Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
18 Kenako Yesu anawauzanso fanizo lowaonetsa kuti iwo ayenela kupemphela nthawi zonse, komanso kuti asamataye mtima. 2 Iye anati: “Mumzinda winawake munali woweluza wina amene sanali kuopa Mulungu, ndipo sanali kusamala za munthu. 3 Mumzindawo munalinso mkazi wamasiye amene mobwelezabweleza anali kupita kwa iye kukamupempha kuti, ‘Weluzani mlandu umene ulipo pakati pa ine ndi munthu amene ndikutsutsana naye kuti pacitike cilungamo.’ 4 Kwakanthawi, woweluzayo sanali kufuna kuiweluza nkhaniyo, koma pambuyo pake anati mumtima mwake, ‘Ngakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu aliyense, 5 ndidzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa mkazi wamasiyeyu, cifukwa iye sakuleka kundivutitsa. Conco kuti aleke kubwela n’kumanditopetsa,* ndidzacita zimene akupempha.’” 6 Ndiyeno Ambuye anati: “Mwamva, izi n’zimene woweluzayo ananena, ngakhale kuti ndi wosalungama! 7 Ndiye kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa anthu ake osankhidwa, amene amamulilila usana ndi usiku pamene akuwalezela mtima? 8 Ndithu ndikukuuzani, iye adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa iwo mwamsanga. Ngakhale n’telo, kodi Mwana wa munthu akadzabwela adzapezadi cikhulupililo ngati cimeneci* padziko lapansi?”
9 Yesu anafotokozanso fanizo lotsatilali kwa ena amene anali kudzidalila kuti ndi olungama, komanso amene anali kuona ena kuti ndi opanda pake. Iye anati: 10 “Amuna awili anapita ku kacisi kukapemphela. Mmodzi anali Mfarisi ndipo winayo anali wokhometsa misonkho. 11 Mfarisi uja anaimilila n’kuyamba kupemphela camumtima kuti, ‘Mulungu wanga, ndikuyamikilani kuti ine sindili monga ena onsewa, amene ndi olanda, opanda cilungamo, komanso acigololo. Ndiponso sindili ngati uyu wokhometsa misonkho. 12 Ndimasala kudya kawili pa mlungu, ndipo ndimapeleka cakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’ 13 Koma wokhometsa misonkho uja anaimilila capatali, ndipo sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Koma anali kungodziguguda pacifuwa n’kumanena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomeleni mtima* ine munthu wocimwa.’ 14 Ndithu ndikukuuzani, munthu ameneyu atapita kunyumba kwake anaonedwa wolungama kwambili kuposa Mfarisi uja. Conco aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa.”
15 Tsopano anthu analinso kumubweletsela ana aang’ono kuti awaike manja. Koma ophunzila ake ataona izi anayamba kuwakalipila. 16 Komabe, Yesu anaitana anawo n’kukamba kuti: “Alekeni anawo abwele kwa ine, musawaletse, cifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa. 17 Ndithu ndikukuuzani kuti, aliyense wosalandila Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowamo n’komwe mu Ufumuwo.”
18 Ndiyeno mmodzi wa olamulila anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, kodi ndiyenela kucita ciyani kuti ndikapeze moyo wosatha?” 19 Yesu anamuyankha kuti: “N’cifukwa ciyani ukundichula kuti wabwino? Palibe aliyense wabwino koma Mulungu yekha. 20 Iwe umawadziwa malamulo akuti: ‘Usacite cigololo, usaphe munthu, usabe, usapeleke umboni wonama, ndiponso lakuti uzilemekeza atate ako ndi amayi ako.’” 21 Munthuyo anayankha kuti: “Ndakhala ndikutsatila malamulo onsewa kuyambila ndili mwana.” 22 Yesu atamva zimenezi anamuuza kuti, “Pali cinthu cimodzi cimene cikusowekabe mwa iwe: Kagulitse zinthu zonse zimene uli nazo, ndipo ndalama zake ukazigawile osauka. Ukatelo udzakhala ndi cuma kumwamba. Kenako ubwele udzakhale wotsatila wanga.” 23 Atamva zimenezi, anamva cisoni kwambili cifukwa anali wolemela kwambili.
24 Yesu anamuyang’ana ndipo ananena kuti: “Cidzakhala covuta kwambili kuti anthu a ndalama akalowe mu Ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, n’capafupi ngamila kulowa pa diso la singano, kusiyana n’kuti munthu wolemela akalowe mu Ufumu wa Mulungu.” 26 Amene anamva zimenezi anafunsa kuti: “Ndiye pali amene angadzapulumuke ngati?” 27 Iye anayankha kuti: “Zinthu zosatheka kwa anthu n’zotheka kwa Mulungu.” 28 Koma Petulo anati: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu n’kukutsatilani.” 29 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe aliyense amene wasiya nyumba, mkazi, abale, makolo, kapena ana cifukwa ca Ufumu wa Mulungu, 30 amene sadzapeza zoculuka kwambili m’nthawi ino, ndipo m’nthawi imene ikubwelayo* adzapeza moyo wosatha.”
31 Ndiyeno iye anatengela pambali ophunzila ake 12 aja n’kuwauza kuti: “Tsopano tikupita ku Yerusalemu, ndipo zinthu zonse zimene zinalembedwa kupitila mwa aneneli zokhudza Mwana wa munthu zidzakwanilitsidwa. 32 Mwacitsanzo, iye adzapelekedwa kwa anthu a mitundu ina ndi kucitidwa zacipongwe, ndipo adzamunyoza ndi kumuthila mata. 33 Pambuyo pomukwapula, adzamupha, koma patsiku lacitatu adzaukitsidwa.” 34 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la zinthu zonsezi, cifukwa mawu amenewa anali obisika kwa iwo, ndipo sanamvetse zimene iye anakamba.
35 Tsopano pamene Yesu anali kuyandikila ku Yeriko, munthu wina wakhungu anali khale m’mbali mwa msewu akupemphapempha. 36 Munthuyo atamva khamu la anthu likudutsa, anayamba kufunsa kuti adziwe zimene zinali kucitika. 37 Anthuwo anamuuza kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!” 38 Pamenepo munthuyo anafuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, ndicitileni cifundo!” 39 Ndiyeno anthu amene anali patsogolo anayamba kumudzudzula kuti akhale cete, koma m’pamene iye anakuwa kwambili, amvekele: “Mwana wa Davide, ndicitileni cifundo!” 40 Conco Yesu anaima n’kulamula kuti munthuyo amubweletse kwa iye. Atafika pafupi, Yesu anamufunsa kuti: 41 “Ufuna ndikucitile ciyani?” Iye anati: “Ambuye, ndithandizeni ndiyambe kuona.” 42 Yesu anamuuza kuti: “Yamba kuona, cikhulupililo cako cakucilitsa.” 43 Nthawi yomweyo munthuyo anayamba kuona, ndipo anayamba kutsatila Yesu akutamanda Mulungu. Komanso anthu onse ataona izi, anatamanda Mulungu.