Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
7 Yesu atatsiliza kukamba zimene anali kufuna kuuza anthu, analowa mu mzinda wa Kaperenao. 2 Tsopano kapitawo wa asilikali anali ndi kapolo amene anali kum’konda kwambili. Kapoloyo anadwala kwambili, ndipo anali atatsala pang’ono kumwalila. 3 Kapitawoyo atamva za Yesu, anatumiza akulu a Ayuda kuti akamupemphe kuti abwele kudzacilitsa kapolo wakeyo. 4 Iwo anafika kwa Yesu n’kuyamba kumucondelela ndi mtima wonse kuti: “Munthu ameneyu ndi woyeneladi kum’citila zimenezi, 5 cifukwa amatikonda ife Ayuda, ndipo ndiye anatimangila ngakhale sunagoge wathu.” 6 Conco Yesu anapita nawo limodzi. Koma atatsala pang’ono kufika pa nyumba, kapitawo wa asilikali uja anali atatuma kale anzake kuti akauze Yesu kuti: “Bambo, musavutike kudzalowa m’nyumba mwanga, ine sindine woyenelela kuti inu mudzalowe m’nyumba mwanga. 7 N’cifukwa cake ndaona kuti sindine woyenela kubwela kwa inu. Conco mungokamba mawu kuti wanchito wanga acile. 8 Pakuti inenso ndili ndi akuluakulu amene amandilamulila, ndipo ndili ndi asilikali amene ndimawalamulila. Ndikauza uyu kuti, ‘Pita!’ amapita. Ndikauza wina kuti, ‘Bwela!’ amabwela, ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Cita ici!’ amacita.” 9 Yesu atamva zimenezi anadabwa naye kwambili munthuyo, ndipo anatembenuka n’kuuza khamu la anthu limene linali kumutsatila kuti: “Kukuuzani zoona, ngakhale mu Isiraeli sindinapezemo munthu wa cikhulupililo cacikulu ngati ici.” 10 Amene anatumidwawo atabwelela kunyumba kwa kapitawo wa asilikaliyo, anapeza kuti kapolo uja wacila.
11 Posapita nthawi, iye ananyamuka n’kupita ku mzinda wochedwa Naini, ndipo ophunzila ake pamodzi ndi khamu lalikulu la anthu anali kuyenda naye limodzi. 12 Atatsala pang’ono kufika pa geti ya mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula malilo. Amene anamwalilayo anali mwana wamwamuna mmodzi yekhayo wa mayi amenenso anali wamasiye. Ndipo gulu lalikulu ndithu la anthu ocokela mu mzindawo linali naye. 13 Ambuye atamuona mayiyo, anamumvela cisoni ndipo anamuuza kuti: “Usalile.” 14 Atatelo, anafika pafupi n’kugwila macila, ndipo onyamula mtembowo anaima. Kenako Yesu anati: “Mnyamatawe, ndikukuuza kuti, uka!” 15 Munthu wakufayo anakhala tsonga n’kuyamba kulankhula, ndipo Yesu anamupeleka kwa mayi ake. 16 Ndiyeno anthu onsewo anagwidwa ndi mantha, ndipo anayamba kutamanda Mulungu, amvekele: “Mneneli wamkulu waonekela pakati pathu,” ndipo anali kunenanso kuti, “Mulungu wakumbukila anthu ake.” 17 Mbili yokhudza iye inafalikila mu Yudeya monse komanso m’madela onse ozungulila.
18 Tsopano ophunzila a Yohane anamufotokozela zinthu zonsezi Yohaneyo. 19 Conco Yohane anaitana awili mwa ophunzila ake, ndipo anawatuma kwa Ambuye kukafunsa kuti: “Kodi Mesiya uja amene tikumuyembekezela ndinu, kapena tiyembekezelebe wina?” 20 Amunawo atafika kwa iye, anamuuza kuti: “Yohane M’batizi watituma kuti tidzakufunseni kuti, ‘Kodi Mesiya uja amene tikumuyembekezela ndinu, kapena tiyembekezelebe wina?’” 21 Nthawi imeneyo Yesu anacilitsa anthu ambili odwala matenda aang’ono komanso aakulu. Ndipo anatulutsa mizimu yonyansa ndi kuthandiza anthu ambili akhungu kuyamba kuona. 22 Poyankha iye anawauza kuti: “Pitani mukamuuze Yohane zimene mwaona ndi kumva: Tsopano akhungu akuona, olemala akuyenda, akhate akuyeletsedwa, ogontha akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino. 23 Wacimwemwe ndi munthu amene sapeza copunthwitsa mwa ine.”
24 Ophunzila a Yohane atapita, Yesu anayamba kulankhula ndi khamu la anthulo za Yohane kuti: “Kodi munapita ku cipululu kukaona ciyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo? 25 Nanga munapita kukaona ciyani? Munthu wovala zovala zapamwamba?* Iyai, anthu ovala zovala zabwino kwambili komanso okhala umoyo wawofuwofu amapezeka m’nyumba za mafumu. 26 Ndiye munapita kukacita ciyani kumeneko? Kukaona mneneli? Inde, ndikukuuzani kuti iye amaposanso aneneli. 27 Uyu ndi amene Malemba amati za iye: ‘Taona! Ndikutumiza mthenga wanga patsogolo pako,* amene adzakukonzela njila.’ 28 Ndikukuuzani kuti, pa anthu onse obadwa kwa akazi, palibe aliyense wamkulu kuposa Yohane. Koma wocepelapo mu Ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.” 29 (Pamene anthu onse ndi okhometsa misonkho anamva zimenezi, anavomeleza kuti Mulungu ndi wolungama, popeza onsewo anabatizidwa ndi ubatizo wa Yohane. 30 Koma Afarisi ndi anthu odziwa bwino Cilamulo ananyalanyaza uphungu* umene Mulungu anawapatsa, cifukwa sanabatizidwe ndi Yohane.)
31 “Ndiye kodi amuna a m’badwo uwu ndiwayelekezele ndi ndani? Nanga kodi afanana ndi ndani? 32 Ali ngati ana aang’ono opezeka m’misika, amene akuitanana kuti: ‘Tinakuimbilani citolilo, koma inu simunavine ayi. Tinalila mokweza, koma inu simunalile ayi.’ 33 Mofananamo, Yohane M’batizi anabwela ndipo sakudya mkate kapena kumwa vinyo, koma inu mukumunena kuti: ‘Iye ali ndi ciwanda.’ 34 Mwana wa munthu wabwela, ndipo amadya ndi kumwa, koma inu mumati: ‘Taonani! Munthu wosusuka komanso wokondetsetsa kumwa vinyo, bwenzi la okhometsa misonkho ndi ocimwa!’ 35 Mulimonsemo, nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama mwa zotulukapo zake.”*
36 Tsopano mmodzi wa Afarisi anali kumucondelela kuti akadye naye. Conco Yesu analowa m’nyumba ya Mfarisiyo, ndipo anadya naye pa thebulo. 37 Ndipo mayi wina amene anali kudziwika kuti ndi wocimwa mu mzindamo, anadziwa kuti Yesu akudya cakudya* m’nyumba ya Mfarisiyo. Conco iye anabweletsa botolo lamwala wa alabasitala, mmene munali mafuta onunkhila. 38 Mayiyo anagwada pa mapazi ake n’kuyamba kulila, ndipo ananyowetsa mapazi a Yesu ndi misozi yake. Kenako anawapukuta ndi tsitsi lake. Komanso anapsompsona mapazi ake ndi kuwathila mafuta onunkhila. 39 Mfarisi amene anamuitanayo ataona zimenezo, anati mumtima mwake: “Munthuyu akanakhaladi mneneli, akanadziwa kuti mayiyu ndi munthu wotani. Akanadziwa kuti ndi wocimwa.” 40 Koma Yesu anamuuza kuti: “Simoni, ndifuna ndikuuze zinazake.” Iye anati: “Mphunzitsi, ndiuzeni!”
41 “Amuna awili anali ndi nkhongole kwa munthu wokongoza ndalama. Mmodzi anali ndi nkhongole yokwana madinari 500, koma winayo madinari 50. 42 Iwo atasowa comubwezela, wowakongozayo anawakhululukila onse awili ndi mtima wonse. Pa awiliwo, ndani adzakonda kwambili wowakongozayo?” 43 Simoni anayankha kuti: “Ndiona kuti ndi uja amene anali ndi nkhongole yaikulu.” Yesu anamuuza kuti: “Wayankha bwino.” 44 Pamenepo Yesu anayang’ana mayiyo n’kuuza Simoni kuti: “Wamuona mayiyu? Ndalowa m’nyumba mwako, koma iwe sunandipatse madzi osambikila mapazi anga. Koma mayiyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake n’kuwapukuta ndi tsitsi lake. 45 Iwe sunandipsompsone. Koma mayiyu, kucokela pomwe ndalowa muno, sanaleke kupsompsona mapazi anga mwacikondi. 46 Iwe sunathile mafuta pamutu panga, koma mayiyu wathila mapazi anga mafuta onunkhila. 47 Pa cifukwa cimeneci, ndikukuuza kuti ngakhale kuti macimo ake ndi ambili,* iye wakhululukidwa cifukwa waonetsa cikondi cacikulu. Koma amene wakhululukidwa zocepa, amaonetsa cikondi cocepa.” 48 Kenako anamuuza kuti: “Macimo ako akhululukidwa.” 49 Anthu amene anali kudya naye pa thebulopo anayamba kufunsana kuti: “Munthu ameneyu ndani kodi, amene amatha ngakhale kukhululukila macimo?” 50 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Cikhulupililo cako cakupulumutsa, pita mu mtendele.”