Kwa Aroma
15 Ife olimba tiyenela kuganizila amene ndi ofooka, osati kumadzikondweletsa tokha. 2 Aliyense wa ife azicita zinthu zokondweletsa mnzake kuti amulimbikitse. 3 Cifukwa ngakhale Khristu sanacite zinthu zodzikondweletsa yekha, koma anacita mmene Malemba amanenela kuti: “Manyozo a anthu amene amakunyozani andigwela.” 4 Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatithandiza kupilila, komanso amatitonthoza ndi colinga coti tikhale ndi ciyembekezo. 5 Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tipilile, komanso amene amatitonthoza, akuthandizeni nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo, 6 kuti ndi pakamwa panu, nonsenu capamodzi mutamande Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
7 Cotelo landilanani ngati mmene Khristu anakulandililani, kuti ulemelelo upite kwa Mulungu. 8 Kunena zoona, Khristu anakhala mtumiki wa anthu odulidwa potsimikizila kuti Mulungu ndi wokhulupilika. Mwakutelo, anaonetsa kuti malonjezo amene Mulungu anapatsa makolo awo akale ndi odalilika. 9 Anatelo kutinso anthu a mitundu ina alemekeze Mulungu kaamba ka cifundo cake, malinga n’kunena kwa Malemba kuti: “N’cifukwa cake ndidzakulemekezani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndipo ndidzakuimbilani nyimbo zotamanda dzina lanu.” 10 Komanso Malemba amati: “Kondwelani inu anthu a mitundu ina pamodzi ndi anthu ake.” 11 Ndiponso amati: “Tamandani Yehova inu mitundu yonse ya anthu, ndipo anthu onse amutamande.” 12 Komanso Yesaya anakamba kuti: “Padzakhala muzu wa Jese, ndipo winawake wolamulila mitundu adzatuluka. Anthu a mitundu ina adzaika ciyembekezo cawo pa iye.” 13 Mulungu amene amapeleka ciyembekezo adzaze mitima yanu ndi cimwemwe cacikulu komanso mtendele wonse, mwa kumudalila kuti ciyembekezo canu cizikulilakulila* mothandizidwa ndi mphamvu ya mzimu woyela.
14 Abale anga, ine ndine wotsimikiza kuti inu ndinu okonzeka kucita zabwino. Mumadziwa zambili komanso mumatha kulangizana wina ndi mnzake. 15 Komabe, ndakulembelani mfundo zina mosapita mʼmbali kuti ndikukumbutseninso. Ndacita izi cifukwa ca cisomo cimene Mulungu anandicitila 16 pondiika kukhala mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Ndikugwila nchito yopatulika yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu kuti anthu a mitundu inawa, akhale monga nsembe yovomelezeka kwa Mulungu, imene yayeletsedwa ndi mzimu woyela.
17 Cotelo ndikusangalala kukhala wophunzila wa Khristu Yesu, komanso kugwila nchito ya Mulungu. 18 Pakuti sindidzalankhula ciliconse cimene ndacita pandekha, koma zokhazo zimene Khristu wacita ndi kulankhula kupitila mwa ine, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kukhala omvela. 19 Iwo akhala omvela cifukwa ca zizindikilo komanso zodabwitsa zamphamvu zimene mzimu wa Mulungu wacita. Conco ndalalikila mokwanila uthenga wabwino wonena za Khristu, kuyambila ku Yerusalemu mpaka ku Iluriko. 20 Pocita zimenezi ndinatsimikiza mtima kuti ndisalengeze uthenga wabwino kumene anthu anali kulidziwa kale dzina la Khristu, nʼcolinga cakuti ndisamange pamaziko a munthu wina, 21 koma ndicite monga Malemba amanenela kuti: “Amene sanauzidwepo za iye adzamuona, ndipo amene sanamve adzazindikila.”
22 Ndiye cifukwa cakenso ndakhala ndikulephela kubwela kwa inu. 23 Koma tsopano kulibenso gawo lililonse limene sindinafikeko mʼmadela amenewa, ndipo kwa zaka zambili* ndakhala ndikulakalaka kubwela kwanuko. 24 Conco ndikuyembekezela kudzakuonani popita ku Sipaniya, ndipo ndikadzaceza nanu kwakanthawi, mudzandipelekeze pa ulendo wangawo. 25 Koma apa tsopano, ndatsala pang’ono kupita ku Yerusalemu kukatumikila oyela. 26 Abale a ku Makedoniya ndi a ku Akaya apeleka mosangalala mphatso kwa oyela ena a ku Yerusalemu omwe ndi osauka. 27 Nʼzoona kuti iwo anacita zimenezo mokondwela, komabe anali ndi nkhongole kwa oyelawo. Cifukwa ngati anthu a mitundu ina alandilako zinthu zauzimu kucokela kwa oyelawo, ndiye kuti nawonso ayenela kutumikila oyelawo mwa kuwapatsa zinthu zofunikila pa umoyo. 28 Cotelo ndikadzatsiliza kuwapatsa zopelekazi,* ndidzadzela kwanuko popita ku Sipaniya. 29 Komanso ndikudziwa kuti ndikadzafika kwanuko ndidzakubweletselani madalitso ambili ocokela kwa Khristu.
30 Conco abale, kupitila mwa Ambuye wathu Yesu Khristu komanso mwa cikondi ca mzimu oyela, ndikukupemphani kuti mulimbikile kundipemphelela kwa Mulungu, ndipo inenso ndilimbikila kupemphela, 31 kuti ndikalanditsidwe kwa anthu osakhulupilila a ku Yudeya, ndiponso kuti oyela a ku Yerusalemu akalandile bwino mphatso imene ndawanyamulila. 32 Ngati Mulungu alola, ndidzabwela kwa inu mokondwela, ndipo tidzalimbikitsana. 33 Mulungu amene amapeleka mtendele akhale nanu nonsenu. Ameni.