Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
9 Ndiyeno Yesu anasonkhanitsa atumwi ake 12 aja n’kuwapatsa mphamvu ndi ulamulilo kuti azitha kutulutsa ziwanda zonse ndi kucilitsa matenda. 2 Iye anawatumiza kuti akalalikile za Ufumu wa Mulungu, komanso kucilitsa anthu. 3 Anawauza kuti: “Musanyamule ciliconse pa ulendowu, kaya ndodo, cola ca zakudya, mkate, ndalama,* kapena zovala ziwili.* 4 Koma nthawi zonse mukalowa m’nyumba, muzikhala mmenemo mpaka nthawi yocoka kumeneko. 5 Ndipo kulikonse kumene anthu sakakulandilani, pocoka mu mzindawo muzikutumula fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni wowatsutsa.” 6 Ndiyeno ananyamuka n’kuyamba kuyenda m’cigawoco mudzi ndi mudzi akulengeza uthenga wabwino ndi kucilitsa anthu kulikonse.
7 Tsopano Herode* wolamulila cigawo* ca Galileya, anamva zonse zimene zinali kucitika. Iye anadabwa kwambili, cifukwa anthu ena anali kunena kuti Yohane waukitsidwa kwa akufa. 8 Koma ena anali kunena kuti Eliya waonekela, ndipo ena anali kunena kuti mmodzi wa aneneli akale wauka. 9 Herode anati: “Yohane ndinamudula mutu, nanga amene akucita zimene ndikumvazi ndani?” Conco iye anali kufunitsitsa kuona Yesu.
10 Atumwiwo atabwelako, anafotokozela Yesu zonse zimene iwo anacita. Pambuyo pake, iye anawatenga n’kupita nawo kwaokha ku mzinda wochedwa Betsaida. 11 Koma khamu la anthu litadziwa zimenezi linamutsatila, ndipo iye anawalandila mokoma mtima. Kenako anayamba kuwauza za Ufumu wa Mulungu, komanso anacilitsa odwala. 12 Ndiyeno madzulo tsiku limenelo, atumwi ake 12 aja anabwela kwa iye n’kumuuza kuti: “Uzani khamu la anthuwa kuti apite m’midzi ya pafupi ndi m’madela ozungulila kuti akapezeko malo ogona komanso cakudya, cifukwa kuno tili n’kopanda anthu.” 13 Koma iye anawauza kuti: “Inuyo muwapatse cakudya.” Iwo anati: “Tili cabe ndi mitanda isanu ya mkate ndi nsomba ziwili. Kapena mwina tipite ndife kukagula cakudya ca anthu onsewa?” 14 Panali amuna pafupifupi 5,000. Koma iye anauza ophunzila ake kuti: “Auzeni anthuwa kuti akhale pansi m’magulumagulu a anthu pafupifupi 50.” 15 Ophunzilawo anatelo, ndipo anthu onsewo anakhala pansi. 16 Atatenga mitanda isanu ija ndi nsomba ziwili zija, anayang’ana kumwamba n’kuzidalitsa. Kenako anazinyemanyema n’kuyamba kuzipeleka kwa ophunzila ake kuti agawile khamu la anthulo. 17 Cotelo onse anadya n’kukhuta. Zotsala anazisonkhanitsa pamodzi, ndipo zinadzaza matadza 12.
18 Patapita nthawi Yesu akupemphela kwayekha, ophunzila ake anabwela kwa iye, ndipo anawafunsa kuti: “Kodi anthu amati ndine ndani?” 19 Iwo poyankha anati: “Amati ndinu Yohane M’batizi, koma ena amati ndinu Eliya. Ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneli akale amene wauka.” 20 Ndiyeno anafunsa ophunzilawo kuti: “Nanga inu mumati ndine ndani?” Petulo anamuyankha kuti: “Ndinu Khristu wa Mulungu.” 21 Ndiyeno anawalamula mwamphamvu kuti asauzeko aliyense zimenezi. 22 Iye anakambanso kuti: “Mwana wa munthu ayenela kukumana ndi masautso ambili, ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu, komanso alembi, kenako adzaphedwa. Ndipo pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa.”
23 Ndiyeno anauza onsewo kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatila adzikane yekha, ndipo anyamule mtengo wake wozunzikilapo* tsiku ndi tsiku n’kupitiliza kunditsatila. 24 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine ndi amene adzaupeza. 25 Kunena zoona, kodi pali phindu lanji munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli, koma n’kutaya moyo wake kapena kudzivulaza? 26 Pakuti aliyense wocita manyazi ndi ine komanso mawu anga, Mwana wa munthu adzacitanso naye manyazi akadzabwela mu ulemelelo wake, wa Atate wake, komanso wa angelo oyela. 27 Koma ndithu ndikukuuzani, pali ena pano amene sadzalawa imfa ngakhale pang’ono, mpaka coyamba ataona Ufumu wa Mulungu.”
28 Patapita masiku pafupifupi 8 Yesu atakamba mawu amenewa, anatenga Petulo, Yohane, ndi Yakobo n’kukwela nawo m’phili kukapemphela. 29 Ali mkati mopemphela, maonekedwe a nkhope yake anasintha. Zovala zakenso zinayela mbee n’kunyezimila. 30 Kenako panaonekela amuna awili akulankhula naye. Amunawo anali Mose ndi Eliya. 31 Maonekedwe awo anali aulemelelo, ndipo anayamba kukambilana za mmene Yesu adzacokele pa dziko. Izi zinali zitatsala pang’ono kukwanilitsika ku Yerusalemu. 32 Tsopano Petulo ndi amene anali naye anamva tulo kwambili. Koma tulo tutawathela, anaona ulemelelo wa Yesu komanso amuna awili ataimilila naye. 33 Pamene amunawo anali kusiyana naye, Petulo anauza Yesu kuti: “Mlangizi, zili bwino kuti ife tizikhala pompano. Ngati mufuna, ndingakhome matenti atatu pano. Ina yanu, ina ya Mose, inanso ya Eliya.” Iye sanadziwe zimene anali kukamba. 34 Koma pamene anali kukamba izi, kunacita mtambo ndipo unayamba kuwaphimba. Pamene mtambowo unali kuwaphimba, iwo anacita mantha. 35 Kenako mumtambomo munamveka mawu akuti: “Uyu ndi Mwana wanga amene ndinamusankha. Muzimumvela.” 36 Pamene mawuwo anali kumveka, iwo anangoona kuti Yesu ali yekha. Koma pa masiku amenewo, iwo anangokhala cete osauzako aliyense zimene anaonazo.
37 Tsiku lotsatila iwo atatsika m’phili muja, khamu lalikulu linamucingamila. 38 Ndiyeno munthu wina anafuula m’khamulo kuti: “Mphunzitsi, ndikukupemphani kuti mudzaone mwana wanga wamwamuna, cifukwa ndi mmodzi yekhayo. 39 Mzimu umamugwila, ndipo mwadzidzidzi amakuwa. Zikatelo, umamugwetsela pansi ndipo amayamba kupalapata uku akucoka thovu kukamwa. Komanso umavuta kuti umuleke ngakhale utamuvulaza. 40 Ndinacondelela ophunzila anu kuti autulutse koma analephela.” 41 Yesu anayankha kuti: “Inu m’badwo wopanda cikhulupililo komanso wopotoka maganizo, kodi ndikhalabe nanu ndi kukupililani mpaka liti? M’bweletse kuno mwana wako.” 42 Koma ngakhale pamene mwanayo anali kupita kwa iye, ciwandaco cinamugwetsela pansi, n’kumupangitsa kupalapata mwamphamvu. Koma Yesu anakalipila mzimu wonyansawo ndi kucilitsa mnyamatayo, ndipo anamupeleka kwa atate ake. 43 Anthu onsewo anadabwa ndi mphamvu zazikulu za Mulungu.
Pamene anthu onsewo anali kudabwa ndi zonse zimene Yesu anali kucita, iye anauza ophunzila ake kuti: 44 “Mvetselani mwachelu ndipo muzikumbukila mawu awa, cifukwa Mwana wa munthu adzapelekedwa m’manja mwa anthu.” 45 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la zimene iye anali kukamba. Zinabisidwa kwa iwo kuti asamvetse tanthauzo lake, ndipo anaopa kumufunsa tanthauzo la zimene ananenazo.
46 Kenako ophunzilawo anayamba kukangana pakati pawo zakuti wamkulu kwambili ndani. 47 Yesu atazindikila zimene anali kuganiza m’mitima yawo, anatenga mwana wamng’ono n’kumuimika pambali pake. 48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense wolandila mwana wamng’ono ngati uyu* cifukwa ca dzina langa, walandilanso ine. Ndipo aliyense wolandila ine walandilanso Iye amene anandituma. Pakuti aliyense wocita zinthu ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndiye wamkulu.”
49 Ndiyeno Yohane anati: “Mlangizi, ife taona winawake akutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndipo tamuletsa cifukwa sayenda nafe.” 50 Koma Yesu anati kwa iye: “Musamuletse, cifukwa aliyense amene satsutsana nanu ali ku mbali yanu.”
51 Masiku atayandikila* oti Yesu atengedwe kupita kumwamba, iye anatsimikiza mtima kupita ku Yerusalemu. 52 Conco anatumiza ena mwa ophunzila ake kuti atsogole. Iwo anapita ndipo anakalowa m’mudzi winawake wa Asamariya kuti akonzekele kufika kwake. 53 Koma anthu a m’mudziwo ataona kuti Yesu watsimikiza mtima kuti apita ku* Yerusalemu, sanamulandile. 54 Ophunzila ake, Yakobo ndi Yohane ataona izi, anati: “Ambuye, kodi mufuna kuti tiwaitanile moto kucokela kumwamba kuti uwanyeketse?” 55 Koma iye anaceuka n’kuwadzudzula. 56 Cotelo iwo anapita ku mudzi wina.
57 Pamene iwo anali kuyenda m’njila, munthu wina anauza Yesu kuti: “Ndikutsatilani kulikonse kumene mungapite.” 58 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga awo, ndipo mbalame za mumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibe nyumba yakeyake.”* 59 Kenako anauza munthu wina kuti: “Khala wotsatila wanga.” Munthuyo anati: “Ambuye, ndiloleni coyamba ndipite ndikaike malilo a atate anga.” 60 Koma iye anamuyankha kuti: “Aleke akufa aike akufa awo. Koma iwe pita ukalengeze Ufumu wa Mulungu kulikonse.” 61 Winanso anati: “Ine ndikutsatilani Ambuye, koma ndiloleni coyamba ndipite ndikalayile kwa a m’banja langa.” 62 Yesu anamuuza kuti: “Munthu wogwila pulawo n’kumayang’ana zinthu zakumbuyo sayenelela Ufumu wa Mulungu.”