Macitidwe a Atumwi
3 Tsopano Petulo ndi Yohane anali kupita kukalowa m’kacisi pa nthawi yopemphela. Nthawiyo inali 3 koloko masana.* 2 Ndiyeno panali mwamuna wina amene anabadwa wolemala. Tsiku lililonse, anali kumuika pafupi ndi khomo la kacisi lochedwa Geti Yokongola, kuti azipempha mphatso zacifundo kwa amene anali kulowa m’kacisi. 3 Iye ataona kuti Petulo ndi Yohane akufuna kulowa m’kacisimo, anayamba kuwapempha mphatso zacifundo. 4 Koma Petulo pamodzi ndi Yohane anamuyang’anitsitsa, ndipo anamuuza kuti: “Tiyang’ane.” 5 Conco munthuyo anawayang’anitsitsa, akuyembekezela kuti iwo amupatsa kenakake. 6 Koma Petulo anati: “Ine ndilibe siliva ndi golide, koma ndikupatsa cimene ndili naco. M’dzina la Yesu Khristu Mnazareti, yenda!” 7 Atatelo anamugwila dzanja lamanja n’kumuimilika. Nthawi yomweyo, mapazi ndi miyendo* yake inalimba. 8 Munthuyo analumpha n’kuyamba kuyenda, ndipo analowa nawo m’kacisimo. Iye anali kuyenda ndi kulumpha akutamanda Mulungu. 9 Ndipo anthu onse anamuona akuyenda ndi kutamanda Mulungu. 10 Iwo anamuzindikila kuti ndi munthu uja amene anali kukhala pa geti ya kacisi yochedwa Geti Yokongola, n’kumayembekezela kupatsidwa mphatso zacifundo. Anthuwo anadabwa kwambili, ndipo anakondwela ndi zimene zinacitikila munthuyo.
11 Munthu uja akali wogwililila manja a Petulo ndi Yohane, anthu onse anathamangila kwa iwo ku Khonde la Zipilala la Solomo. Ndipo anthuwo anadabwa kwambili. 12 Petulo ataona izi, anauza anthuwo kuti: “Aisiraeli inu, n’cifukwa ciyani mwadabwa kwambili ndi zimenezi? N’cifukwa ciyani mukutiyang’anitsitsa monga kuti ife tamuyendetsa mwa mphamvu zathu, kapena cifukwa ca kudzipeleka kwathu kwa Mulungu? 13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki, komanso wa Yakobo, Mulungu wa makolo athu akale, walemekeza Mtumiki wake Yesu amene inu munamupeleka ndi kumukana pamaso pa Pilato. Ngakhale kuti Pilatoyo anafuna kumumasula. 14 Inde, inu munamukana munthu woyela komanso wolungama ameneyo. Ndipo munapempha kuti iye akumasulileni munthu wopha anthu. 15 Inu munamupha Mtumiki Wamkulu wa moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, ndipo ife ndife mboni za nkhaniyi. 16 Conco kupitila m’dzina lake komanso mwa cikhulupililo cathu m’dzinalo, munthu uyu amene mukumuona ndi kum’dziwa wacilitsidwa. Cikhulupililo cimene tili naco cifukwa ca Yesu, cacititsa kuti munthu uyu acililetu monga mmene nonsenu mukumuonela. 17 Tsopano abale, ndikudziwa kuti munacita zinthu mosazindikila monga mmene olamulila anu nawonso anacitila. 18 Koma mwa njila imeneyi, Mulungu wakwanilitsa zinthu zimene analengezelatu kupitila mwa aneneli onse, kuti Khristu wake adzavutika.
19 “Conco lapani ndi kutembenuka kuti macimo anu afafanizidwe. Mukatelo, nyengo zotsitsimula zocokela kwa Yehova* zidzabwela kwa inu. 20 Ndipo iye adzatumiza Yesu, amene ndi Khristu wosankhidwa cifukwa ca inu. 21 Kumwamba kuyenela kumusunga ameneyu kufikila nthawi ya kubwezeletsa zinthu zonse zimene Mulungu analankhula kudzela mwa aneneli ake oyela akale. 22 Ndipo Mose anati: ‘Yehova Mulungu wanu adzakuutsilani mneneli ngati ine pakati pa abale anu. Mudzamumvele pa zonse zimene adzakuuzani. 23 Ndithudi, aliyense amene sadzamvela Mneneliyo adzawonongedwa kothelatu pakati pa anthu.’ 24 Ndipo aneneli onse kuyambila pa Samueli komanso amene anabwela pambuyo pake, onse amene analosela, anakambanso mosapita m’mbali za masiku amenewa. 25 Inu ndinu ana a aneneliwo, komanso a cipangano cimene Mulungu anacita ndi makolo anu akale. Iye anauza Abulahamu kuti: ‘Kudzela mwa mbadwa* yako, mabanja onse pa dziko lapansi adzadalitsidwa.’ 26 Mulungu atasankha Mtumiki wake, anamutumiza kwa inu coyamba kuti adzakudalitseni mwa kubweza aliyense wa inu kuti aleke nchito zake zoipa.”