Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
12 Pa nthawiyi, khamu la anthu masauzande ambilimbili anasonkhana pamodzi, moti anali kupondanapondana. Coyamba, Yesu analankhula ndi ophunzila ake kuti: “Samalani ndi zofufumitsa za Afarisi zimene ndi cinyengo. 2 Koma palibe cobisidwa mosamala kwambili cimene sicidzaululidwa, ndipo palibe cinsinsi cimene sicidzadziwika. 3 Conco ciliconse cimene munganene mu mdima, cidzamveka poyela. Ndipo zilizonse zimene mukunong’onezana kwanokha m’zipinda zanu, zidzalalikidwa pa mitenje ya nyumba. 4 Komanso ndikukuuzani mabwenzi anga, musamaope amene amapha thupi, omwe pambuyo pake sangathe kucita ciliconse. 5 Koma ndikuuzani amene muyenela kumuopa. Muziopa amene pambuyo pa kupha munthu, amakhalanso ndi mphamvu zoponya munthuyo m’Gehena.* Inde ndikukuuzani, muziopa ameneyo. 6 Mpheta zisanu amazigulitsa makobili awili ocepa mphamvu, si conco kodi? Koma palibe ngakhale mpheta imodzi imene Mulungu amaiiwala.* 7 Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu amaliwelenga lonse. Conco musaope, ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zambili.
8 “Ndikukuuzani kuti, aliyense wondivomela pamaso pa anthu, Mwana wa munthu nayenso adzamuvomela pamaso pa angelo a Mulungu. 9 Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu, adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu. 10 Ndipo aliyense wokamba mawu onyoza Mwana wa munthu adzakhululukidwa, koma aliyense wonyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa. 11 Akadzakupelekani ku mabwalo a milandu, kwa akuluakulu a boma ndi olamulila, musadzade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukakamba ciyani, 12 cifukwa mzimu woyela udzakudziwitsani* pa nthawi yomweyo zoyenela kunena.”
13 Ndiyeno munthu wina m’khamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, uzani m’bale wanga kuti andigawileko colowa.” 14 Iye anamuyankha kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika kukhala woweluza pakati panu kapena wogawa cuma canu?” 15 Kenako anati kwa iwo: “Khalani maso, ndipo samalani ndi dyela la mtundu uliwonse,* cifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zoculuka motani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.” 16 Atakamba zimenezi, iye anawafotokozela fanizo lakuti: “Munda wa munthu wina wolemela unabala bwino. 17 Zitatelo iye anayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndicite ciyani tsopano popeza ndilibe kosungila zokolola zangazi?’ 18 Ndiyeno anati, ‘Ndidzacita izi: Ndidzapasula nyumba zanga zosungilamo zinthu ndi kumanga zina zikuluzikulu, ndipo mmenemo ndidzaikamo mbewu zanga zonse ndi zinthu zanga zonse. 19 Ndiye ndidzati kwa ine mwini:* “Uli* ndi zinthu zambili zabwino zimene ungazigwilitse nchito kwa zaka zambili. Mtima m’malo, idya, imwa, ndi kusangalala.”’ 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopusa iwe, usiku womwe uno anthu aufune moyo wako. Kodi ndani adzatenga zinthu zimene wasungazi?’ 21 Umu ndi mmenenso zidzakhalila ndi munthu wodziunjikila cuma, amene si wolemela kwa Mulungu.”
22 Ndiyeno anauza ophunzila ake kuti: “Ndiye cifukwa cake ndikukuuzani kuti, lekani kudela nkhawa za moyo* wanu kuti mudzadya ciyani, kapena za matupi anu kuti mudzavala ciyani. 23 Pakuti moyo ndi wofunika kwambili kuposa cakudya, ndipo thupi ndi lofunika kwambili kuposa covala. 24 Ganizilani za akhwangwala: Safesa mbewu kapena kukolola. Iwo alibe nkhokwe kapena nyumba yosungilamo zinthu, koma Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ndinu ofunika kwambili kuposa mbalame? 25 Ndani wa inu angatalikitse moyo wake ngakhale pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa? 26 Conco ngati simungakwanitse kucita kanthu kakang’ono aka, n’cifukwa ciyani mukuda nkhawa ndi zinthu zinazo? 27 Ganizilani mmene maluwa amakulila: Iwo sagwila nchito kapena kupanga nsalu. Koma ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. 28 Tsopano ngati umu ndi mmene Mulungu amavekela zomela zakuchile, zimene zimangokhalapo lelo mawa n’kuziponya pa moto, ndiye kuti inu adzakuvekani kuposa pamenepo, a cikhulupililo cocepa inu! 29 Conco, lekani kuda nkhawa kuti mudzadya ciyani komanso kuti mudzamwa ciyani. Ndipo lekani kuda nkhawa ndi zimene zingakucitikileni, 30 pakuti anthu a mitundu ina m’dzikoli akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu akudziwa kuti mufunikila zinthu zimenezi. 31 M’malo mwake, pitilizani kufunafuna Ufumu wake, ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.
32 “Kagulu ka nkhosa inu, musaope, cifukwa Atate wanu wavomeleza kukupatsani Ufumu. 33 Gulitsani zinthu zanu ndi kupeleka mphatso zacifundo. Mupange zikwama za ndalama zimene sizikutha, kutanthauza cuma cosatha kumwamba, kumene mbala singafikeko komanso njenjete sizingawononge. 34 Pakuti kumene kuli cuma canu, mitima yanu idzakhalanso komweko.
35 “Valani ndi kukhala okonzeka ndipo nyale zanu zikhale zikuyaka. 36 Mukhale ngati anthu amene akuyembekezela mbuye wawo kuti abwele kucokela ku phwando la ukwati, n’colinga coti akafika ndi kugogoda am’tsegulile nthawi yomweyo. 37 Acimwemwe ndi akapolo omwe mbuye wawo pofika adzawapeza ali maso! Ndithu ndikukuuzani, iye adzavala zovala kuti ayambe kuwatumikila, ndipo adzawauza kuti adye naye pathebulo n’kumawatumikila. 38 Ndipo ngati angafike paulonda waciwili,* ngakhale wacitatu,* n’kuwapeza ali okonzeka, iwo adzakhala acimwemwe! 39 Koma dziwani izi, ngati mwininyumba angadziwe ola limene mbala ingabwele, sangalole kuti mbalayo ithyole n’kulowa m’nyumba mwake. 40 Inunso khalani okonzeka, cifukwa pa ola limene simukuganizila, Mwana wa munthu adzafika.”
41 Ndiyeno Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi mukuuza ife tokha fanizo ili kapena mukuuzanso aliyense?” 42 Ambuye anati: “Ndani kwenikweni amene ali woyang’anila* wokhulupilika komanso wanzelu, amene mbuye wake adzamuika kuti aziyang’anila gulu la anchito ake,* ndiponso kuwapatsa cakudya pa nthawi yoyenela? 43 Kapoloyo adzakhala wacimwemwe ngati mbuye wake pobwela adzamupeza akucita zimenezo! 44 Ndithu ndikukuuzani, adzamuika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse. 45 Koma ngati kapoloyo mumtima mwake anganene kuti, ‘Mbuye wanga akucedwa,’ ndiyeno n’kuyamba kumenya anchito anzake aamuna komanso aakazi ndiponso n’kumadya, kumwa ndi kuledzela, 46 mbuye wa kapoloyo adzabwela pa tsiku limene iye sakuliyembekezela, komanso pa ola limene sakulidziwa. Pamenepo adzamupatsa cilango cowawa zedi, n’kumuika pamodzi ndi anthu osakhulupilika. 47 Ndiyeno kapolo amene anadziwa zimene mbuye wake anali kufuna, koma sanakhale wokonzeka kapena kucita zimene mbuye wakeyo anamupempha,* adzakwapulidwa zikoti zambili. 48 Koma amene sanadziwe ndipo anacita zinthu zomukwapulitsa, adzakwapulidwa zikoti zocepa. Ndithudi, aliyense wopatsidwa zambili, zambilinso zidzafunidwa kwa iye. Ndipo amene anaikidwa kuyang’anila zoculuka, zoculukanso zidzafunidwa kwa iye.
49 “Ine ndinabwela kudzayatsa moto padziko lapansi. Ndiye ndingafunenso ciyani ngati motowo wayatsidwa kale? 50 Ndithudi, pali ubatizo winawake umene ndiyenela kubatizika nawo, ndipo ndikuvutika kwambili m’maganizo kufikila utacitika! 51 Kodi muganiza ndinabwela padziko lapansi kudzakupatsani mtendele? Ayi ndithu, koma kudzagawanitsa anthu. 52 Pakuti kuyambila tsopano, anthu asanu a m’nyumba imodzi adzasemphana maganizo. Atatu kukangana ndi awili, awili kukangana ndi atatu. 53 Iwo adzagawikana. Tate adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, ndipo mwana wamwamuna adzakangana ndi atate ake. Mayi adzakangana ndi mwana wake wamkazi, ndipo mwana wamkazi adzakangana ndi amayi ake. Apongozi aakazi adzakangana ndi mkazi wa mwana wawo, ndipo mkazi wokwatiwa adzakangana ndi apongozi ake aakazi.”
54 Ndiyeno anauzanso khamu la anthulo kuti: “Mukaona mtambo kumadzulo ukukwela m’mwamba, nthawi yomweyo mumati, ‘Kukubwela cimvula,’ ndipo zimacitikadi. 55 Ndipo mukaona mphepo ya kum’mwela ikuwomba, mumati, ‘Kudzatentha,’ ndipo zimacitikadi. 56 Onyenga inu, mumadziwa maonekedwe a dziko lapansi ndi kumwamba, nanga n’cifukwa ciyani simudziwa tanthauzo la zimene zikucitika pa nthawi ino? 57 N’cifukwa ciyani panokha simudziwa cimene cili colungama? 58 Mwacitsanzo, ukamapita kwa wolamulila ndi munthu wokuimba mlandu, muli m’njila uziyesetsa kukamba naye kuti uthetse mlanduwo. Uzicita zimenezi kuti mwina iye asakakupeleke kwa woweluza, komanso kuti woweluzayo asakakupeleke kwa msilikali wapakhoti, msilikaliyo n’kukuponya m’ndende. 59 Ndikukuuza kuti, sudzatulukamo mpaka utalipila kakhobili kothela.”*