Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
1 Paciyambi panali Mawu. Mawuyo anali ndi Mulungu, ndipo Mawuyo anali mulungu.* 2 Ameneyo paciyambi anali ndi Mulungu. 3 Zinthu zonse zinakhalako kudzela mwa iye, ndipo palibe ngakhale cinthu cimodzi cinakhalako popanda iye.
4 Moyo unakhalako kupyolela mwa iye, ndipo moyo wa iyeyo unali kuwala kounikila anthu. 5 Kuwalako kukuunika mumdima, koma mdimawo sunagonjetse kuwalako.
6 Ndiyeno kunabwela munthu wina wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake Yohane. 7 Munthu ameneyo anabwela monga mboni, kudzacitila umboni za kuwalako n’colinga cakuti anthu a mtundu uliwonse akhulupilile kudzela mwa iye. 8 Iyeyo sanali kuwalako ayi, koma anatumidwa kudzacitila umboni za kuwalako.
9 Kuwala kwenikweni kumene kumaunikila anthu a mtundu uliwonse kunali kutatsala pang’ono kubwela m’dziko. 10 Iye anali m’dziko, ndipo dziko linakhalako kupitila mwa iye, koma dzikolo silinamudziwe. 11 Iyeyo anabwela kwawo, koma anthu akwawo sanamulandile. 12 Komabe onse amene anamulandila, anawapatsa mphamvu kuti akhale ana a Mulungu, cifukwa anakhulupilila m’dzina lake. 13 Amenewa anabadwa kucokela kwa Mulungu, osati kucokela kwa anthu* kapena mwa kufuna kwa anthu,* osatinso mwa kufuna kwa munthu.
14 Conco Mawuyo anakhala munthu, ndipo anali kukhala pakati pathu. Tinaona ulemelelo wake, ulemelelo wofanana ndi umene mwana wobadwa yekha amalandila kucokela kwa atate ake. Iye nthawi zonse anali kuyanjidwa ndi Mulungu,* ndiponso anali kuphunzitsa coonadi. 15 (Yohane anacitila umboni za iye, inde anali kufuula kuti: “Uyu ndi amene ndinali kukamba za iye kuti, ‘Amene akubwela m’mbuyo mwanga ndi wamkulu kuposa ine, cifukwa iye anakhalako ine ndisanabadwe.’”) 16 Cifukwa cakuti anali ndi cisomo cacikulu, nthawi zonse tinali kulandila cisomo cacikulu cosefukila. 17 Popeza Cilamulo cinabwela kupitila mwa Mose, cisomo ndi coonadi zinabwela kupitila mwa Yesu Khristu. 18 Palibe munthu anaonapo Mulungu cikhalile, mulungu wobadwa yekha amene ali kumbali ya Atate,* ndi amene anafotokoza za Mulungu.
19 Yohane anapeleka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kucokela ku Yerusalemu kuti akamufunse kuti: “Kodi ndiwe ndani?” 20 Iye anawayankha mosapita m’mbali, ndipo anakana kuti: “Sindine Khristu.” 21 Kenako iwo anamufunsa kuti: “Ndiye ndiwe ndani? Kodi ndiwe Eliya?” Iye anayankha kuti: “Ayi.” “Kodi ndiwe Mneneli?” Iye anayankhanso kuti: “Ayi!” 22 Conco iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Tiuze kuti tikawayankhe amene atituma. Kodi iweyo mwiniwake umati ndiwe ndani?” 23 Iye anati: “Ndine mawu a winawake amene akufuula m’cipululu kuti, ‘Wongolani njila ya Yehova,’ monga anakambila mneneli Yesaya.” 24 Anthuwo anatumidwa ndi Afarisi. 25 Conco iwo anamufunsa kuti: “Ngati si ndiwe Khristu, kapena Eliya, kapenanso Mneneli, n’cifukwa ciyani umabatiza anthu?” 26 Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza anthu m’madzi. Koma pali wina waimilila pakati panu, amene inu simum’dziwa. 27 Iye akubwela m’mbuyo mwanga, ndipo ine sindine woyenela kumasula nthambo za nsapato zake.” 28 Zinthu zimenezi zinacitikila ku Betaniya kutsidya la Yorodano, kumene Yohane anali kubatiza anthu.
29 Tsiku lotsatila, Yohane anaona Yesu akubwela kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akucotsa ucimo wa dziko! 30 Uyu ndi uja amene ndinali kukamba kuti: ‘Amene akubwela m’mbuyo mwanga ndi wamkulu kuposa ine, cifukwa iye anakhalako ine ndisanabadwe.’ 31 Ngakhale ine sindinali kumudziwa, koma cifukwa cimene ndikubatizila anthu m’madzi n’cakuti iye adziwike kwa Isiraeli.” 32 Yohane anacitilanso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kucokela kumwamba, ndipo unakhazikika pa iye. 33 Ngakhale ine sindinali kumudziwa, koma amene ananditumayo kuti ndidzabatize anthu m’madzi, anandiuza kuti: ‘Aliyense amene udzaona kuti mzimu watsikila pa iye n’kukhazikika, ameneyo ndiye amabatiza ndi mzimu woyela.’ 34 Ine ndinauona, ndipo ndikucitila umboni kuti ameneyu ndi Mwana wa Mulungu.”
35 Kenako tsiku lotsatila, Yohane anaimilila pamodzi ndi awili mwa ophunzila ake. 36 Ndipo iye ataona Yesu akuyenda, anati: “Onani, Mwanawankhosa wa Mulungu!” 37 Ophunzila awiliwo atamva kuti wakamba zimenezi, anatsatila Yesu. 38 Ndiyeno Yesu ataceuka n’kuona kuti akumulondola, anawafunsa kuti: “Mukufuna ciyani?” Iwo anamuyankha kuti: “Rabi (liwuli likamasulidwa, limatanthauza, “Mphunzitsi”), mukhala kuti?” 39 Iye anawauza kuti: “Tiyeni mukaoneko.” Conco iwo anapita kukaona kumene iye anali kukhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo, apo nthawi inali itatsala pang’ono kukwana 4 koloko madzulo.* 40 Andireya, m’bale wake wa Simoni Petulo, anali mmodzi wa ophunzila awili aja omwe anamva zimene Yohane ananena n’kutsatila Yesu. 41 Iye coyamba anapita kukafunafuna m’bale wake Simoni n’kumuuza kuti: “Ife tapeza Mesiya” (dzinali likamasulidwa, limatanthauza “Khristu”), 42 ndipo anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuona, anamuuza kuti: “Iwe ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Kuyambila lelo, uzichedwa Kefa” (dzinali kumasulila kwake ndi “Petulo”).
43 Tsiku lotsatila, Yesu anafuna kupita ku Galileya. Ndiyeno anakumana ndi Filipo n’kumuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” 44 Filipo anali wocokela ku Betsaida, mzinda umene kunacokela Andireya ndi Petulo. 45 Filipo anapeza Nataniyeli n’kumuuza kuti: “Ife tapeza Yesu mwana wa Yosefe, wa ku Nazareti, amene Mose analemba za iye m’Cilamulo. Aneneli nawonso analemba za iye.” 46 Koma Nataniyeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke munthu aliyense wabwino?” Filipo anamuuza kuti: “Tiye ukaone.” 47 Yesu ataona Nataniyeli akubwela kwa iye, anati: “Onani, Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe cinyengo.” 48 Nataniyeli anamufunsa kuti: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ndinakuona uli munsi mwa mtengo wamkuyu.” 49 Nataniyeli anakamba kuti: “Mphunzitsi,* inu ndinudi Mwana wa Mulungu, komanso ndinu Mfumu ya Isiraeli.” 50 Yesu anamuyankha kuti: “Kodi wakhulupilila cifukwa ndakuuza kuti ndinakuona uli munsi mwa mtengo wamkuyu? Udzaona zinthu zazikulu kuposa izi.” 51 Kenako anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, ndipo mudzaona angelo a Mulungu akukwela ndi kutsika kupita kumene kuli Mwana wa munthu.”