Macitidwe a Atumwi
13 Mumpingo wa ku Antiokeya munali aneneli ndi aphunzitsi. Iwo anali Baranaba, Sumiyoni wochedwanso Nigeri, Lukiyo wa ku Kurene, Saulo komanso Manayeni amene anaphunzila pamodzi ndi Herode wolamulila cigawo. 2 Pamene iwo anali kutumikila Yehova* komanso kusala kudya, mzimu woyela unawauza kuti: “Mundipatulile Baranaba ndi Saulo kuti agwile nchito imene ine ndinawaitanila.” 3 Ndiyeno atatsiliza kusala kudya ndi kupemphela, iwo anawagwila pamutu* pawo n’kuwatumiza.
4 Conco amuna amenewa, amene anatumizidwa ndi mzimu woyela, anapita ku Selukeya, ndipo atacoka kumeneko anayenda ulendo wa pamadzi kupita ku Kupuro. 5 Atafika ku Salami anayamba kulalikila mawu a Mulungu mʼmasunagoge a Ayuda. Iwo analinso ndi Yohane amene anali kuwatumikila.*
6 Iwo anayenda pa cisumbu conse ca Kupuro mpaka kukafika ku Pafo. Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Bara-Yesu, amene anali wamatsenga komanso mneneli wabodza. 7 Ameneyu anali pamodzi ndi bwanamkubwa* Serigio Paulo, munthu wanzelu kwambili. Bwanamkubwayu anaitana Baranaba ndi Saulo, cifukwa anali kufunitsitsa kumva mawu a Mulungu. 8 Koma Elima, wamatsenga uja, (cifukwa umu ndi mmene dzina lakeli amalimasulila) anayamba kuwatsutsa. Iye anayesetsa kuti bwanamkubwayo asakhale wokhulupilila. 9 Kenako Saulo, wochedwanso Paulo, atadzazidwa ndi mzimu woyela, anamuyangʼanitsitsa, 10 ndipo anati: “Iwe munthu wodzaza ndi cinyengo camtundu uliwonse ndiponso zoipa, mwana wa Mdyelekezi komanso mdani wa cinthu ciliconse colungama, kodi sudzaleka kupotoza njila za Yehova zowongoka? 11 Tamvela! Dzanja la Yehova lili pa iwe ndipo ukhala wakhungu. Kwakanthawi, sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo anaona nkhungu yamphamvu mʼmaso mwake ndiponso mdima wandiweyani, ndipo anayamba kufunafuna munthu amene angamugwile dzanja ndi kumutsogolela. 12 Bwanamkubwayo ataona zimene zinacitikazi, anakhala wokhulupilila, cifukwa anadabwa kwambili ndi zimene anaphunzila zokhudza Yehova.
13 Kenako Paulo ndi anzake ananyamuka ulendo wa panyanja kucoka ku Pafo, ndipo anakafika ku Pega, ku Pamfuliya. Koma Yohane Maliko anawasiya nʼkubwelela ku Yerusalemu. 14 Koma atacoka ku Pega anakafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa mʼsunagoge pa tsiku la Sabata ndi kukhala pansi. 15 Atatsiliza kuwelenga Cilamulo ndi zolemba za aneneli pamaso pa anthu, atsogoleli a sunagoge anatumiza mawu kwa iwo kuti: “Abale inu, ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa anthu awa, lankhulani.” 16 Conco Paulo anaimilila ndipo anakweza dzanja lake nʼkunena kuti:
“Anthu inu, Aisiraeli, komanso ena nonsenu oopa Mulungu, tamvelani. 17 Mulungu wa anthu awa Aisiraeli, anasankha makolo athu akale. Iye anapangitsa anthu amenewa kukhala mtundu wamphamvu, pamene anali alendo mʼdziko la Iguputo. Ndipo anawatulutsa mʼdzikolo ndi dzanja lake lamphamvu. 18 Kwa zaka pafupifupi 40, iye anapilila khalidwe lawo mʼcipululu. 19 Atawononga mitundu 7 mʼdziko la Kanani, anapeleka dzikolo kwa Aisiraeli kuti likhale colowa cawo. 20 Zonsezi zinacitika mʼzaka pafupifupi 450.
“Pambuyo pa zimenezi iye anawapatsa oweluza mpaka kudzafika pa nthawi ya mneneli Samueli. 21 Koma pambuyo pake iwo anafuna kukhala ndi mfumu. Ndipo Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini. Iye anakhala mfumu yawo kwa zaka 40. 22 Atamucotsa pa ufumu, anawapatsa Davide kuti akhale mfumu yawo. Iye anamucitila umboni mwa kukamba kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Jese, munthu wapamtima panga. Iyeyu adzacita zonse zimene ndikufuna.’ 23 Mogwilizana ndi lonjezo lake, kucokela pa mbadwa za munthu ameneyu, Mulungu wabweletsa mpulumutsi kwa Isiraeli, amene ndi Yesu. 24 Mpulumutsi ameneyu asanafike, Yohane analalikila kwa anthu onse a ku Isiraeli za ubatizo, ngati cizindikilo ca kulapa. 25 Koma kumapeto kwa utumiki wake, Yohane anali kunena kuti, ‘Kodi mukuganiza kuti ndine ndani? Munthu amene mukuyembekezela si ndine ayi. Koma wina akubwela pambuyo panga, amene ine si ndine woyenela kumasula nsapato zake.’
26 “Anthu inu, abale, inu mbadwa za Abulahamu, komanso anthu amene amaopa Mulungu amene ali pakati panu, mawu a cipulumutso cimeneci atumizidwa kwa ife. 27 Cifukwa anthu a ku Yerusalemu ndi olamulila awo sanamuzindikile ameneyu. Koma pamene anali kumuweluza, anakwanilitsa zimene aneneli anakamba, zimene zimawelengedwa mokweza sabata lililonse. 28 Ngakhale kuti sanapeze cifukwa comuphela, iwo anakakamiza Pilato kuti ameneyu aphedwe. 29 Ndiyeno atakwanilitsa zonse zimene zinalembedwa zokhudza iye, anamutsitsa pamtengo nʼkukamuika mʼmanda.* 30 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. 31 Ndipo kwa masiku ambili anaonekela kwa anthu amene anayenda naye kucoka ku Galileya kupita ku Yerusalemu. Palipano amenewa ndi mboni zake kwa anthu.
32 “Conco tikulengeza kwa inu uthenga wabwino wokamba za lonjezo limene linapelekedwa kwa makolo athu akale. 33 Uthengawo ndi wakuti Mulungu wakwanilitsa zonse zimene anawalonjezazo kwa ife ana awo mwa kuukitsa Yesu, monga zinalembedwa mu salimo laciwili kuti: ‘Iwe ndiwe mwana wanga. Lelo ndakhala tate wako.’ 34 Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa kwa akufa, ndipo sadzabwelelanso kuthupi limene lingawole, anaifotokoza motele: ‘Ine ndidzakuonetsani cikondi cokhulupilika cimene ndinalonjeza Davide. Ndipo lonjezo limeneli ndi lodalilika.’ 35 Ndipo salimo lina limakambanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupilika kwa inu liwole.’ 36 Davide anacita cifunilo ca Mulungu pa nthawi ya mʼbadwo wake, anamwalila nʼkuikidwa mʼmanda a makolo ake, ndipo thupi lake linawola. 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa, thupi lake silinawole.
38 “Tsopano abale anga, dziwani kuti ife tikulalikila kwa inu kuti kupitila mwa ameneyu, macimo akukhululukidwa. 39 Mudziwenso kuti pa zinthu zonse zimene kunali kosatheka kuti muonedwe opanda mlandu kudzela mʼCilamulo ca Mose, aliyense wokhulupilila akuonedwa wopanda mlandu kudzela mwa ameneyu. 40 Conco samalani kuti zimene aneneli analemba zisakucitikileni, zimene zimati: 41 ‘Inu onyoza onani zimene ine ndikucita ndipo mudabwe nazo, kenako mudzatha, cifukwa nchito zimene ndikucita mʼmasiku anu, ndi nchito zimene inu simungazikhulupilile ngakhale wina atakufotokozelani mwatsatanetsatane.’”
42 Tsopano pamene iwo anali kutuluka, anthuwo anawacondelela kuti akawauzenso zinthu zimenezo Sabata lotsatila. 43 Conco msonkhano wamʼsunagoge utatha, Ayuda ndi anthu ambili amene analowa Ciyuda, omwe anali kulambila Mulungu, anatsatila Paulo ndi Baranaba. Ndipo iwo analimbikitsa anthuwo kuti apitilize kukhala oyenela kulandila cisomo ca Mulungu.
44 Sabata lotsatila, pafupifupi mzinda wonse unasonkhana pamodzi kuti umvetsele mawu a Yehova. 45 Ayuda ataona khamu la anthulo, anacita nsanje ndipo anayamba kutsutsa mwamwano zimene Paulo anali kulankhula. 46 Conco Paulo ndi Baranaba anakamba molimba mtima kuti: “Kunali koyenela kuti inu mukhale oyamba kuuzidwa mawu a Mulungu. Koma popeza mukuwakana ndipo mukudziweluza nokha kuti ndinu osayenela moyo wosatha, taonani ife tikupita kwa anthu a mitundu ina. 47 Pakuti Yehova watilamula kuti, ‘Ine ndakupatsani udindo woti mukhale kuwala kwa anthu a mitundu ina, kuti mukhale cipulumutso mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’”
48 Pamene anthu a mitundu ina anamva izi, anayamba kusangalala ndi kutamanda mawu a Yehova. Anthu onse amene anali ndi maganizo abwino ofunadi moyo wosatha anakhala okhulupilila. 49 Kuwonjezela apo, mawu a Yehova anali kufalitsidwa mʼdziko lonselo. 50 Koma Ayuda anatuntha azimayi ochuka amene anali oopa Mulungu komanso amuna olemekezeka a mumzindawo. Ndipo iwo anacititsa kuti Paulo ndi Baranaba ayambe kuzunzidwa, ndipo anawaponya kunja kwa mzinda wawo. 51 Conco iwo anakutumula fumbi kumapazi awo, kenako anapita ku Ikoniyo. 52 Ndipo ophunzilawo anapitiliza kukhala acimwemwe komanso odzazidwa ndi mzimu woyela.