Kalata Yoyamba kwa Akorinto
12 Tsopano kunena za mphatso zauzimu abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa zinthu. 2 Inu mudziwa kuti pamene munali osakhulupilila,* munali kutsogoleledwa komanso kusoceletsedwa ndi mafano osalankhula. 3 Tsopano ndikufuna kuti mudziwe kuti palibe munthu wotsogoleledwa ndi mzimu wa Mulungu amene angakambe kuti: “Yesu ndi wotembeleledwa!” Palibenso amene angakambe kuti: “Yesu ndi Ambuye!” popanda kutsogoleledwa ndi mzimu woyela.
4 Pali mphatso zosiyana-siyana koma mzimu ulipo umodzi. 5 Ndipo pali mautumiki osiyana-siyana koma Ambuye alipo mmodzi. 6 Palinso nchito zosiyana-siyana, koma Mulungu amene amapeleka mphamvu zogwilila nchitozo kwa aliyense alipo mmodzi. 7 Koma thandizo la mzimu woyela limaonekela mwa aliyense, ndipo Mulungu amaupeleka kuti upindulile ena. 8 Pakuti mzimu umathandiza wina kulankhula mau anzelu, ndipo mzimu womwewo umathandiza wina kulankhula mau ozindikila. 9 Mzimu umodzi-modziwo umathandiza wina kukhala ndi cikhulupililo, pamene wina umamuthandiza kukhala ndi mphatso za kucilitsa. 10 Koma wina umam’patsa mphatso yocita nchito zamphamvu, wina kulosela, wina kuzindikila mau ouzilidwa, wina kulankhula malilime,* komanso wina kumasulila malilime. 11 Koma nchito zonsezi zimatheka ndi mzimu umodzi-modziwo, ndipo umapatsa munthu aliyense mphatsozi malinga ndi mmene ukufunila.
12 Thupi lili ndi ziwalo zambili, ngakhale ntelo, ziwalozo zimapanga thupi limodzi. N’cimodzi-modzinso ndi Khristu. 13 Pakuti tonsefe, tinabatizidwa ndi mzimu umodzi kuti tikhale thupi limodzi. Kaya Ayuda kapena Agiriki, akapolo kapena mfulu, tonsefe tinalandila* mzimu umodzi.
14 Pakuti thupi silikhala ndi ciwalo cimodzi, koma zambili. 15 Ngati phazi lingakambe kuti: “Popeza ine si ndine dzanja, sindili mbali ya thupi,” zimenezo sizitanthauza kuti si lilidi mbali ya thupi. 16 Ndipo ngati khutu lingakambe kuti: “Popeza kuti ine si ndine diso, si ndili mbali ya thupi,” zimenezo sizitanthauza kuti si lilidi mbali ya thupi. 17 Thupi lonse likanakhala diso, tikanamva ndi ciani? Thupi lonse likanakhala khutu, tikananunkhiza ndi ciani? 18 Koma Mulungu anaika ciwalo ciliconse pamalo ake, malinga ndi kufuna kwake.
19 Kodi thupi likanakhalapo ngati ziwalo zonse zinakakhala ciwalo cimodzi? 20 Conco pali ziwalo zoculuka, koma thupi ndi limodzi. 21 Diso silingauze dzanja kuti: “Ndilibe nawe nchito,” kapena mutu sungauze mapazi kuti: “Ndilibe nanu nchito.” 22 Koma ziwalo za thupi zooneka ngati zofooka, ndi zofunika. 23 Ndipo ziwalo za thupi zimene timaziyesa kuti n’zocepelapo ulemu, timazipatsa ulemu woonjezeleka. Conco, ziwalo zathu zotsikilapo timazilemekeza mokulilapo, 24 pamene ziwalo zathu zooneka bwino kale sizifunikila cisamalilo cimeneco. Ngakhale n’conco, Mulungu analumikiza bwino thupi lonse, anaika ulemu woculuka pa ziwalo zimene panalibe ulemuwo. 25 Anatelo kuti thupi lake likhale losagawika, koma kuti ziwalo zake zizisamalilana. 26 Cotelo, ciwalo cimodzi cikabvutika ziwalo zina zonse zimabvutikila naco limodzi. Komanso ciwalo cimodzi cikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalalila naco limodzi.
27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi ciwalo ca thupilo. 28 Ndipo Mulungu wapatsa munthu aliyense zocita zosiyana-siyana mumpingo. Coyamba atumwi, caciwili aneneli, cacitatu aphunzitsi, ndiyeno nchito zamphamvu, mphatso zakucilitsa, utumiki wothandiza anthu, luso loyendetsa zinthu, komanso mphatso yolankhula malilime osiyana-siyana. 29 Sizingatheke kuti onse akhale atumwi. Sizingatheke kuti onse akhale aneneli, zingatelo ngati? Kodi onse angakhale aphunzitsi? Si onse amene amacita nchito zamphamvu, ndi onse ngati? 30 Ndipo si onse amene ali ndi mphatso zocilitsa, ndi onse ngati? Si onse amene amalankhula malilime, ndi onse ngati? Si onse amene ndi omasulila,* ndi onse ngati? 31 Conco, yesetsani* kuti mulandile mphatso zazikulu. Komabe, ndidzakuonetsani njila yopambana.