Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
17 Kenako Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Zopangitsa munthu kupunthwa zidzabwela ndithu, ndipo n’zosapeweka. Koma tsoka kwa munthu wobweletsa zopunthwitsazo! 2 Zingakhale bwino kum’mangilila cimwala camphelo m’khosi ndi kumuponya m’nyanja kuposa kuti apunthwitse mmodzi wa ana aang’ono awa. 3 Khalani osamala. Ngati m’bale wako wakucimwila mudzudzule, ndipo ngati walapa mukhululukile. 4 Ngakhale atakucimwila maulendo 7 patsiku, ndipo wabwela kwa iwe maulendo 7 n’kunena kuti, ‘Ndalapa,’ uyenela kumukhululukila.”
5 Tsopano atumwi anauza Ambuye kuti: “Tiwonjezeleni cikhulupililo.” 6 Ndiyeno Ambuye anati: “Mukanakhala ndi cikhulupililo ngakhale cocepa ngati kanjele ka mpilu, mukanatha kuuza mtengo wa malubeni uwu kuti, ‘Zuka apa ukadzibyale m’nyanja!’ ndipo ukanakumvelani.
7 “Ndani wa inu amene kapolo wake atangofika kumene kucokela kumunda kukalima ndi pulawo, kapena atacokela kuchile kukawetela nkhosa, angamuuze kuti, ‘Fulumila bwela kuno udzadye pathebulo’? 8 Kodi sangamuuze kuti, ‘Ndikonzele cakudya camadzulo, uvale epuloni ndi kuyamba kunditumikila mpaka n’tatsiliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso ungadye ndi kumwa’? 9 Ndipo iye sangamuyamikile kapolo wakeyo, cifukwa zimene wacitazo ndi nchito yake, si conco? 10 Mofanana ndi izi, mukacita zonse zimene munauzidwa kucita, muzinena kuti: ‘Ndife akapolo opanda pake, tangocita zimene tinayenela kucita.’”
11 Pamene iye anali kupita ku Yerusalemu, anadutsa m’malile a Samariya ndi Galileya. 12 Ndipo pamene anali kulowa m’mudzi winawake, amuna 10 akhate anakumana naye, koma iwo anaimilila capatali. 13 Amunawo anafuula kuti: “Yesu, Mlangizi, ticitileni cifundo!” 14 Yesu atawaona anawauza kuti: “Pitani mukadzionetse kwa ansembe.” Ndiyeno pamene iwo anali kupita anayeletsedwa. 15 Mmodzi wa iwo ataona kuti wacilitsidwa, anabwelela akutamanda Mulungu mokweza mawu. 16 Iye anagwada mpaka nkhope yake pansi kumapazi a Yesu, n’kumuyamikila. Munthu ameneyu anali Msamariya. 17 Yesu anakamba kuti: “Anthu onse 10 ayeletsedwa, nanga ena 9 aja ali kuti? 18 Kodi palibenso wina amene wabwelela kudzatamanda Mulungu kupatulapo munthu wa mtundu winayu?” 19 Yesu anauza munthuyo kuti: “Nyamuka uzipita, cikhulupililo cako cakucilitsa.”
20 Afarisi atafunsa Yesu kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela liti, iye anawayankha kuti: “Sikuti Ufumu wa Mulungu udzabwela ndi maonekedwe ocititsa cidwi ayi. 21 Ndipo anthu sadzanena kuti, ‘Onani uli kuno!’ kapena, ‘Uli uko!’ Pakuti Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”
22 Kenako Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Masiku adzabwela pamene mudzalakalaka kuona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa munthu, koma simudzaliona. 23 Ndipo anthu adzakuuzani kuti, ‘Onani ali uko!’ kapena, ‘Onani ali kuno!’ Musakapiteko kapena kuwatsatila. 24 Cifukwa monga mmene mphenzi imang’animila kucokela kumbali ina ya thambo kufika kumbali ina ya thambo, ndi mmenenso zidzakhalile m’tsiku la Mwana wa munthu. 25 Koma coyamba iye ayenela kukumana ndi masautso ambili, ndipo m’badwo uwu udzamukana. 26 Komanso, monga mmene zinacitikila m’masiku a Nowa, ndi mmenenso zidzakhalile m’masiku a Mwana wa munthu. 27 Anthu anali kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatila, ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analowa m’cingalawa. Ndipo Cigumula cinabwela n’kuwawononga onsewo. 28 Ndi mmenenso zinalili m’masiku a Loti. Anthu anali kudya ndi kumwa, anali kugula ndi kugulitsa, anali kubyala, komanso kumanga. 29 Koma pa tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule n’kuwawononga onsewo. 30 Ndi mmenenso zidzakhalile patsikulo Mwana wa munthu akadzaonekela.
31 “Patsikulo, munthu amene adzakhale pa mtenje koma katundu wake uli m’nyumba asadzatsike kukautenga. Cimodzimodzinso munthu amene adzakhale ku munda, asadzabwelele ku zinthu zimene wasiya kumbuyo. 32 Kumbukilani mkazi wa Loti. 33 Aliyense wofunitsitsa kuteteza moyo wake adzautaya, koma aliyense woutaya adzausunga. 34 Ndithu ndikukuuzani, anthu awili adzakhala akugona pabedi imodzi, wina adzatengedwa koma wina adzasiyidwa. 35 Akazi awili adzakhala akupela pamphelo imodzi, wina adzatengedwa koma wina adzasiyidwa.” 36* —— 37 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi zimenezi zidzacitikila kuti?” Iye anawauza kuti: “Kumene kuli thupi lakufa, nazonso ziwombankhanga zidzasonkhana kumeneko.”