Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
13 Pa nthawi imeneyo, ena amene analipo anamufotokozela za anthu a ku Galileya amene Pilato anasakaniza magazi awo ndi nsembe zawo. 2 Iye anawayankha kuti: “Muganiza kuti Agalileyawo anali ocimwa kwambili kuposa Agalileya ena onse cifukwa zimenezo zinawacitikila? 3 Ayi ndithu. Koma ndikukuuzani kuti ngati simungalape, nonsenu mudzawonongedwa ngati iwo. 4 Kapena muganiza kuti anthu 18 aja omwe nsanja inawagwela ku Siloamu n’kuwapha anali ocimwa kwambili kuposa anthu ena onse okhala mu Yerusalemu? 5 Ayi ndithu, koma ndikuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzawonongedwa ngati iwo.”
6 Ndiyeno anayamba kuwauza fanizo ili: “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu m’munda wake wampesa, ndipo anapita kukafuna zipatso mu mtengowo, koma sanapezemo ciliconse. 7 Kenako munthuyo anauza wosamalila munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu ndakhala ndikubwela kudzafunafuna zipatso mu mtengo wamkuyu uwu, koma sindikupezamo kalikonse. Udule! N’cifukwa ciyani ukungowononga nthaka?’ 8 Poyankha, wosamalila mundayo anati, ‘Mbuyanga, ulekeni kwa caka cina cimodzi, ndipo ndidzakumba m’mbali mwake n’kuikamo manyowa. 9 Ngati udzabala zipatso m’tsogolo zidzakhala bwino. Koma ngati sudzabala mudzaudule.’”
10 Tsopano Yesu anali kuphunzitsa m’sunagoge winawake pa Sabata. 11 Ndiyeno mmenemo munali mayi wina amene anali ndi mzimu umene unali kumufooketsa* kwa zaka 18. Iye anali wopindika kwambili msana, ndipo sanali kuwelamuka ngakhale pang’ono. 12 Yesu atamuona mayiyo analankhula naye n’kumuuza kuti: “Mayinu, mwamasulidwa ku matenda anu.” 13 Ndiyeno anaika manja ake pa mayiyo, ndipo nthawi yomweyo anawelamuka n’kuyamba kutamanda Mulungu. 14 Koma mtsogoleli wa sunagoge ataona izi anakwiya, cifukwa cakuti Yesu anacilitsa munthu pa Sabata. Conco anauza khamu la anthulo kuti: “Pali masiku 6 amene tiyenela kugwila nchito. Cotelo muzibwela kudzacilitsidwa pa masiku amenewo, osati pa tsiku la Sabata ayi.” 15 Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Onyenga inu, kodi aliyense wa inu samasula ng’ombe yake kapena bulu wake m’khola pa Sabata n’kupita naye kukamumwetsela madzi? 16 Kodi mayiyu, amene ndi mwana wamkazi wa Abulahamu, amenenso Satana anamumanga kwa zaka 18, sayenela kumasulidwa m’maunyolo amenewa pa tsiku la Sabata?” 17 Iye atakamba zimenezi, anthu onse omutsutsa anacita manyazi. Koma khamu lonse la anthu linayamba kukondwela cifukwa ca zinthu zodabwitsa zimene iye anacita.
18 Conco anapitiliza kunena kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati ciyani, nanga ndingauyelekezele ndi ciyani? 19 Uli ngati kanjele ka mpilu, kamene munthu anatenga n’kukabyala m’munda wake. Ndiyeno kanakula n’kukhala mtengo, ndipo mbalame za mumlengalenga zinamanga zisa m’nthambi zake.”
20 Iye anakambanso kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu ndingauyelekezele ndi ciyani? 21 Uli ngati zofufumitsa zimene mayi wina anatenga n’kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zikuluzikulu zopimila,* ndipo mtanda wonsewo unafufuma.”
22 Ndiyeno iye anayenda mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi akuphunzitsa, n’kupitiliza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 23 Tsopano munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi amene adzapulumuka ndi ocepa?” Iye anawauza kuti: 24 “Yesetsani mwamphamvu kulowa pa khomo lopanikiza, cifukwa ndikukuuzani kuti ambili adzafuna kulowa koma sadzakwanitsa kutelo. 25 Mwininyumba akadzauka n’kukhoma citsekoco, mudzaimilila panja n’kumagogoda, ndipo mudzakamba kuti ‘Ambuye, titsegulileni.’ Koma iye adzakuyankhani kuti: ‘Sindikudziwani.’ 26 Ndiyeno mudzayamba kukamba kuti, ‘Tinali kudya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munali kuphunzitsa m’misewu yathu ikuluikulu.’ 27 Koma ine ndidzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwani. Cokani pamaso panga nonsenu ocita zosalungama!’ 28 Kumeneko, muzikalila ndi kukukuta mano mukadzaona Abulahamu, Isaki, Yakobo, ndi aneneli onse mu Ufumu wa Mulungu, koma inu mutaponyedwa kunja. 29 Komanso anthu adzabwela kucokela kum’mawa ndi kumadzulo, ndiponso kucokela kumpoto ndi kum’mwela n’kudzakhala pathebulo mu Ufumu wa Mulungu. 30 Ndipo pali othela amene adzakhala oyamba, komanso pali oyamba amene adzakhala othela.”
31 Nthawi yomweyo Afarisi ena anabwela n’kumuuza kuti: “Pitani, cokani kuno, cifukwa Herode akufuna kukuphani.” 32 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe imeneyo kuti, ‘Ndikutulutsa ziwanda ndi kucilitsa anthu lelo komanso mawa, ndipo ndidzatsiliza pa tsiku lacitatu.’ 33 Ngakhale n’telo, ndipitiliza kugwila nchito yanga lelo, mawa, komanso mkuca. Pambuyo pake, ndidzapita ku Yerusalemu, cifukwa n’kosayenela* kuti mneneli amuphele kunja kwa Yerusalemu. 34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneli komanso woponya miyala anthu otumidwa kwa iwe. Mobwelezabweleza ndinafuna kusonkhanitsa pamodzi ana ako, monga mmene nkhuku imasonkhanitsila anapiye ake m’mapiko ake! Koma inu simunafune zimenezo. 35 Tsopano mvelani, Mulungu wakusiyilani nyumba yanu. Ndikukuuzani kuti, simudzandionanso kufikila mutanena kuti: ‘Wodalitsika ndi iye wobwela m’dzina la Yehova!’”