Kwa Aroma
5 Popeza kuti tsopano tikuonedwa kuti ndife olungama cifukwa cokhala ndi cikhulupililo, tiyeni tikhale pa mtendele* ndi Mulungu kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 2 Kukhulupilila Yesu kumatithandiza kuti tizitha kufika kwa Mulungu komanso kuti tizisangalala ndi cisomo cake. Ndipo tiyeni tisangalale* cifukwa tili ndi ciyembekezo colandila ulemelelo wa Mulungu. 3 Si zokhazo, koma tiyeni tizisangalala* tikakumana ndi masautso cifukwa tikudziwa kuti masautso amacititsa kuti tipilile. 4 Kupilila nakonso kumacititsa kuti tikhale ovomelezeka kwa Mulungu, ndipo kukhala ovomelezeka kwa Mulungu kumacititsa kuti tikhale ndi ciyembekezo. 5 Ciyembekezoco sicitigwilitsa mwala cifukwa Mulungu amaonetsa kuti amatikonda mwa kutipatsa mzimu wake woyela.
6 Tikusowa mtengo wogwila, Khristu anafela anthu ocimwa pa nthawi yoikidwilatu. 7 Cifukwa n’capatali kuti munthu aliyense afele munthu wolungama. Koma mwina munthu angalimbe mtima n’kufela munthu wabwino. 8 Koma Mulungu akutionetsa cikondi cake cifukwa pamene tinali ocimwa Khristu anatifela. 9 Ndiponso adzacita zoposa pamenepo mwa kutipulumutsa ku mkwiyo wake kudzela mwa Khristu, popeza tikuonedwa olungama cifukwa ca magazi a Khristuyo. 10 Pakuti pamene tinali adani ake, tinagwilizanitsidwa ndi Mulungu kudzela mu imfa ya Mwana wake. Kuwonjezela pamenepo, moyo wake udzatipulumutsa popeza tsopano tagwilizanitsidwa. 11 Si izi cabe ayi, koma tikusangalalanso mwa Mulungu kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu amene kupitila mwa iye tagwilizanitsidwa ndi Mulungu.
12 N’cifukwa cake monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo inafalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa. 13 Pakuti ucimo unalimo kale m’dziko Cilamulo cisanabwele, koma palibe aliyense amene angaimbidwe mlandu wakuti wacimwa ngati palibe lamulo. 14 Ngakhale n’telo, imfa inalamulila ngati mfumu kuyambila nthawi ya Adamu mpaka ya Mose, ngakhalenso kwa anthu amene sanacimwe mofanana ndi mmene Adamu anacimwila. Adamuyo ndi wofanana ndi amene anali kubwela.
15 Koma mphatsoyo siili ngati ucimowo. Anthu ambili anafa cifukwa ca ucimo wa munthu mmodzi. Koma cisomo cacikulu ca Mulungu ndiponso mphatso yake yaulele imene anaipeleka mokoma mtima kupitila mwa munthu mmodzi, Yesu Khristu, n’zapamwamba kwambili. Mulungu anapeleka mphatso imeneyi kwa anthu onse, ndipo inabweletsa madalitso osaneneka.* 16 Komanso pali kusiyana pakati pa mphatso yaulele imeneyi, ndi mmene zinthu zinakhalila kudzela mwa munthu mmodzi amene anacimwa. Pakuti ciweluzo ca chimo limodzi lija cinali kulandila cilango. Koma mphatso imene inapelekedwa kaamba ka macimo ambili inapangitsa kuti anthu azionedwa kuti ndi olungama. 17 Imfa inalamulila monga mfumu cifukwa ca kucimwa kwa munthu mmodziyo. Koma anthu amene analandila cisomo cacikulu ca Mulungu ndiponso mphatso yake yaulele ya cilungamo, adzakhala ndi moyo kuti alamulile ngati mafumu kudzela mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.
18 Conco monga mmene chimo limodzi linapangitsila kuti anthu a mitundu yonse aweluzidwe kuti ndi ocimwa, cimodzimodzinso kucita cinthu cimodzi colungama, kunacititsanso kuti anthu a mitundu yonse aonedwe kuti ndi olungama kuti akhale ndi moyo. 19 Pakuti monga mmene kusamvela kwa munthu mmodziyo kunacititsila kuti ambili akhale ocimwa, cimodzimodzinso kudzela mwa kumvela kwa munthu mmodziyo kudzacititsa kuti ambili akhale olungama. 20 Cilamulo cinapelekedwa kuti kucimwa kwa anthu kuonekele poyela. Koma pamene ucimo unaonekela kwambili, cisomo ca Mulungu cinawonjezekanso kwambili. 21 Cifukwa ciyani? Kuti monga mmene ucimo unalamulila ngati mfumu pamodzi ndi imfa, momwemonso cisomo cilamulile monga mfumu kudzela m’cilungamo. Izi zidzacititsa kuti anthu akapeze moyo wosatha kupyolela mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.