Kalata Yoyamba kwa Akorinto
14 Khalani ndi cikondi, koma yesetsani kuti mulandile mphatso zauzimu, maka-maka mphatso ya kulosela. 2 Pakuti wolankhula malilime salankhula ndi anthu, koma amalankhula ndi Mulungu. Cifukwa palibe amene amamva zimene akulankhula, koma amalankhula zinsinsi zopatulika mothandizidwa ndi mzimu. 3 Komabe wolosela amathandiza, kulimbikitsa, komanso kutonthoza anthu ndi mau ake. 4 Wolankhula malilime amadzilimbikitsa yekha, koma wolosela amalimbikitsa mpingo. 5 Ndikanakonda kuti nonsenu muzilankhula malilime, koma comwe ndingakonde kwambili ndi coti muzilosela. Ndithudi wolosela amaposa wolankhula malilime, pokhapo wolankhula malilimeyo atamasulila kuti mpingo ulimbikitsidwe. 6 Abale, ngati panthawi ino ndingabwele kwa inu ndikulankhula malilime, kodi mungapindulepo ciani ngati simukuwadziwa? Zingakhale zothandiza ngati ndingabwele kwa inu ndi bvumbulutso locokela kwa Mulungu, kapena mphatso yodziwa zinthu, kapena kulosela, kapenanso kuphunzitsa.
7 N’cimodzi-modzinso ndi zipangizo zoimbila monga citolilo kapena zeze. Ngati malilidwe a citolilo kapena zeze sasintha-sintha, kodi zingatheke bwanji kudziwa nyimbo imene ikuimbidwa? 8 Ngati lipenga silikulila momveka bwino, ndani angakonzekele nkhondo? 9 Mofananamo, ngati mukulankhula zinthu zobvuta kumvetsa, kodi munthu angadziwe bwanji zimene mukunena? Mudzakhala mukulankhula ku mphepo. 10 Padziko lapansi pali zinenelo zambili, koma palibe ngakhale cimodzi cimene cilibe tanthauzo. 11 Ngati sindikumva tanthauzo la zimene munthu akulankhula, ndimakhala mlendo kwa munthu wolankhulayo, ndipo amene akulankhulayo amakhala mlendo kwa ine. 12 N’cimodzi-modzinso ndi inu, pakuti mukufunitsitsa mphatso za mzimu, muziyesetsa kukhala ndi mphatso zimene zingalimbikitse mpingo.
13 Conco amene amalankhula malilime, apemphele kuti azitha kumasulila. 14 Pakuti ngati ndikupemphela m’malilime, mphatso yanga ya mzimu ndi imene ikupemphela, koma maganizo anga sakucita ciliconse. 15 Ndiye ndicite ciani? Ndidzapemphela ndi mphatso ya mzimu, ndipo ndidzapemphelanso ndi maganizo anga. Ndidzaimba nyimbo zotamanda ndi mphatso ya mzimu, koma ndidzaimbanso nyimbo zotamanda ndi maganizo anga. 16 Ngati mukutamanda Mulungu ndi mphatso ya mzimu, kodi munthu wamba amene ali pakati panu adzanena bwanji kuti “ameni” pa pemphelo lanu loyamikila, pakuti munthuyo sakudziwa zimene mukukamba? 17 N’zoona kuti mukupeleka pemphelo loyamikila Mulungu m’njila yabwino, koma munthu winayo sakulimbikitsidwa. 18 Ndimayamika Mulungu kuti ndimalankhula zinenelo* zambili kuposa nonsenu. 19 Ngakhale n’telo, ndi bwino kuti mumpingo ndizilankhula mau asanu omveka bwino* kuti ndiphunzitsenso ena, m’malo molankhula mau 10,000 m’cinenelo* cacilendo.
20 Abale, musakhale ana aang’ono pa kumvetsa zinthu. Koma khalani ana aang’ono ku zinthu zoipa. Ndipo khalani aakulu pa nkhani yomvetsa zinthu. 21 M’Cilamulo muli mau akuti: “‘Ndi malilime a anthu acilendo komanso milomo ya anthu acilendo, ndidzalankhula ndi anthu awa. Ngakhale n’telo, iwo adzakana kundimvela,’ watelo Yehova.” 22 Conco malilime si cizindikilo ca anthu okhulupilila, koma anthu osakhulupilila. Pamene kulosela ndi cizindikilo ca anthu okhulupilila, osati osakhulupilila. 23 Conco ngati mpingo wonse wasonkhana pamodzi, ndipo onse akulankhula malilime, ndiyeno anthu wamba kapena osakhulupilila alowa, kodi iwo sadzanena kuti mwacita misala? 24 Koma ngati nonse mukulosela, ndipo munthu wosakhulupilila kapena munthu wamba walowa, iye adzadzudzulidwa komanso kufufuzidwa mosamala ndi nonsenu. 25 Ndiyeno zinsinsi za mumtima mwake zimaonekela, moti amawelama n’kulambila Mulungu, ndipo amalengeza kuti: “Mulungu alidi pakati panu.”
26 Ndiye zinthu zizicitika motani abale? Mukasonkhana pamodzi, wina angakhale ndi salimo, wina kuphunzitsa, wina bvumbulutso, wina kulankhula cinenelo* cacilendo, wina n’kumamasulila. Muzicita zonsezi kuti mulimbikitsane. 27 Ngati pali anthu olankhula zinenelo* zacilendo, azingokhala awili kapena atatu basi, ndipo azilankhula mopatsana mpata, komanso wina azimasulila. 28 Koma ngati palibe womasulila, wolankhula malilimeyo azikhala cete mumpingo, ndipo azikamba ndi Mulungu camumtima. 29 Aneneli awili kapena atatu azilankhula, ndipo ena onse azimvetsa tanthauzo lake. 30 Koma ngati wina walandila bvumbulutso locokela kwa Mulungu ali khale pansi, woyamba uja azikhala cete. 31 Pakuti nonse mungalosele, koma mopatsana mpata kuti onse aphunzile komanso kulimbikitsidwa. 32 Ndipo aneneli ayenela kukhala odziletsa akamagwilitsa nchito mphatso za mzimu woyela. 33 Pakuti Mulungu si Mulungu wacisokonezo, koma wamtendele.
Monga mmene zilili m’mipingo yonse ya oyelawo, 34 akazi azikhala cete m’mipingo, pakuti n’kosaloleka kuti azilankhula. M’malomwake, iwo azigonjela monga mmene Cilamulo cimakambila. 35 Ngati iwo akufuna kumvetsa zinazake, azifunsa amuna ao kunyumba, pakuti n’zocititsa manyazi mkazi kulankhula ndi mpingo.*
36 Kodi mau a Mulungu anacokela kwa inu, kapena anangofika kwa inu nokha basi?
37 Ngati wina akuganiza kuti ndi mneneli, kapena ali ndi mphatso ya mzimu, abvomeleze kuti zinthu izi zimene ndakulembelani ndi lamulo la Ambuye. 38 Koma ngati wina akunyalanyaza zimenezi, nayenso adzanyalanyazidwa.* 39 Conco abale anga, yesetsani kuti muzilosela, komabe musaletse kulankhula malilime.* 40 Koma zinthu zonse zizicitika moyenela ndi mwadongosolo.