Macitidwe a Atumwi
11 Tsopano atumwi ndi abale amene anali ku Yudeya anamva kuti anthu a mitundu ina nawonso alandila mawu a Mulungu. 2 Conco Petulo atapita ku Yerusalemu, anthu olimbikitsa mdulidwe anayamba kumuimba mlandu.* 3 Anali kumuuza kuti: “Iwe unalowa m’nyumba ya anthu osadulidwa ndipo unadya nawo.” 4 Petulo atamva izi anayamba kuwafotokozela mwatsatanetsatane zimene zinacitika kuti:
5 “Ndinali kupemphela mumzinda wa Yopa ndipo ndinaona masomphenya. M’masomphenyawo ndinaona cinthu cooneka ngati cinsalu cacikulu, cikutsika kucokela kumwamba. Cinthuco anacigwila m’makona ake anayi n’kucitsitsila pamene panali ine. 6 N’taciyang’anitsitsa, ndinaonapo nyama za miyendo inayi za padziko lapansi, nyama zakuchile, nyama zokwawa, komanso mbalame za mumlengalenga. 7 Ndinamvanso mawu ondiuza kuti: ‘Petulo, nyamuka, uphe ndi kudya zinthu zimenezi!’ 8 Koma ine ndinati: ‘Ayi Ambuye, cinthu codetsedwa komanso conyansa sicinalowepo m’kamwa mwanga.’ 9 Kaciwili, ndinamvanso mawu ocokela kumwamba akuti: ‘Ulekeletu kuchula zinthu zimene Mulungu waziyeletsa kuti zodetsedwa.’ 10 Mawuwa anamvekanso kacitatu, ndipo zonse zinatengedwa n’kubwelela kumwamba. 11 Nthawi yomweyo amuna atatu ocokela ku Kaisareya amene anatumidwa kwa ine, anafika panyumba imene tinali kukhala. 12 Kenako mzimu unandiuza kuti ndipite nawo ndisakayikile ngakhale pang’ono. Abale 6 awa anapita nane, ndipo tinakalowa m’nyumba ya munthuyo.
13 “Iye anatifotokozela kuti ali m’nyumba mwake anaona mngelo ataimilila, ndipo anamuuza kuti: ‘Tuma anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni wodziwikanso kuti Petulo. 14 Iye adzakuuza zimene iwe ndi a m’banja lako mungacite kuti mupulumuke.’ 15 Koma nditangoyamba kulankhula, mzimu woyela unafika pa iwo monga unacitila kwa ife poyamba paja. 16 Zitatelo, ndinakumbukila mawu amene Ambuye anali kukonda kukamba akuti: ‘Yohane anali kubatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyela.’ 17 Conco, ngati Mulungu anawapatsa mphatso yaulele imenenso anapeleka kwa ife amene tinakhulupilila mwa Ambuye Yesu Khristu, ndiye ndine ndani kuti ndimuletse Mulungu?”*
18 Iwo atamva zimenezi analeka kumutsutsa,* ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Ndiye kuti Mulungu wapatsanso anthu a mitundu ina mwayi wakuti alape ndi kukapeza moyo.”
19 Anthu amene anabalalika kaamba ka mavuto amene anayamba cifukwa ca zimene zinacitikila Sitefano, anafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro, ndi Antiokeya. Koma anali kungolalikila kwa Ayuda okha. 20 Komabe, ena mwa anthu ocokela ku Kupuro ndi Kurene atafika ku Antiokeya anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ambuye Yesu kwa anthu okamba Cigiriki. 21 Kuwonjezela apo, dzanja la Yehova linali nawo, ndipo anthu ambili anakhala okhulupilila, ndiponso anayamba kutsatila Ambuye.
22 Mpingo wa ku Yerusalemu unamva zokhudza anthuwa, ndipo unatumiza Baranaba kuti apite ku Antiokeya. 23 Atafika kumeneko n’kuona cisomo ca Mulungu, anasangalala ndipo anayamba kulimbikitsa onse kuti apitilize kukhala okhulupilika kwa Ambuye ndi mtima wonse. 24 Baranaba anali munthu wabwino wa cikhulupililo colimba, komanso wodzazidwa ndi mzimu woyela. Cifukwa ca zimenezo, khamu la anthu linayamba kukhulupilila Ambuye. 25 Kenako iye anapita ku Tariso kukafunafuna Saulo mosamala. 26 Atamupeza, anapita naye ku Antiokeya. Kwa caka cathunthu, iwo anali kusonkhana ndi mpingo, ndipo anaphunzitsa anthu ambili. Motsogoleledwa ndi Mulungu, ku Antiokeya n’kumene ophunzilawo anayamba kuchedwa Akhristu.
27 M’masiku amenewo, aneneli ocokela ku Yerusalemu anapita ku Antiokeya. 28 Mmodzi wa iwo dzina lake Agabo analosela mothandizidwa ndi mzimu woyela kuti padziko lonse lapansi padzagwa njala yaikulu. Ndipo zimenezi zinadzacitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo. 29 Conco ophunzilawo anatsimikiza mtima kutumiza thandizo* kwa abale a ku Yudeya, aliyense malinga n’zimene akanakwanitsa. 30 Iwo anacitadi zimenezo, ndipo anatumiza thandizolo kwa akulu mwa kupatsila Baranaba ndi Saulo.