Kalata Yoyamba kwa Akorinto
3 Conco abale, sindinalankhule nanu ngati anthu auzimu, koma ngati anthu okonda zinthu za mʼdzikoli, ngati makanda mwa Khristu. 2 Ndinakupatsani mkaka, osati cakudya cotafuna, cifukwa munali musanalimbe mokwanila. Ndipo mpaka pano simunalimbebe, 3 pakuti mukuganizabe ngati anthu a m’dzikoli.* Popeza pakati panu pali nsanje ndiponso kukangana, kodi si ndiye kuti ndinu akuthupi, ndipo mukuyenda ngati anthu a m’dzikoli? 4 Ngati wina akunena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” koma wina n’kumati: “Ine ndine wa Apolo,” kodi si ndiye kuti mwangofanana ndi anthu a dziko?
5 Kodi Apolo ndani? Nanga Paulo ndani? Ife ndife cabe atumiki amene tinakuthandizani kukhala okhulupilila, mogwilizana ndi nchito imene Ambuye anapatsa aliyense wa ife. 6 Ine ndinabzala, Apolo anathilila, koma Mulungu ndiye anakulitsa. 7 Conco wofunika kwambili si wobzala kapena wothilila, koma Mulungu amene amakulitsa. 8 Wobzala ndi wothilila amakhala ndi colinga cimodzi,* koma aliyense adzalandila mphoto yake malinga ndi nchito yake. 9 Pakuti ndife anchito anzake a Mulungu. Inu ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa, nyumba ya Mulungu.
10 Mogwilizana ndi cisomo ca Mulungu cimene ndinacitilidwa, ndinayala maziko ngati munthu waluso* pa nchito zomangamanga. Koma amene akumanga pamaziko amenewo ndi munthu wina. Conco aliyense asamale mmene akumangilapo. 11 Cifukwa palibe munthu wina amene angayale maziko ena kupatulapo amene anayalidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. 12 Tsopano ngati anthu akumanga pamazikowo ndi golide, siliva, miyala yamtengo wapatali, mitengo, udzu kapena mapesi, 13 nchito ya aliyense idzadziwika kuti ndi yotani.* Tsiku lina nchitoyo idzadziwika mmene ilili, cifukwa moto ndi umene udzaionetsa poyela. Ndipo motowo udzaonetsa kuti nchito ya munthu aliyense ndi yotani. 14 Ngati zimene munthu wamanga pamazikowo zidzakhalapobe, munthuyo adzalandila mphoto. 15 Ngati zimene wamangazo zidzapsya ndi moto, ndiye kuti zake zatayika, koma iyeyo adzapulumuka. Komabe zidzakhala monga wapulumuka pamoto.
16 Kodi inu simudziwa kuti ndinu kacisi wa Mulungu ndipo mzimu wa Mulungu ukukhala mwa inu? 17 Munthu aliyense ngati waononga kacisi wa Mulungu, Mulungu adzamuononga munthuyo, pakuti Mulungu ndi woyela, ndipo inu ndinu kacisiyo.
18 Munthu asamadzinamize. Ngati wina wa inu akuganiza kuti ndi wanzelu nthawi* ino, akhale wopusa kuti akhale wanzelu. 19 Kwa Mulungu, nzelu za m’dzikoli n’zopusa, cifukwa Malemba amati: “Iye amacititsa kuti anthu anzelu agwele m’misampha yao.” 20 Amanenanso kuti: “Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu anzelu ndi opanda pake.” 21 Conco pasakhale wina wodzitama cifukwa ca anthu, popeza zinthu zonse ndi zanu, 22 kaya Paulo, Apolo, Kefa,* dziko, moyo, imfa, zinthu zimene zilipo kapena zimene zikubwela, zonse ndi zanu. 23 Inu ndinu a Khristu ndipo Khristu ndi wa Mulungu.