Wolembedwa na Maliko
10 Yesu atacoka kumeneko, anapita ku madela a ku malile kwa Yudeya, kutsidya lina la Yorodani. Kumeneko, khamu lalikulu la anthu linasonkhananso kwa iye. Ndipo mwa cizoloŵezi cake, iye anayambanso kuwaphunzitsa. 2 Ndiyeno Afarisi anamufikila n’colinga cakuti amuyese. Iwo anamufunsa ngati n’kololeka mwamuna kusudzula mkazi wake. 3 Iye anawafunsa kuti: “Kodi Mose anakulamulani ciyani?” 4 Iwo anati: “Mose analola kuti mwamuna azilembela mkazi wake cikalata ca cisudzulo n’kumuleka.” 5 Koma Yesu anawauza kuti: “Iye anakulembelani lamulo limeneli cifukwa ca unkhutukumve wanu. 6 Komabe, kuyambila pa ciyambi pa cilengedwe, ‘Mulungu anawalenga mwamuna na mkazi. 7 Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya atate ake na amayi ake, 8 ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi.’ Conco iwo salinso aŵili, koma thupi limodzi. 9 Cotelo, cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” 10 Ataloŵanso m’nyumba, ophunzilawo anayamba kumufunsa za nkhaniyi. 11 Iye anawauza kuti: “Aliyense wosudzula mkazi wake n’kukwatila wina, wacita cigololo ndipo akumulakwila mkaziyo. 12 Ndipo ngati mkazi wasudzula mwamuna wake n’kukwatiwa na mwamuna wina, wacita cigololo.”
13 Lomba anthu anayamba kum’bweletsela ana aang’ono kuti awaike manja, koma ophunzila ake anawadzudzula. 14 Yesu ataona izi anakwiya kwambili, ndipo anawauza kuti: “Alekeni anawo abwele kwa ine, musawaletse, cifukwa Ufumu wa Mulungu ni wa anthu amene ali ngati ana amenewa. 15 Ndithu nikukuuzani kuti, aliyense wosalandila Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono, sadzaloŵamo ngakhale pang’ono.” 16 Ndiyeno anakumbatila anawo, kuwaika manja, n’kuyamba kuwadalitsa.
17 Pamene anali kupita, munthu wina anamuthamangila n’kugwada pamaso pake, ndipo anam’funsa kuti: “Mphunzitsi wabwino, kodi niyenela kucita ciyani kuti nikapeze moyo wosatha?” 18 Yesu anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ukunichula kuti wabwino? Palibe aliyense wabwino, koma Mulungu yekha. 19 Umadziŵa malamulo akuti: ‘Usaphe munthu, usacite cigololo, usabe, usapeleke umboni wonama, usabe mwacinyengo, ndiponso lakuti uzilemekeza atate ako na amayi ako.’” 20 Munthuyo anayankha kuti: “Mphunzitsi, nakhala nikutsatila malamulo onsewa kuyambila nili mwana.” 21 Yesu anamuyang’ana ndipo anamukonda. Kenako anati, “Cinthu cimodzi cikusoŵeka mwa iwe. Pita ukagulitse zinthu zako, ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatelo udzakhala na cuma kumwamba. Kenako ubwele udzakhale wotsatila wanga.” 22 Koma atamva zimenezi anakhumudwa, ndipo anacoka ali wacisoni cifukwa anali na katundu wambili.
23 Yesu atayang’ana uku na uku, anauza ophunzila ake kuti: “Cidzakhala covuta kwambili anthu a ndalama kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu!” 24 Koma ophunzilawo atamva mawu akewa, anadabwa. Kenako Yesu anati kwa iwo: “Ana inu, cidzakhala covuta kwambili kuti munthu akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu! 25 N’capafupi ngamila kuloŵa pa diso la singano, kusiyana n’kuti munthu wolemela akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” 26 Iwo anadabwa kwambili ndipo anamufunsa* kuti: “Ndiye pali amene angadzapulumuke ngati?” 27 Yesu atawayang’anitsitsa anati: “Kwa anthu n’zosathekadi, koma sizili conco kwa Mulungu, pakuti kwa Mulungu zinthu zonse n’zotheka.” 28 Petulo anayamba kumuuza kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse n’kukutsatilani.” 29 Yesu anati: “Ndithu nikukuuzani, palibe aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, amayi, atate, ana, kapena minda cifukwa ca dzina langa, komanso cifukwa ca uthenga wabwino, 30 amene sadzapeza zoculuka kuŵilikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana, na minda, pamodzi na mazunzo, ndipo m’nthawi* imene ikubwelayo adzapeza moyo wosatha. 31 Koma ambili amene ni oyamba adzakhala othela, ndipo othela adzakhala oyamba.”
32 Tsopano Yesu na ophunzila ake anali m’njila kupita ku Yerusalemu, ndipo iye anali patsogolo pawo. Ophunzilawo anadabwa kwambili, koma anthu amene anali kumutsatila anayamba kucita mantha. Apanso, Yesu anatengela ophunzila 12 aja pambali, n’kuyamba kuwauza zinthu zimene zinali pafupi kumucitikila. Anati: 33 “Lomba, tikupita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa munthu akapelekedwa kwa ansembe aakulu na alembi. Iwo adzamuweluza kuti aphedwe, komanso adzamupeleka kwa anthu a mitundu ina. 34 Iwo akamucita zacipongwe, akamuthila mata, akamukwapula, na kumupha. Koma pambuyo pa masiku atatu adzaukitsidwa.”
35 Yakobo na Yohane, ana aamuna a Zebedayo anafika kwa iye n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi, tifuna muticitile ciliconse cimene tikupempheni.” 36 Iye anawafunsa kuti: “Mufuna nikucitileni ciyani?” 37 Iwo anayankha kuti: “Lolani kuti mmodzi wa ife akakhale ku dzanja lanu lamanja, ndipo wina kumanzele kwanu mu ulemelelo wanu.” 38 Koma Yesu anawauza kuti: “Simudziŵa cimene mukupempha. Kodi mungamwe zimene nikumwa m’kapu iyi, kapena kubatizika na ubatizo umene ine nikubatizika nawo?” 39 Iwo anamuyankha kuti: “Inde tingatelo.” Pamenepo Yesu anawauza kuti: “Za m’kapu zimene ine nikumwa, mudzamwadi. Ndipo mudzabatizikadi na ubatizo umene ine nikubatizika nawo. 40 Koma kusankha munthu wokakhala ku dzanja langa lamanja kapena lamanzele, si udindo wanga. Malo amenewo adzapelekedwa kwa anthu amene anawakonzela malowo.”
41 Ophunzila 10 enawo atamva zimenezi, anamukwiyila kwambili Yakobo na Yohane. 42 Koma Yesu anawaitana n’kuwauza kuti: “Inu mukudziŵa kuti amene amaoneka kuti* akulamulila anthu a mitundu ina amapondeleza anthu awo, ndipo akulu-akulu awo amaonetsa mphamvu zawo pa iwo. 43 Siziyenela kukhala conco pakati panu. Koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. 44 Ndipo aliyense wofuna kukhala woyamba pakati panu, akhale kapolo wa onse. 45 Cifukwa ngakhale Mwana wa munthu sanabwele kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila na kudzapeleka moyo wake dipo kuti awombole anthu ambili.”
46 Ndiyeno iwo anafika ku Yeriko. Koma pamene iye na ophunzila ake, komanso gulu lalikulu la anthu, anali kutuluka mu Yeriko, Batimeyu (mwana wa Timeyu), amene anali wopempha-pempha komanso wakhungu, anali atakhala pansi m’mbali mwa msewu. 47 Atamva kuti Yesu Mnazareti ndiye anali kudutsa, anayamba kufuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, nicitileni cifundo!” 48 Pamenepo anthu ambili anayamba kumudzudzula kuti akhale cete. Koma m’pamene iye anakuwa kwambili, amvekele: “Nicitileni cifundo, inu Mwana wa Davide!” 49 Conco Yesu anaima n’kukamba kuti: “Muitaneni abwele kuno.” Anthuwo anamuitana n’kumuuza kuti: “Limba mtima! Nyamuka, akukuitana.” 50 Iye anangoti covala cake cakunja kuja cii! n’kuimilila mwamsanga kupita kwa Yesu. 51 Ndiyeno Yesu anamufunsa kuti: “Ufuna nikucitile ciyani?” Munthu wakhunguyo anayankha kuti: “Raboni,* nithandizeni niyambe kuona.” 52 Yesu anamuuza kuti: “Pita. Cikhulupililo cako cakucilitsa.” Nthawi yomweyo munthuyo anayamba kuona, ndipo anayamba kumutsatila.