Kalata Yoyamba kwa Akorinto
9 Kodi si ndine womasuka? Kodi si ndine mtumwi? Kodi ine sindinamuonepo Yesu Ambuye wathu? Kodi inu si ndinu nchito yanga mwa Ambuye? 2 Ngakhale kuti kwa ena si ndine mtumwi, koma kwa inu ndithu ndine mtumwi. Pakuti inu ndinu cidindo cotsimikizila utumwi wanga mwa Ambuye.
3 Kwa amene akunditsutsa, kudziteteza kwanga ndi uku: 4 Ndili ndi ufulu* wa kudya ndi kumwa, si conco? 5 Tili ndi ufulu woyenda ndi akazi* athu okhulupilila monga atumwi ena onse, komanso monga abale athu mwa Ambuye amacitila kuphatikizapo Kefa,* si conco? 6 Kodi Baranaba ndi ine ndife tokha amene tilibe ufulu woleka kugwila nchito kuti tizipeza zofunikila pa umoyo? 7 Ndani amene amagwila nchito ya usilikali koma n’kumadzilipila yekha? Ndani amene amalima munda wampesa koma osadyako zipatso zake? Ndi m’busa wanji amene amaweta ziweto koma osamwako mkaka wake?
8 Kodi ndikunena izi potengela maganizo a anthu? Kodi sizimenenso Cilamulo cimanena? 9 Pakuti Cilamulo ca Mose cimanena kuti: “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbeu.” Kodi Mulungu amadela nkhawa ng’ombe zokha? 10 Kapena kwenikweni anakamba mau amenewa poganizila ife? Mau amenewa anawalembadi kaamba ka ife, cifukwa munthu amene akulima komanso amene akupuntha mbeu amagwila nchito ali ndi ciyembekezo kuti alandila kenakake.
11 Ngati tinabzala zinthu zauzimu mwa inu, kodi n’kulakwa kulandila* zinthu zofunikila pa umoyo kucokela kwa inu? 12 Ngati anthu ena amakuyembekezelani kuti muzicita zimenezi, kodi ife si ndiye oyenelela kwambili kuticitila zimenezi? Ngakhale n’telo, ife sitinagwilitse nchito ufulu umenewo, koma tikupilila zonse kuti mwa njila inayake tisatsekeleze uthenga wabwino wokamba za Khristu. 13 Kodi inu simukudziwa kuti anthu amene amagwila nchito zopatulika amadya za m’kacisi? Ndiponso kodi simukudziwa kuti anthu amene amatumikila paguwa lansembe nthawi zonse, amalandilako zinthu zina zopelekedwa paguwa lansembelo? 14 Mwa njila imeneyi, Ambuye analamula kuti amene amalengeza uthenga wabwino azipeza zofunikila pa umoyo wawo kudzela mu uthenga wabwino.
15 Koma ine sindinagwilitseko nchito makonzedwe amenewo. Kukamba zoona, sikuti ndakulembelani zimenezi kuti muyambe kugwilitsa nchito makonzedwe amanewa pa ine, cifukwa ndi bwino kuti ndife kusiyana n’kuti ndicite zimenezi. Palibe munthu amene angandicotsele zifukwa zimene ndili nazo zodzitamila! 16 Tsopano ngati ndikulengeza uthenga wabwino, cimeneco cisakhale cifukwa codzitamila, cifukwa ndinalamulidwa kuti ndizicita zimenezo. Ndipo tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino! 17 Ndikamacita zimenezi modzifunila, ndidzalandila mphoto. Koma ngati ndimacita mokakamizika, ndinebe mtumiki woyang’anila malinga ndi udindo umene unaikidwa mwa ine. 18 Kodi ndiye mphoto yanga ndi yotani? Ndi yakuti ndikalengeza uthenga wabwino, ndiziulengeza kwaulele, kuti ndisagwilitse nchito ulamulilo* wanga molakwika pa zinthu zokhudza uthenga wabwino.
19 Ngakhale kuti ndine womasuka kwa anthu onse, ndadzipanga kukhala kapolo kwa anthu onse, kuti ndikope anthu ambili mmene ndingathele. 20 Kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda kuti ndikope Ayuda. Kwa amene amatsatila Cilamulo ndinakhala ngati munthu amene amatsatila Cilamulo kuti ndikope amene amatsatila Cilamulo, ngakhale kuti ine sinditsatila Cilamulo. 21 Kwa anthu amene satsatila Cilamulo, ndinakhala ngati wopanda Cilamulo, ngakhale kuti ine ndimatsatila malamulo a Mulungu komanso lamulo la Khristu. Ndinacita izi kuti ndikope anthu amene satsatila Cilamulo. 22 Kwa ofooka ndinakhala wofooka, kuti ndikope ofooka. Ndakhala zinthu zonse kwa anthu a mtundu uliwonse, kuti ngati n’kotheka ndipulumutseko ena. 23 Koma ndimacita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti ndiugawile kwa ena.
24 Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano onse amathamanga, koma ndi mmodzi cabe amene amalandila mphoto? Muzithamanga m’njila yoti mukalandile mphotoyo. 25 Koma munthu amene amacita nao mpikisano amakhala wodziletsa m’zinthu zonse. Amatelo kuti alandile mphoto ya nkhata yamaluwa imene imaonongeka. Koma ife timafuna kukapeza nkhata yamaluwa imene singaonongeke. 26 Conco, mmene ndikuthamangila sikuti ndikungothamangilamo, osadziwa kumene ndikupita. Mmene ndikuponyela makofi anga, sikuti ndikungomenya m’mphepo ai. 27 Koma ndimapumphuntha* thupi langa ndi kulipangitsa kukhala ngati kapolo, ndi colinga coti pambuyo polalikila ena, ndisapezeke wosayenela* mwa njila ina.