kuyesetsa kuchita mbali yake ndipo zimenezi zinaonekera bwino pa mawu opezeka pa Namalaleya 12:9, 10, omwe amafotokoza kuti anaganizira mozama, kufufuza mosamala kwambiri komanso kuika mwandondomeko “mawu osangalatsa ndipo analemba mawu olondola a choonadi.” — Yerekezerani na Luk 1:1-4.