Kwa Aroma
6 Ndiye kodi tinene kuti ciyani? Tipitilize kucimwa kuti cisomo ciwonjezeke? 2 Ayi ndithu! Popeza kuti tinamasulidwa* ku ucimo, ndiye n’cifukwa ciyani tipitilize kucimwa? 3 Kapena simukudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa, ndipo tsopano ndife ogwilizana ndi Khristu Yesu, tinabatizidwanso mu imfa yake? 4 Conco ife tinaikidwa naye m’manda pamene tinabatizidwa mu imfa yake, monga mmene Khristu anaukitsidwila kudzela mu ulemelelo wa Atate, kuti tikhale umoyo watsopano. 5 Ngati takhala ogwilizana naye mwa kufa imfa yofanana ndi yake, mosakaikila tidzagwilizananso naye poukitsidwa mofanana naye. 6 Pakuti tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pa mtengo limodzi naye n’colinga coti thupi la ucimo likhale lopanda mphamvu, kuti tisakhalenso akapolo a ucimo. 7 Pakuti munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu* wa macimo ake.
8 Cina, ngati tinafa limodzi ndi Khristu, timakhulupilila kuti tidzakhalanso ndi moyo limodzi ndi iye. 9 Tikudziwa kuti popeza Khristu waukitsidwa, iye sadzafanso ayi, ndipo imfa siikumulamulilanso monga mfumu. 10 Pakuti anafa kuti acotse ucimo kamodzi kokha basi, ndipo moyo umene ali nawo, ali nawo kuti azicita cifunilo ca Mulungu. 11 Inunso muzidziona ngati akufa pa nkhani ya ucimo, koma ngati amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
12 Conco musalole kuti ucimo upitilize kulamulila monga mfumu m’matupi anu amene akhoza kufa kuti muzitsatila zilakolako zawo. 13 Komanso musapeleke matupi* anu ku ucimo monga zida za nchito zosalungama, koma dzipelekeni kwa Mulungu monga anthu amene aukitsidwa kwa akufa, ndiponso matupi* anu muwapeleke kwa Mulungu monga zida za nchito zolungama. 14 Pakuti ucimo suyenela kukulamulilani monga mfumu, cifukwa simukutsatila Cilamulo, koma mumapindula ndi cisomo ca Mulungu.
15 Ndiye kodi tizicita ciyani? Tizicimwa cifukwa cakuti sitikutsatila Cilamulo koma tikupindula ndi cisomo ca Mulungu? Ayi ndithu! 16 Kodi simukudziwa kuti mukadzipeleka kwa wina aliyense ngati akapolo omvela, mumakhala akapolo a munthu amene mukumvelayo? Mumakhala akapolo a ucimo umene umatsogolela ku imfa, kapena akapolo a kumvela kumene kumatsogolela ku cilungamo. 17 Koma tikumuyamikila Mulungu kuti ngakhale kuti poyamba munali akapolo a ucimo munamvela mocokela pansi pa mtima mfundo zimene munaphunzitsidwa. 18 Inde, popeza kuti munamasulidwa ku ucimo, munakhala akapolo a cilungamo. 19 Ndikulankhula ngati munthu cifukwa ca kufooka kwa matupi anu. Pakuti munapeleka ziwalo zanu ngati akapolo a zonyansa, ndiponso akapolo a kusamvela malamulo kuti muzicita zinthu zophwanya malamulo. Tsopano pelekaninso ziwalo zanu kuti zikhale ngati akapolo a cilungamo kuti muzicita zoyela. 20 Pakuti pamene munali akapolo a ucimo munali omasuka ku cilungamo.
21 Kodi munali kubala zipatso zotani pa nthawiyo? Zinali zinthu zimene mumacita nazo manyazi palipano. Ndipo mapeto a zinthu zimenezo ndi imfa. 22 Koma tsopano, cifukwa cakuti munamasulidwa ku ucimo ndipo munakhala akapolo a Mulungu, mukubala zipatso zoyela, ndipo pa mapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha. 23 Pakuti malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.