Macitidwe a Atumwi
15 Ndiyeno amuna ena ocokela ku Yudeya anafika n’kuyamba kuphunzitsa abale kuti: “Ngati simudulidwa mogwilizana ndi mwambo wa Mose, simungapulumuke.” 2 Koma Paulo ndi Baranaba sanagwilizane nazo, ndipo anatsutsana nawo. Conco iwo anasankha Paulo, Baranaba, komanso anthu ena, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu, kuti akawauze za nkhaniyi.*
3 Conco mpingo utawapelekeza, anthu amenewa anapitiliza ndi ulendo wawo kupitila ku Foinike ndi ku Samariya. Kumeneko anawafotokozela mwatsatanetsatane mmene anthu a mitundu ina anatembenukila n’kuyamba kulambila Mulungu. Ndipo abale onse atamva zimenezi anakondwela kwambili. 4 Atafika ku Yerusalemu, mpingo, atumwi, komanso akulu anawalandila ndi manja awili. Ndipo anawafotokozela zinthu zambili zimene Mulungu anacita kudzela mwa iwo. 5 Koma ena amene kale anali m’gulu lampatuko la Afarisi omwe anakhala okhulupilila, anaimilila m’mipando yawo n’kunena kuti: “M’pofunika kuwadula ndi kuwalamula kuti azisunga Cilamulo ca Mose.”
6 Conco atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti aikambilane nkhaniyo. 7 Pambuyo potsutsana kwambili za nkhaniyo, Petulo anaimilila n’kuwauza kuti: “Anthu inu, abale, mukudziwa bwino kuti kucokela m’masiku oyambilila, Mulungu anandisankha kuti kudzela pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino ndi kukhulupilila. 8 Ndipo Mulungu, amene amadziwa za mumtima akucitila umboni mwa kuwapatsa mzimu woyela, mmenenso anacitila kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse ngakhale pang’ono pakati pa ife ndi iwo. Koma anayeletsa mitima yawo cifukwa ca cikhulupililo cawo. 10 Ndiye n’cifukwa ciyani inu tsopano mukumuyesa Mulungu ponyamulitsa ophunzila joko imene makolo athu, ngakhale ifeyo, sitinathe kuinyamula? 11 Koma tsopano ife tikhulupilila kuti tidzapulumuka cifukwa ca cisomo ca Ambuye Yesu, mofanananso ndi anthu amenewa.”
12 Atatelo gulu lonse linakhala cete, ndipo anayamba kumvetsela pamene Paulo ndi Baranaba anali kuwafotokozela zizindikilo ndi zodabwitsa zambili zimene Mulungu anacita pakati pa anthu a mitundu ina kudzela mwa iwo. 13 Atatsiliza kulankhula, Yakobo anayankha kuti: “Anthu inu, abale, ndimvetseleni. 14 Sumiyoni wafotokoza bwino kwambili mmene Mulungu anaceukila anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti pakati pawo atengepo anthu ena odziwika ndi dzina lake. 15 Ndipo zimenezi zikugwilizana ndi zimene aneneli analemba kuti: 16 ‘Zinthu zimenezi zikadzatha ine ndidzabwelela ndipo ndidzautsanso tenti* ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso mbali yogumuka ya nyumbayo ndi kuikonzanso. 17 Ndidzacita zimenezi kuti anthu otsalawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ochedwa ndi dzina langa, watelo Yehova amene akucita zinthu zimenezi, 18 zomwe anatsimikiza kalekale kuti adzazicita.’ 19 Conco cigamulo canga* n’cakuti, tisawavutitse anthu a mitundu ina amene atembenukila kwa Mulungu. 20 Koma tiwalembele kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,* ciwelewele,* zopotola,* komanso magazi. 21 Pakuti kuyambila kalekale, nthawi zonse anthu akhala akulalikila mu mzinda ndi mzinda mawu ocokela m’mabuku a Mose, cifukwa sabata lililonse mabukuwa amawelengedwa mokweza m’masunagoge.”
22 Ndiyeno atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwilizana zakuti amuna amene anasankhidwa pakati pawo, awatumize ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Conco anatumiza Yudasi wochedwanso Barasaba, ndi Sila, amene anali kutsogolela abale. 23 Iwo analemba kalata n’kuwapatsila. Kalatayo inati:
“Ife abale anu atumwi ndi akulu, tikukulembelani inu abale athu ocokela m’mitundu ina, amene muli ku Antiokeya, ku Siriya, ndi ku Kilikiya: Tikuti landilani moni wathu! 24 Tamva kuti ena ocokela pakati pathu akukuvutitsani ndi kukusokonezani mwa zolankhula zawo ngakhale kuti ife sitinawapatse malangizo alionse. 25 Conco tonse tagwilizana kuti tisankhe amuna n’kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa, Baranaba ndi Paulo. 26 Anthu amenewa apeleka miyoyo yawo cifukwa ca dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu. 27 Conco tikutumiza Yudasi ndi Sila, kuti nawonso adzakufotokozeleni zinthu zimodzimodzi ndi mawu apakamwa. 28 Cifukwa mzimu woyela komanso ife taona kuti ndi bwino kuti tisakunyamulitseni mtolo wolemela, kupatulapo zinthu zofunika zokhazi zimene ndi: 29 kupitiliza kupewa zinthu zopelekedwa nsembe ku mafano, magazi, zopotola,* ndi ciwelewele.* Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambili, zinthu zidzakuyendelani bwino. Tikukufunilani zabwino zonse!”*
30 Conco amuna amenewa atanyamuka, anapita ku Antiokeya. Kumeneko anasonkhanitsa gulu lonse la anthu n’kuwapatsa kalatayo. 31 Ataiwelenga, anakondwela ndi mawu acilimbikitso amene analimo. 32 Popeza kuti Yudasi ndi Sila analinso aneneli, anawakambila nkhani zambili abalewo ndipo anawalimbikitsa. 33 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abalewo analailana nawo, ndipo anabwelela kwa amene anawatuma mwamtendele. 34* —— 35 Koma Paulo ndi Baranaba anakhalila ku Antiokeya. Iwo anali kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova pamodzi ndi anthu enanso ambili.
36 Patapita masiku, Paulo anauza Baranaba kuti: “Tiyeni tibwelele tsopano ku mizinda yonse kumene tinalalikila mawu a Yehova kuti tikacezele abale ndi kukawaona kuti ali bwanji.” 37 Baranaba anali kufunitsitsa kuti atenga Yohane, wochedwanso Maliko. 38 Koma Paulo sanafune kumutenga cifukwa ulendo wina Yohane anawasiya ku Pamfuliya, ndipo sanapite nawo ku nchitoyo. 39 Mwa ici, iwo anakangana koopsa mpaka anapatukana. Baranaba anatenga Maliko ndipo anayenda ulendo wa pamadzi kupita ku Kupuro. 40 Koma Paulo anasankha Sila, ndipo abale atamupemphelela Pauloyo kuti Yehova amuonetse cisomo cake, ananyamuka. 41 Iye anapitila ku Siriya ndi ku Kilikiya, ndipo anali kulimbitsa mipingo.