Macitidwe a Atumwi
24 Patapita masiku asanu, mkulu wa ansembe Hananiya anabwela pamodzi ndi akulu ena, komanso munthu wina wodziwa kulankhula,* dzina lake Teritulo. Iwo anafotokoza mlandu wa Paulo kwa bwanamkubwayo. 2 Teritulo atapatsidwa mwayi wolankhula, anayamba kuimba mlandu Paulo kuti:
“Ife tikusangalala ndi mtendele waukulu cifukwa ca inu. Komanso cifukwa ca nzelu zanu zoona patali. Zinthu zikusintha mu mtundu wathuwu. 3 Conco nthawi zonse komanso kulikonse timaona zimenezi, inu Wolemekezeka a Felike, ndipo timayamikila kwambili. 4 Koma kuti ndisakutayitseni nthawi, ndikukupemphani mwa kukoma mtima kwanu kuti mutimvetseleko pang’ono. 5 Ife tapeza kuti munthu uyu ndi kadoyo kowononga,* iye akuyambitsa zoukila boma pakati pa Ayuda ndi dziko lonse. Ndipo akutsogolela gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti. 6 Iye anali kufunanso kudetsa kacisi, conco tinamugwila. 7* —— 8 Mukamufunsa, mupeza kuti zonse zimene tikunenazi, n’zoona.”
9 Atakamba zimenezi, Ayuda nawonso analowelelapo n’kuyamba kutsimikizila kuti zinthuzo zinali zoona. 10 Bwanamkubwayo atagumulila mutu Paulo kuti alankhule, Paulo anayankha kuti:
“Podziwa bwino kuti inu mwakhala woweluza wa mtundu uwu kwa zaka zambili, ndine wokonzeka kulankhula kuti ndidziteteze. 11 Inu mukhoza kupeza umboni wotsimikizila kuti sipanapite masiku 12 kucokela pamene ndinapita ku Yerusalemu kukalambila. 12 Ndipo anthu awa sanandipeze kuti ndikukangana ndi wina aliyense m’kacisi, kapena kuyambitsa cipolowe m’masunagoge, kapenanso pena paliponse mumzinda wonsewo. 13 Ndipo pano anthu awa sangapeleke umboni wotsimikizila zinthu zimene akundinenezazi. 14 Koma cinthu cimene ndikuvomeleza kwa inu n’cakuti: Njila imene iwowa akuichula kuti gulu lampatuko, ndi imene ine ndikuitsatila pocita utumiki wopatulika kwa Mulungu wa makolo anga akale. Cifukwa ndimakhulupilila zinthu zonse za m’Cilamulo, komanso zolemba za aneneli. 15 Ndipo ine ndili ndi ciyembekezo ngati cimenenso anthu awa ali naco, kuti Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe. 16 Cifukwa ca izi, ndimayesetsa kukhala ndi cikumbumtima cabwino kwa Mulungu komanso kwa anthu. 17 Ndiyeno pambuyo pa zaka zambili, ndinabwela kudzapeleka mphatso za cifundo kwa anthu a mtundu wanga, komanso kudzapeleka nsembe. 18 Pamene ndinali kucita zimenezi, anthu awa anandipeza m’kacisi nditadziyeletsa motsatila mwambo. Panalibe khamu la anthu kapena cipolowe, koma panali Ayuda ena ocokela m’cigawo ca Asia. 19 Iwo akanakhala nane n’cifukwa, ndi amene akanayenela kubwela kwa inu kudzandiimba mlandu. 20 Kapena muwalole anthu ali panowa kuti akambe okha ngati anandipeza ndi mlandu nditaimilila pamaso pa Bungwe Lalikulu la Ayuda.* 21 Mawu amodzi okha amene ndinakamba pamene ndinaimilila pakati pawo ndi akuti: ‘Lelo ndikuweluzidwa pamaso panu cifukwa ca ciyembekezo cakuti akufa adzauka’”
22 Koma popeza Felike anali kudziwa bwino nkhani yonse yokhudza Njila imeneyi, anaimitsa mlanduwo ndipo anati: “Mkulu wa asilikali Lusiya akadzabwela, ndidzapeleka cigamulo pa nkhani yanu imeneyi.” 23 Iye analamula mtsogoleli wa asilikali kuti amusungebe m’ndende. Koma anam’patsako ufulu woti azilola anzake kudzamuthandiza pa zofunikila zake.
24 Patapita masiku angapo Felike anafika pamodzi ndi mkazi wake Durusila, amene anali Myuda. Kenako Felike anaitanitsa Paulo ndipo anamumvetsela pamene anali kufotokoza za kukhulupilila Khristu Yesu. 25 Koma pamene Paulo anali kukamba za cilungamo, kudziletsa, komanso ciweluzo cimene cikubwela, Felike anacita mantha moti anati: “Pita coyamba, ndikadzapeza nthawi, ndidzakuitananso.” 26 Pa nthawi imodzimodzi, iye anali kuyembekezela kuti Paulo amupatsa ndalama. Conco anali kumuitanitsa pafupipafupi n’kumakambilana naye. 27 Koma patapita zaka ziwili, Felike analowedwa m’malo ndi Porikiyo Fesito. Ndipo popeza Felike anali kufuna kuti Ayuda azimukonda, anangomusiya m’ndende Paulo.