Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
20 Tsiku lina Yesu akuphunzitsa anthu m’kacisi ndi kulengeza uthenga wabwino, ansembe aakulu, alembi pamodzi ndi akulu anabwela, 2 ndipo anamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi ulamulilo wocita zimenezi munautenga kuti? Nanga ndani anakupatsani ulamulilo umenewu?” 3 Iye anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani funso, ndipo mundiyankhe: 4 Kodi ubatizo wa Yohane unacokela kumwamba kapena kwa anthu?” 5 Pamenepo iwo anayamba kukambilana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unacokela kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciyani simunamukhulupilile?’ 6 Komanso sitingakambe kuti, ‘Unacokela kwa anthu,’ cifukwa onse angatiponye miyala, popeza iwo amakhulupilila kuti Yohane anali mneneli.” 7 Conco iwo anayankha kuti sadziwa kumene unacokela. 8 Yesu anati: “Inenso sindikuuzani kumene ndinatenga ulamulilo wocita zimenezi.”
9 Ndiyeno iye anayamba kuuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wampesa, kenako anausiya m’manja mwa alimi n’kupita ku dziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali. 10 Nyengo yokolola itakwana, iye anatuma kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso za m’munda wampesawo. Koma alimiwo anam’menya ndi kumubweza cimanjamanja. 11 Iye anatumanso kapolo wina. Koma nayenso anamumenya ndi kumucita zacipongwe,* ndipo anamubweza cimanjamanja. 12 Ngakhale n’telo, iye anatumanso wacitatu. Koma nayenso anamuvulaza ndi kumuthamangitsa. 13 Mwinimunda wa mpesa uja ataona izi anati, ‘Ndiye ndicite ciyani pamenepa? Cabwino, nditumiza mwana wanga wokondeka. Mosakayikila iwo adzamulemekeza.’ 14 Alimiwo atamuona mwanayo anayamba kukambilana kuti, ‘Eya! uyu ndiye wolandila colowa. Tiyeni timuphe kuti colowaci cikhale cathu.’ 15 Conco iwo anamutulutsila kunja kwa munda wampesawo ndi kumupha. Ndiye kodi mwinimundayo adzawacita ciyani alimiwo? 16 Adzabwela n’kuwapha alimiwo, ndipo adzapeleka mundawo kwa ena.”
Anthuwo atamva zimenezi anati: “Izi siziyenela kucitika!” 17 Koma iye anawayang’anitsitsa n’kunena kuti: “Kodi Malemba amatanthauzanji ponena kuti: ‘Mwala umene omanga anaukana wakhala mwala wapakona wofunika kwambili’?* 18 Aliyense wogwela pa mwalawo adzaphwanyika. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwele udzamupelelatu.”
19 Ndiyeno alembi ndi ansembe aakulu, anadziwa kuti Yesu ponena fanizo limeneli anali kukamba za iwo. Conco anafuna kumugwila nthawi yomweyo koma anaopa anthu. 20 Ndiyeno iwo atayang’anitsitsa mmene iye anali kucitila zinthu, mwakabisila analemba ganyu akazitape kuti akadzipange kukhala olungama n’colinga coti akamutape m’kamwa. Iwo anacita izi kuti akamupeleke ku boma komanso kwa bwanamkubwa. 21 Conco anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tidziwa kuti zimene mumakamba ndi kuphunzitsa n’zolondola, ndipo mulibe tsankho. Mumaphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi: 22 Kodi n’kololeka* kuti ife tizipeleka misonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 23 Koma iye atazindikila ukambelembele wawo anawauza kuti: 24 “Ndionetseni khobili la dinari. Kodi cithunzi ndi mawu omwe ali pamenepo ndi za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” 25 Iye anawauza kuti: “Conco, pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara koma za Mulungu kwa Mulungu.” 26 Iwo analephela kumutapa m’kamwa pa zimene ananena pamaso pa anthu, koma anadabwa ndi yankho lake, ndipo anangokhala cete.
27 Komabe, Asaduki ena amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwela n’kumufunsa kuti: 28 “Mphunzitsi, Mose anatilembela kuti, ‘Ngati mwamuna wamwalila n’kusiya mkazi, koma sanabeleke naye mwana, m’bale wake wa mwamunayo ayenela kukwatila mkazi wamasiyeyo ndi kumubelekela ana m’bale wake uja.’ 29 Tsopano panali amuna 7 apacibale. Woyamba anakwatila mkazi, koma anamwalila asanabeleke naye mwana. 30 Zinacitika cimodzimodzi kwa waciwili. 31 Kenako wacitatu anamukwatila. Zinacitikanso cimodzimodzi ngakhale kwa onse 7, onse anamwalila osabeleka naye ana. 32 Pamapeto pake mkazi uja nayenso anamwalila. 33 Malinga ndi mmene zinakhalilamu, pamene akufa adzauka, kodi mkaziyo adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatilapo?”
34 Yesu anawauza kuti: “Ana a m’nthawi* ino amakwatila ndi kukwatiwa. 35 Koma amene aonedwa kuti ndi oyenelela kudzapeza moyo m’nthawi ikubwelayo n’kudzaukitsidwa kucokela kwa akufa, sadzakwatila kapena kukwatiwa. 36 Ndiponso iwo sadzafanso, cifukwa adzakhala monga angelo. Ndipo iwo ndi ana a Mulungu pokhala ana a kuuka kwa akufa. 37 Koma zakuti akufa amauka, ngakhale Mose anafotokoza m’nkhani yokhudza citsamba caminga, pamene anakamba kuti Yehova ‘ndi Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki, komanso Mulungu wa Yakobo.’ 38 Iye si Mulungu wa akufa ayi, koma wa anthu amoyo, pakuti kwa iye onse ndi amoyo.”* 39 Poyankha, ena mwa alembiwo anati: “Mphunzitsi, mwakamba bwino.” 40 Iwo anakamba izi cifukwa sanalimbenso mtima kuti amufunse funso lina.
41 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani anthu amakamba kuti Khristu ndi mwana wa Davide? 42 Cifukwa Davide iyemwini, m’buku la Masalimo ananena kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43 kufikila n’taika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’ 44 Davide anamuchula kuti Ambuye, ndiye akhala bwanji mwana wake?”
45 Kenako anthu onse akumvetsela, iye anauza ophunzila ake kuti: 46 “Samalani ndi alembi amene amakonda kumayendayenda atavala mikanjo, amenenso amakonda kupatsidwa moni m’misika. Iwo amakondanso kukhala pa mipando yakutsogolo* m’masunagoge, komanso pa malo olemekezeka kwambili pa cakudya camadzulo. 47 Iwo amalandanso cuma ca akazi* amasiye, komanso amapeleka mapemphelo ataliatali pofuna kudzionetsela.* Amenewa adzalandila cilango cowawa kwambili.”*