Kwa Aroma
10 Abale, cimene mtima wanga ukufuna komanso pemphelo langa locondelela kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe. 2 Cifukwa ndikuwacitila umboni kuti ndi okangalika potumikila Mulungu, koma samudziwa molondola. 3 Koma cifukwa cosadziwa cilungamo ca Mulungu, koma n’kumafuna kukhazikitsa cilungamo cawocawo, iwo sanagonjele cilungamo ca Mulungu. 4 Khristu ndiye kutha kwa Cilamulo, kuti aliyense wokhulupilila akhale wolungama.
5 Mose analemba zokhudza cilungamo mogwilizana ndi Cilamulo kuti: “Munthu aliyense amene akucita zinthu zimenezi adzakhala ndi moyo mwa kucita zinthu zimenezo.” 6 Koma ponena za cilungamo cobwela cifukwa ca cikhulupililo, mawu a Mulungu amati: “Mu mtima mwako usamanene kuti, ‘Ndani adzapita kumwamba?’ kuti akatsitse Khristu. 7 Kapena ‘Ndani adzapita ku phompho,’ kuti akaukitse Khristu kwa akufa?” 8 Koma kodi lemba limati ciyani? Limati: “Mawu a Mulungu ali pafupi ndi inu, ali m’kamwa mwanu komanso m’mitima yanu.” Amenewo ndi “mawu” a cikhululupililo amene tikulalikila. 9 Pakuti ngati ukulengeza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo umakhulupilila mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10 Cifukwa kuti munthu akhale wolungama amafunikila kukhala ndi cikhulupililo mumtima mwake, koma ndi pakamwa pake, amalengeza poyela cikhulupililo cake kuti akapulumuke.
11 Pakuti lemba lina limati: “Palibe munthu wokhulupilila mwa iye amene adzagwilitsidwa mwala.” 12 Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki, cifukwa onsewo Ambuye wawo ndi mmodzi, amene amapeleka mowolowa manja kwa onse oitana pa iye. 13 Pakuti “aliyense woitanila pa dzina la Yehova, adzapulumuka.” 14 Koma kodi iwo angaitane bwanji pa dzina lake ngati samukhulupilila? Nanga angamukhulupilile bwanji ngati sanamvepo za iye? Ndipo angamve bwanji za iye popanda wina kuwalalikila? 15 Ndiye kodi angalalikile bwanji ngati sanatumidwe? Zili monga mmene Malemba amakambila kuti: “Ndithudi, mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwambili!”
16 Ngakhale n’telo, iwo sanalabadile uthenga wabwino. Pakuti Yesaya anakamba kuti: “Yehova, ndani wakhulupilila zimene wamva kwa ife?”* 17 Conco munthu amakhala ndi cikhulupililo cifukwa ca zimene wamva. Ndipo zimene wamvazo zimacokela m’mawu okamba za Khristu. 18 Koma ndifunse kuti, Kodi iwo sanamve? Kukamba zoona “mawu anamveka pa dziko lonse lapansi, ndipo uthenga unamveka mpaka kumalekezelo a dziko lapansi kumene kuli anthu.” 19 Komanso ndifunse kuti, Kodi Aisiraeli sanadziwe? Coyamba Mose anati: “Ndidzakucititsani nsanje mwa kugwilitsa nchito anthu a mitundu ina. Ndidzakukwiyitsani koopsa mwa kugwilitsa nchito mtundu wopusa.” 20 Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambili kuti: “Amene anandipezawo ndi anthu amene sanali kundifunafuna. Ndinadziwika kwa anthu amene sanali kufunsa za ine.” 21 Koma ponena za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamvela ndiponso ouma khosi.”