Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
9 Pamene Yesu anali kuyenda, anaona munthu wina amene anabadwa wakhungu. 2 Ophunzila ake anamufunsa kuti: “Mphunzitsi,* anacimwa ndani kuti munthu uyu abadwe wakhungu, ndi iyeyo kapena makolo ake?” 3 Yesu anayankha kuti: “Munthu uyu kapena makolo ake, onse sanacimwe. Koma zinakhala conco kuti nchito za Mulungu zionekele pa iye. 4 Tiyenela kugwila nchito za Mulungu amene anandituma kukali masana, cifukwa usiku ukubwela pamene munthu sangagwile nchito. 5 Pamene ine ndili m’dziko, ndine kuwala kwa dziko.” 6 Atakamba zimenezi, analavulila mata pansi n’kukanda matope ndi matawo, kenako anapaka matopewo m’maso mwa munthuyo. 7 Ndipo anamuuza kuti: “Pita ukasambe m’dziwe la Siloamu” (dzinali kumasulila kwake ndi “Wotumizidwa”). Iye anapitadi kukasamba, ndipo anabwelako akuona.
8 Ndiyeno anthu okhala naye pafupi komanso amene kale anali kumuona akupemphapempha anayamba kukamba kuti: “Kodi munthu uyu si uja anali kukhala pansi n’kumapemphapempha?” 9 Anthu ena anali kukamba kuti: “Ndi ameneyu.” Pomwe ena anali kukamba kuti: “Ayi angofanana cabe.” Koma mwiniwakeyo anali kukamba kuti “Ndine amene.” 10 Conco iwo anamufunsa kuti: “Nanga zinatheka bwanji kuti maso ako atseguke?” 11 Iye anayankha kuti: “Munthu wina dzina lake Yesu anakanda matope n’kundipaka m’maso ndipo anandiuza kuti, ‘Pita ku Siloamu ukasambe.’ Conco ine ndinapitadi kukasamba, ndipo ndinayamba kuona.” 12 Atatelo, iwo anamufunsa kuti: “Munthu ameneyo ali kuti?” Iye anayankha kuti: “Kaya sindidziwa.”
13 Anthuwo anapeleka munthu amene anali wakhungu uja kwa Afarisi. 14 Zinangocitika kuti tsiku limene Yesu anakanda matope n’kutsegula maso ake linali la Sabata. 15 Pa nthawiyo, Afarisi nawonso anayamba kumufunsa munthuyo zimene zinacitika kuti ayambe kuona. Iye anawauza kuti: “Anapaka matope m’maso mwanga, ndipo ine ndinasamba, kenako ndinayamba kuona.” 16 Ena mwa Afarisiwo anayamba kunena kuti: “Munthuyo si wocokela kwa Mulungu, cifukwa sasunga Sabata.” Enanso anali kukamba kuti: “Kodi munthu wocimwa angathe bwanji kucita zozizwitsa* ngati izi?” Conco pakati pawo panakhala magawano. 17 Iwo anafunsanso munthu amene anali wakhungu uja kuti: “Ukutipo ciyani za munthu uyu popeza watsegula maso ako?” Munthuyo anayankha kuti: “Iye ndi mneneli.”
18 Koma Ayudawo sanakhulupilile kuti munthuyu analidi wakhungu ndipo wayamba kuona, mpaka anaitana makolo ake. 19 Iwo anafunsa makolowo kuti: “Kodi uyu ndiye mwana wanu uja amene mumati anabadwa wakhungu? Nanga zatheka bwanji kuti ayambe kuona?” 20 Makolo ake anayankha kuti: “Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, komanso kuti anabadwa wakhungu. 21 Koma zakuti wayamba bwanji kuona, ife sitidziwa, komanso zakuti watsegula maso ake ndani, sitidziwanso. Mufunseni, ndi wamkulu afotokoze yekha.” 22 Makolo ake anayankha conco cifukwa anali kuopa Ayuda, pakuti Ayudawo anali atagwilizana kale zakuti munthu aliyense amene avomeleze kuti Yesu ndi Khristu, afunika kucotsedwa m’sunagoge. 23 Ndiye cifukwa cake makolo akewo anati: “Ndi wamkulu, mufunseni.”
24 Conco iwo anaitananso munthu amene anali wakhungu uja kaciwili n’kumuuza kuti: “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthuyu ndi wocimwa.” 25 Iye anayankha kuti: “Zakuti iye ndi wocimwa ine sindizidziwa. Cimene ndidziwa n’cakuti ndinali wakhungu, koma tsopano ndikuona.” 26 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Anakucita ciyani? Nanga anatsegula bwanji maso ako?” 27 Iye anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma simunamve. Kodi n’cifukwa ciyani mufuna kumvanso? Kodi nanunso mufuna kukhala ophunzila ake?” 28 Pamenepo iwo anamuyankha monyoza kuti: “Iwe ndiwe wophunzila wa munthu amene uja, koma ife ndife ophunzila a Mose. 29 Ife tidziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose, koma za munthu uyu sitidziwa kumene anacokela.” 30 Munthuyo anawayankha kuti: “Zimenezi n’zodabwitsa kwambili, kuti simudziwa kumene iye anacokela, koma watsegula maso anga! 31 Tidziwa kuti Mulungu samvetsela wocimwa, koma ngati munthu amaopa Mulungu ndi kucita cifunilo cake, amamumvetsela munthuyo. 32 Kuyambila kalekale sitinamvepo kuti wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu. 33 Ngati munthuyu sanacokele kwa Mulungu, sakanakwanitsa kucita ciliconse.” 34 Iwo anamuyankha kuti: “Nonsenu munabadwila mu ucimo, koma kodi ukufuna kutiphunzitsa?” Basi pamenepo anamucotsa m’sunagoge!
35 Ndiyeno Yesu anamva kuti munthu uja amucotsa m’sunagoge, ndipo atamupeza, anamufunsa kuti: “Kodi umukhulupilila Mwana wa munthu?” 36 Munthuyo anayankha kuti: “Kodi Mwana wa munthuyo ndi uti kuti ndikhulupilile mwa iye?” 37 Yesu anamuuza kuti: “Wamuona kale, ndipo ndi amene akukamba nawe.” 38 Iye anati: “Ndakhulupilila mwa inu Ambuye.” Kenako anamugwadila.* 39 Ndiyeno Yesu anati: “Ndinabwela m’dziko kuti anthu aweluzidwe n’colinga cakuti amene saona ayambe kuona, ndipo amene akuona akhale akhungu.” 40 Afarisi amene anali ndi munthuyo anamva zimene Yesu anali kukamba, ndipo anamuuza kuti: “Kodi uganiza kuti nafenso ndife akhungu?” 41 Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala akhungu simukanakhala ndi chimo. Koma cifukwa mukunena kuti, ‘Mukuona,’ chimo lanu likhalabe nanu.”