Macitidwe a Atumwi
28 Titapulumuka, tinamva kuti cisumbuco cimachedwa Melita. 2 Ndipo anthu olankhula cinenelo cacilendo* anationetsa kukoma mtima kwapadela. Iwo anatisonkhela moto ndi kutilandila tonse mokoma mtima cifukwa kunali kugwa mvula, ndiponso kunali kozizila. 3 Koma Paulo atatenga nkhuni n’kuziponya pamoto, panatuluka njoka yamphili cifukwa ca kutentha kwa motowo, ndipo inamuluma n’kukangamila kudzanja lake. 4 Anthu olankhula cinenelo cacilendowo, ataona kuti njoka yapoizoni ikulendewela ku dzanja lake anayamba kuuzana kuti: “Ndithu munthu uyu ndi wopha anthu, ndipo ngakhale kuti anayenda panyanja kudzafika kuno ali bwinobwino, Cilungamo* sicinalole kuti akhalebe ndi moyo.” 5 Koma iye anangokutumulila njokayo pa moto ndipo sanavulazidwe. 6 Koma iwo anali kuyembekezela kuti atupa kapena kugwa mwadzidzidzi n’kufa. Atayembekezela kwa nthawi yaitali n’kuona kuti palibe coipa ciliconse cimene cikumucitikila, anasintha maganizo awo n’kuyamba kunena kuti iye ndi mulungu.
7 Tsopano pafupi ndi malowa panali minda ya woyangʼanila cisumbuco, dzina lake Papuliyo. Iye anatilandila bwino kwambili ndipo anaticeleza kwa masiku atatu. 8 Koma atate ake Papuliyo, anali gone cifukwa codwala malungo* komanso m’mimba mwakamwazi. Conco Paulo anapita kukalowa mmene munali bambowo n’kuwapemphelela, ndipo anaika manja ake pa iwo n’kuwacilitsa. 9 Izi zitacitika, anthu ena onse odwala okhala pa cisumbuco, nawonso anayamba kubwela kwa iye ndipo anawacilitsa. 10 Komanso iwo anatilemekeza potipatsa mphatso zambili, ndipo pamene tinali kunyamuka anatipatsa zonse zimene tinali kufunikila.
11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pa ngalawa yokhala ndi cifanizilo ca “Ana a Zeu.” Ngalawayo inali ya ku Alekizandiriya, ndipo inaima pa cisumbupo poyembekezela kuti nyengo yozizila ithe. 12 Kenako tinafika padoko lina ku Surakusa, ndipo tinakhalapo masiku atatu. 13 Titacoka kumeneko, tinayenda mpaka kukafika ku Regio. Pambuyo pa tsiku limodzi, kunayamba kuwomba mphepo ya kum’mwela ndipo tinafika ku Potiyolo pa tsiku laciwili. 14 Kumeneko tinapeza abale, ndipo anaticondelela kuti tikhale nawo masiku 7. Pambuyo pake tinapitiliza ulendo wathu wa ku Roma. 15 Abale a kumeneko atamva za ife, anayenda mpaka kudzafika ku Msika wa Apiyo ndi ku Nyumba Zitatu za Alendo kudzaticingamila. Paulo atawaona, anathokoza Mulungu ndipo analimba mtima. 16 Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kumakhala yekha ndi msilikali womulonda.
17 Pambuyo pa masiku atatu, Paulo anaitanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana pamodzi, iye anawauza kuti: “Amuna inu, abale, ngakhale kuti sindinacite ciliconse cotsutsana ndi anthu, kapena miyambo ya makolo athu akale, ndinapelekedwa m’manja mwa Aroma monga mkaidi kucokela ku Yerusalemu. 18 Ndipo atafufuza, anafuna kundimasula cifukwa sanandipeze ndi mlandu ulionse woyenela cilango ca imfa. 19 Koma Ayuda atakana ndinakakamizika kucita apilo kwa Kaisara. Koma osati cifukwa cakuti ndinali kufuna kudzaneneza mtundu wanga ayi. 20 N’cifukwa cake ndinapempha kudzaonana nanu n’kulankhula nanu, pakuti ndamangidwa unyolowu cifukwa ca ciyembekezo cimene Aisiraeli ali naco.” 21 Iwo anamuyankha kuti: “Ife sitinalandilepo makalata alionse okamba za iwe kucokela ku Yudeya. Palibenso m’bale aliyense wocokela kumeneko amene watiuza kapena kunena ciliconse coipa cokhudza iwe. 22 Koma tikuona kuti ndibwino titamva maganizo ako, cifukwa kukamba zoona, ife tidziwa kuti gulu lampatuko limeneli amalinenela zoipa kulikonse.”
23 Conco iwo anakonza tsiku loti akakumane naye, ndipo anabwela ambili kumene iye anali kukhala. Conco kuyambila m’mawa mpaka madzulo, iye anawafotokozela nkhaniyo, ndipo anacitila umboni mokwanila za Ufumu wa Mulungu. Anawalimbikitsa kukhulupilila Yesu mwa kugwilitsa mfundo zocokela m’Cilamulo ca Mose ndi zimene aneneli analemba. 24 Ena anayamba kukhulupilila zimene iye ananena, koma ena sanazikhulupilile. 25 Conco, popeza anali kutsutsana, anayamba kucoka. Koma Paulo ananena mawu awa othela:
“Mzimu woyela unakamba zoona kwa makolo anu kudzela mwa mneneli Yesaya 26 kuti, ‘Pita kwa anthu awa ndipo ukawauze kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma simudzamvetsa tanthauzo lake. Kuona mudzaona ndithu, koma simudzazindikila zimene mukuona. 27 Pakuti anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi matu awo, koma osacitapo kanthu, komanso atseka maso awo. Acita zimenezi kuti asaone ndi maso awo, komanso kuti asamve ndi matu awo. Ndiponso kuti mitima yawo isamvetse zinthu n’kutembenuka kuti ine ndiwacilitse.”’ 28 Conco dziwani kuti cipulumutso cimeneci cocokela kwa Mulungu catumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo mosakayikila, iwo adzamvetsela.” 29* ——
30 Conco Paulo anakhalabe kumeneko kwa zaka ziwili zathunthu m’nyumba imene anali kucita lendi, ndipo anthu onse amene anali kubwela kudzamuona anali kuwalandila mokoma mtima. 31 Iye anali kuwalalikila za Ufumu wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu, ali ndi ufulu wonse wa kulankhula* popanda coletsa.