Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
18 Yesu atakamba zimenezi, anatuluka pamodzi ndi ophunzila ake n’kuwoloka cigwa ca Kidironi kupita kumene kunali munda winawake. Ndipo iye pamodzi ndi ophunzila ake analowa m’mundawo. 2 Yudasi womupeleka uja, nayenso anali kudziwako kumalo amenewo, cifukwa nthawi zambili Yesu anali kukumana ndi ophunzila ake kumeneko. 3 Conco Yudasi anabwela ndi gulu la asilikali pamodzi ndi alonda ocokela kwa ansembe aakulu ndi Afarisi. Iwo anabwela atanyamula miyuni, nyale, ndi zida. 4 Ndiye popeza Yesu anali kudziwa zonse zimene zimucitikile, anawayandikila n’kuwafunsa kuti: “Kodi mukufuna ndani?” 5 Iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.” Iye anawauza kuti: “Ndine.” Ndipo Yudasi womupeleka uja anali nawo limodzi.
6 Koma Yesu atawauza kuti, “Ndine,” iwo anabwelela m’mbuyo n’kugwa pansi. 7 Ndiyeno iye anawafunsanso kuti: “Kodi mukufuna ndani?” Iwo anati: “Yesu Mnazareti.” 8 Yesu anayankha kuti: “Ndakuuzani kale kuti ndine. Conco ngati mukufuna ine, alekeni awa azipita.” 9 Izi zinacitika kuti mawu amene iye anakamba akwanilitsidwe, akuti: “Pa anthu amene munandipatsa, sindinatayepo ngakhale mmodzi.”
10 Ndiyeno Simoni Petulo, amene anali ndi lupanga, analisolola n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kumudula khutu la kudzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Makasi. 11 Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bweza lupangalo m’cimake. Kodi sindiyenela kumwa za m’kapu zimene Atate andipatsa?”
12 Kenako asilikaliwo, mkulu wa asilikali, komanso alonda a Ayuda, anagwila Yesu n’kumumanga manja. 13 Iwo coyamba anapita naye kwa Anasi, cifukwa anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe m’cakaco. 14 Kayafa ameneyu ndi amene analangiza Ayudawo kuti zinali zowapindulila kuti munthu mmodzi afele anthu onse.
15 Tsopano Simoni Petulo ndi wophunzila wina anali kulondola Yesu. Wophunzilayo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe uja, ndipo iye pamodzi ndi Yesu analowa m’bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembeyo. 16 Koma Petulo anaimilila pakhomo* panja. Conco wophunzila winayo amene mkulu wa ansembe uja anali kumudziwa, anatuluka n’kukakamba ndi mlonda wapakhomo n’kulowetsa Petulo. 17 Ndiyeno mtsikana wanchito amene anali mlonda pakhomopo anafunsa Petulo kuti: “Kodi inunso sindinu mmodzi wa ophunzila a munthu uyu?” Iye anati: “Ayi sindine.” 18 Ndiyeno atumiki ndi alonda anaimilila akuwotha moto wamalasha umene anayatsa cifukwa kunali kozizila. Nayenso Petulo anaimilila nawo pamodzi akuwotha motowo.
19 Conco wansembe wamkulu anafunsa Yesu za ophunzila ake, komanso zimene iye anali kuphunzitsa. 20 Yesu anayankha kuti: “Ndalankhula poyela ku dzikoli. Nthawi zonse ndinali kuphunzitsa m’masunagoge ndi m’kacisi mmene Ayuda onse anali kusonkhana pamodzi, ndipo ine sindinalankhulepo ciliconse mobisa. 21 Ndiye n’cifukwa ciyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinali kuwauza. Onani! Anthuwa akudziwa zimene ndinanena.” 22 Yesu atakamba izi, mmodzi wa alonda amene anaimilila naye pafupi, anamuwaza mbama kumaso n’kunena kuti: “Kodi umu ndi mmene ungayankhile wansembe wamkulu?” 23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati ndakamba colakwika, peleka* umboni wa colakwikaco. Koma ngati ndakamba zoona, n’cifukwa ciyani wandimenya?” 24 Ndiyeno Anasi anatumiza Yesu kwa Kayafa mkulu wa ansembe atam’manga manja.
25 Tsopano Simoni Petulo anali cilili akuwotha moto pamenepo. Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Kodi inunso si ndinu mmodzi wa ophunzila ake?” Iye anakana ndipo anati: “Ayi si ndine.” 26 Mmodzi wa akapolo a mkulu wa nsembe uja, yemwe anali wacibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu, anati: “Ndinakuona uli naye m’munda muja, ndi bodza?” 27 Petulo anakananso, ndipo nthawi yomweyo tambala analila.
28 Kenako iwo anamutenga Yesu kwa Kayafa n’kupita naye kunyumba kwa bwanamkubwa. Apa kunali m’mamawa kwambili. Koma iwo sanalowe m’nyumba ya bwanamkubwayo poopa kuti angadetsedwe, cifukwa anali kufuna kudya Pasika. 29 Conco Pilato anatuluka panja n’kuwafunsa kuti: “Kodi munthuyu mwamubweletsa kuno pa mlandu wanji?” 30 Iwo anamuyankha kuti: “Munthu uyu akanakhala kuti sanalakwe,* sitikanamubweletsa kwa inu.” 31 Pilato anawauza kuti: “M’tengeni mukamuweluze nokha malinga ndi malamulo anu.” Ayudawo anamuuza kuti: “Ife tilibe ulamulilo wopha munthu aliyense.” 32 Izi zinakwanilitsa mawu amene Yesu anakamba oonetsa mmene adzafele pakangopita nthawi yocepa.
33 Conco Pilato analowanso m’nyumba ya bwanamkubwayo, ndipo anaitana Yesu n’kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” 34 Yesu anayankha kuti: “Kodi mukufunsa zimenezi cifukwa mwangoganiza nokha, kapena cifukwa cakuti ena akuuzani za ine?” 35 Pilato anayankha kuti: “Ine sindine Myuda. Anthu a mtundu wako komanso ansembe aakulu ndiwo akupeleka kwa ine. Kodi unacita ciyani?” 36 Yesu anayankha kuti: “Ufumu wanga si wa m’dzikoli. Ufumu wanga ukanakhala wa m’dzikoli, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisapelekedwe kwa Ayuda. Koma mmene zililimu, Ufumu wanga si wocokela m’dzikoli.” 37 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Cabwino, ndiye kodi ndiwe mfumu?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu. Ici n’cimene ndinabadwila komanso n’cimene ndinabwelela m’dziko, kuti ndidzacitile umboni coonadi. Aliyense amene ali kumbali ya coonadi amamvela mawu anga.” 38 Pilato anamufunsa kuti: “Kodi coonadi n’ciyani?”
Atakamba zimenezi, anatulukanso panja n’kupita kwa Ayuda, ndipo anawauza kuti: “Munthu uyu sindikum’peza ndi mlandu uliwonse. 39 Paja inu mumafuna kuti nthawi zonse pacikondwelelo ca Pasika ndizikumasulilani munthu mmodzi. Ndiye kodi mufuna ndikumasulileni Mfumu ya Ayuda?” 40 Iwo anafuulanso kuti: “Osati munthu uyu, koma Baraba!” Barabayo anali wacifwamba.