Kalata Yoyamba kwa Atesalonika
5 Koma tsopano za nthawi ndi nyengo abale, m’posafunika kuti tikulembeleni ciliconse. 2 Pakuti inu nomwe mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati mbala usiku. 3 Akadzangonena kuti, “Bata ndi mtendele!” nthawi yomweyo cionongeko cidzawafikila modzidzimutsa ngati mmene ululu umene mkazi woyembekezela amamva akangotsala pang’ono kucila,* ndipo sadzapulumuka. 4 Koma inu abale simuli mumdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mmene mbala zimadzidzimukila kukazicela. 5 Pakuti nonsenu ndinu ana a kuwala komanso ana a masana. Si ndife anthu a usiku kapena a mdima.
6 Cotelo tisapitilize kugona ngati mmene ena onse akucitila. M’malomwake, tikhalebe maso komanso oganiza bwino. 7 Pakuti ogona amagona usiku, ndipo amene amaledzela, amaledzela usiku. 8 Koma popeza ndife a usana, tiyeni tikhalebe oganiza bwino, ndipo tibvalebe codzitetezela pacifuwa ca cikhulupililo ndi ca cikondi. Tibvalenso ciyembekezo ca cipulumutso ngati cisoti, 9 pakuti Mulungu sanatisankhe kuti adzatilange, koma anatisankha kuti tikapulumuke kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 10 Iye anatifela kuti kaya tikhale maso kapena tigone,* tikhale ndi moyo limodzi ndi iye. 11 Conco pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake ngati mmene mukucitila.
12 Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwila nchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolelani mwa Ambuye komanso kukulangizani. 13 Muziwakonda komanso kuwacitila ulemu waukulu cifukwa ca nchito yao. Muzikhala mwamtendele pakati panu. 14 Komanso tikukulimbikitsani abale, kuti muzicenjeza* anthu ocita zosalongosoka. Muzikamba mau olimbikitsa kwa opsyinjika maganizo,* muzithandiza ofooka, ndiponso muzikhala oleza mtima kwa onse. 15 Onetsetsani kuti pasapezeke wina aliyense wobwezela coipa pa coipa kwa mnzake. Koma nthawi zonse muziyesetsa kucitilana zabwino wina ndi mnzake komanso kucitila zabwino anthu ena onse.
16 Muzikondwela nthawi zonse. 17 Muzipemphela nthawi zonse. 18 Muziyamika pa ciliconse. Cimeneci ndi cifunilo ca Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu. 19 Musazimitse moto wa mzimu. 20 Musamanyoze mau aulosi. 21 Muzitsimikizila zinthu zonse. Muzigwilitsitsa cabwino mwamphamvu. 22 Muzipewa zoipa za mtundu uliwonse.
23 Mulungu wamtendeleyo mwiniyo akuyeletseni kothelatu. Ndipo m’mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu, komanso thupi lanu, zikhale zopanda ulemali kapena colakwa ciliconse pa nthawi yakukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 24 Amene akukuitanani ndi wokhulupilika ndipo sadzalephela kucita zimenezi.
25 Abale, pitilizani kutipemphelela.
26 Mupeleke moni kwa abale onse, mwa kupsyompsyonana mwacikondi.*
27 Ndikukulamulani mwa Ambuye kuti mukawelenge kalatayi kwa abale onse.
28 Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Khristu cikhale nanu.