Kwa Aroma
8 Conco anthu ogwilizana ndi Khristu Yesu alibe mlandu. 2 Pakuti lamulo la mzimu limene limapatsa moyo mogwilizana ndi Khristu Yesu, lakumasulani ku lamulo la ucimo ndi imfa. 3 Cilamulo sicinathe kukumasulani cifukwa anthu ndi ofooka komanso ocimwa. Koma Mulungu anakumasulani mwa kutumiza Mwana wake ali ndi thupi ngati la anthu ocimwa kuti athane ndi ucimo. Conco Mulungu anagonjetsa ucimo mwa kugwilitsa nchito thupi. 4 Mulungu anacita izi kuti ife amene timayenda motsogoleledwa ndi mzimu, osati motsogoleledwa ndi zofuna za thupi, tikwanilitse zolungama zimene Cilamulo cimafuna. 5 Cifukwa otsatila zofuna za thupi, amaika maganizo awo pa zinthu za thupi, koma otsatila mzimu, amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu. 6 Pakuti kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweletsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele. 7 Cifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi kumapangitsa munthu kukhala pa udani ndi Mulungu popeza thupi siligonjela lamulo la Mulungu, ndipo kukamba zoona silingaligonjele. 8 Conco amene amacita zofuna za thupi sangakondweletse Mulungu.
9 Komabe inu simukucita zofuna za thupi koma za mzimu, ngati mzimu wa Mulungu ulidi mwa inu. Koma ngati wina alibe mzimu wa Khristu, ndiye kuti munthu ameneyo si wa Khristu. 10 Ngati Khristu ndi wogwilizana ndi inu, ngakhale kuti thupi ndi lakufa cifukwa ca ucimo, mzimu umacititsa kuti mukhale ndi moyo cifukwa ca cilungamo. 11 Tsopano ngati mzimu wa amene anaukitsa Yesu kwa akufa uli mwa inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu adzacititsanso matupi anu amene angathe kufawo kukhala ndi moyo, kupitila mwa mzimu wake umene uli mwa inu.
12 Conco abale, tisalole matupi athu kumatilamulila n’kumacita zinthu zimene matupiwo amafuna. 13 Cifukwa ngati mumacita zofuna za thupi, ndithu mudzafa. Koma mukalola mphamvu ya mzimu kupha nchito za thupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Pakuti onse otsogoleledwa ndi mzimu wa Mulungu, alidi ana a Mulungu. 15 Cifukwa simunalandile mzimu wa ukapolo wokupangitsani kukhalanso ndi mantha, koma munalandila mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: “Abba,* Atate!” 16 Mzimuwo umacitila umboni pamodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu. 17 Conco ngati ndife ana ake, ndiye kuti ndifenso olandila colowa kucokela kwa Mulungu. Koma tidzalandilanso colowa pamodzi ndi Khristu, ngati tikuvutika naye limodzi kuti tikalandile naye ulemelelo.
18 Ndikuona kuti mavuto amene tikukumana nawo palipano ndi aang’ono powayelekezela ndi ulemelelo umene udzaonekele kudzela mwa ife. 19 Cifukwa cilengedwe cikuyembekezela mwacidwi nthawi imene ulemelelo wa ana a Mulungu udzaonekela. 20 Pakuti cilengedwe cinaweluzidwa kuti cikhale copanda pake, osati mwa kufuna kwake koma kudzela mwa amene anaciweluza. Ndipo anapelekanso ciyembekezo 21 cakuti cilengedweco naconso cidzamasulidwa ku ukapolo wa thupi limene limawonongeka, n’kukhala ndi ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu. 22 Pakuti tikudziwa kuti cilengedwe conse pamodzi cikubuula komanso kumva zowawa mpaka pano. 23 Koma sizokhazi. Ifeyo amene tili ndi zipatso zoyambilila zimene ndi mzimu, tikubuula mu mtima mwathu pamene tikuyembekezela mwacidwi kuti Mulungu atitenge kukhala ana ake, kutimasula ndi dipo ku matupi athuwa. 24 Cifukwa tinapulumutsidwa tili ndi ciyembekezo cimeneci, koma cimene ukuciyembekezela cikacitika, sicikhalanso ciyembekezo. Kodi cimene munthu anali kuyembekezela cikacitika, amaciyembekezelabe? 25 Koma ngati zimene tikuyembekezela sizinacitike, timapitiliza kuziyembekezela mwacidwi komanso mopilila.
26 Mofananamo, mzimu umatithandiza pa zimene timalephela kucita. Cifukwa vuto n’lakuti sitidziwa zimene tikufunika kuchula popemphela, koma mzimu umacondelela m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. 27 Koma iye amene amafufuza mitima amadziwa zimene mzimu ukutanthauza, cifukwa umacondelela m’malo mwa oyela mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.
28 Tikudziwa kuti Mulungu amagwilizanitsa zocita zake zonse pofuna kuthandiza amene amakonda Mulunguyo, anthu amene anawaitana mogwilizana ndi colinga cake. 29 Amatelo cifukwa amene anawadziwa coyamba anawasankhilatu kuti akakhale ofanana ndi Mwana wake, kuti iye akhale woyamba kubadwa pakati pa abale ake ambili. 30 Kuwonjezela apo, amene anawasankhilatuwo ndi amenenso anawaitana. Ndipo amene anawaitanawo ndi amenenso iye amawaona kuti ndi olungama. Ndipo anthu amene amawaona kuti ndi olungamawo ndi amenenso anawapatsa ulemelelo.
31 Ndiye kodi tinene ciyani pamenepa? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe? 32 Popeza sanatimane ngakhale Mwana wake koma anamupeleka m’malo mwa ife tonse, kodi sangatipatsenso mokoma mtima zinthu zina zonse pamodzi ndi Mwana wakeyo? 33 Ndani adzaimba mlandu anthu a Mulungu osankhidwa? Popeza Mulungu ndi amene amawaona kuti ndi olungama, 34 ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndi amene anafa. Inde, kuwonjezela pamenepo ndi amene anaukitsidwa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndipo amacondelela m’malo mwathu.
35 Ndani adzatilekanitsa ndi cikondi ca Khristu? Kodi ndi masautso, zothetsa nzelu, mazunzo, njala, usiwa, zoopsa, kapena lupanga? 36 Malemba amati: “Cifukwa ca inu, tikuphedwa nthawi zonse. Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.” 37 Koma tikugonjetsa zinthu zonsezi kothelatu mothandizidwa ndi iye amene anatikonda. 38 Pakuti ndatsimikiza mtima kuti kaya imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwela, mphamvu, 39 msinkhu, kuzama, kapena colengedwa ciliconse, sizidzatha kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu cimene cili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.