Kalata Yoyamba kwa Akorinto
16 Ponena za nkhani ya zopeleka zopita kwa oyelawo, mungatsatile malangizo amene ndinapeleka ku mipingo ya ku Galatiya. 2 Pa tsiku loyamba la mlungu uliwonse, aliyense wa inu aziika kenakake pambali malinga ndi mapezedwe ake, kuti pasadzakhale zosonkha-sonkha zopeleka ine ndikadzafika. 3 Koma ndikadzafika kumeneko, ndidzatumiza amuna amene inu munawabvomeleza m’makalata anu kuti adzapeleke mphatso zanu za cifundo ku Yerusalemu. 4 Koma ngati m’pofunika kuti inenso ndipite kumeneko, tidzapitila limodzi.
5 Koma ndidzafika kwa inu pocoka ku Makedoniya, cifukwa ndidzadzela ku Makedoniya. 6 Ndikhoza kudzakhala nanu kumeneko, mwinanso nthawi yonse yozizila, kuti mudzandipelekeze kumene ndidzapite. 7 Cifukwa ulendo uno sindifuna ndidzakuoneni mothamanga ai. Yehova akalola, ndikufuna kuti ndidzakhale nanu kwa kanthawi ndithu. 8 Koma ndidzakhalabe kuno ku Efeso kufikila nthawi ya Cikondwelelo ca Pentekosite, 9 cifukwa khomo lalikulu la zocita landitsegukila, koma pali otsutsa ambili.
10 Tsopano Timoteyo akadzafika, mudzaonetsetse kuti asadzacite mantha pakati panu, cifukwa iye akugwila nchito ya Yehova mmene ine ndikucitila. 11 Conco pasapezeke munthu womudelela. Mukamupelekeze mwamtendele kuti abwele kuno, cifukwa ine ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale.
12 Tsopano ponena za Apolo m’bale wathu, ndinamucondelela kwambili kuti abwele kwa inu pamodzi ndi abale. Sicinali colinga cake kuti abwele kwa inu palipano, koma adzabwela akapeza mpata.
13 Khalani maso, imani zolimba m’cikhulupililo, citani zinthu molimba mtima,* ndipo khalani amphamvu. 14 Zinthu zonse zimene mukucita, muzizicita ndi cikondi.
15 Mukudziwa abale, kuti anthu a m’banja la Sitefana ndiwo anali oyamba kukhala okhulupilila* ku Akaya, ndipo iwo anadzipeleka kutumikila oyelawo. Cotelo ndikukulimbikitsani kuti, 16 inunso pitilizani kugonjela anthu ngati amenewo, komanso onse amene akugwila nchito molimbika. 17 Koma ndine wosangalala kuti Sitefana, Fotunato, ndi Akayiko ali nane kuno. 18 Popeza inu simuli kuno, iwo alowa m’malo mwanu. Anthu amenewa anditsitsimula komanso atsitsimula inu. Conco amuna ngati amenewa muziwalemekeza.
19 Mipingo ya ku Asia ikukutumizilani moni. Akula pamodzi ndi Purisika komanso mpingo umene umasonkhana m’nyumba yao, akukupatsani moni wacikondi mwa Ambuye. 20 Abale onse akuti moni. Muzipatsana moni wacikondi.*
21 Tsopano landilani moni wanga ine Paulo, wolembedwa ndi dzanja langa.
22 Ngati wina sakonda Ambuye, ameneyo atembeleledwe. Inu Ambuye wathu, bwelani! 23 Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale nanu. 24 Ndikukutsimikizilani kuti ndimakukondani inu nonse ophunzila a Khristu Yesu.