Macitidwe a Atumwi
9 Koma Saulo anapitilizabe kuopseza ophunzila a Ambuye, ndipo anali kufunitsitsa kuwapha. Conco iye anapita kwa mkulu wa ansembe 2 kukapempha makalata opita nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti akhale ndi cilolezo cokamanga mwamuna kapena mkazi aliyense amene angapezeke kuti akutsatila Njilayo* n’kubwela naye ku Yerusalemu.
3 Tsopano ali pa ulendo wake umenewo, atatsala pang’ono kufika ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kocokela kumwamba kunamuzungulila. 4 Izi zitacitika, anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti: “Saulo, Saulo, n’cifukwa ciyani ukundizunza?” 5 Saulo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi ndinu ndani?” Iye anamuyankha kuti: “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza. 6 Koma nyamuka ulowe mu mzindawo ndipo udzauzidwa zoyenela kucita.” 7 Anthu amene anali naye pa ulendowo anangoima cilili kusowa conena. Iwo anamva ndithu mawuwo koma sanaone aliyense. 8 Ndiyeno Saulo anaimilila, koma ngakhale kuti maso ake anali otseguka, sanali kuona ciliconse. Conco anamugwila dzanja n’kulowa naye mumzinda wa Damasiko. 9 Kwa masiku atatu Saulo sanali kuona, ndipo sanadye kapena kumwa ciliconse.
10 Ku Damasiko kunali wophunzila wina dzina lake Hananiya, ndipo Ambuye anamuuza m’masomphenya kuti: “Hananiya!” Iye anayankha kuti: “Ine pano Ambuye.” 11 Ambuye anamuuza kuti: “Nyamuka upite ku msewu wochedwa Wowongoka. Ukakafika panyumba ya Yudasi, ukafunse za munthu wina dzina lake Saulo wa ku Tariso. Pakuti iye akupemphela. 12 Ndipo m’masomphenya, iye waona munthu wina dzina lake Hananiya akubwela kwa iye n’kumuika manja pamutu kuti ayambenso kuona.” 13 Koma Hananiya anayankha kuti: “Ambuye, ndamva kwa anthu ambili za munthu ameneyu, komanso zoipa zonse zimene anacitila oyela anu ku Yerusalemu. 14 Ndipo anatenga cilolezo kwa ansembe aakulu kuti amange aliyense woitanila pa dzina lanu.” 15 Koma Ambuye anamuuza kuti: “Pita! Cifukwa munthu ameneyu ndi ciwiya cosankhidwa kwa ine kuti cikacitile umboni dzina langa kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi kwa Aisiraeli. 16 Pakuti ndidzamuonetsa bwinobwino mavuto onse amene adzakumana nawo cifukwa ca dzina langa.”
17 Conco Hananiya anapita n’kukalowa m’nyumbamo, ndipo anaika manja ake pa iye n’kunena kuti: “Saulo m’bale wanga, Ambuye Yesu amene anaonekela kwa iwe pa msewu pamene unali kubwela kuno, wandituma kwa iwe kuti uyambenso kuona komanso kuti udzazidwe ndi mzimu woyela.” 18 Nthawi yomweyo m’maso mwake munagwa tinthu tooneka ngati mamba, ndipo anayambanso kuona. Kenako iye anapita kukabatizidwa. 19 Ndiyeno anadya cakudya n’kupeza mphamvu.
Iye anakhala ndi ophunzila ku Damasiko kwa masiku angapo. 20 Posapita nthawi, iye anayamba kulalikila za Yesu m’masunagoge kuti ameneyu ndi Mwana wa Mulungu. 21 Koma onse amene anamumva anadabwa kwambili, ndipo anali kukamba kuti: “Kodi munthu ameneyu si uja amene anazunza koopsa anthu oitanila pa dzina limeneli ku Yerusalemu? Kodi sanabwele kuno n’colinga coti awamange n’kuwapeleka* kwa ansembe aakulu?” 22 Koma Saulo anapitiliza kukhala ndi mphamvu zambili, ndipo anali kuwathetsa nzelu Ayuda okhala ku Damasiko pamene anali kuwatsimikizila momveka bwino kuti Yesu ndi Khristu.
23 Tsopano patapita masiku ambili, Ayudawo anakonza ciwembu cakuti amuphe. 24 Koma Saulo anadziwa za ciwembu cawo. Iwo anali kuyembekezelanso pa mageti a mumzindawo mosamala kwambili usana ndi usiku kuti amuphe ndithu. 25 Conco ophunzila ake anamuika m’dengu n’kumutsitsila kunja usiku kupitila pa cibowo ca mpanda.
26 Atafika ku Yerusalemu, iye anayesetsa kugwilizana ndi ophunzila kumeneko, koma onse anali kumuopa cifukwa sanakhulupilile kuti anakhaladi wophunzila. 27 Conco Baranaba anamuthandiza ndipo anapita naye kwa atumwi. Iye anawafotokozela mwatsatanetsatane mmene Saulo anaonela Ambuye pa msewu pamene analankhula naye, komanso mmene Saulo analankhulila molimba mtima m’dzina la Yesu ku Damasiko. 28 Cotelo iye anakhalabe nawo, ndipo anali kuyenda momasuka mu Yerusalemu, akulankhula molimba mtima m’dzina la Ambuye. 29 Iye anali kulankhula komanso kutsutsana ndi Ayuda olankhula Cigiriki. Iwo anayesayesa kupeza njila yoti amuphele. 30 Abale atadziwa zimenezi, anapita naye ku Kaisareya n’kumutumiza ku Tariso.
31 Ndiyeno, mpingo ku Yudeya konse, Galileya komanso ku Samariya unayamba kukhala pamtendele ndipo unalimba. Cifukwa cakuti mpingo unali kuopa Yehova komanso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyela, mpingowo unapitilizabe kukula.
32 Pamene Petulo anali kuyenda m’cigawo conseco, anafikanso kwa oyela amene anali kukhala ku Luda. 33 Kumeneko anapeza munthu wina dzina lake Eneya. Iye anali kukhala gone pa bedi lake kwa zaka 8 cifukwa anali wakufa ziwalo. 34 Petulo anamuuza kuti: “Eneya, Yesu Khristu akukucilitsa. Uka konza bedi lako.” Ndipo nthawi yomweyo ananyamuka. 35 Pamene anthu onse a ku Luda komanso ku cigawo ca Sharoni anamuona anayamba kukhulupilila Ambuye.
36 Tsopano ku Yopa kunali wophunzila wina dzina lake Tabita, dzinali mu Cigiriki limamasulidwa kuti “Dorika.”* Mayiyu anali kucita zinthu zambili zabwino, ndipo anali kupatsa ena mphatso zambili zacifundo. 37 Koma m’masiku amenewo iye anadwala n’kumwalila. Conco iwo anamusambika n’kumugoneka m’cipinda cam’mwamba. 38 Popeza kuti mzinda wa Luda unali pafupi ndi mzinda wa Yopa, ophunzilawo atamva kuti Petulo ali mumzindawo, anatuma anthu awili n’kukamupempha kuti: “Conde bwelani kuno mwamsanga.” 39 Petulo atamva zimenezi, ananyamuka n’kupita nawo. Ndiyeno iye atafika, iwo anapita naye m’cipinda cam’mwamba cija. Akazi onse amasiye anapita kwa iye akulila, ndipo anali kumuonetsa zovala zambili ndi mikanjo* imene Dorika anawasokela pamene anali nawo. 40 Petulo anauza anthu onse kuti atuluke, kenako anagwada n’kupemphela. Ndiyeno anatembenuka n’kuyang’ana thupilo, ndipo anati: “Tabita, uka!” Ndiyeno mayiyo anatsegula maso ake, ndipo ataona Petulo anauka n’kukhala tsonga. 41 Petulo anamugwila dzanja n’kumuimilika mayiyo. Iye anaitana oyelawo komanso akazi amasiye, ndipo anamupeleka kwa iwo ali wamoyo. 42 Nkhaniyi inamveka mu Yopa monse, ndipo anthu ambili anakhulupilila Ambuye. 43 Petulo anakhalabe ku Yopa kwa masiku angapo. Iye anali kukhala kwa munthu wina wofufuta zikumba dzina lake Simoni.