Mande, July 28
Amene ali wogwilizana ndi inu ndi wamkulu kuposa amene ali wogwilizana ndi dziko.—1 Yoh. 4:4.
Mukakhala na mantha, muzisinkhasinkha zimene Yehova adzacita m’tsogolo Satana akadzacotsedwapo. Msonkhano wa cigawo wa mu 2014 unali na citsanzo coonetsa tate akukambilana na banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likanalembedwela cikanakhala kuti linali kulosela mmene Paradaiso adzakhalile. Analiŵelenga motele: “Masiku a m’dziko latsopano adzakhala nthawi yapadela komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambila Mulungu, odzicepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvela makolo, oyamika, okhulupilika, okonda acibale awo, ofuna kugwilizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalilika, oganizila ena, osadzitukumula, ndiponso osanyada, okonda Mulungu m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odzipelekadi kwa Mulungu, anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambilana nawo a m’banja lanu kapena alambili anzanu za mmene umoyo udzakhalile m’dziko latsopano? w24.01 6 ¶13-14
Ciŵili, July 29
Umandisangalatsa kwambili.—Luka 3:22.
N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova amakonda gulu lonse la anthu ake! Baibo imati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe, nthawi zina ena amalefuka moti amafika podzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amakondwela nane?’ Ena mwa alambili okhulupilika a Yehova ochulidwa m’Baibo anavutikapo na maganizo otelo. (1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11) Baibo imakamba momveka bwino kuti anthu opanda ungwilo angapeze ciyanjo ca Yehova. Motani? Mwa kukhulupilila Yesu Khristu na kubatizika. (Yoh. 3:16) Mwa kutelo, timaonetsa poyela kuti tinalapa macimo athu, komanso kuti tinapanga lonjezo kwa Mulungu lakuti tidzacita cifunilo cake. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amakondwela ngati tapanga masitepe amenewa kuti tikhale naye pa ubale. Kuwonjezela apo, amakondwela nafe ngati tipitiliza kucita zonse zimene tingathe posunga lumbilo lathu la kudzipatulila. Ndipo amationa kukhala mabwenzi ake a pamtima.—Sal. 25:14. w24.03 26 ¶1-2
Citatu, July 30
Sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.—Mac. 4:20.
Tingatengele citsanzo ca ophunzila mwa kupitiliza kulalikila ngakhale pamene maboma atilamula kuti tileke kulalikila. Tili na cidalilo kuti Yehova adzatithandiza kukwanilitsa utumiki wathu. Conco mupemphani kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima, akupatseni nzelu komanso kuti akuthandizeni kuthana na mavuto. Ambili a ife tikulimbana na mavuto monga matenda, kupsinjika maganizo, kutaikilidwa wokondedwa wathu mu imfa, mavuto a m’banja, mazunzo, kapena vuto lina. Ndipo zinthu monga milili na nkhondo, zapangitsa kuti cikhale covuta kwambili kuthana na mavuto ngati amenewa. Conco, m’khuthulileni za kumtima kwanu Yehova. Muuzeni za vuto lanu mmene mungauzile bwenzi lanu lapamtima. Khalani wotsimikiza kuti Yehova “adzakuthandizani.” (Sal. 37:3, 5) Kulimbikila kupemphela kudzatithandiza ‘kupilila mavuto.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziŵa mavuto amene atumiki ake amakumana nawo, “amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Sal. 145:18, 19. w23.05 5-6 ¶12-15