Macitidwe a Atumwi
21 Cifukwa cakuti tinali kusiyana nawo, tinayamba ulendo wathu wa panyanja tili acisoni kwambili. Tinayenda osakoneka mpaka kukafika ku Ko. Tsiku lotsatila tinafika ku Rode, ndipo titacoka kumeneko tinakafika ku Patara. 2 Titapeza ngalawa yopita ku Foinike, tinakwela n’kupita nayo. 3 Cisumbu ca Kupuro citayamba kuonekela, tinapatukila kumanzele* n’kucisiya, ndipo tinalowela ku Siriya. Kenako tinaima ku Turo kuti ngalawayo itsitse katundu. 4 Tinafufuza ophunzila n’kuwapeza, ndipo tinakhala kumeneko masiku 7. Koma iwo atauzilidwa ndi mzimu, anauza Paulo mobwelezabweleza kuti asakapondeko phazi ku Yerusalemu. 5 Conco masiku athu okhala kumeneko atatha, tinanyamuka kuti tipitilize ulendo wathu. Koma abale onse ndi azimayi komanso ana, anatipelekeza mpaka kunja kwa mzindawo. Kumeneko tinagwada m’mbali mwa nyanja n’kupemphela. 6 Kenako tinalailana nawo. Ndiyeno ife tinakwela ngalawa, ndipo iwo anabwelela kunyumba kwawo.
7 Conco tinanyamuka ku Turo pa ngalawa ndipo tinafika ku Tolemayi. Kumeneko tinapeleka moni kwa abale n’kukhala nawo tsiku limodzi. 8 Tsiku lotsatila tinanyamuka n’kufika ku Kaisareya, ndipo tinalowa m’nyumba ya mlaliki wina dzina lake Filipo. Iye anali mmodzi wa amuna 7 aja a mbili yabwino, ndipo tinakhala naye. 9 Munthu ameneyu anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa* amene anali kunenela. 10 Koma titakhala kumeneko kwa masiku ndithu, mneneli wina dzina lake Agabo anabwela kucokela ku Yudeya. 11 Iye anabwela kwa ife n’kutenga lamba wa Paulo ndipo anadzimanga manja ndi miyendo n’kunena kuti: “Mzimu woyela wanena kuti, ‘Mwiniwake wa lambayu, adzamangidwa conci ndi Ayuda ku Yerusalemu, ndipo adzamupeleka m’manja mwa anthu a mitundu ina.’” 12 Titamva zimenezi, ifeyo ndi anthu omwe analipo, tinayamba kumucondelela kuti asapite ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukulila ndiponso mukufuna kundifooketsa? Ndithu ndikukuuzani, ndine wokonzeka osati cabe kumangidwa koma ngakhale kukafa ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.” 14 Titalephela kumusintha maganizo, tinaleka* kumucondelela ndipo tinati: “Cifunilo ca Yehova cicitike.”
15 Pambuyo pake tinakonzekela n’kuuyamba ulendo wopita ku Yerusalemu. 16 Nawonso ophunzila ena a ku Kaisareya anatipelekeza mpaka kukafika kunyumba kwa Mnaso wa ku Kupuro. Munthu ameneyu anali mmodzi wa ophunzila oyambilila. Iye anatilandila monga alendo. 17 Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandila mokondwela. 18 Koma tsiku lotsatila Paulo anapita nafe kwa Yakobo, ndipo akulu onse anali komweko. 19 Paulo anapeleka moni kwa iwo, n’kuyamba kuwafotokozela mwatsatanetsatane zimene Mulungu anacita kwa anthu a mitundu ina kudzela mu utumiki wake.
20 Atamva zimenezi, anayamba kutamanda Mulungu, koma anamuuza kuti: “Ona m’bale, pali Ayuda masauzande ambili okhulupilila, ndipo ndi okangalika potsatila Cilamulo. 21 Koma iwo anamva mphekesela zakuti iwe ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti apatuke pa Cilamulo ca Mose. Akuti ukuwaletsa kucita mdulidwe wa ana awo komanso kutsatila miyambo imene akhala akuitsatila. 22 Ndiye titani pamenepa? Mosakayikila iwo adzamva kuti iwe wabwela. 23 Conco ucite zimene tikuuze. Tili ndi amuna anayi amene anacita mdulidwe. 24 Utenge amuna awa, ndipo ukadziyeletse mwamwambo pamodzi ndi iwo. Uwalipilile zofunikila kuti amete tsitsi lawo. Ukatelo onse adzadziwa kuti mphekesela zimene anamva zokhudza iwe sizinali zoona. Koma adzaona kuti ukucita zinthu mwadongosolo ndiponso kuti ukutsatila Cilamulo. 25 Ponena za okhulupilila ocokela m’mitundu ina, iwo tinawalembela kalata yofotokoza cigamulo cathu cakuti azipewa zinthu zopelekedwa nsembe ku mafano komanso magazi, zopotola* ndiponso ciwelewele.”*
26 Conco tsiku lotsatila Paulo anatenga amunawo, ndipo anadziyeletsa mwamwambo pamodzi ndi iwo. Ndiyeno analowa m’kacisi n’kunena pamene masiku awo a mwambo wa kudziyeletsa adzathela, ndiponso pamene wansembe adzapeleke nsembe ya aliyense wa iwo.
27 Masiku 7 atatsala pang’ono kutha, Ayuda a ku Asia anaona Paulo ali m’kacisi. Iwo anatuntha khamu lonse la anthu kuti ligwile Paulo, ndipo anamugwila. 28 Iwo anali kufuula kuti: “Amuna inu, Aisiraeli, tithandizeni! Uyu ndiye munthu amene amaphunzitsa anthu kulikonse zotsutsana ndi anthu a mtundu wathu, Cilamulo cathu, ndi malo ano. Kuwonjezela apo, walowetsa Agiriki mʼkacisi ndipo waipitsa malo oyelawa.” 29 Anatelo cifukwa anali ataona Paulo ali ndi Telofimo wa ku Efeso mumzindawo, ndiye anaganiza kuti Paulo analowa naye m’kacisi. 30 Conco mumzinda wonsewo munali cipolowe, ndipo anthu anali kuthamangila ku kacisiko. Iwo anagwila Paulo ndi kumuguzila kunja kwa kacisi. Ndipo nthawi yomweyo zitseko zinatsekedwa. 31 Pamene anali kufuna kumupha, uthenga unafika kwa mkulu wa gulu la asilikali kuti mu Yerusalemu monse muli cipwilikiti. 32 Nthawi yomweyo, iye anatenga asilikali ndi atsogoleli awo nʼkuthamangila komweko. Anthuwo ataona mkulu wa asilikali ndi asilikaliwo, analeka kumumenya Paulo.
33 Ndiyeno mkulu wa asilikaliyo anafika pafupi ndi kumugwila ndipo analamula kuti amumange ndi maunyolo awili. Kenako anafunsa anthu kuti iye ndi ndani komanso kuti anacita ciyani. 34 Koma anthu ena m’khamulo anayamba kufuula zinthu zina, enanso zina. Conco atalephela kutolapo mfundo yeniyeni cifukwa ca phokoso, analamula kuti apite naye kumalo okhala asilikali. 35 Koma atafika pa masitepe, asilikaliwo anacita kumunyamula cifukwa ca ciwawa ca khamulo. 36 Pakuti khamu limene linali kuwatsatila linali kufuula kuti: “Aphedwe ameneyo!”
37 Atatsala pang’ono kufika kumalo okhala asilikali, Paulo anafunsa mkulu wa asilikaliwo kuti: “Kodi mungandilole ndilankhule nanu pang’ono?” Mkulu wa asilikaliyo anati: “Kansi umalankhula Cigiriki? 38 Kodi si ndiwe munthu wa ku Iguputo amene kumbuyoku unayambitsa cipolowe coukila boma n’kutsogolela zigawenga 4,000 kupita nazo ku cipululu?” 39 Ndiyeno Paulo anayankha kuti: “Ine ndine Myuda wa ku Tariso ku Kilikiya, nzika ya mzinda wochuka. Conco ndikukupemphani kuti mundilole ndilankhule nawo anthuwa.” 40 Atamulola, Paulo anaimilila pa masitepe ndi kukwezela anthuwo dzanja lake. Onse anakhala cete, ndiyeno analankhula nawo m’Ciheberi kuti: