Wolembedwa na Maliko
11 Tsopano atayandikila Yerusalemu, anafika pa Phili la Maolivi, kumene kunali Betifage na Betaniya. Ali kumeneko, Yesu anatuma ophunzila ake aŵili 2 n’kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi uwo, ndipo mukangoloŵamo mupeza mwana wa bulu wamphongo amene munthu sanamukwelepo n’kale lonse, atam’mangilila. Mukamumasule n’kumubweletsa kuno. 3 Munthu aliyense akakakufunsani kuti, ‘N’cifukwa ciyani mukucita zimenezi?’ mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna. Ndipo abwela naye akangotsiliza kumuseŵenzetsa.’” 4 Conco anapita ndipo anapezadi mwana wa bulu atamumangilila pakhomo kunja m’mbali mwa njila, ndipo anam’masula. 5 Koma ena amene anaimilila pamenepo anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukum’masula buluyu?” 6 Iwo anawauza zimene Yesu anakamba ndipo anawalola kupita.
7 Ndiyeno mwana wa buluyo anabwela naye kwa Yesu. Kenako anayanzika zovala zawo zakunja pa buluyo, ndipo Yesu anakwelapo. 8 Komanso anthu ambili anayanzika zovala zawo zakunja mu msewu, koma ena anali kudula zitsamba m’minda. 9 Ndiponso anthu amene anali patsogolo na pambuyo pake anali kufuula kuti “Mpulumutseni! Wodalitsika ni iye wobwela m’dzina la Yehova! 10 Wodala ni Ufumu wa atate wathu Davide umene ukubwela! Mpulumutseni inu amene muli kumwambamwambako!” 11 Iye ataloŵa mu Yerusalemu anapita kukaloŵa m’kacisi, ndipo anayang’ana-yang’ana zinthu zonse mmenemo. Koma popeza nthawi inali itatha kale, anacoka n’kupita ku Betaniya pamodzi na atumwi ake 12 aja.
12 Tsiku lotsatila pamene anali kucoka ku Betaniya anamva njala. 13 Ali capatali, anaona mtengo wa mkuyu umene unali na masamba, ndipo anapitako kuti akaone ngati angapezemo kanthu. Koma atafika pa mtengowo sanapezemo ciliconse koma masamba okha-okha cifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. 14 Conco anauza mtengowo kuti: “Munthu asadzadyenso zipatso zako mpaka kale-kale.” Ndipo ophunzila ake anali kumva.
15 Tsopano iwo anafika ku Yerusalemu. Kumeneko, analoŵa m’kacisi ndipo anayamba kupitikitsila panja anthu omwe anali kugulitsa na kugula zinthu m’kacisimo. Komanso anagudubula matebulo a osintha ndalama na mabenchi a ogulitsa nkhunda. 16 Ndipo sanalole aliyense kupitila pa kacisi atanyamula ciwiya ciliconse. 17 Iye anali kuwaphunzitsa na kuwauza kuti: “Kodi si paja Malemba amanena kuti, ‘Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo anthu a mitundu yonse’? Koma inu mwaisandutsa phanga la acifwamba.” 18 Ansembe aakulu na alembi atamva zimenezi, anayamba kufuna-funa njila yomuphela cifukwa iwo anali kumuopa, popeza khamu lonse la anthu linali kudabwa na kaphunzitsidwe kake.
19 Pa tsikulo ca kumadzulo, iwo anatuluka mumzindawo. 20 Koma m’mamaŵa pamene anali kudutsa, anaona kuti mtengo wa mkuyu uja wafota kale na mizu yake yomwe. 21 Petulo ataukumbukila mtengowo, anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi* onani! Mtengo wa mkuyu uja munautembelela wafota.” 22 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Muzikhulupilila Mulungu. 23 Ndithu nikukuuzani kuti ngati aliyense angauze phili ili kuti, ‘Nyamuka ukadziponye m’nyanja,’ ndipo sakayikila mumtima mwake, koma ali na cikhulupililo pa zimene wakamba kuti zidzacitika, zidzacitikadi. 24 Ndiye cifukwa cake nikukuuzani kuti pa zinthu zonse zimene mumapemphela na kupempha, khalani na cikhulupililo ngati kuti mwazilandila kale, ndipo mudzazilandiladi. 25 Komanso mukaimilila kuti mupemphele muzikhululukila aliyense pa ciliconse cimene anakulakwilani, kuti nayenso Atate wanu wa kumwamba akukhululukileni macimo anu.” 26* ——
27 Iwo anafikanso ku Yerusalemu. Ndipo pamene anali kuyenda mu kacisi, ansembe aakulu, alembi, na akulu anafika kwa iye, 28 ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ulamulilo wocita zimenezi munautenga kuti? Nanga ndani anakupatsani ulamulilo wocita zimenezi?” 29 Yesu anawayankha kuti: “Nikufunsani funso limodzi. Muniyankhe, ndipo mukatelo, nikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi. 30 Kodi ubatizo wa Yohane unacokela kumwamba kapena kwa anthu?* Niyankheni.” 31 Conco iwo anayamba kukambilana n’kumati: “Tikanena kuti, ‘Unacokela kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciyani simunamukhulupilile?’ 32 Koma kodi tinganene kuti, ‘Unacokela kwa anthu’?” Iwo anali kuopa khamu la anthu, cifukwa anthu onsewo anali kukhulupilila kuti Yohane analidi mneneli. 33 Conco pomuyankha Yesu, iwo anati: “Sitidziŵa.” Yesu anati: “Inenso sinikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi.”