Kwa Aroma
4 Popeza zili telo, kodi tingakambe ciyani za kholo lathu Abulahamu? 2 Mwacitsanzo, ngati Abulahamu anaonedwa kuti ndi wolungama cifukwa ca zimene anacita, akanakhala ndi cifukwa codzitamandila, koma osati pamaso pa Mulungu. 3 Kodi paja Malemba amati ciyani? Amati: “Abulahamu anakhulupilila mwa Yehova, ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama.” 4 Munthu amene wagwila nchito, saona malipilo ake ngati cisomo, koma ngati cinthu cimene ayenela kulandila.* 5 Koma Mulungu amene amaona anthu ocimwa kukhala olungama amaona kuti munthu yemwe sanagwile nchito, koma amamukhulupilila, ndi wolungama. 6 Davide anakamba za munthu wacimwemwe amene Mulungu amamuona kuti ndi wolungama ngakhale kuti zimene wacita sizikugwilizana kwenikweni ndi Cilamulo. Iye anakamba kuti. 7 “Acimwemwe ndi anthu amene akhululukidwa zocita zawo zophwanya malamulo, ndipo macimo awo akhululukidwa.* 8 Wacimwemwe ndi munthu amene Yehova sadzamuwelengela chimo lake.”
9 Kodi ndi anthu odulidwa cabe amene amakhala acimwemwe? Kapena osadulidwa nawonso amakhala acimwemwe? Paja timati: “Abulahamu anaonedwa wolungama cifukwa ca cikhulupililo cake.” 10 Ndiye kodi iye anaonedwa wolungama ali mu mkhalidwe wotani? Ali wodulidwa kapena wosadulidwa? Iye anali asanadulidwe. 11 Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe ngati cizindikilo cotsimikizila kuti iye anamuona kuti ndi wolungama asanadulidwe cifukwa ca cikhulupililo cake. Anacita zimenezi kuti adzakhale tate wa onse osadulidwa amene ali ndi cikhulupililo kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama. 12 Kuti adzakhalenso tate wa ana odulidwa, osati kwa odulidwa okha ayi, komanso wa amene amayenda moyenela potsatila cikhulupililo cimene tate wathu Abulahamu anali naco asanadulidwe.
13 Cifukwa Abulahamu kapena mbadwa* zake sanalonjezedwe kuti adzalandila dziko monga colowa cawo cifukwa ca Cilamulo ayi. Koma analonjezedwa cifukwa anali ndi cikhulupililo, ndipo Mulungu anamuona kuti ndi wolungama. 14 Pakuti ngati anthu amene akutsatilabe Cilamulo ndi amene adzalandile colowaco, ndiye kuti cikhulupililo cilibenso nchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa. 15 Zoona zake n’zakuti, kuphwanya Cilamulo kumacititsa kuti munthu alandile cilango, koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.
16 N’cifukwa cake iye anapatsidwa lonjezolo cifukwa ca cikhulupililo, kuti likhale logwilizana ndi cisomo. Komanso anapatsidwa lonjezolo kuti likhale lotsimikizika kwa anthu onse amene ndi mbadwa* zake, osati otsatila Cilamulo okha, koma kuphatikizapo otsatila cikhulupililo ca Abulahamu amene ndi tate wa tonsefe. 17 (Izi n’zogwilizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Ndakusankha kuti ukhale tate wa mitundu yambili.”) Zinali conco pamaso pa Mulungu amene Abulahamu anali kukhulupilila, amenenso amaukitsa akufa ndipo amachula zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.* 18 Abulahamu anali ndi ciyembekezo ndiponso cikhulupililo cakuti adzakhala tate wa mitundu yambili, ngakhale kuti zimenezi zinali kuoneka kuti n’zosatheka. Anakhulupilila izi mogwilizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalile.” 19 Ndipo ngakhale kuti cikhulupililo cake sicinafooke, pa nthawiyo anali kuona thupi lake ngati lakufa (cifukwa anali ndi zaka pafupifupi 100). Anali kudziwanso kuti Sara ndi wokalamba kwambili moti sangabeleke. 20 Koma cifukwa ca lonjezo la Mulungu, iye sanagwedezeke pa cikhulupililo, koma anakhala wamphamvu mwa cikhulupililo, ndipo anapeleka ulemelelo kwa Mulungu. 21 Iye sanakayikile ngakhale pang’ono kuti zimene Mulungu anamulonjeza angathenso kuzicita. 22 Conco, “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama.”
23 Komabe, mawu akuti “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama” sanalembedwele iye cabe. 24 Analembelanso ife, amene timaonedwanso olungama cifukwa timakhulupilila Mulungu amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu. 25 Yesu anapelekedwa kaamba ka macimo athu, ndipo anaukitsidwa kuti tionedwe olungama.