Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
23 Conco gulu lonselo linanyamuka pamodzi n’kupita naye kwa Pilato. 2 Kenako anayamba kumuneneza kuti: “Tapeza munthu uyu akupandutsa mtundu wathu, akuletsa anthu kupeleka misonkho kwa Kaisara, ndipo akunena kuti, iye ndi Khristu mfumu.” 3 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha.” 4 Kenako Pilato anauza ansembe aakulu ndi khamulo kuti: “Munthuyu sindikumupeza ndi mlandu ulionse.” 5 Koma iwo anaumilila kuti: “Munthu ameneyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, kuyambila ku Galileya mpaka kuno.” 6 Pilato atamva zimenezo, anafunsa ngati munthuyo anali Mgalileya. 7 Atazindikila kuti iye wacokela m’cigawo colamulidwa ndi Herode, anamutumiza kwa Herode, amenenso anali ku Yerusalemu pa masiku amenewo.
8 Herode ataona Yesu anakondwela kwambili. Kwa nthawi ndithu, anali kufunitsitsa kumuona cifukwa anamva zambili za iye, ndipo anali kuyembekezela kuti Yesu amuonetse cizindikilo cinacake. 9 Conco anayamba kumufunsa mafunso ambili, koma Yesu sanamuyankhe ciliconse. 10 Komabe, ansembe aakulu ndi alembi anali kungonyamukanyamuka n’kumamuneneza mwaukali. 11 Ndiyeno Herode pamodzi ndi asilikali ake, anamunyoza. Ndipo anamucita zacipongwe mwa kumuveka covala cabwino kwambili. Kenako anamubweza kwa Pilato. 12 Patsikuli, Herode ndi Pilato anakhala mabwenzi, koma kumbuyo konseko anali kudana kwambili.
13 Kenako, Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulila, komanso anthu 14 n’kuwauza kuti: “Mwabweletsa munthu uyu kwa ine, ndipo mwamupatsa mlandu wakuti amatuntha anthu kuukila boma. Onani! Munthuyu ndamufunsa pamaso panu, koma sin’namupeze ndi mlandu ulionse pa zimene mukumuneneza. 15 Nayenso Herode sanamupeze ndi mlandu, ndiye cifukwa cake wamutumizanso kwa ife. Kukamba zoona, munthu ameneyu sanacite ciliconse coyenela cilango ca imfa. 16 Conco, ndidzangomukwapula ndi kumumasula.” 17* —— 18 Koma khamulo linafuula kuti: “Anyongedwe ndithu munthu ameneyu,* ndipo mutimasulile Baraba!” 19 (Munthu ameneyu anaikidwa m’ndende cifukwa ca kuukila boma kumene kunacitika mu mzindawo, komanso cifukwa ca kupha anthu.) 20 Pilato anakambanso nawo kaciwili, cifukwa anali kufuna kumumasula Yesu. 21 Anthuwo anayamba kufuula mwamphamvu kuti: “Apacikidwe! Apacikidwe ndithu!” 22 Anakamba nawo kacitatu kuti: “Cifukwa ciyani? Walakwanji? Ine sindinamupeze ndi mlandu ulionse woyenela cilango ca imfa. Conco, ndidzangomukwapula ndi kumumasula.” 23 Atamva zimenezi, iwo anamuumiliza mokweza mawu kuti Yesu aphedwe.* Iwo anakuwa mwamphamvu cakuti Pilato anangololela. 24 Conco, Pilato anapeleka cigamulo kuti zimene anthuwo anali kufuna zicitike. 25 Iye anawamasulila munthu amene iwo anali kufuna, amene anali ataponyedwa m’ndende cifukwa coukila boma, komanso kupha anthu. Koma anapeleka Yesu m’manja mwawo kuti amucite zimene anali kufuna.
26 Tsopano pamene anali kupita naye, anagwila Simoni wa ku Kurene amene anali kucokela kudela la kumidzi, ndipo iwo anamunyamulitsa mtengo wozunzikilapo,* n’kumulamula kuti azilondola Yesu. 27 Khamu la anthu linali kumulondola, kuphatikizapo azimayi amene cifukwa ca cisoni anali kungodziguguda pacifuwa ndi kumulila. 28 Yesu anaceukila azimayiwo n’kuwauza kuti: “Inu ana aakazi a Yerusalemu, lekani kundilila. M’malo mwake, dzilileni nokha komanso lilani ana anu. 29 Pakuti masiku akubwela pamene anthu adzanena kuti, ‘Odala ndi akazi osabeleka, akazi amene alibe ana, komanso amene sanayamwitsepo!’ 30 Ndiyeno iwo adzayamba kuuza mapili kuti, ‘Tigweleni!’ Komanso adzauza mapili ang’onoang’ono kuti, ‘Tifoceleni!’ 31 Ngati akucita izi mtengo ukali wauwisi, n’ciyani cimene cidzacitika mtengowo ukadzauma?”
32 Amuna awili amene anali zigawenga, nawonso anatengedwa kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu. 33 Ndiyeno atafika pamalo ochedwa Cibade, anamukhomelela pa mtengo pamodzi ndi zigawenga zija, wina anamucipacika ku dzanja lake lamanja, ndipo wina kumanzele kwake. 34 Koma Yesu anali kukamba kuti: “Atate, akhululukileni, pakuti sadziwa zimene akucita.” Iwo anacita maele kuti agawane zovala zake. 35 Anthuwo anangoimilila n’kuyamba kuonelela zimene zinali kucitika. Koma olamulila anali kumunyodola ndi kunena kuti: “Anali kupulumutsa ena, mulekeni adzipulumutse yekha ngati iye alidi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.” 36 Ngakhale asilikali anali kumunyodola. Anali kubwela ndi kumupatsa vinyo wowawasa 37 n’kukamba kuti: “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” 38 Pamwamba pake analembapo mawu akuti: “Iyi ndi Mfumu ya Ayuda.”
39 Ndiyeno mmodzi wa zigawenga zimene anamupacika nazo pamodzi, anayamba kukamba mwacipongwe kuti: “Iwe ndiwe Khristu, si conco? Dzipulumutse, ndi kupulumutsanso ife!” 40 Poyankha mnzakeyo anamudzudzula kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu poona kuti iwenso walandila cilango monga ca munthu ameneyu? 41 Ife tiyenela kulangidwa conci, cifukwa tikulandila zogwilizana ndi zimene tinacita. Koma munthu uyu sanalakwitse ciliconse.” 42 Kenako anakamba kuti: “Yesu, mukandikumbukile mukadzalowa mu Ufumu wanu.” 43 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”
44 Apa nthawi inali ca m’ma 12 koloko masana,* koma m’dziko lonselo munagwa mdima mpaka ca m’ma 3 koloko masana,* 45 cifukwa dzuwa linaleka kuwala. Kenako, cinsalu cochinga ca m’nyumba yopatulika cinang’ambika pakati, kucokela pamwamba mpaka pansi. 46 Kenako Yesu anafuula kuti: “Atate, ndisungiza mzimu wanga m’manja mwanu.” Atakamba zimenezi, anatsilizika.* 47 Kapitawo wa asilikali ataona zimene zinacitika, anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Munthuyu analidi wolungama.” 48 Ndiyeno anthu onse amene anasonkhana kumeneko kudzaonelela zimene zinacitika, ataona zimene zinacitikazo, anabwelela kwawo akudziguguda pacifuwa. 49 Ndipo onse amene anali kumudziwa anaimilila capatali. Nawonso azimayi amene anali kumutsatila kucokela ku Galileya analipo, ndipo anaona zimene zinacitikazo.
50 Ndipo panali munthu wina wabwino komanso wolungama dzina lake Yosefe, wa m’Khoti Yaikulu ya Ayuda. 51 (Munthuyu sanaponyeko voti yovomeleza ciwembu cawo ndi zocita zawo.) Iye anali wocokela ku Arimateya, mzinda wa Ayuda, ndipo anali kuyembekezela Ufumu wa Mulungu. 52 Munthu ameneyu anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. 53 Iye anautsitsa n’kuukulunga m’nsalu yabwino kwambili, ndipo anakamuika m’manda* ogobedwa m’thanthwe, mmene simunaikidwepo mtembo uliwonse. 54 Tsopano linali Tsiku la Cikonzekelo, ndipo Sabata linali litatsala pang’ono kuyamba. 55 Koma azimayi amene anabwela naye kucokela ku Galileya anamutsatila, ndipo anawaona mandawo* ndi mmene anaikila mtembo wake. 56 Iwo anabwelela kukakonza zonunkhilitsa ndi mafuta onunkhila. Koma pa tsiku la Sabata anapumula malinga ndi cilamulo.